Bukhu ili la Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Mndandanda Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.

Bukhu la Chiombolo.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Cholekanitsa...

Tsopano, ine ndinapita pamwamba mu canyon, ndipo ine ndinakwera mmwamba kwambiri monga mmene ine ndikanakhozera kupita. Ndipo ine ndinawafunsa Ambuye, ine nditakhala pamwamba mmenemo, chomwe zonsezi chimatanthawuza, ndi zina zotero. lne ndinakhala ngati ndavutitsidwa, ndipo sindinadziwe chabe choti ndichite. Ndipo chotero pamene ine ndinali kupemphera; chinthu chachirendo chinachitika. lne-ine-ine ndikufuna kukhala woona mtima. Tsopano, ine ndikanakhoza kukhala ndiri mtulo. lzo zikanakhoza kukhala ngati kusinthika, kapena iwo akanakhoza kukhala ma-ma-masomphenya. lne ndikusamila kwambiri kapena pang'ono kukhulupirira kuti iwo anali masomphenya. Kuti, ine ndinali nditatambasula manja anga, kunena, “Ambuye, kodi kuphulika uku kukutanthawuza chiyani? Nanga Angelo asanu ndi awiri awa mu kuwundana kwa piramidi, kundinyamulira ine mmwamba kuchokera pansi ndi kutembenukira chakummawa, kodi izi zikutanthawuza chiyani?”

lne ndinali nditayima pamenepo, mu pemphero, ndipo chinachake chinachitika. Ndipo, tsopano, chinachake chinagwera mdzanja langa. Ndipo ine ndikudziwa, ngati inu simumvetsa zinthu zauzimu, izo zikhoza kuoneka zachirendo kwambiri. Koma chinachake chinakhudza m'dzanja langa. Ndipo, pamene ine ndinayang'ana, ilo linali lupanga. Ndipo chikumbu chinali chopangidwa ndi ngale, ngale yokongoletsetsa imene ine ndinayiwonapo konse. Ndipochotetezera,( inu mukudziwa, kumene. lne ndikuganiza ndi chotetezera manja ako kuti asachekedwe, inu mukudziwa, pamene iwe anthu anali kumenyana) chinali golide. Ndipo mpeni wochekera sunali wawutali koposa, koma iwo unangokhala wakuthwa ngati lumo; ndipo iwo unali siliva wonyezimira. Ndipo icho chinali chinthu chokongoletsetsa chimene ine ndinachionapo. llo linangokwanira mdzanja langa chimodzimodzi. Ndipo ine ndinali kuligwira ilo.

lne ndinati, “Kodi silokongola ili!” lne ndinayang'ana pa ilo. Ndipo ine ndinaganiza, “Koma, inu mukudziwa, nthawizonse ndimachita mantha ndi lupanga.” lne ndikukhala ngati ndikukondwa kuti ine sindinakhale mmasiku amene ankagwiritsa ntchito iwo, chifukwa ine-ine ndimachita mantha ndi mpeni. Ndipo kotero ine-ine ndinaganiza, “lne ndikanachita nalo chiyani ilo?” Ndipo ndiri chigwirizire, mu dzanja langa, Liwu lochokera kwinakwake linati, “llo ndi lupanga la Amfumu.” Ndiyeno ilo linandichokera ine.

-----
Kotero, zinthu izo ife-ife tikungopenekera, chifukwa, mopanda maphunziro, ine ndimafaniziritsa. lne ndimayang'ana ndi kuona chimene chiri, kapena chakhala chiri mu Chipangano Chakale, chimene chiri choyimira kapena mnthunzi wa Chatsopano, ndiye ine ndiri ndi lingaliro lina chimene Chatsopano chiri. Mwaona? Monga ngati.Nowa analowa mu chombo chisautso chisanakhalemo, choyimira; koma ngakhale Nowa asanatero, onani, kulowa mu chombo, Enoki anapita mmwamba, onani, chirichonse chisanati chachitika. Ndipo Loti anayitanidwa kuti atuluke mu Sodomu kachidutswa kamodzi ka chisautso kasanalowemo, ka chionongeko; koma Abrahamu anali, nthawi zonse, kunja kwa icho. Mwaona, zoyimira.

