Chisindikizo Choyamba.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Wokwera kavalo woyera.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Choyamba.Tsopano, mu mutu uwu wa 5, kumatula kwa Zisindikizo izi, ndipo tsopano Bukhu losindikizidwa nazo zisindikizo zisanu ndi ziwiri. Poyamba, ife tikufuna kuwerenga Chisindikizo Choyamba. Usiku wathawu, kuyika maziko a icho chabe mowonjezera pang'ono, ife tikupeza, kuti, pamene Yohane anayang'ana naliwona Bukhu ilo likadali mmanja a Mwini wapachiyambi, Mulungu. Kodi inu mukukumbukira momwe Ilo linatayikira? Ndi Adamu. Iye analanditsa Bukhu la Moyo, potenga nzeru za satana, ndipo anataya cholowa chake, anataya chirichonse; ndipo popanda njira ya chiwombolo. Ndiye, Mulungu, wopangidwa mu chifaniziro cha munthu, anatsika pansi nakhala Woombola kwa ife, kudzatiwombola ife. Ndipo tsopano ife tikupeza kuti, mu masiku apitawa, zinthu izi zimene zinali zachinsinsi ziri zoti zitsegulidwe kwa ife mu masiku otsiriza.
Tsopano ife tikupeza, naponso, mu ichi, kuti, mwamsanga pamene Yohane anamva kulengeza uku kwa-Woombola Wachibale kuti abwere ndi kupanga kutenga Kwake, panalibe munthu amene akanakhoza kuchita ichi; panalibe munthu Kumwamba, panalibe munthu mu dziko lapansi, panalibe munthu pansi pa dziko. Panalibe aliyense anali woyenera ngakhale kuyang'ana pa Bukhulo. Tangoganizani za icho. Popanda munthu woyenera konse ngakhale kuyang'ana pa Ilo. Ndipo Yohane anangoyamba kulira. Iye anadziwa kuti, o, apo panalibe mwayi wa chiwombolo ndiye. Chirichonse chinali chitalephera. Ndipo mwamsanga ife tikupeza kulira kwake kukuleka, mwamsanga, chifukwa kunalengezedwa ndi chimodzi cha Zamoyo zinai, kapena akulu, kani. Mmodzi wa akulu anati, “Usalire, Yohane, pakuti Mkango wa fuko la Yuda walakika,” mwakulankhula kwina, ndipo wagonjetsa.
Yohane, pochewuka, iye anawona Mwana wa nkhosa akutuluka. Iye ayenera kuti anali wamagazi ndi wotemedwa ndi wovulazidwa. Iye anali Mwanawankhosa amene anali ataphedwa. Ndipo, iye anali akadali wamagazi; ngati inu mukanadula mwanawankhosa ndi kumupha iye momwe Mwanawankhosa uyo analiri, chonchobe... Iye anagagadidwa mzidutswa pa mtanda, nthungo mu nthiti, ndipo misomali mmanja ndi mapazi, ndi minga pa zikope apo. Iye anali mu chikhalidwe chowopsya. Ndipo Mwanawankhosa uyu anatulukira, ndipo anapita kwa Iye amene anakhala pa Mpandowachifumu, amene anagwirizira chikalata chaumwini chathunthu cha Chiwombolo. Ndipo Mwanawankhosa akupita nakatenga Bukhu kuchokera m'dzanja la Iye amene anakhala pa Mpandowachifumu, ndipo linatengedwa, ndipo anatsegula Zisindikizo natsegula Bukhulo.
Ndiyeno pamene icho chinachitika, ife tikupeza kuti apo panayenera kukhala-chinachake chachikulu chinachitika Kumwamba. Pakuti, akulu, ndipo akulu anai ndi makumi awiri, ndi Zamoyo, ndipo- ndipo chirichonse Kumwamba, chinayamba kufuula, “Woyenera!” Ndipo apa panadza Angelo, ndipo anatsanulira Mbale za mapemphero a oyera. 0yera pansi pa guwa anafuula, “Woyenera muli Inu, 0 Mwanawankhosa, pakuti Inu mwatiwombola ife, ndipo tsopano Inu mwatipanga ife mafumu ndi ansembe, ndipo ife tidzalamulira pa dziko lapansi.” 0, maine! Ndipo ziri choncho, pamene Iye anatsegula Bukhu ilo.
