Chisindikizo Chachiwiri.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Wokwera kavalo wofiira.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachiwiri.Ndipo tsopano, usiku uno, ife tikuwerenga Chisindikizo Chachiwiri ichi. Ndipo kwa Zisindikizo zoyamba zinayi pali okwera pa kavalo anai. Ndipo ine ndikukuwuzani inu, lero chinachake chinachitika kachiwiri. Ndipo, ine, chinachake chimene ine... ine ndinapita ndi kukatenga zolemba zakale zomwe ine ndinali nazo, zomwe ine ndinalankhulapo, kale kale, ndipo ndinangokhala pansi pamenepo. Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, ine ndinachita chopambana chimene ine ndikanakhoza.” Ndipo olemba ambiri ndi zinthu, ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, ine ndiwerenga kanthawi pang'ono, ndi kuyang'ananso ndi kuwona izi ndi izo.” Ndipo chinthu choyamba inu mukudziwa, chinachake chikungochitika, ndipo ziri palimodzi zosiyana. Izo zimangobwera mosiyana. Ndiye ine ndinatenga pensulo mofulumira pomwepo, ndi kuyamba kulemba mwansanga basi monga ine ndingathere, pamene Iye ali pamenepo.
-----
Tsopano, usiku wathawu monga mmene ife nthawi zonse timakondera mu kuphunzitsa pa zisindikizo, ife timaphunzitsa izo mwanjira yomweyo inu mumachitira pa- pa- mibadwo ya mpingo. Ndipo pamene ife tinatsiriza kuphunzitsa m'badwo wa mpingo, nthawi yotsiriza pamene ine ndinayijambula iyo apa pa- pa guwa, pa bolodi, ndi angati akukumbukira chimene chinachitika? Iye anabwera pomwepo, anapita mpaka kumbuyo pa khoma, mu Kuwala, ndipo anazijambula izo, Iye mwini, pomwepo apo pa khoma, pamaso pa ife tonse. Mngelo wa Ambuye anayima pomwepa apa pamaso pa anthu mazana angapo. Ndipo tsopano Iye ali Iye ali kuchita chinachake chauzimu kwenikweni tsopano, naponso, ndipo kotero ife tikungoyembekezera zinthu zazikulu. Ife sitikudziwa. Inu mukufuna kungoyembekezera izokuyembekezera kwakukulu uko, sindikudziwa chabe chimene chiti chichitike kenako, inu mukudziwa, chabe kumangoyembekezera.Tsopano, ali wamkulu bwanji Mulungu kwa ife, ndipo ndi wodabwitsa bwanji! Ife kotero tikumuyamikira Iye! Tsopano, ndime yoyamba ndi ya chiwiri... ine ndiwerenga Izo, kukhala ngati kuyika maziko pang'ono. Ndiyeno ife tidzatenga ndime ya 3 ndi ya 4, kwa Chisindikizo Chachiwiri. Ndiyeno ndime ya 5 ndi ya 6 ziri Chisindikizo Chachitatu. Ndipo ya 7 ndi ya 8 ziri.... ndime ziwiri kwa aliyense wokwera pa kavalo.
Ndipo tsopano ine ndikufuna inu mupenye momwe anyamata awa. Pa kavalo wotumbululuka uyu, mwina. Apa iye akubwera, akungomasintha pamene iye akupita mmusi. Ndiyeno chopambana icho, Chisindikizo chotsiriza kuti chitsegulidwe, ngati Mulungu alola, Lamlungu likudzali usiku! Icho, pamene icho chinachitika, uko kunali chabe, chinthu chokhacho chimene chinachitika, kunali chete Kumwamba kwa theka la ora. Mulungu atithandize ife. Tsopano ine ndiwerenga ndime ya 3 tsopano.
Ndipo pamene iye anatsegula chisindikizo chachiwiri, ine ndinamva chamoyo chachiwiri nichinena, Bwera ndipo dzawone. Ndipo apo anatuluka kavalo wina (ndime ya 4)... amene anali wofiira: ndipo mphamvu inapatsidwa kwa iye amene anakhala pamenepo kukachotsa mtendere pa dziko lapansi, kuti iwo aziphana wina ndi mzake. iwo aziphana wina ndi mzake: ndipo apo kunapatsidwa kwa iye lupanga lalikulu.