Koma tsopano ife tiwerenga ndime ya 1. lne ndiwerenga ziwiri zoyamba kapena ndime zitatu za lwo.

Ndipo ine ndinaona m'dzanja lamanja la iye amene anakhala pa mpando wachifumu bukhu lolembedwa mkati ndi kunja kwache, losindikizidwa ndi zisindikizo zisanu ndi ziwiri.
Ndipo ine ndinawona mngelo amphamvu wakulalikira ndi liwu lofuula, Ayenera ndani kutsegula bukhu, ndi kumasula zisindikizo zache?
Ndipo panalibe munthu kumwamba, kapena mu dziko lapansi, ngakhale pansi pake-ngakhale pansi pa dziko lapansi, anali wokhoza kutsegula bukhu, ngakhale kuyang'ana pa llo.
(Ndi Bukhu lotani!)
Ndipo ine ndinalira kwambiri, chifukwa panalibe munthu anapezeka woyenera kutsegula ndi kuwerenga bukhulo, ngakhale kuyang'ana pamenepo."

(Tsopano, inu mukalankhula za kusayenera? Wosayenera ngakhale kuyang'ana pa llo; panalibe munthu, kulikonse.)
“Ndipo mmodzi wa akuluwo ananena kwa ine, Usalire: taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula bukhulo, ndi kumasula zisindikizo zache zisanu ndi ziwiri.
Ndipo ine ndinaona, ndipo, taonani, pakati pa mpando wachifumu ndi pa zamoyo zinai,.pakati pa akulu, panayima Mwanawankhosa ngati iye anali ataphedwa, wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri, zomwe ziri Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yotumidwa ilowe mdziko lapansi lonse.
Ndipo iye anadza nalitenga bukhu kuchokera mdzanja lamanja la iye amene anakhala pa mpando wachifumu.”

lfe tiyima pamenepo kwa mphindi zochepa, ku kuwerenga kwa Chivumbulutso 5, kutsika mpaka ku kuphatikiza ndime ya 7.

Bukhu ili la Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri likuululidwa pa nthawi ya Mabingu Asanu ndi awiri a pa Chivumbulutso 10.

-----
Tsopano, onani, chinsinsi cha Bukhu ili la Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri chidzaululidwa pa kuwomba kwa Uthenga wa mngelo wa chisanu ndi chiwiri. Mngelo wachisanu ndi chiwiri akuyamba kuwomba,“ ndipo pali Mauthenga olembedwa pamenepo, ndipo ife tiri nawo lwo mu tepi ndi mwamawonekedwe a bukhu. Tsopano, pa kuyamba kwa kuwomba kwa Uthenga, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kutsirizika, mwaona, pa nthawi imeneyo.“ Tsopano ife tidzazindikira. Bukhu, la chinsinsi cha Mulungu, silikuululidwa mpaka Uthenga wa mngelo wa chisanu ndi chiwiri utawombedwa. Tsopano, nsonga izi zidzakhala zofunikira mu Zisindikizo, ine ndikutsimikiza, chifukwa lzo ziyenera, chidutswa chirichonse, kumangirizana palimodzi. Tsopano, llo ndi lolembedwa mwachinsinsi, chifukwa palibe munthu, kulikonse, amadziwa lzo. Mulungu yekha, Yesu Khristu, mwaona.

Tsopano, koma ili ndi Bukhu, Bukhu lachinsinsi. llo ndi Bukhu la Chiwombolo. lfe tilowa mu izo, mu kanthawi pang'ono. Ndipo tsopano ife tikudziwa kuti Bukhu ili la Chiombolo silidzamvetsedwa bwinobwino; llo lafufuzidwa, popyola mibadwo isanu ndi umodzi ya mpingo. Koma pa mapeto, pamene mngelo wachisanu ndi chiwiri akuyamba kuomba chinsinsi chake, iye akutsirizitsa mfundo zonse zomasuka zimene anthu awa anafufuzapo. Ndipo zinsinsi zikutsika pansi kuchokera kwa Mulungu, monga Mawu a Mulungu, ndi kuulula vumbulutso lonse la Mulungu, ndiye Umulungu ndi china chirichonse chakhazikitsika. Zinsinsi zonse, mbewu ya serepenti, ndi chirichonse chowonjezera, ndi zakuti ziululidwe.

