Ululu wa Kubala.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Kumwamba kwatsopano. Dziko latsopano.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Ululu wa Kubala.Tsopano, ine ndikufuna kuti- kuti ndiyankhule madzulo ano pa phunziro limene ine ndinalirengeza: Ululu wa Kubala. Tsopano, izozikumveka moipa kwambiri, koma izo ziripo mu Baibulo. Ine ndikukhulupirira kutiYesu apa anali kuyankhula za, pamene Iye ankati, “Inu mudzakhala ndizodandaula, koma kudandaula kwanu kudzasanduka chimwemwe ,” akuyankhula kwaophunzira Ake apa, podziwa kuti kubadwa kwa- kwa ChiKhristu kunali kutayandikirakuti kuchitike.
Ndipo tsopano chakale chiyenera kutichife, polinga kuti chatsopano chibadwe. Kuti ukhale ndi chirichonse chimenechimabala, umayenera kuti ukhale ndi ululu wa kusautsika. Ndipo ntheradi analikuti adutsa muululu wa kusautsika ndi kuwawa, kuti achoke ku chilamulo kupitaku chisomo. Kubadwa,kwabwino kwa chirengedwe kumaimira Kubadwa kwauzimu. Zinthu zonse zachirengedwe ndi zoimira chauzimu. Ndipo ife tikupeza apa, ngati ife tiyang'anakunja uku pa- pa nthaka, nkuuwona mtengo mu nthaka, ukumera, iwo ukuvutikirakuti ukhale moyo. Izo zimasonyeza kuti kuli mtengo, kwinakwake, umene sumafa,chifukwa iwo- iwo ukulirira chinachake. Ife timawapeza anthu, ziribe kanthumomwe aliri okalamba, aliri odwala, chikhalidwe chotani, iwo akulirira, kutiakhale moyo, chifukwa izo zimasonyeza kuti kuli moyo kwinakwake kumene ifetimakhala moyo, kukhala moyo kwa nthawizonse. Zindikirani momwe ziririzangwiro.
Tsopano,mu Yohane Woyamba 5:7, ine ndikukhulupirira apo pali, ngati ine sindirikulakwitsa, Ilo limati, “Alipo atatu omwe amachitira umboni Kumwamba: Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera; atatu awa ali M'modzi. Ziripo zitatu zomwe zimachitiraumboni padziko lapansi, ndizo madzi, Magazi, ndi Mzimu, ndipo izo zimagwirizanamu chimodzi.” Tsopano zindikirani. Zoyamba zitatuzo ziri Chimodzi. Zitatuzachiwirizo ndi zapadziko, zomwe zimagwirizana mu chimodzi. Simungakhozekukhala ndi Atate popanda Mwana; simungakhale ndi Mwana popanda kukhala ndiMzimu Woyera. Koma inu mukhoza kukhala ndi madzi popanda kukhala ndi Magazi, ndipo ndi Magazi popanda kukhala ndi Mzimu.
Inendikuganiza, podutsa m'mibadwo yathu, yatsimikizira izi kuti ndi zoona; madzi, Magazi, Mzimu; kulungamitsidwa, kuyeretsedwa, ubatizo waMzimu Woyera. Izo zimaimira, kapena zimapanga.... Kapena, ndi choimiridwacho, zomwe zimatengera pa kubadwa kwachirengedwe. Taonani pamene m- mkazi kapenachirichonse chiri mu kuvutika, pofuna kubala. Chinthu choyamba chimene chimafika pochitika, kuswekakwa madzi, kubala kwabwino bwino; chinthu chachiwiri ndi magazi; ndiyenopamabwera moyo. Madzi, magazi, mzimu; ndipo izo zimapangitsa kubadwa kwabwinobwino, kwa chilengedwe.