Tsopano, chinthu chachinsinsi tsopano, pamene Chamoyo chinamuwuza Yohane, “Ingobwera ndipo dzawone.” Ndipo iye sanawone chimene icho chinali. Iye anangowona chophiphiritsa. Ndipo chophiphiritsa icho, chifukwa chake icho.... Iye anati, “Bwera, dzawone,” koma iye anawona chophiphiritsa, chimene iye amakaphiphiritsira icho kwa mpingo, mwa njira yakuti iwo akanadzayang'ana; mpaka icho chitadza ku m'badwo wotsiriza, ndiyeno Chisindikizo chikanadzatsegulidwa. Tsopano, aliyense akumvetsa izo tsopano, mukuwona, Zisindikizo zikanadzatsegulidwa.
Kodi inu simuli okondwa kuti mukukhala mu tsiku ili? Icho, onani, si chokhacho, amzanga, koma nthawizonse kumbukirani tsopano, Lamlungu lapita mmawa, pamene chinthu chonse chinakhazikitsidwira pa, kuphweka! Mwaona? Kuphweka, kudzichepetsa, zimachitika mwanjira iyo mwakuti anthu amapita basi cha pomwepo ndipo osadziwa nkomwe kuti Izo zikuchitika. Ndipo, kumbukirani, ife tikuyang'anira Kudza kwa Ambuye, nthawi iliyonse. Ndipo pamene ife.Ine ndinapanga chiganizo, kuti ine mwina Mkwatulo udzakhala mwanjira yomweyo. Udzakhala utapita, zitatha, ndipo palibe amene adzaziwe kanthu za icho. Udzangobwera monga choncho.
Kawirikawiri mungobwererabe kupyola mu Baibulo ndi kuyang'ana momwe izi zimachitikira chotero. Ngakhale monga chinthu chopambana monga Ambuye Yesu kubwera, palibe amene anadziwa kanthu za icho. “Iwo ankaganiza kuti chidempete chija, wina wake.” Mipingo inkati, “Wotentheka chabe. Iye ali wopenga kwambiri.” Anati, “Iye ndi munthu wamisala. Ife tikudziwa kuti Iwe uli wamisala. Misala imatanthawuza kupenga. Ife tikudziwa kuti Iwe uli ndi mdierekezi, ndipo iye wakupengetsa Iwe. Ndipo Iwe ukuyesera kutiphunzitsa ife? Pamene, Iwe unabadwa kunja uko, mwapathengo. Ife. Iwe unabadwa mwa chiwerewere. Kuyesa kuphunzitsa anthu monga ife, ansembe, ndi zina zotero, kachisi?” Chabwino, maine, icho chinali chonyoza kwa iwo.
Pamene Yohane anabwera, zinali zitanenedwa, kutsika kupyola mmibadwo, kuchokera kwa Yesaya mpaka Malaki. Ndizo mazana khumi ndi awiri.kapena zaka mazana asanu ndi awiri mphambu khumi ndi ziwiri, iye anali atawonedwa ndi aneneri, akubwera. Aliyense anali akumuyembekezera iye kuti abwere, ankayembekezera icho nthawi iliyonse. Koma njira yomwe iye anabwerera, iye analalikira ndipo anachita ntchito yake, ndipo anapita mpaka mu Ulemerero. Ndipo ngakhale atumwi sanadziwe izo, pakuti iwo anamufunsa Iye. Iwo anati, “Tsopano, ngati-ngati Mwana wa munthu akupita ku Yerusalemu, zinthu zonse izi, kuti akaperekedwe,” anati, “chifukwa chiyani Lemba likunena kuti 'Eliya abwera poyamba'?”
Yesu anati, “Iye wabwera kale, ndipo inu simunadziwe izo. Ndipo iye anachita basi chimodzimodzi chimene Lemba linati iye akanadzachita. Ndipo iwo anachita kwa iye basi zimene zinalembedwa.” Mwaona? Ndipo iwo sankakhoza kumvetsa izo. Iye anati, “Iye anali Yohane.”
