Mkango wa fuko la Yuda.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Ndani ali woyenera?
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Cholekanitsa...Chivumbulutso 5:2-4,
2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?”
3 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zam’kati mwake.
4 Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zam’kati mwake.Tsopano, “Ndipo mngelo wamphamvu....” Tsopano ndime 2.... mngelo wamphamvu, ndi liwu lokweza, kulalikira, “Ndani ali woyenera”. (Kuyenerera kwa chiyani?) Ndani ali woyenera kutenga bukhu ilo,... Tsopano ife tikuzipeza. Kodi liri kuti Bukhulo tsopano? Kwa Mwini Wake wapachiyambi, chifukwa llo linalanditsidwa ndi mwana, mwana woyamba wa Mulungu, mu mtundu wa anthu. Ndipo pamene iye analanditsa ufulu wake, kumvetsera kwa Satana, iye analeka... Kodi iye anachita chiyani? lye anavomereza nzeru za Satana mmalo mwa Mawu a Mulungu.
-----
Kuyitana kwa Mngelo kunali kuyitanira Woombola Wachibale kuti awonekere. Mulungu anati, “lne ndiri nalo lamulo; Woombola Wachibale akhoza-akhoza kukhala cholowa mmalo. Ali kuti Woombola Wachibale uyo? Ndani akhoza kulitenga llo?” Ndipo ilo linachokera kwa Adamu, njira yonse kudutsa atumwi onse, ndi aneneri, ndi china chirichonse, ndipo panalibe wina anapezeka. Tsopano, nanga bwanji izo? Panalibe wina Kumwamba, panalibe wina pa dziko lapansi, panalibe wina amene anakhalapo.... Eliya anali atayimirira pamenepo. Mose anali atayimirira pamenepo. Atumwi onse amayimirira pamenepo, kapena-kapena ena onse amene anali atafa; amuna onse oyera, Yobu, aluntha. Wina yense anali atayimirira pamenepo, ndipo panalibe wina anali woyenera ngakhale kuyang'ana pa Bukhulo, ngakhale kuti alitenge kokha llo ndi kumatula Zisindikizo.-----
Koma, Yohane analira. Apa pali chomwe ine ndikuganiza iye ankalirira. Chifukwa, ngati panalibe wina anali woyenera ndi wokhoza kutsegula Bukhu la Chiombolo ili, chirengedwe chonse chikanatayika. Apa pali Bukhu, apa pali chikalata cha umwini, ndipo llo lidzaperekedwa kwa Woombola Wachibale amene angakwaniritse zofunikirazo. Ndilo lamulo la Mulungu Mwini, ndipo lye sangayipitse lamulo Lake, sanganyoze lamulo Lake, kani. Mwaona? Mulungu ankafuna Woombola Wachibale Amene anali woyenera, Amene anali wokhoza kuchita icho, Amene anali ndi chinthu chochitira icho. Ndipo Mngelo anati, “Tsopano lolani Woombola Wachibale adze patsogolo.”Ndipo Yohane anayang'ana. Ndipo iye anayang'ana padziko lonse lapansi. lye anayang'ana pansi pa dziko lapansi. Ndipo apo panalibe wina. Chirengedwe ndi chirichonse zinatayika. Ndithudi, Yohane analira. Chirichonse chinali chitatayika. Kulira kwake sikunapitirire koma miniti yokha, ngakhale. Ndiye pamenepo panayima mmodzi wa akulu, anati, “Usalire, Yohane.” O, mai! Kulira kwake sikunapitirire koma miniti yokha. Yohane anaganiza, “O, maine, alikuti Munthuyo? Apo payima aneneri; iwo anabadwa monga ine ndinachitira. Apo payima aluntha. Apo payima... O, palibe wina pano?”
