Wamoyo Mawu mndandanda index.

  Wamoyo Mawu mndandanda.

Masomphenya a Mkwatibwi.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Ululu wa Kubala.

Baibulolinati, “Mkazi wake wadzikonzekeretsa Yekha,” pa mapeto a m'badwo. Kodi Iyeanadzikonzekeretsa Yekha chotani? Kuti akhale Mkazi Wake? Ndipo kodi Iyeakuchita chiyani? Kodi Iye anavala chovala cha mtundu wanji? Mawu Ake Omwe. Iyeanavekedwa mu Chilungamo Chake. Nchomwe chiri. Izo nzoona. Mwaona? Masomphenya! Zindikirani, basi potsekera tsopano. Inendikufuna kuti ndinene chinthu chimodzichokha ichi ndisanati nditseke. Ndi chimene chinanditsogolera ine kuti ndineneizi. Tsopano, ndi PAKUTI ATERO AMBUYE. Ngati munthu akanati anene zimenezo,popanda, kuziyika izo mwa kuganiza kwake kwake, iye akanakhala wachinyengo ndiwoyenera kupita ku hade chifukwa cha izo. Ndiko kulondola. Ngati iyeakanayesera kuti atenge gulu la anthu, anthu abwino ngati awa, ndi kuwanyengaiwo, bwanji, iye akanakhala mdierekezi mu mnofu wa umunthu. Mulungusangamulemekeze konse iye. Inu mukuganiza kuti Mulungu angamulemekezemdierekezi kapena bodza? Ayi. Mwaona? Izo zimapita pamwamba pa mitu yawo, ndipoiwo samazimvetsa izo. Iye amawakokamo Osankhidwawo.

Tayang'ananipa aneneri onse kudutsa mu m'badwo, momwe Iye ankawatengera Osankhidwa. Taonani,pobwera Mmusi chodutsa, ngakhale ku kukonzanso. Monga, mpingo wa ChiromaKatolika unamuwotcha Joan waku Arc pa nkhuni, poti anali mfiti. Ndi kulondola. Kenako mtsogolo iwo anadzapeza kuti iye sanali. Iye anali woyera. Ndithudi, iwoanachita zodzitunduza, anakawakumba matupi a ansembewo ndi kukawoponyera iwo mumtsinje. Koma, inu mukudziwa, koma izo sizithetsa izo mu mabuku a Mulungu. Ayi.

Iwo anamutcha Patreki Woyera wao,nayenso, inu mukuona, ndipo iye alipafupi mochuluka monga ine ndiriri wao. Kotero, ife tikuzindikira, tayang'ananipa ana ake. Tayang'anani pa malo ake, m'mwamba, tayang'anani pa angati omweanaphedwa kumeneko. Tayang'anani pa oferawo ndipo muone ndiangati omweanaphedwa uko. Inu mukuona, izo siziri chomwecho. Koma nchodzinenera cha anthu,icho sichimapangitsa izo chomwecho. Ndi zomwe Mulungu ananena ndipoamazitsimikizira, izo kuti ndi Choonadi. “Muzitsimikizira zinthu zonse. Nkugwiritsitsa kwa izo zomwe ziri zabwino.”

Tsopanoife tikupeza, tsopano, kuno pafupi miyezi ingapo yapitayo, ' wina, ine ndinalikuyenda ndikutuluka mu nyumba, ndipo masomphenya anabwera. Ndipo inendingamutsutse aliyense pano, yemwe wazidziwa zaka zonse izi, kuti anene nthawiiliyonse yomwe Ambuye anayamba andilola ine kuti ndinene “PAKUTI ATERO AMBUYE”kupatula zomwe zinachitika. Ndi angati akudziwa kuti icho ndi Choonadi, kwezanidzanja lanu. Kulondola. Kodi winawakeangayankhule mosiyana? Ndizoona.

Musatimuzipereka chidwi chirichonse kwa mtumikiyo. Yang'anani pa Uthenga chomwe uli. Ndichomwe chiri. Mwaona? Si izo ayi. Musati muzizindikira zazing'onozo [Malo osajambulidwa pa tepi.] wa mutu wadazi,inu mukudziwa, munthuyo, chifukwa uyo ndi basi - ndi munthu wokhalapo basi, zonsezo, ndipo ife tonse tiri chimodzimodzi. Koma penyani chimene chikuchitika.Ndi chomwe chimalongosola izo. Ine ndinatengedwa.... Tsopano, ine ndikudziwaanthu amanena zinthu zambiri, ndipo ife timadziwa kuti zambiri za izo sizolondola. Ine sindingakhoze kuyankhira pa chimene wina, munthu aliyense anena. Ine ndiyenera kuyankhira ku chimene ine ndichinena. Ine ndikhoza kungonenakokha ngati chiri choonadi, kapena ayi. Ndipo ine - ine - ndine yemwe ndiyenerakukhala woyankhira pa izo, osati zomwe winawake anena. Ine sindingakhozekumuweruza wina ayi. Ine sindinatumidwe kuti ndidzaweruze, koma kuti ndidzalalikireUthenga.

