Mkwatulo.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Wamoyo Mawu mndandanda.

Mkwatulo.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Mkwatulo.

Masalimo 27:4-5,
4 Chinthu chimodzi ine ndinachipempha kwa AMBUYE, kuti ndichifunefune; ndicho kuti ndikhale mu nyumba ya AMBUYE masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwa AMBUIYE ndi kumafunsa mukachisi wake.
5 Pakuti mu nthawi yansautso iye adzandibisa ine mchipinda: ndipo m’chinsisi cha kachisi wake iye adzandibisa ine; iye adzandikhazika ine pa thanthwe.

Tsopano, Mulungu ali ndi njira yochitira zinthu. Ndipo Iye sasintha dongosolo Lake. Iye sasintha Zake... Iye ndi Mulungu wosasintha. Mu Amosi 3:7, Iye anati, “Iye sangachite kanthu padziko lapansi mpakana poyamba Iye atachiwulula icho kwa akapolo Ake aneneri.” Ndipo basi motsimikiza monga Iye analonjezera icho, Iye adzachita icho.

Tsopano, ife tapyola mu mibadwo ya mipingo. Koma ife talonjezedwa mu masiku otsiriza awa, malinga ndi Malaki 4, kuti padzakhala kubweranso, kwa mneneri mudziko. Izo ndi zolondola. Zindikirani khalidwe lake, ndi mmene iye ati adzawonekere. Mulungu akugwiritsa ntchito Mzimu umenewo kasanu: kamodzi mwa Eliya; mwa Elisha; ndi Yohane m’batizi; kuwutulutsa mpingo; ndi otsalira a Yuda. Kasanu, “chisomo,” (“grace,”)J-e-s-u-s (Yesu), F-a-i-t-h (chikhulupiriro), ndipo iyi ndi nambala ya chisomo. Mwaona? Chabwino.

Tsopano,kumbukirani, uthenga walonjezedwa. Ndipo pamene zinsinsi zonsezi zamangidwa mitolo ndi gulu la azipembedzo, zitengera mneneri wolunjika wochokera kwa Mulungu kukaawulula Icho. Ndipo ndimomwemo zimene iye analonjeza kuti iye achita. Mwaona? Tsopano,kumbukirani, “Mawu a Ambuye amadza kwa mneneri,” osati kwa ophunzira a za umulungu. Mneneri, iye ndi chinyezimiro cha Mawu a Mulungu. Iye sanganene kanthu; iye sanganene maganizo ake omwe. Iye akhoza kungolankhula zokhazo zomwe Mulungu akuulula. Ngakhale kwa mneneri Balamu pamene iye ankayesa kudzigulitsa,kugulitsa ufulu wake, iye anati, “Mneneri aliyense anganene bwanji chirichonse kupatula chimene Mulungu waika m’kamwa mwake?” Ndichinthu chimene Mulungu amachita, kuti iwe sunganene china chake. Ndipo iwe umabadwa mwanjira imeneyo.

Ngat iiwe ukanati, “Ine -sindingatsegule maso anga,” pamane iwe ukuyang'ana. Mwaona? Iwe siungathe. Sungathe kufikira dzanja lako, pamene ukhoza. Mwaona? Iwe siungakhale galu pamene uli munthu. Mukuona? Iwe unapangidwa chotero basi. Ndipo Mulungu wachita nthawi zonse momwemonso, m'mibadwo, kupyolera mwa Yesaya, Yeremiya ndi onse, Eliya, ndi m’mibadwo yapitayo. Pamene magulu azipembedzo amakhoza kusokoneza zinthu zonse, Iye amakhoza kutumiza mneneri, kumudzutsa iye kuchokera kosadziwika. Iye ndi woti asakakhale nawo m'zochitikazawo, ndipo nayankhula Mawu Ake. Nachotsedwapo pamalopo, ndipo napita, munthuuyu wolimba wa Choonadi cha Mulungu. Ndipo nthawi zonse ndi momwe inu mukanamudziwira iye. Iye anati, “Ngati akhalapo wina pakati panu amene ali wauzimu kapena mneneri....”

Tsopano, aneneri. Pali chinthu chonga “mphatso yauneneri” mutchalitchi; koma mneneri ndi wokonzedweratu ndi odzodzedweratu kwa oralo. Mwaona? Inde, bwana. Tsopano, ngati ulosi uchitika, awiri kapena atatu ayenera kukhalapo naweruza ngati zinali zolondola kapena ayi, mpingo usanalandire izo. Koma palibe amene angayime pamaso pa mneneri, chifukwa iye anali mtheradi Mawu a Mulungu. Iyeyo ndi Mawuwo mu tsiku lake. Mwaona Mulungu akuzinyezimiritsidwa... Tsopano, Mulungu walonjeza kuti atitumiziranso ife ameneyo mu masiku otsiriza, kuti adzatulut se Mkwatibwi yokuchokera mu chisokonezo cha zipembedzo, m’njira yokhayo imene zingachitikire.