-----
Ndipo Mkango uwu wa fuko la Yuda unalakika. lye anati, “Usalire ayi, Yohane. Pakuti Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika. lye wagonjetsa kale. lye wachita icho. lzo zatha, Yohane.” O, mai! lye anapereka bulitchi imene imatumiza tchimo kumbuyo kwa manja amafuta amene.ndi nzeru zake, zimene zinadetsa icho, munthu amene. lnde.Koma pamene Yohane anacheuka kuti ayang'ane, iye anawona Mwanawankhosa. Ndi wosiyana bwanji kwa Mkango! lye anati, “Mkango walakika.” Mwaona, ndiponso, ine ndikhoza kugwiritsa ntchito ichi uko, “Mulungu kudzibisa mu kuphweka”. lye anati, “Apo pali Mkango.” (Ndiwo mfumu ya zinyama.) Mkango walakika. Chinthu champhamvu kwambiri chimene chiripo ndi mkango.
lne ndagonapo mu nkhalango mu Afrika, ndi kumvanswala zikulira. Ndipo-ndipo yayikulu njovu yamphamvu, ili ndi, chitamba chake mmwamba, “Khwii, khwii, khwii,” Ndi kumamva zinyama za mchipululu zikulirira magazi awo, kulira kowopsya. Ndipo nkhu-nkhumbutera, mpaka. Ndipo Billy Paul ndi ine kugona mu malo ang'ono akale ofoleredwa ndi zisoso. Ndipo kumva, kutali komwe mu kamtunda, mkango ukubangula, ndipo chirichonse pa chipululu kutonthola. Ngakhale nkhumbutera kuleka kusokosera. Mfumu ikulankhula. O, maine. lne ndikukuuzani inu, ndipo pamene zipembedzo ndi kukayikira kunagwera pansi. Chirichonse chimakhala chete pamene Mfumu ikulankhula. Ndipo Iyi ndi Mfumu, ndiwo Mawu Ake.
-----
Tsopano iye anati, “Mkango wa fuko la Yuda.” Chifukwa chiyani kuchokera mwa Yuda? O, Yuda, “wopereka lamulo sadzapita patsogolo pako, pakati pa maondo ake, mpaka Silo atadza.” Koma lye adzabwera kupyolera mwa Yuda. Ndipo Mkango, chizindikiro cha fuko la Yuda, walakika. lwo wagonjetsa. Ndipo pamene iye anatembenuka nayang'ana kuti awone kumene Mkango unali, iye anawona Mwana wa nkhosa. Zachirendo, kufuna kuwona Mkango ndi kuwona Mwana wa nkhosa. Mkulu anamutcha lye Mkango. Koma pamene Yohane anayang'ana, iye anawona Mwana wa nkhosa, Mwana wa nkhosa monga Wophedwa kuchokera ku maziko a dziko. Mwana wa nkhosa amene anali ataphedwa. Chinali chiyani icho? Mwana wa nkhosayo anali chiyani? lye anali wamagazi, atavulazidwa. Mwana wa nkhosa yemwe anali ataphedwa, koma anali ndi moyo aponso.” Ndipo lye anali wamagazi. O, mai! Mungayang'ane motani pa lcho, abale, ndi kukhalabe wochimwa?Mwana wa nkhosa anafika apo. Mkulu anati, “Mkango walakika, Mkango wa fuko la Yuda.” Ndipo Yohane anayang'ana kuti awone Mkango, ndipo apo pakubwera Mwanawankhosa, akunjenjemera, Magazi ali pa lye, mabala. lye anali atalakika. lnu mukanakhoza kudziwa kuti lye anali mu nkhondo. lye anali ataphedwa, koma lye anali ndi moyo aponso.
Yohane sanamuzindikire Mwanawankhosa uyu poyamba, inu mukudziwa, apa. lye anali asanatchulidwepo poyamba. Palibe pamene lye anali atatchulidwa. Yohane sanamuwone lye, Kumwamba konseko, pamene iye anali kuyang'ana. Koma apa lye akutulukira. Zindikirani kumene lye anachokera. Kodi lye anachokera kuti? lye anachokera ku Mpando wa Atate, kumene lye anali atakhala chiphedwereni Chake ndi kuukitsidwanso. lye ananyamuka nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu, ali moyobe kuti azipanga zitetezero. Ameni. Ananyamuka apo, lero, monga Wotetezera, nawo Mwazi Wake Womwe, kupanga chitetezero pa umbuli wa anthu. Tsopano, ndiye Mmodzi amene ine ndikudalirapo. lye anali wophimbidwabe ndi bulitchi, bulitchi ya chikhululukiro cha tchimo.