Ndipo ndi momweizo ziriri mu dera lauzimu. Ndi madzi; kulungamitsidwa mwa chikhulupiriro, kukhulupirira pa Mulungu. Kumulandira Iye ngati Mpulumitsi wakowako, ndikubatizidwa. Chachiwiri, ndi kuyeretsedwa kwa mzimu, kuti Mulungu amauyeretsamzimu ku zinthu zonse za mdziko, ndi chinkhumbo cha mdziko. Ndiyeno Mzimu Woyera umabweramo ndi kudzapereka Kubadwa kwatsopano ndi kudzazitsa chotengerachoyeretsedwacho.
Mwachitsanzo, monga chonchi. Tsopano, poti, ine ndinakuuzani inu. Zomwe inusimukuzikhulupirira, muziyike pambali, ndi kumadya mkatewo. Zindikirani. Tsopano, tambula ili uko mu khola la nkhuku. Inu simumangokaitola iyo ndikudzaiika pa tebulo panu ndi kuidzazitsa iyo ndi madzi kapena mkaka. Ayi. Kuitola iyo apo, ndi kulungamitsidwa. Kuitsuka iyo, ndi kuyeretsedwa, chifukwamawu Achigriki kuyeretsa ndi mawu apawiri, omwe amatanthauza “kutsukidwa, ndikuikidwa pambali kuti idzagwirirtsidwe ntchito.” Osati kukhala ili mu ntchito;kuti idzagwiritsidwe ntchito. Ndiye pamene inu muidzazitsa iyo, iyo imaikidwamu ntchito.
Mukhululukireichi tsopano, osati kuti ndikupwetekeni. Apo ndi pamene inu a Pilgrim Holiness, Anazerini mukulepherera kuti muyendebe mpaka ku Pentekoste. Inu munatsukidwamwa kuyeretsedwa; koma pamene inu munali okonza kuti muikidwe mu ntchito, ndimphatso za kuyankhula mu malirime ndi zinthu zina, inu munaikana iyo, munakagwera mbwerera mu kholamo kachiwiri. Mwaona? Tsopano, ndizo - ndizo zomwezimachitika. Izo nthawizonse zimachita izo. Tsopano, si kuti ndikutsutseni inutsopano, koma basi ine - ine ndikufuna kuti ndizichotse izi mu mtima mwanga. Ndipo izo zakhala zikundiwotcha inenthawi yonse yomwe ine ndakhala ndiri kuno, kotero ine ndibwino ndingotere. Basi, ngati chisomo cha Carl, ndi Demos ndi iwo, ndi cha inu nonse, ine - inendiyesera mwakukhoza kwanga kuti ndipulumutse solo yanga kwa izo, onani, ndiyeizo ziri kwa inu.
Kwabwinobwino, kuimira kwa uzimu. Tsopano, ife tikupeza apa ndiye, ndipo iye wabadwakwathunthu. Pamene mwana, kawirikawiri.... Tsopano pamene madzi atuluka, inusimumasowa kuti muchite zochuluka kwambiri nawo iwo. Ndipo pamene magaziakutuluka, simuyenera kuchita mochuluka pa izo. Koma polinga kuti mulowetsemoyo mwa mwanayo, inu mumayenera kuti mumumenye iye kakhofi, ndi kumupangitsaiye kuti alire. Ndipo ndizo.... Tsopano, mopanda maphunziro, monga abale angapano ali ophunzitsidwa bwino kwambiri kwa izo, zawozo, koma ine ndimayenerakutenga chirengedwe kuti ndizifanizitse izo. Ndipo apo inu muli. Ndizo zomwezinachitika. Izo zinatengera kumenya kwenikweni, kuti awulowetse uwu kwa iwo.
Tsopano, inu mumatenga pang'ono pa, mtundu wina wa kugwedeza. Mwinamwake, simusowakuchita kumumenya iye, koma kungomugwedeza iye pang'ono. Lingaliro lomwe laiye, pokhala akubadwa, nthawizina, limachita izo. Kumugwira iye, kumugwedezaiye. Iye akapanda kuyamba kupuma, kummenya iye pang'ono, ndiyeno iye amaliraapo, mu malirime osadziwika, kwa mwinawake, ine ndikulingalira. Koma, iye -iye, mulimonse, ndipo iye akupanga phokosotu. Ndipo ine ndikuganiza ngati mwanaabadwa basi - wozizira, wopanda phokoso, wopanda kugwedezeka, ameneyo ndi mwanawakufa.
