Kodi ichi ndi chizindikiro cha mapeto, Bwana?

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Nthawi yotsiriza mndandanda.

Angelo kuwundana.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Kodi ichi ndi chizindikiro cha mapeto, Bwana?

Chivumbulutso 10:7,
Koma mu masiku a liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, pamene iye ati adzayambe kuwomba, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizidwa, monga iye anafotokozera kwa antchito ake aneneri.

Tsopano, motsatira monse, kutsika kupyola mu ulendo, pakhala pali zinthu zimene zachitika, zimene ine sindimakhoza kuzimvetsa. Ndipo chimodzi cha zinthu zimene ine sindimakhoza kuzimvetsa, zinali pamene ine ndinali mnyamata wamng'ono ndipo masomphenya awo amakhoza kubwera pa ine. Ndipo ine ndimakhoza kuwawona iwo ndi kuwawuza makolo anga zinthu zimene zimati zichitike. Iwo ankaganiza kuti ine ndinali wamanjenje chabe. Koma, chinthu chachirendo, izo zinkachitika mwa njira yomweyo basi Iwo ankanenera chotero.

Inu mukuti, “Kodi izo zinali inu musanatembenuke?” Inde. “Mphatso ndi mayitanidwe ndi zopanda kulapa,” Baibulo linatero. Iwe umabadwa pa dziko lino kwa cholinga china. Ndipo iwe siumati... Kulapa kwako sikumabweretsa mphatso; izo zinakonzedweratu kwa iwe. Tsopano, motsatira njira, ndipo pamene ine ndinali mnyamata wamng'ono, kukhumba kwanga kunali... ine ndinali wosakhutitsidwa mu dziko limene ine ndinkakhalamo. Ine ndinkayembekezera, mulimonse, kupita Kumadzulo.

-----
Kuyenera kuti inali teni koloko masana, pamene mkazi wanga anali kuyesera kulowa mu chipinda, ndipo izo zinachitika. Ine ndinalowa mu masomphenya mmawa umenewo, ndipo ine mwinamwake... Tsopano, kumbukirani, awo sanali maloto.

Pali kusiyana pakati pa maloto ndi masomphenya. Maloto ndi pamene iwe upita kukagona. Masomphenya, pamene iwe sunapite kukagona. Ife tinabadwa mwa njira iyo. Munthu wamba, pamene iye alota, izo ziri mu chikumbumtima chake. Ndipo chikumbumtima chake ndi njira yakutali tali kwa iye. Mphamvu zake ziri zochitachita, malingana ngati iye ali mu kukumbukira kwake koyamba. Mu kukumbukira uku, nkuti, iwe uli wabwinobwino; iwe umawona, kulawa, kumverera, kununkhiza, kumva. Koma pamene iwe uli mu chikumbumtima chako, utagona, iwe sikutinso umawona, kulawa, kumverera, kununkhiza, kapena kumva. Koma pali chinachake, pamene iwe ulota, kuti iwe umabwerera ku kukumbukira uku. Pali kukumbukira, kumene iwe umakumbukira chinachake chimene iwe unalota pafupi, zaka zapitazo. Munthu wamba ali mwa njira iyo. Koma pamene Mulungu akonzeratu chinachake, chikumbumtima ichi sichiri njira yakutalitali kuchokera apa, kwa mpenyi, koma zokumbukira zonsezo ziri palimodzi kumene. Ndipo mpenyi, mu masomphenya, samapita kukagona. Iye akadali mu mphamvu zake, ndipo amaziwona izo.

-----
Tsopano, mu masomphenya awa, kapena monga ine ndinali kuyankhula, ine ndinayang'ana ndipo ine ndinawona chinthu chachilendo. Tsopano, izo zinkawoneka ngati kuti mwana wanga wamng'ono, Joseph, anali pa mbali yanga. Ine ndinali kuyankhula kwa iye. Tsopano, ngati inu muti muwayang'ane masomphenyawo mwatcheru kwenikweni, inu muwona chifukwa chimene Joseph anali kuyimirira pamenepo.

Ndipo ine ndinayang'ana, ndipo apo panali thengo lalikulu. Ndipo pa thengo ili mu_mu kuwundana kwa mbalame, mbalame zazing'ono ndithu, pafupi theka la inchesi utali, ndi theka la inchesi usinkhu. Izo zinali zakale zazing'ono. Nthenga zawo zazing'ono zinali zitasosoka. Ndipo apo panali ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba, zisanu ndi imodzi kapena zisanu ndi zitatu pa nthambi inayo, ndipo khumi ndi zisanu kapena makumi awiri pa nthambi inayo; zikubwera pansi mu mawonekedwe a piramidi. Ndipo tinthu tating'ono ito, tiatumiki tating'ono, ndipo izo zinali zotopa kwambiri ndithu. Ndipo izo zinali kuyang'ana chakummawa.