-----
Tsopano penyani mwatcheru kwenikweni. lchi ndi chinthu china chimene inu muyenera kuchimvetsa. Tsopano, lye anali akuchita ntchito Yake yoyimira pakati, kupangira zitetezero wokhulupirira. Kwa zaka zikwi ziwiri lye anali ali kumbuyo uko, Mwanawankhosa. Tsopano lye akutulukira kuchokera ku Muyaya, kudzatenga Bukhu la chikalata cha umwini, ndi kudzamatula Zisindikizo, ndi kuulula zinsinsi. Ndi liti ilo? Pa nthawi yotsiriza. Kodi inu mukuzimva izi? Chabwino, ife tipitirira ndiye. Tsopano, kumatula Zisindikizo ndi kumasula zinsinsi zonse kwa iwo, kwa mngelo wachisanu ndi chiwiri, amene Uthenga wake ndi woti uwulule zinsinsi zonse za Mulungu. Zinsinsi za Mulungu zagona mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri izi. Mwaona? Ndi chimene lye ananena apa. Zinsinsi zonse zagona mu Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri izi.Ndipo Mwana wa nkhosa akubwera tsopano, kuchokera pokhala Woyimira pakati pa Mulungu ndi munthu. lye akukhala Mkango. Ndipo pamene lye akukhala Mkango, lye akutenga Bukhu. Ndiwo ufulu Wake. Mulungu waligwirizira llo, chinsinsi, koma tsopano Mwana wa nkhosa akubwera. Palibe wina akanakhoza kutenga Bukhu. llo likanali mmanja a Mulungu. Palibe papa, wansembe, kaya ndani mwina ali, iwo sangakhoze kutenga (ayi) Bukhu. Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri sizinakhale zitaululidwa. Mwaona. Koma pamene, Woyima pakati, pamene ntchito Yake yachitidwa monga Mtetezi, lye akubwera. Ndipo Yohane. Mkulu anati, “lye ndi Mkango.” Ndipo lye akubwera. Mumuyang'ane lye. O, maine! Mwaona.
lye akubwera kudzatenga Bukhu, (tsopano yang'anani), kudzaulula zinsinsi za Mulungu, zimene ena ankangoganiza pa izo, mu mibadwo ya zipembedzo yonse iyi. Mwaona, ndiye, mngelo wachisanu ndi chiwiri. Ngati Bukhu ili, zinsinsi, ziri Mawu a Mulungu, mngelo wachisanu ndi chiwiri ayenera kukhala mneneri, kuti Mawu a Mulungu afikireko. Palibe ansembe, mapapa, kapena china chirichonse, chingatenge llo; Mawu samabwera kwa oterowo. Mawu a Mulungu amadza kwa mneneri yekha, nthawizonse.
Malaki 4 analonjeza zotero. Ndipo pamene iye akubwera, iye akanatenga zinsinsi za Mulungu, komwe mpingo wachititsa zonse kusokonezeka mu zipembedzo zonse izi, “Ndi kubwezeretsa Chikhulupiriro cha ana kubwerera kwa atate.” Ndiyeno chiweruzo cha dziko chikanadzakantha, ndipo dziko lapansi likanadzaotchedwa. Ndiyeno olungama akanadzayenda pa mapulusa a anthu oyipa, mu Zakachikwi. Kodi inu mukumvetsa izi tsopano? Chabwino.
Ena anaganiza pa izo, mu m'badwo wachipembedzo. Koma, onani, iye ayenera kukhala munthu uyu, mngelo wa chisanu ndi chiwiri wa... Chivumbulutso 10:1-4 ali... Mngelo wachisanu ndi chiwiri ali nazo zinsinsi za Mulungu zitapatsidwa kwa iye, ndipo akutsirizitsa zinsinsi zonse zimene zinasiyidwa, kudutsa mu mibadwo yazipembedzo.
