Mphamvu ya Mulungu yosanduliza.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Kukonzanso kwa malingaliro anu.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Mphamvu ya Mulungu yosanduliza.Tsopano mu Buku la Aroma, mutu 12, ndipo ndime ya 1 ndi 2, ife tikukhumba - tikukhumba kuti tiwerenge Lemba ili.
Ine ndikukupemphani inu chotero, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti inu mupereke matupi anu ngati nsembe zamoyo, zoyera, ndi zovomerezeka kwa Mulungu, komwe kuli kupembedza kwanu koyenera.
Ndipo musakhale inu ofaniziridwa ndi dziko lino: koma inu mukhale osandulika mwa kukonzanso kwa malingaliro anu, kuti inu mukhoze kutsimikizira chomwe chiri chifuniro chabwino, ndi changwiro... chabwino, chovomerezeka, ndi changwiro, cha Mulungu.Tsopano, ngati Ambuye alola, ine ndikufuna kuti nditenge phunziro langa m'mawa uno, pa: Mphamvu Ya Mulungu Yosanduliza. Kuti inu musakhale muli ofaniziridwa ndi dziko lino: koma mukhale... osandulika mwa kukonzanso kwa malingaliro anu, tsopano, ndi kutsimikizira icho chomwe chiri chifuniro chabwino, changwiro, ndi chovomerezeka, cha Mulungu.
Ndi nkhani yakale yodziwika yomwe ambiri a abusa anu aigwiritsa ntchito konse kudutsa mu nthawi yanu. Iyo yakhala ikugwiritsidwa ntchito kuyambira pomwe Iyo inalembedwa. Komabe, chinthu chimodzi chokhudza Mawu a Mulungu, Iwo samakalamba konse, chifukwa Iwo ndi Mulungu. Iwo samakalamba konse. Kupyola mu kam'badwo kalikonse tsopano, kwa pafupi, zaka zikwi ziwiri nd mazana asanu ndi atatu, kapena mwabwinoko, Mawu awa a Mulungu akhala akuwerengedwa ndi anthu, ansembe, ndi ena otero, ndipo Iwo, sakukalambabe. Ine ndakhala ndikuwawerenga Iwo ine mwini, kwa zaka zina makumi atatu ndi zisanu. Ndipo nthawi ili yonse yomwe ine ndimawawerenga Iwo, ine ndimapeza china chake chatsopano chomwe ine ndinachilambalala pa nthawi yoyamba. Chifukwa, Iwo ndi odzozedwa, Iwo ndi Mulungu mu maonekedwe a zolembedwa. Mwaona, Iwo ndi zikhumbo za Mulungu zikuyankhula, ndipo izo zinaikidwa pa pepala.
Nthawi zambiri, munthu amati, “Chabwino, tsopano, munthu analilemba Baibulo ili.” Ayi. Baibulo limati, Ilolo, kuti Mulungu analemba Baibulo. Ilo ndi Mawu a Mulungu. Ndipo Iwo sangakhoze konse kulephera. Yesu anati, “Miyamba ndi dziko la pansi zidzalephera, zidzachoka, koma Mawu Anga sadzalephera konse.” Ndipo Iwo sangakhoze kulephera, ndipo pokhala Mulungu, chifukwa Iwo ali gawo la Iye. Ndiyeno inu pokhala mwana Wake wamwamuna ndi wa mkazi, inu muli gawo la Iwo, ndipo izo zimakupangitsani inu kukhala gawo la Iye. Kotero ndi chifukwa chake ife timabwera kudzayanjana limodzi mozungulira Mawu a Mulungu.
Tsopano mawu awa oti kusandulika, ine ndinawayang'ana iwo mu bukhu lotanthauzira mawu, dzulo. Pamene, ine ndinali pafupi kutaya kulondola kwa nthawi yomwe ine ndimayenera kuti ndidzakhale ndiri kuno, pamene ine ndimaifunafuna nkhaniyi, ndipo ine ndinapeza mawu awa, kapena nkhani iyi, kani, Lemba. Ndipo mu bukhu lotanthauzira mawu ilo limanena kuti ndi “china chake chomwechasinthidwa.” Chirichoti “chisinthidwe.” Kusandulika, “kupangidwa mosiyana ndi chimene icho chinali.” Icho chakhala chiri, “Khalidwe lake ndi chirichonse chasinthidwa mwa icho,” kusandulizidwa.
Ndipo ine ndimaganiza m'mawa uno, mu Genesis 1. Dziko lino linali lopanda maonekedwe, ndipo ilo linali lopanda kanthu, ndipo m'dima unali pa dziko lapansi; panalibe kanthu koma chisokonezo chathunthu. Ndipo pamene dziko lino linali mu chikhalidwe chimenecho, Mzimu wa Mulungu unkayenda pamwamba pa madzi, ndipo chithunzi chonsecho chinasinthidwa; kuchoka ku chisokonezo chathunthu, kukakhala munda wa Edene. Iyo ndi Mphamvu yosanduliza ya Mulungu, yomwe ingakhoze kutenga chinachake chomwe sichiri kanthu ndi kupanga chinachake chodabwitsa kuchokera mwa icho. Mphamvu yosanduliza ya Mulungu!