Zindikirani,Ine ndinali woti ndione - chiwonetsero cha Mpingo. Ndipo ine ndinatengedwa ndiWinawake yemwe ine sindinkakhoza kumuwona, ndipo ndinaikidwa pamwamba, pongachoimikidwa. Ndipo ine ndinamva nyimbo yokometsetsa yomwe ine ndinayambandaimvapo. Ndipo ine ndinayang'ana, akubwera, ndipo gulu la madona aang'ono,apafupi, ankawoneka kuti anali, o, a usinkhu wina cham'makumi awiri, khumizisanu ndi zitatu, makumi awiri. Ndipo iwo onse anali ndi tsitsi lalitali,ndipo anali atavekedwa mu zovala zosiyana, mtundu, zovala. Ndipo iwo analiakuguba mwangwiro basi mu sitepe, ndi nyimbo imeneyo, monga izo zikanakhozakukhalira. Ndipo iwo anapita kuchokera kumanzere kwanga, kupita mozungulira kunjira iyi. Ndipo ine ndinkawayang'ana iwo. Ndipo ine ndinayang'ana ndiye kutindiwone yemwe anali kuyankhula kwa ine, ndipo ine sindinkakhoza kumuwonaaliyense.

Ndiye inendinamva gulu la gwedemula likubwera. Ndipo pamene ine ndinayang'ana chakumbali ya kumanja kwanga, akubwera ku njira iyi, akubwera m,mbuyo, apapanabwera mipingo ya mdziko. Ndipo ena a.... Aliyense atanyamula mbendera yawo,ya kumene iwo anachokerako. Zina za zinthu zowoneka zauve kwambiri zomwe inendinayamba ndaziwopanapo mu moyo wanga! Ndipo pamene mpingo wa Chimerekaunabwerapo, iwo unali choipitsitsa chimene ine ndinayamba ndachiwonapo. AtateAkumwamba ndi wondiweruza wanga. Iwo anali atavala masiketi otuwa awa a nong'onanimiseche, zonga za m'modzi wa asungwana a mumabara awa, zopanda chakumbuyo kwake, mu mtundamu apa; atagwirizira icho mmwamba ngati chidutswa chotuwa chapepala; ndipo ngati kuvina kovula; utoto; zazifupi, tsitsi lodula; akusutandudu; ndi kudzipotokola, pamene iwo ankayenda mwa gwedemula. Ndipo inendinati, “Kodi umenewo ndi mpingo wa United States?” NdipoLiwu linati, “Inde, iwo ndiwo.”

Ndipopamene iwo ankadutsa apo, iwo ankachita kuchigwira icho monga chonchi, ndikuyika chipepalacho kumbuyo kwawoko pamene iwo ankadutsa apo. Ine - ine ndinayamba kulira. Ine - inendinangoganiza, “Kuvutikira kwanga konse, ndi zonse zomwe ine ndazichita.”Ndipo chirichonse chimene ife atumiki tachigwirira ntchito limodzi.... Ndipo,abale, ine - ine sindikudziwa kuchuluka kwa momwe inu mumakhulupirira zamasomphenya awa; koma ndi Choonadi, kwa ine. Iwo nthawizonse atsimikizira kutindi woona. Pamene ine ndinaziwona izo, ndi podziwa zomwe zinali kuchitika,mtima wanga unakhala ngati usweke mwa ine. “Kodi ine ndachita chiani? Kodi inendaziphonya bwanji izo? Ine ndakhala molondola ndi Mawu awo, Ambuye. Ndipo inendikanazichita motani izo? Ine ndinaganiza, ”Bwanji inu munandipatsa inemasomphenya, osati kale litali, ndipo nkudziwona ine ndiri Mmenemo? Ndipo inendinati, 'Chabwino, kodi iwo adzasowa kuti adzaweruzidwe?' Iye anati, 'Gulu la Paulo, nalonso.'

Ine ndinati, 'Ine ndalalikira Mawu omwewoamene iye analalikira.'“ Amuna Amalonda AchiKhristu anatenga nkhani yazimenezo. Ndipo ine ndinati, ”Chifukwa? Chifukwa chiani zikanati zikhale mongachonchi?“ Ine ndinaliwona gulu ilo la achiwerewere akudutsa apo monga choncho,onse atavala monga choncho, ndipo nkumautcha, ”Mpingo wa Abiti U.S.A.“ Ine -ine ndinangokomoka.