Ndipo ine ndinali ku Tucson, Arizona, mu masomphenya, pakuti izo zinapanga izo mwacholinga chotero kuti Iye sanafune kuti ine ndilephere kuwona kumene izo zinali. Ine ndinali kuchotsa chisoso chamu mchenga pa ine, cha ku chipululu, ndipo ine ndinati, “Tsopano, ine ndikudziwa kuti awa ndi masomphenya, ndipo ine ndikudziwa kuti ine ndiri ku Tucson. Ndipo ine ndikudziwa kuti mbalame zazing'ono izo apo zikuyimira chinachake.” Ndipo izo zinali kuyang'ana chakummawa. Ndipo zonse mwadzidzidzi izo zinatenga lingaliro kuti ziwuluke, ndipo kutali izo zinapita, chakummawa.

Ndipo mwamsanga pamene izo zinachoka, kuwundana kwa mbalame zazikulupo kunadza. Izo zinkawoneka ngati nkhunda, zamapiko akuthwa-osongoka, zokhala ngati mtundu wotuwa, mtundu wawung'ono wotuwa kuposa chimene atumiki aang'ono oyamba awa anali. Ndipo izo zinali kubwera chakummawa, mwaliwiro.

Ndipo sipanatenge nthawi pamene izo zinachoka mkupenya kwanga, ine ndinapotolokanso kuti ndiyang'ane chakumadzulo, ndipo apo izo zinachitika. Apo panali kuphulika komwe kunagwedeza kumene dziko lapansi lonse. Tsopano, musati muphonye izi. Ndipo inu, pa tepi, khalani otsimikiza kuti mumvetse izi molondola.

Poyamba, kuphulika. Ndipo ine ndinaganiza iko kunamveka ngati mkokomo waukulu, chirichonse chimene inu mumachitcha icho pamene ndege zidutsa mkokomo, ndipo mkokomowo umabwereranso ku dziko lapansi. Basi kunagwedeza, monga, kunalindima, chirichonse. Ndiye, iko kukanakhoza kukhala ku kuwomba kwakukulu kwa bingu ndi ngati mphenzi; ine sindinayiwone mpheziyo. Ine ndinangomva kuphulika kwakukulu uko kumene kunachitika, komwe kunamveka ngati iko kunali kummwera, kuchokera kwa ine, cha ku Mexico.

Koma, iko kunagwedeza dziko lapansi. Ndipo, pamene iko kunatero, ine ndinali kuyang'anabe chakumadzulo. Ndipo kutali komwe mu Muyaya, ine ndinawona kuwundana kwa chinachake chikubwera. Icho chinkawoneka ngati kuti iko kukanakhala madontho aang'ono. Awo akanakhoza kukhala osachepera asanu, ndipo osaposera asanu ndi awiri. Koma, iwo anali mu mawonekedwe a piramidi, monga atumiki awa akubwera.

Ndipo, pamene iwo anatero, Mphamvu ya Mulungu Wamphamvuzonse inandinyamulira ine mmwamba kukakomana nawo Iwo. Ndipo ine ndikukhoza kuwona Izo. Izo sizinandichokere konse ine. Masiku asanu ndi atatu apita, ndipo ine sindingakhoze kuyiwala izo, panobe. Ine sindinakhalepo konse ndi china chondisautsa ine monga icho chachitira. Banja langa lingakuwuzeni inu.

Ine ndimakhoza kuwawona Angelo amenewo, mapiko opindikira kumbuyo awo, akuyenda mwaliwiro kuposa momwe mkokomo ungakhoze kuyendera. Iwo amabwera kuchokera ku Muyaya, mu kamphindi, ngati kuthwanima kwa diso. Kosati nkukwanira kuphethira diso lako; kuthwanima chabe, Iwo anali apo. Ine sindinakhale nayo nthawi kuti ndiwawerenge. Ine ndinalibe nthawi, wopanda zina kuposa kupenya basi. Amphamvu Awo, Angelo aakulu, amphamvu, oyera ngati chipale; mapiko atayikidwa, ndi mitu. Ndipo iwo anali, “Fyuu-fyuuu!” Ndipo, pamene iwo anatero, ine ndinatengedwa mmwamba kupita mu piramidi iyi ya kuwundana.