Inu mukuwona, Bukhu makamaka linakonzedwa ndi kulembedwa asanakhazikitsidwe maziko a dziko. Bukhu ili, Baibulo, kwenikweni linalembedwa asanakhazikitsidwe maziko a dziko. Ndipo Khristu, pokhala Mwanawankhosa, anaphedwa asanakhazikitsidwe maziko a dziko. Ndipo ziwalo za Mkwatibwi Wake, maina awo anayikidwa mu Bukhu la Moyo la Mwana wa nkhosa asanakhazikitsidwe maziko a dziko. Koma, Ilo lasindikizidwa, ndipo tsopano Ilo likuwululidwa; amene maina awo anali mkati umo, zonse za Ilo, ndi chinthu chachikulu bwanji. Ndipo Yohane, pamene iye anawona izo, iye anati, Chirichonse Kumwamba, chirichonse pansi pa dziko lapansi. Chirichonse chinamumva iye akunena, “Ameni, madalitso, ndi ulemu!” Iye basi anali nayo kwenikweni nthawi yaikulu, ndi, pakuti, Mwana wa nkhosa anali woyenera.
Ndipo tsopano Mwanawankhosa akuyimirira. Tsopano, usiku uno, pamene ife tikulowa mu mutu wa 6 uwu, Iye ali nalo Bukhu mu dzanja Lake, ndipo akuyamba kuwulula Icho. Ndipo, o, ine ndikanakhoza mwamtheradi lero.Ndipo ine ndikuyembekeza kuti anthu ali auzimu. Ine ndikanakhoza kukhala nako kulakwitsa kowopsya pa Icho, ngati zikanati zisakhale, pafupi twelofu koloko lero, pamene Mzimu Woyera unabwera mu chipinda niwundikonza ine pa chinachake chimene ine ndinali kulemba kuti ndidzanene.
Ine ndinali kuzitenga Izo kuchokera mu mndondomeko wakale. Ine ndinalibe chirichonse pa Icho. Ine sindikudziwa chomwe Chisindikizo Chachiwiri chiri, mosaposanso chirichonse. Koma ine ndiri nawo mndondomeko wakale wa chinachake chimene ine ndinalankhulapo zaka zingapo zapitazo, ndipo ndinazilemba izo. Ndipo ine ndinasonkhanitsa mndondomeko iyi, mndondomeko wochokera kwa Dr. Smith, ambiri otchuka, aziphunzitsi odziwika amene ine-ine ndinali nditasonkhanitsa ilo. Ndipo onse a iwo ankakhulupirira zimenezo, kotero ine ndinazilemba izo. Ndipo ine ndinali kukonzekera kunena kuti, “Chabwino, tsopano ine ndiwerenga Icho kuchokera pa nsonga ya kuyima uko.” Ndipo mmenemo, pafupi twelofu koloko masana, Mzimu Woyera unangosesa mpaka kutsikira mchipindamo, ndipo chinthu chonse basi chinatsegulidwa kwa ine, ndipo Ichi chinali pamenepo, onani, za ichi- za Chisindikizo Choyamba ichi kukhala chotsegulidwa.
Ine ndiri wotsimikiza monga ine ndayimira pano usiku uno, kuti ichi ndi Chowonadi cha Uthenga chimene ine nditi ndinene pano. Ine ndikudziwa basi kuti icho chiri. Chifukwa, ngati vumbulutso liri losiyana kwa Mawu, ndiye ilo siliri Vumbulutso. Ndipo, inu mukudziwa, pali zinthu zina zikhoza kuwoneka zoona mwamtheradi, ndipo komabe zisali zoona. Mwawona? Zimawoneka ngati ziri, koma zisali.
Tsopano, ife tikupeza, Mwanawankhosa ali nalo Bukhu, tsopano. Ndipo tsopano mu mutu wa 6 ife tikuwerenga.
Ndipo ine ndinawona pamene Mwanawankhosa anatsegula chimodzi cha zisindikizo, ndipo ine ndinamva, ngati linali phokoso la bingu, ndipo chimodzi mwa zamoyo zinai kunena, Bwera udzawone.