Ndipo ife tikumva kuti, pa kuwerenga Malemba, kuti Mulungu anali ndi zisanu ndi chimodzi - zaka zikwi zisanu ndi chimodzi akupanga kukonzekera uku kwa Edene uyu. Tsopano, Iye mwina akhoza kusakhala kuti anali utali wotero; koma basi kungopenekera, ndi kuzitenga izo kuchokera mu Lemba pamene Iwo anati “tsiku limodzi kwa Mulungu, liri zaka chikwi pa dziko lapansi,” izo ziri, ngati Mulungu akanati aziwerenga nthawi. Ndipo iwo amati zinali zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zomwe Iye anali nazo pa kulipanga dziko lapansi, ndipo Iye anali atabzala pa dziko lapansi mbewu zonse zabwino. Apo panali basi chirichonse chiri changwiro.
Ine ndikuganiza, nthawi zambiri, ngakhale pamene otsutsa ayamba kuwerenga Buku la Genesis, iwo amayamba kulitsutsa Ilo, chifukwa izo zimawoneka kuti mowirikiza Ilo limangodzibwereza Lokha, kapena kukuponyerani inu kunja apa ndi apo.Koma ngati ife tikanati tingozindikira kwa mphindi, ife tisanalowe mu nkhani yathu, kuti, Mose anawona masomphenya. Ndipo Mulungu anayankhula ndi iye. Mulungu ankayankhula kwa Mose maso ndi maso, mulomo kwa khutu. Tsopano, Iye sankayankhula konse ndi munthu wina aliyense monga choncho, momwe Iye ankachitira naye Mose. Tsopano, Mose anali wamkulu, mmodzi wa aneneri aakulu onse. Iye anali choimira cha Khristu.
Ndipo tsopano Mulungu akhoza kulamkhula, Iye ali nalo liwu. Ilo lakhala likumvedwa. Mulungu akhoza kulankhula. Ndipo Mulungu akhoza kulemba. Mulungu analemba Malamulo khumi ndi chala Chake Chomwe. Iye analemba pa makoma a - a Babeloni kamodzi, ndi chala Chake. Iye anawerama pansi ndipo analemba mu mchenga nthawi ina, ndi chala Chake. Mulungu akhoza kulankhula. Mulungu akhoza kuwerenga. Mulungu akhoza kulemba.Mulungu ali kasupe wa chisomo chonse ndi Mphamvu, ndi nzeru zonse za Umulungu, ziri mwa Mulungu.
Kotero chomwecho, podziwa izo, Iye ali Mlengi yekha yemwe alipo. Palibe Mlengi wina kupatula Mulungu. Satana sangakhoze kulenga, nkomwe, iye amangopotoza zomwe zalengedwa. Koma Mulungu ndi Mlengi Yekhayo. Chotero, Iye analenga ndi Mawu Ake. Iye anawatumiza Mawu Ake. Kotero mbewu zonse zomwe Iye anali ataziyika pa dziko lapansi, Iye anaziumba mbewu zimenezo ndi Mawu Ake Omwe, pakuti kunalibe kena kalikonse koti apangire mbewu nako. Iye anali atadziyika izo, ndipo izo zinali pansi pa madzi. Iye anangoti, “Pakhale ichi, ndipo pakhale icho.”
Tsopano ife tikupeza kuti, nthawi zambiri, izo zimawoneka ngati Baibulo likudzibwereza kapena likunena chinachake chomwe Ilo silikunena. Mwa chitsanzo, mu Genesis 1 ife tikupeza kuti “Mulungu anamulenga munthu mu chifanizo Chake Chomwe, mu chifanizo cha Mulungu Iye anamulenga iye; mwamuna ndi mkazi Iye anawalenga iwo.” Ndiyeno Iye akupitirira, ndipo zinthu zambiri zinachitika pa dziko lapansi.
Ndiye ife tinafika popeza kuti, panalibe munthu woti adzilima m'nthaka. “Ndiye Mulungu anamulenga munthu kuchokera mu fumbi la dziko lapansi.” Uyo anali munthu wosiyana. “Ndipo Iye anapumira mzimu wa moyo mwa iye, ndipo iye anadzakhala solo ya moyo.”
Munthu woyamba anali mu chifaniziro cha Mulungu, umene uli Mzimu. Yohane 4, amati, “Mulungu ndi Mzimu, ndipo iwo amene amupembedza Iye ayenera adzimupembeza Iye mu Mzimu ndi mu Choonadi.” Koma Mulungu ndi Mzimu. Ndipo munthu woyamba, yemwe Iye anamulenga, anali munthu - wauzimu, ndipo iye anali mu chifanizo ndi m'mawonekedwe a Mulungu. Ndiyeno Iye anamuika munthu uyu mu mnofu, ndipo munthu anagwa. Koterono Mulungu anadzabwera pansi ndipo anadzakhala mu chifanizo cha munthu, kuti Iye adzakhoze kumuwombola munthu wakugwa uyo. Imeneyo ndi nkhani yeniyeni ya Uthenga, mwa - mwa kulingalira kwanga.