Sizidzachitika konse; Mpingo siungamulandire Khristu. Ife, a chi Pentekoste, ife sitingapitirire ndi Uthenga uwu ndi chikhalidwe chomwe mpingo ulimo lero. Ife tingapitirire bwanji munthawi yotsiriza mu chikhalidwe chimene iwo alimo lero, pamene aliyense atsutsana ndi nzake, ndi china chirichonse, ndi mwa chipembedzo? O, chifundo! Ndi nyansi. Zapitiratu mu zipembedzo. Ndipo nthawi iriyonse... ine ndikufunsa wa zambiri yakale aliyense kuti anene chosiyana. Nthawi ili yonse pamene uthenga umafalitsidwa mu dziko lapansi, ndipo pamene iwo awupanga bungwe iwo umafera pomwepo. Ndipo a chi Pentekoste apanga zinthu zomwezo zimene ena onse anachita, a chi Pentekoste amene anatuluka.

Inu Assembliesof God, pamene azibambo anu akalewo ndi azimayi anu anatuluka mu mabungwe amenewo kalelo, mu General Council yakaleyo, anafuula nayamikira Mulungu, nayankhula motsutsa zinthu zimenezo. Ndipo inu munapotoloka, “ngati galu kumasanzi ake, ndi nkhumba kumatope ake,” ndikuchita chinthu chomwecho chimene iwo anachita. Ndipo tsopano mwa chipembedzo motero,inu mukutsekereza kukhuzika kwa mkati mwanu. Iwe uyenera kukhala ndi khadi lachiyanjano usanayanjane nawo, mpang'ono nkomwe.

Inu, aUmodzi, Mulungu anakupatsani inu uthenga chotero,ndipo mmalo moti mupitirire nawo kutsogolo, ndikumadzichepetsa ndi kupitapa tsogolo, munalekerera ndi kupanga ka bungwe ka gulu lanu. Ndipo inu nonse muli pati? Mu chidebe chomwecho. Ndi momwemo!. Ndipo Mzimu wa Mulungu, ukupitirirabe. “Ine Ambuye Ndadzala; Ine ndidzathirira icho usana ndi usiku. Kupangira kuti ena angadze....” Iye anadzodzeratu zinthu izi kuti zidzakhalepo, ndipo Iye ayenera kutumiza Izi.

Chinthu choyamba kudza, pamene Iye akuyamba kutsika kuchokera ku mwamba, kuli mfuu. Ndi chiyani icho? Ndi Uthenga,wobweretsa anthu palimodzi. Uthenga ukudza, choyamba. Tsopano, ndi nthawi yoyatsa nyali, “Dzukani ndipo muyatse nyali zanu.” Unali ulonda uti umenewo? Wa chisanundi chiwiri, osati wa chisanu ndi chimodzi. Wa chisanu ndi chiwiri, “Onani Mkwati akudza. Dzukani nimuyatse nyali zanu.” Ndipo iwo anatero. Ena aiwo anapeza kuti analibe ngakhale Mafuta munyali zawo. Mwaona? Koma ndi nthawi yoyatsa nyali. Ndi nthawi ya Malaki 4. Zimene Iye analo... Ndi Luka 17. Ndi Yesaya Maulosi onsewo kuti Izo zikakhale mwangwiro mudongosolo la tsiku ili. Mu malemba, ife ikuziona izo zikukhala momwemo. Palibe....

Kuona zinthu izi zikuchitika, M'bale wanga wokondedwa, Mlongo. Pamene Mulungu ku Mwamba akudziwa kuti ine ndikhoza kufa pansanja iyi pakali pano. Inu - Mungoyenera kuyenda mozungulira pang'ono. Izo basi.... Izo ndizopambana, pamene inu mukuona Mulungu akudza kuchokera kumwamba kuyima pamaso pa gulu la anthu, Ayima pamenepo, kudziwonetsa Yekha monga momwe Iye ankachitira. Ndipo icho ndi Choonadi, ndipo Baibulo ili lotsegulidwa. Mwaona? Kulondola. Ife tiripano.