Ndiye,molunjika, ine ndinamva nyimbo yokoma kwenikweni ija ikubwera kachiwiri, ndipoapa panabwera Mkwatibwi wamng'ono yemwe uja akudzera apo kachiwiri. Iye anati, “Uyu ndi yemwe akutuluka umo, apobe.” Ndipo pamene Iye anadzera apo, Iye alindendende monga Uja yemwe analipo mu malo oyamba, akuyenda mwa sitepe ya nyimboya Mawu a Mulungu, akuguba chodutsa apo. Ndipo pamene ine ndinamuwona uyo, inendinaima apo ndi manja onse ali m'mwamba, ndikulira, monga choncho. Pamene inendinkatsitsimuka, ine ndinali nditaima pa khonde langa kunja uko, ndikuyang'anakumene cha ku bwalolo.

Chiani?Iye ndi woti akhale Mkwatibwi wofanana, mtundu wofanana, womangidwa kuchokeraku zipangizo za mtundu wofanana yemweyo amene anali mu malo oyambirira. Tsopano kawerengeni Malaki 4 ndipokawoneni ngati ife sitikuyenera kuti tikhale ndi Uthenga mu masiku otsirizawa, womwe kuti “Utembenuze mitima ya ana kubwerera kwa makolo,” kubwerera kuUthenga wa chipentekoste chapachiyambi, Mawu ndi Mawu. Abale, ife tafika. Tsopano,mpingo uwu ukuyenera kuti ulandire chizindikiro, ndipo ndi chizindikiro chakechotsiriza. Ife tikupeza apa, mu Lemba, onani tsopano, onani, ululuwaukulu wa kubala womwe uti ukhale ulipo mu m'badwo wa Laodikaya uno. Iwo ukutopetsa.Mpingo wawo uli nkubadwa kachiwiri. Osati....

Sipadzakhalakonse bungwe lina. Aliyense akudziwa kuti nthawi iliyonse pamene uthengaunkapitapo.... Afunseni a zambiriyakale awa. Uthenga ukakhala utapita apo, bungwe limatulukira apo kuchokera mwa iwo; o, Alexander Campbell, chinachirichonse, Martin Luther, ndi chirichonse. Iwo anapanga bungwe pa iwo. Ndipokawirikawiri uthenga umangopita kwa pafupi zaka zitatu, chitsitsimutso. Uwuwakhala ukupitirira kwa zaka khumi ndi zisanu, ndipo pakhala palibe bungwelomwe lachokera pa iwo. Chifukwa? Nkhusu inali yotsiriza. Ife tiri pa mapeto.

Mukuonaululu wa kubalawo? Mukuona lomwe liri vuto? Otsalira okha ndi omwe atiatulutsidwe. Otsalira okha ndi omwe ati adzatulutsidwe. Ndipo ndi chifukwachake ine ndikulira, ndi kulimbikira, ndi kukankha, ndi kuyika kumbalikukondera kulikonse kwa munthu pa dziko lapansi, kuti ndipeze kukondedwa ndiMulungu, ndi kumangosunthira mtsogolo mu Mawu Ake. Iwo ulimu ululu. Ndilo lomwe liri vuto. Iwo ukuti ubale. Iwo uyenera kuti upangekusankha kwake. Kulemba kwa dzanja kuli pa khoma. Ife tikuwona dziko lapansi liripafupi basi kuti lizipita. Uko nkulondola. Ndipo ife tikuwuwona mpingo, iwowavunda kwambiri, iwo uli pafupi kuti uzipita. Ndipo ululu wa kubala uli pazonse izo, pa zonse dziko ndi mpingo. Ndipo patsala pang'ono kuti dzikolatsopano kuti libadwe, ndipo Mpingo watsopano ukubadwa, kuti upite mu ilo, kwaZakachikwi. Ife tikuzidziwa izo.

Taonani. Mulungu akumupatsa iye.... Ndipo tamvetserani kwa izi mwatcheru, ndiye inendikutseka. Chizindikiro chake chotsiriza; Uthenga wake wotsiriza, chizindikirochake chotsiriza. Chizindikiro chake chotsiriza, ndicho, iye akuyenera kutiafike mu zikhalidwe monga iwo unaliri pachiyambi; dziko, mpingo. Yang'ananimomwe izo zinaliri pachiyambi, zaka zonse izo, popanda kuyambira kwa Malakimpaka Yesu. Yang'anani pa izo, zaka zonse tsopano. Yang'anani pa izo, monsemmbuyomo uko, chivundi chomwe iwo analowamo. Yang'anani pa dziko lapansi, momweilo linaliri pa nthawi iliyonse, monga mu masiku a Nowa, ena otero. Zakhalaziri mwa mtundu womwewo wa choimira, ndipo ife tikuziwona izo. “Monga momwezinaliri m'masiku a Nowa.” Tikuziona zinthu zonsezi zikungofanizana apo.

Werengani akaunti yonse mu... Ululu wa Kubala.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.

Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa m’dziko lapansi.

Yohane 16:20-21


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

As the Eagle
Stireth her nest.

(PDF Chingerezi)

 

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)
Kumene lupanga
laonekera.


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.