Ndi lomweliri vuto ndi mpingo lero, kachitidwe; ife tiri ndi ana ochuluka kwambiri ali obadwaakufa. Ndiko kulondola. Iwo akusowa kumenya kwa Uthenga, inu mukuona, ndichotero kuti muwadzutse iwo, kuti iwo atsitsimuke, kotero kuti Mulungu akhozekupumira mpweya wa Moyo mwa iwo. Ndipo tsopano ife tikupeza kuti izo ndi zoonakwambiri. Iyo ndi phunziro la za umulungu lophweka, koma ndi Choonadi, mulimonse.
-----
Ifetimauzidwa ndi aneneri a Mulungu kuti ndife oti tikhale nalo dziko latsopano, Kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano. Ngati inu mukufuna Lemba la izo, ndiChivumbulutso 21. Ine ndikhoza kubwerezera izo kwa inu, ndiri nazo izo apa.Yohane anati: “Inendinawona Kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano pakuti kumwamba koyamba ndidziko loyamba zinachoka.” [Izozinali zitapita.]Tsopano, ngati ife titi tikhale ndi dzikolatsopano, dziko lakale ndi dziko latsopano sizingakhoze kukhalapo pa nthawiyomweyo. Kapena, dziko latsopano ndi dziko lakale sizingakhoze kukhalapo panthawi yomweyo. Sipangakhoze kukhala machitidwe awiri a maiko limodzi pa nthawiyomweyo. Tsopano, polinga kuti tikhale ndi dziko latsopano, lakalelo liyenerakuti life. Tsopano, ngati lakalelo liyenera kuti life, ndiye kuti ilolikupereka ululu wa kubala kwa latsopanolo tsopano.
Ndiyenongati dotolo akanapita kukamupima wodwala yemwe anali mu kuvutika tsopano, a... chimodzi cha zinthu zomwe dotoloyo akanachita. Pomwe, ine ndikuyankhula mukukhalapo kwa awiri kapena atatu, ine ndikuwadziwa, madotolo abwinoazamankhwala pano, madotolo AchiKhristu. Ndipo ine - ine - ine ndikanakufunsaniinu ichi. Chimodzi cha zinthu zoyambachomwe dotolo amachita, iye akatha kumuyang'anira wodwalayo, ndi kudziwa nthawiza ululuwo, ululu wa kubala. Iye amadziwa nthawi za ululuwo, momwe iwo uliri moyandikirana mwake,ndi kuchuluka kwa kuwopsya kulikonse kukufikapo. Kumodzi kuli kovuta kwambirikukhala nako kuposa kwinako. Kwina kotsatirako, kovutirako, kovutirabe, kufikamoyandikana limodzi. Ndi momwe iye amafufuzira vutolo, ndi ululu wa kubalako.
Chabwino, ngati dziko lingati lipereke njira ku kubadwa kwa dziko latsopano, tiyenitingofufuza ululu wa kubala wina womwe ife tikumakhala nawo pa dziko lapansi, ndiyeno ife tiwona za tsiku ndi utali womwe ilo lakhala liri kupitirira mukuvutika kwake.
NkhondoYoyamba ya Dziko lonse inasonyeza ululu waukulu wa kubala. Iyo inasonyezaumodzi wa ululu woyamba wa kubala wa ilo wa kukalowa mu kuvutika. Chifukwa chanthawi iyo kwa ilo, ife tinali titabweretsapo mabomba, ndipo ife tinali ndimufti zamakina, ndi mpweya wa chiphe. Ndipo inu mukukumbukira mwinamwake ambiriainu simungakumbukire. Ndinali mnyamata wam'ng'ono chabe wa pafupi usinkhu wazaka eyiti, koma ine ndikukumbukira iwo akuyankhula za mpweya wa mpiru ndikhlorini, ndi zina zotero. “Momwe zimaonekera ngati zangoyamba kumene ndi,” iwoanati, “izo zikanaliwotcha dziko lonse lapansi. Izo zikanamupha aliyense. Chabwino, izo zikhoza kukhala - ku - kuswa kwa izo, basi mpheponkungozikupizira izo kudutsa pa dziko lapansi.” Ndi momwe aliyense ankachitiramantha pafupi kufa ndi chida chachikulu icho cha mpweya wa chiphe! Dzikolinadutsa, linali nawo ululu wake woyamba wa kubala.