Ndipo dongosolo la zipembedzo ndi lakufa. ilo lapita. Ilo silidzadzukanso. Ilo lidzawotchedwa. Umo ndi momwe inu mumachita ndi mankhusu kumunda. Thawani kwa izo. Kaloweni mwa Khristu. Musati “Ine ndine wa Methodisti. Ine ndine wa Baptisti. Ine ndine wa chi Pentekoste.” Inu mulowe mwa Khristu. Ngati inu muli mwa Khristu, palibe Liwu limene lalembedwa umu koma limene inu mumakhulupirira. Si ndikusamala zimene wina aliyense akunena. Ndiyeno Mulungu amapangitsa chinthu chimenecho kuonetseredwa. Chifukwa, inu, pamene iye Atsanulira Mzimu Wake pa Mawu, chimachitika ndi chiyani? Monga ngati kuthira madzi pambewu ina iriyonse. Iyo ikhala ndi moyo, ndipo ibala mtundu Wake.

Inu mukuti, “Ine ndiri ndi ubatizo, Mzimu Woyera.” Izo sizikutanthauza kuti iwe wapulumutsidwa. Ayi kutalitali ndithu. Tayang'anani kuno. Inu ndinu chinthu chapatatu. Inu muli. Mkati mwa kanthu kakang’ono aka muli solo, chotsatira ndi mzimu ndipo chotsatira ndi thupi. Tsopano, inu muli ndi zokhuzira zisanu mu thupi iri, kuti muzikhudzira kwanu kwa pansi pano. Izo sizimakhuza zina zonsezo. Inu muli ndi zokhuzira zisanu zamzimu mkatimu: chikondi ndi chikumbumtima, ndi zina zotero, zazimenezo. Koma mkati umu ndi momwe inu mumakhalamo. Ndi chomwe inu muli.

Kodi Yesu sanati, “Mvula imagwa pa olungama ndi osalingama”? Ikani chisoso apa, ndi tirigu apo, ndi kutsanulira madzi pa izo, ndi kuthirira fetereza ndi zinthu zotero, kodi zonsezo sizikhala moyo ndimadzi omwewo? Nzoona! Chabwino, ndi chiyani icho? Wina wa iwo adzabala chisoso, chifukwa ndicho chonse chomwe ali. Chisoso chidzakweza manja ake nachifuula basi chimodzimodzi ngati tirigu.

Kodi Baibulo silimanena, “M'masiku otsiriza,kudzabwera a Khristu onyenga osati ”a Yesu onyenga,“ tsopano. ”A Khristu onyenga,“ odzozedwawo, odzozedwa monyenga ku Mawu; odzozedwa Mwa chipembedzo, koma osati ku Mawu. Pakuti, Mawu adzazichitira okha umboni. Iwo sasowa china chirichonse. Iwo adzazichitira okha umboni. ”Ndipo kudzabwera odzozedwa monyenga.“ Inu muli nayo tepi yanga pa izo. Ndipo awo odzo.... O, ngati mungayitane mmodzi waiwo, nkunena, ”O, inu, kodi ndinu Yesu?“ ”O, ndithudi ayi.“ Iwo sanakhoza kuimira izo. Koma pamene ziti zibwere pakuti, ”O, ulemerero! Ine ndiri ndi kudzoza!“ Ndipotu ndi kudzoza kweni kweni.

Kumbukirani, Kayafa anali nakonso, ndipo ananenera. Chimodzi modzinso Balam anali nako, ndipo ananenera. Koma izo ziribe chochita ndi ichi, mkatimu. Pokhapokha ngati iyo iri mbewu ya Mulungu, kambewu kake kuchokera pachiyambi, kokonzedweratu, Inu mwatha. Ine sindikusamala kuti mwafuula motani, kulankhula ndi malirime, kuthamanga, kufuula. Zimenezo ziribe chochita ndi ichi. Chisoso chikhoza kuwerenga chimodzimodzi ndi momwe ena onsewo. Ine ndawonapo achikunja akudzuka, nafuula, nalankhula m'malirime, ndipo namamwa magazi kuchokera muchigaza chamunthu, naitanira pa mdierekezi. Mwaona? Kotero inu simunga... zirizonse zazotengeka ndi zinthu, iwalani izo. Ndi mtima wanu mu mawu amenewo, ndipo iwo ndi Khristu. Alowetseni iwo mmenemo, ndipo yang’anani Iwo akudzipangitsa okha kudziwidwa, basi monga Iyo imatseguka ngati mbewu ina ili yonse, ndikuzilengeza Yokha kwa m'badwo omwe Iyo ikukhalamo.