-----
Zindikirani. Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri pa Bukhu, zakhala. Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri izi zasindikiza Bukhulo. Mwaona? Bukhulo liri mwamtheradi losindikizidwa. Kodi inu mukuona icho? Bukhulo liri mwamtheradi Bukhu losindikizidwa mpaka Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri zimatulidwe. llo ndi lomatidwa ndi Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri.

Tsopano, ndizo zosiyana ndi Mabingu Asanu ndi awiri. Mwaona? lzi ndi Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri pa Bukhu. Ndipo Bukhulo silidza, Zisindikizo sizidzamasulidwa mpaka Uthenga wa mngelo wa chisanu ndi chiwiri. Mwaona? Chotero ife-ife tikungopenekera; koma vumbulutso lenileni la Mulungu lidzapangidwa kukhala langwiro mukuomba uko, Choonadi chotsimikizidwa. Tsopano, ndicho chimodzimodzi chimene Mawu akunena, Chinsinsi chiyenera kudzatsirizika pa nthawi iyo. Ndipo Bukhu ili la Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri, kumbukirani, llo linali lotsekedwa apa, mu Chivumbulutso mutu wa 5, ndipo mu Chivumbulutso mutu wa 10 llo latsegulidwa.

Ndipo tsopano ife tiona chimene Bukhu likunena momwe llo liti likhalire lotseguka. Ndipo sizikudziwitsidwa mpaka Mwanawankhosa atatenga Bukhu, ndi kumatula Zisindikizo, natsegula Bukhulo. Mwaona? Mwanawankhosa ayenera kulitenga Bukhu. lzo zabisika. Tsopano kumbukirani, Palibe munthu Kumwamba, palibe munthu mu dziko lapansi,“ papa, bishopu, kadinolo, mkulu wa mdziko, kapena aliyense amene ali, angathe kutsegula Zisindikizo izo, kapena kuulula Bukhu, koma Mwanawankhosa.” Ndipo ife tafufuzamo, ndi kufanizira, ndi kuphunthwa, ndi kudabwa, ndi-ndipo ndicho chifukwa ife tonse tiri mu chisokonezo choterechi. Koma ndi lonjezo Lauzimu kuti Bukhu ili la Chiombolo lidzatsegulidwa mwangwiro ndi Mwanawankhosa, ndipo Zisindikizo zachezo zidzamasulidwa ndi Mwanawankhosa, mu masiku otsiriza mmene ife tikukhalamo tsopano. Ndipo izo sizinadziwitsidwe mpaka Mwanawankhosa atatenga Bukhu ndi kumatula Zisindikizo. Chifukwa, kumbukirani, Bukhu linali litagwiridwa mmanja a lye amene anakhala pa Mpando wachifumu. Ndipo Mwanawankhosa akudza kwa lye amene akukhala pa Mpando wachifumu, natenga Bukhu kuchokera mdzanja Lake lamanja.“ Akutenga Bukhu!

O, ndizo zakuya. lfe tiyesa kuzifotokoza izo ngati ife tingathe, mwa chithandizo cha Mzimu Woyera. Tsopano ife tikudalira pa lye. Ndipo ife tidzaona, kenako, izo ziri pa nthawi yotsiriza, Pamene nthawi yatha.“ Palibe zipembedzo ziri ndi ufulu wa kutanthauzira kwa Bukhu. Palibe munthu ali ndi ufulu wa kutanthauzira llo. Ndi Mwanawankhosa Amene akulitanthauzira llo. Ndipo Mwanawankhosa ndi lye Amene akulankhula lzo, ndipo Mwanawankhosa akuwapanga Mawu kuti adziwike, mwa kuwatsimikizira ndi kuwabweretsa Mawu ku Moyo. Mwaona? Chimodzimodzi.