Ndiye, “O!” Onani, iwo anadzuka, kwa izo. Ngakhale, potsiriza, zitatha zinthu zonse Iye-Iye anali atazichita, ndi zizindikiro zomwe Iye anawasonyeza iwo, ndipo iye anali ngakhale atawayitana iwo. Anati, “Ndani mmodzi wa inu angakhoze kunditsutsa Ine za tchimo, kusakhulupirira? Ngati ine sindinachite basi zomwe Lemba linati udindo Wanga ukanadzachita pamene Ine ndibwera ku dziko lapansi, ndiye mundisonyeze Ine pamene ndinachimwa. Mwaona? Ndiye Ine ndidza- Ine ndidzakusonyezani inu chimene inu mukuyenera kukhala, ndipo tiyeni tiwone ngati inu mukukhulupirira izo, kapena ayi.” Mwaona? Iye akanakhoza kubwereranso mmbuyo ndi kuti, “Inu mumayenera kukhulupirira pa Ine pamene ine ndadza.” Iwo sanachite izo, mukuwona, kotero iwo anadziwa bwino kuposa kumangiriza pa Iye, pa izo. Koma Iye anati, “Ndani mmodzi wa inu angakhoze kunditsutsa Ine za kusakhulupirira? Kodi Ine sindinachite basi chimene izo zinali?”
-----
Tsopano, iye poyamba ankatchedwa wotsutsakhristu, siteji yachiwiri, iye ankatchedwa mneneri wabodza, chifukwa mzimu umenewo pakati pa anthu unadzakhala mu thupi. Inu mukukumbukira, wokwera pakavalo woyera tsopano analibe korona pamene iye anayamba, koma ndiye iye adzakhoza.anapatsidwa korona. Chifukwa? Iye anali mzimu Wachinikolai, kuyamba ndi kuyamba; ndiyeno iye anadzakhala mu thupi mwa munthu; ndiyeno iye anavekedwa korona, ndi kulandira mpandowachifumu ndipo anavekedwa korona.Ndiyeno iye anatumikira chimenecho kwa nthawi yayitali, monga momwe ife tiwonere pamene ife.Zisindikizo zikumatulidwa. Ndiyeno ife tikupeza, itatha nthawi yaitali iyo, satana anachotsedwa Kumwamba. Ndipo iye anabwera pansi, molingana nawo Malemba, ndipo anadzadzipatsa mpandowachifumu yekha. Tangoganizani, kudzipatsa mpandowachifumu yekha mwa munthu ameneyo, ndi kukhala chirombo. Ndipo iye anali nayo mphamvu, mphamvu yapamwamba, monga kuti iye anachita, zozizwitsa zonse ndi chirichonse chimene... kupha ndi kumenyana kwa magazi ndi chirichonse chimene Roma akanakhoza kupereka.
-----
Tsopano apa pali vumbulutso langa la izo. Uyu ndi satana, panonso. Iye ndi Mdierekezi, panonso, mwa mawonekedwe ena. Tsopano, ife tikudziwa kuti Zisindikizo zinkafotokozera. Monga ine ndinanenera usiku wina. Ndipo malipenga amafotokoza za- nkhondo wamba, inu mukuwona, pakati pa anthu, pakati pa mafuko. Koma inu mukupeza, apa, kuti munthu uyu ali nalo lupanga, kotero akufotoza za nkhondo, yandale za mpingo. Tsopano inu mukhoza kusaganiza zimenezo, koma ingoyang'anani izo miniti, maminiti pang'ono chabe.Zindikirani kusintha kwa mtundu wa akavalo awa. Wokwera yemweyo; kusintha kwa mtundu wa akavalo. Ndipo kavalo ndi chamoyo. Ndipo chamoyo, mu Baibulo, pansi pa chophiphiritsa, chimayimirira mphamvu. Kachitidwe komweko kakukwera pa mtundu wina, mphamvu, kuchokera kwa woyera wosalakwa kupita kwa wamagazi wofiira. Mwaona? Muyang'aneni iye tsopano, momwe iye akubwerera.
Pamene iye anayamba koyamba, iye anali chabe, chabwino, iye anali chabe kachiphunzitso kakang'ono mu-mu, pakati, kotchedwa Chinikolai. Zedi, icho sichikanakhoza kupha chirichonse. Ndicho Chivumbulutso 2:6, ngati inu mukufuna kulemba izo. Iye sakanakhoza kupha chirichonse. Icho chiri chiphunzitso chabe, mzimu chabe pakati pa anthu. Tsopano, iwo sukanakhoza kupha kanthu.