Tsopano, Mulungu, mu zaka zikwi zisanu ndi chimodzi, anali atabzala mbewu zonse zodabwitsa izi, kapena Iye anali atayankhula Mawu Ake. “Izo zidzakhala ziri mwanjira iyi. Mtengo uwu udzakhala uli. Izi zidakhala ziri.” Chirichonse chinali changwiro. Izo zinali zabwino basi. Ndipo Iye anailamulira ili yonse ya Mbewu zimenezo chimene zikanadzakhala, izo zikanamadzadzisintha zokha kukhala mbewu ya mtundu wake wa moyo umene Mawu a Mulungu anali atauyankhulira mwa izo kuti umayenera kukhala uli. Ngati iwo unali mtengo wa mgwalangwa, iwo unali woti udzibala mgwalangwa. Ngati iwo unali kanjedza, iwo unali woti udzibala kanjedza. Chifukwa, Mlengi wamkulu anali basi atangotumiza Mawu Ake, ndipo mbewu ya Mawu inali apo mbewu yeniyeni isanaumbidwe konse. Ndipo Mawuwo anapanga mbewuyo. Mwaona, “Iye anapanga dziko kuchokera mu zinthu zomwe siziri kuwoneka.” Mwaona, Iye anapanga dziko ndi Mawu Ake. Mulungu anayankhula chirichonse kuti chikhalepo.
Ndipo pokhala Mulungu, Mlengi, akuyankhula zinthu zonse kuti zikhalepo, ilo liyenera kuti linali dziko langwiro. Awo anali - malo okongola. Iyo inali pa - paradaiso yeniyeni pano pa dziko lapansi. Tsopano, monga, malo aliwonse ayenera akhale ali ndi likulu kwina kwake. Msonkhano waukulu uno uli ndi likulu, ndipo chaputala chino chiri ndi likulu, ndipo mpingo uli ndi likulu. Ndipo Mulungu ali nalo likulu. Ndipo chomwecho malo aakulu ano, fuko lomwe ife tiri kukhalamo, liri nalo likulu. Ndipo kotero Edene wamkulu uyu anali ndi likulu, ndipo likulu lake linaikaidwa mu munda wa Edene, kapena mu Edene, kum'mawa kwa kwake m'mundamo. Ndipo Mulungu Anaika pamwamba pa uwu, kuti azilamulira pa chilengedwe Chake chopambana chonse pano pa dziko lapansi, mwana Wake ndi mkwatibwi wa mwana Wakeyo, Adamu ndi Hava.
Mulungu anali Atate wa Adamu. “Adamu anali... mwana wa Mulungu,” monga mwa Malemba. Iye anali mwana wa Mulungu. Ndipo Mulungu anamupangira iye womuthandizira, kuchokera mu thupi lake lomwe; mwinamwake nthiti kuchokera pamwamba pa mtima wake, kotero kuti iye azikhala wapafupi kwa iye, ndipo anamupangira iye womuthandizira. Iye kwenikweni sanali mkazi wake apabe, mosaposa momwe iye analiri mwamuna apabe; Iye anali atangoyankhula izo. Ndipo apo ndi pamene vuto linabwerera, Satana anamupeza iye Adamu asanatero. Kotero, awo anali basi Mawu Ake omwe Iye anawayankhula.
-----
Ndipo ife tonse tikadali mu chifanizo cha Mulungu. Koma ena ndi olumala kwambiri, ngati ana a Mulungu, omwe amayenda mosiyana ndi Mawu Ake ndi ku njira yomwe Iye anali nayo ndipo anaipereka kwa ife kuti tiziyendamo. Kuyikamo china chake, dziko limatipotokola ife kutichotsa m'njirayo kutikokera ife pafupi ndi ilo, ndi kutalikira ndi kanjira kowongoka, kopapatiza komwe Iye anatibzalamo ife, kuti tikhale ana a amuna ndi a akazi a Mulungu. Tchimo lachita chinthu choipa ichi kwa ana a amuna ndi a akazi a Mulungu.-----
Tsopano kwa inu muli kunja kofalitsidwira, kulikonse komwe inu muli, ine ndikufuna kuti inu mulandire Khristu uko komwe, ngati mpuliumutsi wanu wanu, ndikuti mudzadzidwe ndi Mzimu Wake. Mawu omwe anenedwa mmawa uno, mulole iwo agwere mu mtima mwanu ndipo mulole apo inu mumulandire Yesu. Ndipo muupenye moyo wanu, ndipo muone chomwe inu muzikhala pa mbuyo pake. Ndipo mutenge Sefa ya mwamuna woganiza pano. Pamene inu mudziwona nokha mukuchita chinachake chomwe chiri chosiyana ndi Mawu awa, muzisuntha kuchoka kwa icho, mwansanga kumene. Mwaona? Chifukwa, pali sefa yomwe imatchingira imfa kutali ndi inu, awo ndiwo Mawu a Mulungu. Mawu Ake ali Moyo, ndipo iwo azikutetezani inu ku imfa.Werengani akaunti yonse mu...
Mphamvu ya Mulungu yosanduliza.