Ndipo ine ndinaganiza, “Tsopano, izi ndizo.” Ine ndinali wadzanzi paliponse. Ndipo ine ndinati, “O, mai! Izi zikutanthauza kuti padzakhala kuphulika kumene kuti kudzandiphe ine. Ine ndiri pa mapeto a msewu wanga tsopano. Ine sindiyenera kuwawuza anthu anga, pamene masomphenya awa andichokera. Ine sindikufuna kuti iwo adziwe za izo. Koma, Atate Akumwamba andilora ine kudziwa tsopano kuti nthawi yanga yatha. Ndipo ine sindiliwuza banja langa, kuti iwo azidandaula za ine, 'Chifukwa, iye akukonzekera kupita.' Ndipo Angelo awa abwerera ine, ndipo ine ndiphedwa posakhalitsapa tsopano mu mtundu wina wa kuphulika.”

Ndiye icho chinabwera kwa ine, pamene ine ndinali mu kuwundana uku, “Ayi, izo si ndizo. Ngati iko kukanakupha iwe, iko kukanamupha Joseph.” Ndipo ine ndimakhoza kumumva Joseph akundiyitana ine. Chabwino, ndiye ine ndinabwerera kachiwiri, ine ndinaganiza, “Ambuye Mulungu, kodi masomphenya awa akutanthauza chiyani?”

Ndipo ine ndinadadwa. Ndiyeno izo zinabwera kwa ine, (osati liwu) kungobwera kwa ine. “O! Awo ndi Angelo a Ambuye, amene akubwera kudzandipatsa ine utumiki wanga watsopano.” Ndipo pamene ine ndinaganiza izo, ine ndinakweza manja anga mmwamba, ndipo ine ndinati, “O Ambuye Yesu, kodi Inu mukufuna kuti ine ndichite chiyani?” Ndipo masomphenyawo anandichokera ine. Kwa pafupi ora, ine sindimakhoza kumverera.

Tsopano, inu anthu mukudziwa chimene madalitso a Ambuye ali. Koma, Mphamvu ya Ambuye ili palimodzi yosiyana, Mphamvu ya Ambuye mu malo a mtundu uwo. Ine ndinakumverera Iko, nthawi, zambirimbiri, kale, mu masomphenya, koma osati monga choncho. Iko kumamverera ngati mantha a kulemekeza. Ine ndinali wowopsyezedwa kwambiri mpaka ine ndinali wazanzi, mu kukhalapo kwa Zinthu izi. Ine ndikunena Zoona. Monga Paulo ananena, “Ine sindinama ayi.” Inu simunandigwirepo ine ndikunena chirichonse cholakwika za chinachake chonga icho. Chinachake chikukonzekera kuchitika.

Ndiye, patapita kanthawi, ine ndinati, “Ambuye Yesu, ngati ine nditi ndiphedwe, mundirole ine ndidziwe, kuti ine ndisawawuze abale anga za izi. Koma ngati icho chiri chinachake, mundirole ine ndidziwe.” Koma, palibe chimene chinayankha. Utatha Mzimu kundichokera ine, kwa pafupi theka la ora, ine ndikuganiza, kapena kuposera, ine ndinati, “Ambuye, ngati izo ziri, ndiye, kuti ine ndikukaphedwa, ndipo Inu mwathana nane ine pa dziko lapansi, ndipo_ndipo ine nditengedwera Kwathu tsopano; chimene, ngati izo ziri, izo nzabwino, izo ziri bwino. Kotero,” ine ndinati, “ngati izo ziri, mundirole ine ndidziwe. Tumizaninso Mphamvu Yanu kubwerera pa ine kachiwiri, ndiye ine ndidziwa kuti ndisawawuze abale anga kapena aliyense za izo, chifukwa Inu mukukonzekera kubwera kudzanditengera ine kwina.” Ndipo palibe kanthu kanachitika. Ndipo ine ndinayembekezera kanthawi.

Ndiye ine ndinati, “Ambuye Yesu, ngati izo sizimatanthauza izo, ndipo izo zikutanthauza kuti Inu muli nacho chinachake choti ine ndichite, ndipo kuti icho chidzaululidwa kwa ine mtsogolo, ndiye tumizani mphamvu Yanu.” Ndipo Iyo pafupifupi inandichotsa ine mchipindamo!

Ine ndinadzipeza ndekha, penapake, uko mu ngodya. Ine ndimakhoza kumumva mkazi wanga, penapake, akuyesera kugwedeza chitseko. Chitseko mu chipinda chogona chinali chokhomedwa. Ndipo ine ndinali nditatsegula Baibulo, ndipo ndinali kuwerenga, ine sindikudziwa, koma ilo linali mu, ine ndikukhulupirira, Aroma mutu wa 9, ndime yotsiriza. Taona, ine ndayika mu Zioni mwalawapangodya, mwalawopunthwitsa, mwalawapangodya wofunika, ndipo aliyense amene akhulupirira pa iye sadzachita manyazi.