-----
Lamulo la Mulungu linafuna cholowa mmalo chosalakwa. Ndipo ndani anali wosalakwa? Munthu aliyense anali atabadwa mwakugonana, chotsatira kugonana, aliyense. Ndipo mmodzi yekha amene sanali, anali atalanditsa ufulu ku Moyo Wamuyaya ndi kukhala mfumu pa dziko lapansi. O, pamene ine ndiganiza za Lemba ilo, “Pakuti inu mwatiombola ife kubwerera kwa Mulungu, ndipo ife tikhoze kulamulira ndi kukhala mafumu ndi ansembe pa dziko lapansi.” O, mai! Chiyani? Woombola Wachibale...! O, ndi nkhani yotani ife tikanakhala nayo apa! Zindikirani, lamulo linafuna Woombola Wachibale kuti akaombole chinthu chotayika. Chisomo chinakwaniritsa kufunika uku mu Umunthu wa Yesu Khristu. Wachibale ayenera kubadwa mwa mtundu wa anthu.

Tsopano, ife tikanakhala bwanji, pamene munthu aliyense amene abadwa ayenera ku.Ndipo aliyense amene sakanakhoza kuwona kuti unali mchitidwe wa kugonana pamenepo, chabwino, iye ali wakhungu kwathunthu, mwaona, chifukwa munthu aliyense amene anabadwa anabadwa mwa mkazi. Ndipo Mulungu anafuna Woombola Wachibale, ndipo lye ayenera kukhala munthu. O, mai! Nchiyani chomwe inu muti muchite tsopano? Lamulo linafuna Woombola Wachibale.

Tsopano, lye sakanakhoza kutenga Mngelo. lye anayenera kukhala ndi munthu, chifukwa ife sitiri achibale kwa Mngelo. lfe tiri achibale kwa wina ndi mzache. Mngelo sanagwe konse. lye ndi cholengedwa cha mtundu wina, ali ndi thupi losiyana. lye sanachimwepo kapena chirichonse. lye ndi wosiyana. Koma lamulo linafuna Woombola Wachibale. Ndipo munthu aliyense padziko lapansi anabadwa mwa kugonana. Tsopano, kodi inu simukuona, apo ndi pamene izi zinachokera. Ndipo pamene tchimo linayambira. Kotero inu mukuona pamene ilo liri tsopano? Pamenepo iyo ikudza, mbewu yanu ya serpenti, mkati. Mwaona.

Tsopano, zindikirani, anafuna Woombola Wachibale. Ndipo Woombola, Woombola Wachibale, ayenera kubadwa wa mtundu wa anthu. Apa, izo zikutisiya ife pa nthambi. Koma ndiroleni ine ndiwombe Lipenga kwa inu. Kubadwa mwa namwali kunabala-chobadwa. Ameni. Kubadwa mwa namwali kunabala Woombola wathu Wachibale. Palibe wina koma Mulungu Wamphamvuzonse kukhala Emmanuele, mmodzi wa ife. Emmanuele! Woombola Wachibale“ anapezeka.... lnu mukuona momwe Mulungu amapangira chofunikira, ndipo apo palibe kanthu ife tingakhoze kuchita. Koma ndiye chisomo chikulowamo ndi kudzaphimba lamulolo, ndi kubala chobadwa. Ameni!

-----
Tsopano yang'anani. Bukhu la Rute limapereka chithunzi chokongola cha izi, momwe Boazi. Ndipo Naomi anali atataya chuma. lnu, inu mukudziwa. lnu mwandimva ine ndikulalikira pa izo, sichoncho inu? Kwezani manja anu mmwamba ngati inu munandimva ine ndikulalikira izo. Kotero, inu mukumvetsa, mwaona. Boazi anayenera kukhala woombola. Ndipo iye anali yekhayo amene akanakhoza. lye anayenera kukhala wachibale, wapachibale chapafupi. Ndipo, mu kuwombola Naomi, iye anatenga Iute. Ameneyo anali Yesu, Boazi kuyimira Khristu. Ndipo pamene lye anawombola lsraeli, lye anatenga Mkwatibwi wa Amitundu. Kotero ndiye, inu mukuona, zokongola chotero kwambiri! lfe tiri nazo izo pa tepi, ine ndikutsimikiza, kuno kwina kwake, inu mukanakonda mutakhala nayo.