Ndipo ifetikupeza tsopano, ife tinali nayo nkhondo yachiwiri, Nkhondo ya mu Dziko lonse,ndipo ululu wake unali wawukulupo kwambiri. Izo zimakhala zowopsya kwambirinthawizonse, ululu wa kubala kwa dziko lapansi. Ilo linali pafupifupi kuti lipereke njira, mu nthawi ya bomba laatomiki, chifukwa ilo likanawononga mzinda wonse. Izo zinali zazikulupokwambiri kuposa ululu wa Nkhondo Yoyamba ya Dziko Lonse, ya chiwonongeko chadziko.
Tsopano, ilo likudziwa kuti nthawi yake ya chiwombolo ili pafupi. Nchifukwa chake iloliri lamanjenje kwambiri, lokhumudwitsidwa, monga ilo liri, nchifukwa cha kutipali bomba la haidirojeni, ndi mizinga ya mu mlengalenga yomwe ingakhozekuliwononga dziko lonse. Fuko linalikuwopa limzake, ziribe kanthu momwe ilo liriri laling'ono. Iwo ali nayo mizinga iyo yomweiwo akudzinenera kuti idzangoti.... Imodzi ya iwo. Iwo akhoza kuyilunjika iyomoonera nyenyezi ndi kuyigwetsera iyo paliponse mu dziko kumene iwo akufunakutero.
Russia,monga ine ndinama pa nkhani, tsiku lina, iye akudzinenera kuti akhozakuliwononga dziko lino, ndi - ndi kuletsa maatomu kapena zinthu kutizisawononge fuko lake. Ife sitikudziwa choti tichite nazo izo. Aliyenseakupanga kudzinenera uku, ndipo ziri chomwecho. Sayansi ya anthu yalowerera mulaboratare yaikulu ya Mulungu, mpaka iwo adziwononga okha. Mulungu amalola, nthawizonse amalolanzeru izidziwononge yokha. Mulungu samawononga chirichonse. Munthu amadziwonongayekha ndi nzeru, monga iye anachitira pachiyambi, potenga nzeru za Satana mmalomwa Mawu a Mulungu.
-----
Kotero ilo silingakhoze kupilira izo. Anthuakudziwa kuti ilo silingapilirebe ku izo. Ndipo dziko likudziwa kuti iwoakupita koti, izo zichitika. 36 Pakuti,Mulungu anati izo zinali. “Miyamba yonse ndi dziko lapansi zidzakhala zikuyakamoto.” Kudzakhala kukonzanso kwa chinthu chonsechi, chotero kuti dzikolatsopano likhoze kubadwa. Mulungu ananenera izo.Ilolavunda, mu kachitidwe kake konse, ndipo ilo liyenera kuti lichite izo, kutilivunde nilichokapo. Nchifukwa chake ilo, ine ndinati, ilo liri lamanjenjekwambiri ndi lofiira pa nkhope, ndi lokhumudwitsidwa. Ndipo zivomezi, zirikonsekonse, ndipo kukwera - ndi - kutsika gombe. Ndi mafunde aakulu mu Alaska,ndipo akugwedeza chokwera - ndi - chotsika gombelo, ndi zivomezi ndi zinthu. Ndipo anthu akumalemba, “Kodi tichokeko uko? Kodi tichokeko uko?” Mwaona? Iwosakudziwa choti achite. Palibe malo otetezeka kupatula Amodzi, ndiwo Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo. Ndipo pali chinthu chimodzi chokha chomwe chiri malootetezeka, ndipo awo ali iyeyo. Onse a kunja kwa Awo adzawonongeka, motsimikizabasi monga Mulungu ananena chomwecho.