Tsopano inu mukhoza kuona chifukwa ine sindikukanthira pa okondedwa anga mu chipembedzo. Ndi kachitidwe ka chipembedzo! lwo samachita ayi, palibe kufunika kwa iwo kuyesa kuti adziwe lzi, chifukwa lzo sizikanakhoza kuululidwa. Ndizo monga mwa Mawu. lwo anapenekera pa lzo, nakhulupirira kuti lzo zinali pamenepo, ndipo mwa chikhulupiriro anayenda mwa lzo, koma tsopano lzo zatsimikiziridwa mooneka. Ameni. O, maine, ndi Lemba lotani!
-----
Malamulo a Mulungu amafuna. (lye ali Mmodzi amene akusungira llo). Lamulo la Mulungu linkafuna Woombola Wachibale. Ndipo Mwanawankhosa anaturuka, atagwirizira llo, “lne ndine Wachibale wawo. lne ndine Woombola wawo. lne tsopano.lne ndapanga chitetezero cha iwo, ndipo tsopano ine ndabwera kudzawatengera iwo ufulu wao.” Ameni. “Pali Mmodzi yekhayo. lne ndadza kudzawatengera ufulu wawo. Mu icho, iwo ali ndi ufulu kwa chirichonse chimene chinatayika mu kugwa, ndipo ine ndalipira mtengo wake.” O, m'bale! Whyuu! Kodi icho sichikukupangitsani inu kumva mwachipembedzo mkati mwanu? Osati mwa ntchito zabwino zimene ife tazichita, koma mwa chifundo Chake. O, dikirani ka miniti! Ndipo akulu awo ndi chinthu chirichonse anayamba kuchotsa akorona, ndipo olemekezeka anayamba kuyima pa nthaka, mwaona.Palibe mmodzi, palibe mmodzi akanachita izo. Ndipo lye akupita molunjika mpaka ku dzanja lamanja la Mulungu, ndipo anatenga Bukhu kuchokera mdzanja Lake, ndi kutenga ufulu Wake. “lne ndinafa chifukwa cha iwo. lne ndine Woombola Wachibale wawo. lne ndine. lne ndine Woyimira pakati. Mwazi Wanga unakhetsedwa. lne ndakhala Munthu. Ndipo lne ndachita ichi ndi cholinga kuti ndiwutenge Mpingo uwo kuubwezeranso, Womwe ine ndinawuwoneratu asanakhazikitsidwe maziko adziko. lne ndinalinga za lwo. lne ndinalankhula za lwo, lwo ukanadzakhala pamenepo. Ndipo palibe wina anali wokhoza kulitenga llo, koma lne ndinapita pansi ndipo ndachita icho, lnemwini. lne ndine Wachibale wawo. lne ndakhala wapachibale.” Ndipo lye akulitenga Bukhu. Ameni! O, ndi Yani akundiyembekezera Uko ine usiku uno? Ndi ndani Mmodzi uja, mpingo, amene akuyembekezera Uko? Ndi chiyaninso chikanakhoza kukuyembekezerani inu Uko? Woombola Wachibale uja! O, mai! Ndi mfundo yapamwamba bwanji, kapena chochitika.
Tsopano lye ali ndi chikalata cha umwini kwa chiombolo. lye ali ndi lcho mu dzanja Lake. Kuyimira pakati kwachitika tsopano. lye ali nalo llo mu dzanja Lake. Kumbukirani, llo lakhala liri mu dzanja la Mulungu, nthawi yonse, koma tsopano llo liri mu dzanja la Mwanawankhosa. Tsopano penyani. Chikalata chaumwini cha chiombolo, cha chirengedwe chonse, chiri mu dzanja Lake. Ndipo lye wabwera kuti atenge lcho chibwererenso, kwa mtundu wa anthu. Osati kuchitengera lcho kwa Angelo, Kuchitenga lcho kubwerera kwa anthu, chimene lcho chinaperekedwera, kuti chipangenso ana amuna ndi akazi a Mulungu; kuwabwezeranso iwo ku munda wa Edeni, chirichonse chimene iwo anataya; chirengedwe chonse, mitengo, moyo wazinyama, china chirichonse. O, maine! Kodi icho sichikukupangani inu kumva bwino?
Werengani akaunti yonse mu...
Cholekanitsa...