-----
Chisomo chinabala Umunthu wa Yesu Khristu. Ndipo ife tikulipeza, Bukhu ili tsopano.Mulungu anatambasula hema Lake, kuchokera kwa Mulungu, kuti akhale munthu. lye anasintha maonekedwe Ake, kuchokera mu Wamphamvuzonse, kuti akhale munthu; kudzitengera maonekedwe a munthu, kotero lye akanakhoza kufa, kuti awombole munthu. Yembekezani mpaka ife timuwone lye, pamene palibe wina woyenera.“ Mwaona.

Chabwino. Mu Baibulo, mu Bukhu la Rute, pamene inu mukuwerenga ilo, inu mukapeza kuti, munthu woteroyo ankatchedwa fisi, “f-i-s-i.” Anali kutchedwa fisi, kapena, anali munthu amene akanakhoza kukwaniritsa chofunikiracho. Ndipo fisi ayenera kukhala wokhoza kuchita icho, ayenera kukhala wololera kuchichita icho, ndipo ayenera kukhala wachibale, wapafupi kwa wachibale, kuti achite icho. Ndipo Mulungu, Mlengi, wa Mzimu, anakhala wachibale kwa ife pamene lye anakhala munthu, ndi cholinga kuti lye akanakhoza kutenga tchimo lathu pa lye, ndi kulipira mtengo wake, ndi kutiombola ife kubwereranso kwa Mulungu. Ndi izo apo. Pamenepo pali Woombola. Khristu watiombola ife tsopano. lfe tsopano taomboledwa. Koma lye sanatengebe zomwe ziri za lye. Tsopano, inu mukhoza kutsutsana nacho icho, koma tangoyembekezani miniti yokha, mwaona. lfe tiona.

lye sanatengebe icho. Mwaona? Ngati lye anatenga Bukhu la Chiombolo, chirichonse chimene Adamu anali nacho ndi chirichonse chimene iye anataya, Khristu akuziwombolanso izo. Ndipo lye watiombola ife kale. Koma lye sanatengebe zomwe ziri zake; lye sangatero mpaka nthawi yoyikidwa. Ndiyeno padzabwera chiukitsiro, ndiyeno dziko lapansi lidzakonzedwa kachiwiri. Ndiyeno lye adzatenga zake, za lye zimene lye anazipeza pamene lye anatiombola ife, koma adzachita izo pa nthawi yoyikidwa. O, maine. lzi zikufotokozedwa mu Bukhu la Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri ili limene ife tikukamba za ilo tsopano. Cholekanitsa Pakati Pa Mibadwo Isanu Ndi Iwiri Ya Mpingo Ndi Zisindikizo Zisanu Ndi Ziwiri 14 Chabwino. Bukhu la Chiombolo, zonsezo zikufotokozedwa mmenemu. Zonse izo zimene Khristu ati adzachite pa matsiriziro zidzaululidwa kwa ife sabata ino, mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ngati Mulungu angatilole ife. Mwaona. Chabwino. lzo zidzaululidwa.

Werengani akaunti yonse mu...
Cholekanitsa...


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto.

M’dzanja lake munali kabuku kakang’ono kotsekulidwa. Phazi lake lamanja linaponda m’nyanja ndipo phazi lake lamanzere linaponda pa mtunda.

Mngeloyo anafuwula kwambiri ngati kubangula kwa mkango. Atangofuwula, kunamveka kugunda kwa mabingu asanu ndi awiri.

Chivumbulutso 10:1-3


Bukhu ili la
Zisindikizo-Zisanu
ndi ziwiri likuululidwa
pa nthawi ya
Mabingu Asanu
ndi awiri a pa
Chivumbulutso 10.


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet.

(PDF Chingerezi)

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.