Ndipo ine ndinawona, ndipo taonani kavalo woyera: ndipo iye amene anakwera pa iye anali nawo uta; ndipo korona anapatsidwa kwa iye: ndipo iye anapita akugonjetsa, ndi kukagonjetsa.Tsopano, ndicho Chisindikizo Choyamba, chimodzi chomwe ife titi tiyese, mwa chisomo cha Mulungu, kuchifotokoza Icho usiku uno. Mwa kukhoza konse. Ndipo ine ndikuzindikira kuti munthu, kuyesera kufotokoza Icho, ali kuyenda pa malo owopsya ngati iwe sukudziwa chimene ukuchita. Kotero ngati izo zibwera kwa ine mwa vumbulutso, ine ndikuwuzani inu choncho. Ngati ine ndingotenga izo kupyolera mu malingaliro anga omwe, ndiye ine ndidza- ine ndidzakuwuzani inu izo ine ndisanalankhule za izo. Koma ine ndiri wotsimikiza, monga ine ndayima pano usiku uno, Icho chabwera mwatsopano kwa ine, lero, kuchokera kwa Wamphamvuzonse. Ine sindimakonda kungonena zinthu chotero, pamene izo zifika ku gawo ili la Lemba. Ine ndikuyembekeza inu mukudziwa chimene ine ndikunena tsopano, inu mukuwona. Tsopano, inu mukudziwa, ndipo iwe siwunganene zinthu. Ngati chinachake chiyenera kukhala chitagona cha apa icho chisanachitike, iwe sungachinene icho mpaka chinachake chitakachiyika icho pamenepo. Mwawona? Kodi inu mukuwerenga? Kodi inu mukumvetsera kwa chinachake?
Tsopano, Bukhu la Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri, lokulungidwa liri tsopano kumasulidwa ndi Mwanawankhosa. Ife tikufika malo awo usiku uno. Mulungu, atithandize ife. Pamene Zisindikizo zikumatulidwa ndi kumasulidwa, zinsinsi za Bukhu zikuwululidwa. Tsopano, inu mukuona, Ili liri Bukhu losindikizidwa. Tsopano, ife timakhulupirira izo. Kodi ife sititero? Ife tikukhulupirira kuti Ilo liri Bukhu losindikizidwa. Tsopano, ife sitinkadziwa izi mmbuyomu, koma Ilo liri. Ilo liri losindikizidwa nazo Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri. Zomwe ziri, pa chikutiro cha Bukhu, Bukhulo liri losindikizidwa nazo Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.
Ngati ife tikanamalankhula za bukhu la mtundu uwu, izo zikanakhoza kukhala monga kuyika chingwe pa ilo, zingwe zisanu ndi ziwiri. Koma ilo siliri bukhu la mtundu uwu. Ilo liri mpukutu. Ndiyeno pamene mpukutu ufutukulidwa, icho ndi chimodzi; ndiye mkati mwa mpukutumo muli chachiwiri. Ndipo cha apa Ilo likunena chimene Icho chiri, koma Icho chiri chinsinsi. Komabe, ife tafufuza mu Icho; koma, kumbukirani, Bukhulo liri losindikizidwa. Ndipo Bukhulo liri Bukhu la chinsinsi, cha chivumbulutso. Ilo liri vumbulutso la Yesu Khristu, mwaona, Bukhu la mavumbulutso. Ndipo tsopano inu mukudziwa, kutsika kupyola mu mbadwo, munthu wafufuza ndipo wayesa kulowa mu Icho. Ife tonse tatero.
-----
Ndiye, pamene Mwanawankhosa anatenga Bukhu namatula Chisindikizo Choyambacho, Mulungu analankhula kuchokera ku Mpandowachifumu Wake Wamuyaya, kuti anene chomwe Chisindikizo icho chinali, kuti chiwululidwe. Koma pamene Icho chinayikidwa pamaso pa Yohane, Icho chinali mwa chophiphiritsa. Pamene Yohane anawona Icho, Icho chinali chikadali chinsinsi. Chifukwa? Icho chinali chisanaululidwe nkomwe panthawiyo. Icho sichingawululidwe mpaka chimene Iye ananena apa, pa nthawi yotsiriza.“ Koma icho chinadza mwa chophiphiritsa. Pamene, kunagunda. “Kumbukirani, phokoso lowomba lalikulu la Bingu liri Liwu la Mulungu.” Ndicho chimene Baibulo limanena, onani, kuwomba kwa Bingu. Iwo ankaganiza kuti ilo linali bingu, koma Ilo linali Mulungu. Iye analimvetsa Ilo, pakuti Ilo linawululidwa kwa Iye. Mwaona? Ilo linali Bingu. Ndipo, zindikirani, Chisindikizo Choyamba chinatsegulidwa. Chisindikizo Choyamba, pamene Icho chinatsegulidwa mwa mawonekedwe ophiphiritsa, uko kunagunda. Tsopano kuli bwanji pamene Icho chitsegulidwa mwa mawonekedwe Ake enieni?-----