Luther sakanadza ndi kena kalikonse koma timphukira. Enawa akanadzabweretsa zinthu zinazi. Ife tiri mu m'badwo wa tirigu tsopano. A Luterani enieni a Luterani anayenera kubala Luterani weniweni. Pentekoste yeniyeni inayenera kubala Pentekoste yeniyeni. Ndizo zomwezo. Koma ife tapyola m'badwo umenewo, ndipo tikupirirabe. Inu mukudziwa, mpingo wa Katolika anayambitsa chi Pentekoste? Ndipo ngati mpingo wachi Pentekoste utati ukhalepo zaka zikwi ziwiri, udzakhala mmaonekedwe oyipa kuposa momwe Katolika aliri pano. Ndizo ndendende. Ine ndikunena izo kuti abale anga, alongo anga amene ine ndimawakonda. Ndipo Mulungu akudziwa izo. Koma kumbukirani, amzanga, ine ndiyenera kudzakumana nanu kutsidya pachiweruzo. Ndipo ilo mwina silingakhale kale kwambiri. Ine ndiyenera kuchitira umboni wa chomwe chiri choonadi.

Pamene ine ndinapita m’misonkhano ndiinu, kupempherera odwala, zinali zabwino. Koma pamene ine ndikudza ndi Uthenga! Ngati Uthenga aliwonse ufika, uwo ndi Uthenga woona.... Ngati izo ndi zozizwitsa zenizeni zoona za Mulungu, ndipo nangokakamira mu bungwe lomwelo, inu mudziwa kuti siza Mulungu, chifukwa chinthu chimenecho chawonetsedwa kale. Yesu anapita kukachiritsa odwala, ndi cholinga choti akope maso awo, anthu, kenako Uthenga wake. Uko nkulondola.

Izo ziyenera kukhala china chake chimene Mulungu ati achionetsere. Machiritso auzimu, zozwizwitsa Zake monga izo, zimangokopa maso a anthu. Mtima wake wa izo ndi Uthenga. Apo ndi pamene pali, ndi chomwe chikuchokera m’katimu. Iye akuyesa kupeza kukonderedwa ndi anthu, kuti iwo akhoze kukhala namumvera Iye, mwaona, pakuti pali ena m'menemo amene ali odzozedwera ku Moyo. Ndipo njere zina, tirigu,anagwera pa nthaka, mbalame zinadzazitola izo. Ndi zina zinagwera paminga. Ndipo zina zinali, zinapita panthaka yokonzedwa, nthaka yokonzedweratu ndipo zinabereka.

Tsopano, chinthu choyamba, ndikuwomba. -kapena chinthu choyamba ndi lipenga ndi kapena liwumfuu; ndipo kenako Liwu; ndipo kenako lipenga. Mfuu: wamthenga kuwapangitsa anthu kukhala okonzeka. Cha chiwiri ndi liwu la chiukitsiro: liwu lomwero, limene, liwu lofuula mu Yohane Woyera 11:38 mpaka 44, limene linamuitana Lazaro kuchokera mmanda. Kubweretsa Mkwatibwi palimodzi; ndipo kenako chiukitsiro cha akufa, Mwaona; kuti akwatulidwe nawo. Tsopano penyani zinthu zitatu zozikuchitika. Chotsatira ndi chiyani? Linali lipenga. Liwu... Mfuu; Liwu; Lipenga.

Tsopano, chinthu cha chitatu, ndi lipenga,chimene, nthawi zonse, pa phwando la malipenga, ndi kuitanira anthu ku phwando. Ndipo umenewo udzakhala m'gonero wa Mkwatibwi, mgonero wa Mwana wa Nkhosa ndi Mkwatibwi, mu mlengalenga. Mwaona, chinthu choyamba kubwerapo ndi Uthenga Wake, kuitana Mkwatibwi pamodzi. Chinthu chotsatira ndi chiukitsiro cha Mkwatibwi wogona; amene anafa, m'mbuyomo m'mibadwo yina, iwo akudzakwatulidwa limodzi. Ndipo lipenga, Phwando m’miyamba, mu mlengalenga. Chifukwa, ndicho chinthu chomwe chiti chidzachitike, amzanga. Ife tiri pamenepo kumene, okonzeka tsopano. Chinthu chokhacho, mpingo umene ukutuluka, uyenera kukhala pamaso pa Mwana kuti ukhwime. Chokolola chachikulu chidzabwera kuno pakangopita kanthawi. Tirigu adzawotchedwa, mapesi, koma mbewu zidzasonkhanidwira mu nkhokwe Yake.

Werengani akaunti yonse mu... Mkwatulo.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.

Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo m’mitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya.

N’chifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

1 Atesalonika 4:16-18


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Madzi ochokera
m’thanthwe.

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

Pearry Green personal
testimony.

(PDF Chingerezi)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.