Tsopanotiyeni tiyang'anen pa Buku la Adotolo, ngati iye ali mu mtundu uwu wachikhalidwe, ndipo tiwone ngati izi zikuyenera kuti zichitike pamene dzikolatsopano likuti libalidwe. Mateyu 24, mu Buku la Dotolo, lomwe liri Baibulo, ndipo tiyeni tiwone zomwe zinaneneredwa, zomwe zisonyezo zake ziti zikhale. Tsopano,ngati dotolo adziwa zisonyezo za kubadwa kwa mwana.... Ndipo basi pafupi nthawiyoti mwanayo abwere, iye amakonzekeretsa chirichonse, chifukwa iye amadziwakuti iyo ndi - nthawi yoti mwanayo abadwe. Chifukwa, zisonyezo zonsezikusonyeza; ma - madzi aphulika, magazi. Ndipo tsopano.... Ndi nthawi. Mwanayowagwetsedwa, ndipo ndi nthawi yoti mwanayo abadwe. Ndipo chotero iyeamakonzekeretsa chirichonse cha izo.
Tsopano,Yesu anatiuza ife ndendende basi zomwe zikanati zidzachitike basi pa nthawiino. Iye anatiuza ife, mu Mateyu 24, kuti Mpingo, Mpingo woona, ndi mpingowinawo, ukanadzakhala uli.... Mpingo wachirengedwe, Mpingo wauzimu, “Ukanadzakhala uli wapafupi kwambiri limodzi, otsanzira mpaka iwoukanadzanyenga osankhidwa omwe, ngati kukanakhala kotheka.” Momwe izo zinalirimu masiku a Nowa, “Momwe iwo anali kudyera, kumwa, kukwatira, kuperekedwa muchikwati,” ndi kupanda makhalide konse uku kwa mdziko komwe ife tikukuwonalero. Baibulo, Buku, Buku la Dotolo linati izo zikanadzachitika. Kotero, pameneife tikuziwona izi zikuchitika, ife tikudziwa kuti kubadwa kuli pafupi. Izoziyenera kukhala ziri. Inde, bwana.
-----
Chiyani? Mpingo uwu ukudutsa mu ululu wa kubala. Kodi inu simupanga kusankha kwanutsopano mu Kukhalapo Kwake? Ine ndakusonyezani inu ndendende Mawu, zomwe Iyeanati Iye akanadzamachita. Kusesa kudutsa mu chipinda chino, mufunseni aliyenseyemwe anayamba wakhudzidwapo, kapena anayankhulidwapo, Kapena chirichonsechomwe chinali, ndikuona ngati ine ndiyamba ndawaonapo iwo, kuwadziwa iwo, kapena chirichonse cha iwo. Inu mukuganiza kuti munthu angakhoze kuzichita izo? Izo ndi zosatheka kwathunthu kuti izo zichitike. Chabwino, ndi chiyani Icho? Mwana wa munthu. “Mawu a Mulungu ndi okuthwa kuposa lupanga lakuthwakonsekonse, ozindikira za mu mzimu, zinsinsi za m'mitima.” Ndendende basi momweIzo zinaliri pamene Iwo anapangidwa thupi kuno pa dziko lapansi, mwa Mwana wa Mulungu, tsopano Iwo wakhala ukuululudwa ndi Mwana wa Mulungu pamene Iye wabwerakuti adzaitane Mkwatibwi kuchokera ku kachitidwe ako.“Tulukani mwa izo. Khalani olekanitsidwa, atero Mulungu. Musakhudze konse zinthu zawo zosayerazo, ndipo Mulunguakulandirani inu.” Kodi inu mwakonzeka kuti mupereke moyo wanu wonse kwa Mulungu? Ngati inu muli, imirirani pa mapazi anu, ndi kuti, “Ine nditero, mwachisomo cha Mulungu, ndikuvomereza Izo pakali pano, mwa zonse zomwe ziri mwaine.”
Werengani akaunti yonse mu... Ululu wa Kubala.