Zindikirani, Khristu sali kuwonekanso, onani, kuchokera pa nthawi iyo pamenepo. Koma Iye ali pa kavalo woyera. Kotero ngati munthu uyu akukwera kavalo woyera, iye ali chabe wonamizira wa Khristu. Mwaona? Inu mukuzimva izo? Zindikirani, wokwera wa pa kavalo woyera alibe dzina lirilonse. Iye akhoza kugwiritsa ntchito maudindo awiri kapena atatu, mukuwona, koma iye alibe dzina lirilonse. Koma Khristu ali nalo Dzina! Ndi chiyani ilo? Mawu a Mulungu. Ndi chimene ilo liri. “Pa chiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu... Ndipo Mawu, anasandulika thupi.” Mwaona?Wokwerayo alibe dzina, koma Khristu akutchedwa “Mawu a Mulungu.” Ndicho chimene Iye ali. Iye akutchedwa limenelo. Tsopano Iye ali nalo Dzina limene palibe munthu akulidziwa; koma Iye akutchedwa, “Mawu a Mulungu.” Mnyamata uyu sakutchedwa kanthu, onani, koma iye ali pa kavalo woyera. Wokwerayo alibe mivi kwa uta wake. Kodi inu munazindikira? Iye anali nawo uta, koma apo palibe chirichonse chikunenedwa za kukhala nayo mivi iliyonse, kotero iye ayenera kukhala wopusitsa. Kulondola. Mwina iye ali nawo mabingu ambiri, ndipo alibe mphezi. Koma inu mukupeza, Khristu anali nazo zonse mphezi ndi bingu, pakuti kuchokera mkamwa Mwake likupita Lupanga lakuthwa konsekonse, ndipo Iye akukantha mafuko nalo Ilo. Bambo uyu sangakhoze kukantha kanthu, mwaona, koma iye akusewera gawo la wachinyengo. Iye akupita, atakwera pa kavalo woyera, kupita uko kuti akagonjetse.
Khristu ali nalo Lupanga lakuthwa, ndipo, taonani, Ilo likubwera kuchokera mkamwa Mwake. Mawu amoyo, ndiwo, Mawu a Mulungu owululidwa kwa antchito Ake. Monga Iye ananenera kwa Mose, Pita, ukayime apo, ndipo ukagwire ndodo iyo kumemeko; ukayitanitse ntchentche,“ ndipo apo panali ntchentche. Ndithudi. Chirichonse chimene iye ananena, Iye anachichita icho; ndipo icho chinakwaniritsidwa, Mawu Ake amoyo. Mulungu ndi Mawu Ake ali Munthu yemweyo. Mulungu ali Mawu. Ndani uyu wonyumwitsa wokwera wa m'badwo wa mpingo woyamba ndiye? Ali ndani iye? Tiyeni tiganize za icho. Ndani uyu wokwera wonyumwitsa amene akuyambira mu m'badwo wa mpingo woyamba ndipo akukwera mpaka kunja kukafika mu Muyaya, akupita ku matsiriziro?
Chisindikizo Chachiwiri chikudza ndipo chikupitirirabe kunja mpaka ku matsiriziro. Chisindikizo Chachitatu chikudza ndipo chikupitirira mpaka kumapeto. Chachinayi, Chachisanu, Chachisanu ndi chimodzi, Chachisanu ndi chiwiri, chirichonse cha izo, zingotsirizira apa mu mapeto. Ndipo pa nthawi yotsiriza, Mabuku awa amene akulungidwa nthawi yonseyi, ndi zinsinsi izi mmenemo, Iwo akumatulidwa. Ndiye umo mukutuluka zinsinsi, kuti tiwone zomwe ziri. Koma, makamaka, izo zinayambira mu m'badwo wa mpingo woyamba, chifukwa mpingo, m'badwo wa mpingo woyamba, unalandira Uthenga wonga Uwu.
“Wokwera pa kavalo-woyera anatuluka.” Mwaona? Ndi ndani iye? Iye ali wamphamvu mu mphamvu yake yogonjetsa. Iye ali munthu wamkulu mu mphamvu yake yogonjetsa. Inu mukufuna ine ndikuwuzeni inu amene iye ali? Iye ndi wotsutsakhristu. Momwemo chomwe iye ali. Tsopano, chifukwa, inu mukuwona, ngati wotsutsakhristu; Yesu anati, kuti, “Awiriwo adzakhala ofanana kwambiri mpaka akanadzanyenga ngakhale osankhidwa omwe (Mkwatibwi) ngati kukanakhala kotheka.” Wotsutsakhristu, ndiwo mzimu wotsutsakhristu.
Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Choyamba.