Ndipo ine ndinaganiza, “Icho nchachirendo ine kukhala ndikuwerenga izo.” Mzimu ukundinyamulabe ine, mchipindamo! Ine ndinatseka Baibulo ndipo ndinayima pamenepo. Ine ndinapita cha ku zenera. Iyo inali pafupi teni koloko mu tsiku, kapena kupitirira. Ndipo ine ndinakwezera mmwamba manja anga, ndipo ine ndinati, “Ambuye Mulungu, ine sindikumvetsa. Ili ndi tsiku lachirendo, kwa ine. Ndipo ine ndiri pambali pa inemwini, pafupifupi.”

Ine ndinati, “Ambuye, kodi izo zikutanthauza chiyani? Mundirole ine ndiwerengenso, ngati uyo ali Inu.” Tsopano, izi zikumveka zachibwana. Ndipo ine ndinatenga Baibulo, kulitsegula ilo. Apo ilo linalinso, pa malo omwewo, Paulo akuwawuza Ayuda kuti iwo amayesera ku... kuwawuza Aroma kuti Ayuda ankayesera kulandira Izo mwa ntchito, koma izo ziri mwa chikhulupiriro kuti ife timakhulupirira Izo.

-----
Ine ndikukhulupirira kuti “mngelo wa chisanu ndi chiwiri” wa Chivumbulutso 10 ali mtumiki wa mpingo wa m'badwo wa chisanu ndi chiwiri wa Chivumbulutso 3:14. Kumbukirani. Tsopano ndiroleni ine ndiwerenge. Penyani pamene ine ndingakhoze kuwerenga. Tsopano, uyu anali mngelo wachisanu ndi chiwiri.
Koma mu masiku a liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, (ndime ya 7) pamene iye ati adzayambe kuwomba, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizidwa, monga iye anafotokozera kwa antchito ake aneneri.
Tsopano, inu zindikirani, uyu anali mngelo. Ndipo iye ndi mngelo wa m'badwo wa mpingo wa chisanu ndi chiwiri, chifukwa akunena apa, iye ndi “mngelo wa chisanu ndi chiwiri” wa m'badwo wa mpingo wa chisanu ndi chiwiri. Tinapeza izo, ngati inu mukufuna kuwona yemwe ku... kumene mngeloyo ali, Chivumbulutso 3:14, ndiye, “Mngelo kwa mpingo wa Laodikaya.”

-----
Tsopano mvetserani mwatcheru. Mngelo wachisanu ndi chiwiri wa Chivumbulutso 10:7 ndi mtumiki wa m'badwo wa mpingo wa chisanu ndi chiwiri. Mwaona? Tsopano yang'anani. “Ndipo mu masiku...” Tsopano yang'anani apa.
Koma mu masiku a liwu la mngelo wachisanu ndi chiwiri, pamene iye adzayamba kuwomba, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizidwa....
Tsopano, kuwomba, mtumiki uyu, mngelo wachisanu ndi chiwiri apa akuwomba Uthenga wake kwa mpingo wa Laodikaya. Zindikirani mtundu wa Uthenga wake. Tsopano, izo sizinali kwa mngelo woyamba, sanapatsidwe Izo; mngelo wachiwiri, wachitatu, wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chimodzi. Koma ndi mngelo wachisanu ndi chiwiri amene anali nawo mtundu wa Uthenga uwu. Chinali chiyani icho? Zindikirani mtundu wa Uthenga wake, “Kutsirizitsa zinsinsi zonse za Mulungu, zimene zalembedwa mu Bukhu.” Mngelo wachisanu ndi chiwiri akumaliza zinsinsi zonse zomwe zagona ndi mbali-zomasuka, onse uko kupyola mu mabungwe awa ndi zipembedzo. Mngelo wachisanu ndi chiwiri akuzisonkhanitsa izo, ndi kutsirizitsa chinsinsi chonse. Tsopano, icho ndi chimene Baibulo linanena, “Kutsirizitsa chinsinsi cha Bukhu lolembedwa.”

Werengani akaunti yonse mu...
Kodi ichi ndi chizindikiro cha mapeto, Bwana?

Onani... Mtambo wauzimu.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Mateyu 24:30


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Kodi ichi ndi
chizindikiro cha
mapeto, Bwana?

(PDF)- Mt Sunset.
Komwe mtambo
udawonekera.

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)

Chapter 11
- The Cloud

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.