O, iye anali wosalakwa kwambiri, akukwera pa kavalo woyera uyu. “Chabwino, inu mukudziwa, ife tikhoza kukhala nawo mpingo wawukulu wa mdziko lonse. Ife tikhoza kuwutcha iwo mpingo wa konsekonse.” Iwo akuchitabe. Chabwino. Mwaona? Tsopano, “Ife tikhoza kukhala.” O, anali mwangwiro wosalakwa. Ndipo, o, ali wosalakwa kwambiri. Liri chabe gulu la anthu. Ife tonse tidzakhala pamodzi pa chiyanjano.” Mukuwona, ali wosalakwa kumene; ali woyera, kavalo woyera anali. Mwawona.
-----
Penyani. Zindikirani. Pamene satana... Tsopano, aliyense, kuti, amazindikira kuti satana akulamulira mphamvu zandale zonse za mdziko. Iye ananena choncho. Mateyu mutu wa 4, inu mupeza zimenezo, ndi ndime ya 8. Maufumu onse ali a iye. Ndicho chifukwa chake iwo amamenyana, nkhondo, kupha. Tsopano kumbukirani. Kodi sizachirendo zimenezo? Iwo anapatsidwa lupanga ili, kuti aphane wina ndi mzake. O, maine! Zindikirani tsopano. Tsopano, pamene iye anachita izo, iye sikuti anali ali nayo mphamvu ya zazipembedzo. Koma iye anayambamo ndi chiwanda cha kuphunzitsa kwabodza. Ndipo kuphunzitsa kumeneko kunadzakhala chiphunzitso. Chiphunzitso chimenecho chinadzakhala mu thupi mwa mneneri wabodza. Ndiyeno iye anangopita kumalo oyenera. Iye sanapite konse ku Israeli, tsopano. Iye anapita ku Roma; Nicaea, Roma.Khonsolo inachitika, ndipo iwo anasankha bishopu wamkulu. Ndiyeno, pochita ichi, iwo analumikizanitsa mpingo ndi dziko palimodzi. Ndiye, iye anagwetsa uta wake. Iye anatsikapo pa kavalo wake woyera. Iye anakwera pa kavalo wake wofiira, pakuti iye akhoza kupha aliyense amene sagwirizana naye iye. Ndi chimenechotu Chisindikizo chanu. Munthu yemweyo! Muyang'aneni iye akukwerabe mpaka mu Muyaya kutali, ndi chimenecho, mukuwona, walumikizitsa mphamvu zake palimodzi. Chinthu chomwecho iwo akuyesera kuchita pakali pano, chinthu chomwecho.
-----
Tsopano kumbukirani, iye ali nalo lupanga. Iye akupita apo, lupanga mu dzanja lake; atakwera, kavalo wofiira, kudutsa kupyola mu magazi a aliyense amene sakugwirizana naye iye. Tsopano kodi inu mukumvetsa izi? Ndi angati akumvetsa chimene Chisindikizo icho chiri tsopano? Chabwino. Tsopano, Kodi Yesu anati chiyani? “Iwo amene atenga lupanga adzawonongedwa nalo lupanga.” Kodi nkulondola uko? Chabwino.Chabwino Wokwera uyu ndi onse omumvera a ufumu wake amene akupha popyola mu m'badwo, amene amwa magazi onse awa a ofera oyera, adzaphedwa nalo Lupanga la Yesu Khristu pamene Iye akubwera. “Iwo amene atenga lupanga adzaphedwa nalo lupanga.” Iwo anatenga lupanga la miyambi ndi kutsutsakhristu, ndi kudulira pansi enieni, opembedza owona, monse mmusi kupyola mibadwo, mwa mamilioni. Ndipo pamene Khristu akubwera nalo Lupanga, pakuti ali Mawu Ake amene akutuluka kuchokera mkamwa Mwake, Iye adzadula mdani aliyense amene alipo patsogolo Pake. Kodi inu mukukhulupirira izo?
Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachiwiri.