Nkhondo yaikulu imene yakhala ikumenyedwa.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Malo a nkhondo. Mmalingaliro a munthu.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Nkhondo yaikulu imene yakhala ikumenyedwa.Tsopano, nkhondo iliyonse isanayalidwe, iwo poyamba amayenera kuti asankhe bwalo lokomaniranapo, kapena malo amene nkhondoyo iti ikamenyedwere, malo osankhidwa. Mu Nkhondo Yoyamba ya Dziko Lonse, iyo inaikidwa chomwecho, ku malo opanda mwini ndi kumalo kumene iwo ankamenyanako. Ndipo iwo amayenera kukhala malo ochita kusankhidwa. Monga pamene Israeli anapita ku nkhondo ndi Afilisiti, uko kunali phiri kumbali iliyonse kumene iwo anakasonkhanako. Ndipo uko ndi kumene Goliati anatulukirako ndipo naitanira pa ankhondo a Israeli. Uko ndi kumene Davide anakomana naye iye, mu chigwa, pamene iye anadutsa ka mtsinje kakang'ono kamene kamayenda pakati pa mapiri awiriwo, iye anatolako miyala. Apo pamayenera kusankhidwa malo.
Ndipo mu izi, pamakhala-malo ogwirizana, dziko lopanda mwini, ndipo iwo amakamenyana pa malo amenewa. Iwo sikuti amangoti, wina amenyera apa, ndi wina akamenyera uko, ndi wina kuthawira uko. Pamakhala bwalo la nkhondo kumene iwo amakakomanako ndipo amakayeserako zida zawo, kumene ankhondo aliwonse amakayeserako mphamvu zawo mofanizitsa ndi ankhondo enawo, malo ogwirizana okomaniranapo. Tsopano, musati (mufike) pophonya izi.
Pamene nkhondo yayikulu iyi inayambika padziko lapansi, pankayenera kuti pakhale malo ogwirizana oti akakumanepo. Pankayenera kuti pakhale malo osankhidwa kuti nkhondoyo ikayambikirepo, ndi akuti nkhondoyo ikamenyedwerepo. Ndipo malo a nkhondo amenewo anayambikira mmalingaliro a munthu. Umo ndi mmene nkhondoyo inayambikira. Mmalingaliro a munthu munasankhidwa kuti mukhale malo a nkhondoyo, mmene iyo inayambikira, ndipo izo zinali choncho chifukwa chakuti zigamulo zimapangidwa kuchokera mmalingaliro, mmutu. Tsopano, iwo sanakaiyambitse iyo kuchokera ku bungwe linalake. Iwo sanakaiyambitse iyo kuchokera ku zochitika zina za zipangizo. Malowo sanayambikire kumeneko. Choncho, bungwe limenelo silingathe nkomwe, kugwira ntchito ya Mulungu, chifukwa mabwalo a nkhondo, kumene iwe umayenera kuti ukakomane ndi mdani wako, ndi mmalingaliro. Iwe umayenera kuti upange kusankha kwako. Izo zimakakupeza iwe.
Ine ndikufuna msungwana wamng'ono uyu apa, yemwe akudwala kwambiri, kuti amvetsere kwa izi tsopano, mwatcheru kwenikweni.Zigamulo zimapangidwira mmalingaliro, mmutu. Umo ndi mmene Satana amakakomana ndi iwe, ndipo zigamulo zimakhalamo, chifukwa chakuti Mulungu anamupanga munthu mwanjira imeneyo. Tsopano, ine ndiri ndi (ngati inu mukanati mukuyang'ana pa cholemba changa apa) mapu aang'ono amene ndawajambula apa. Ine ndinali nawo iwo kuno osati kale kwenikweni, pa... ndinawagwiritsa ntchito pa bolodi. Munthu anapangidwa ngati njere ya tirigu. Iyo ndi mbewu. Ndipo munthu ndi mbewu. Mwachithupi, ndinu mbewu ya bambo anu ndi amanu; ndipo moyo umachokera kwa bambo, chimnofu chimachokera kwa amayi. Chotero, awiriwo, limodzi, dzira ndi... magazi, amabwera pamodzi. Ndipo mu khungu la magazi mumakhala moyo. Ndipo mmenemo mumayambika, kupangika, kupanga... mwanayo.
Tsopano, mbewu iliyonse imakhala ndi chikhungwa kunjako; mkatimo mumakhala chimnofu; ndipo mkati mwa chimnofucho mumakhala nyongolosi ya moyo. Chabwino, umo ndi momwe ife tinapangidwira. Ife tiri thupi, moyo, ndi mzimu. Chakunjachi, thupi, chikhungwa; mkati mwa icho, chikumbumtima ndi zina zotero, ndi moyo; ndipo mkati mwa moyomo, mumakhala mzimu. Ndipo mzimu umalamulira zina zonsezo.
Tsopano, ngati inu mungati mukakhale pansi pamene inu mukafike kwanu, ndipo mukajambule mikombero itatu yaing'ono. Inu mukapeza kuti thupi lakunjalo liri ndi zokhudzira zisanu zomwe ilo limakhudzidwira nazo, ndipo zimenezo ndi kupenya, kulawa, kukhudza, kununkhiza, kumva. Zimenezo ndi zokhudzira zisanu zimene zimalamulira thupi la munthu.
Mkati mwa thupilo muli moyo, ndipo moyo umenewo umalamuliridwa ndi kuganizira, chikumbumtima, kukumbukira, kulingalira, ndi kukonda. Ndicho chinthu chimene chimalamulira moyo. Koma, mzimu, uli ndi chokhudzira chimodzi chokha. Mzimu... O, tiyeni tichipeze icho. Mzimu uli ndi chokhudzira chimodzi, ndipo chokhudzira chimenecho ndi, chimodzi chimalamulira, ndi chikhulupiriro kapena kukaikira. Ndizo ndendende. Ndipo ulipo mpita umodzi wokha wofikira kwa iwo, umenewo ndi ufulu wochita zimene ukufuna. Iwe ukhoza kuvomereza kukaikira kapena iwe ukhoza kuvomereza chikhulupiriro, chimodzi chirichonse chimene iwe ukuchifuna kugwirirapo ntchito. Choncho, Satana anayambira pa gawo loyambiriralo, kuti akapangitse mzimu wa munthu kuti ukaikire Mawu a Mulungu. Mulungu anayambira gawo lofunikiralo, kuti akayike Mawu Ake mwa mzimu umenewo. Ndi zimenezotu. Ndi chimene chimachita izo.
Ngati mpingo uno, pakali pano ungathe kuikidwa pamodzi, ndi kulukana pamodzi mwakuti munthu aliyense nkukhala mu mtima umodzi, popanda mthunzi umodzi wa kukaikira paliponsepo, apo sipangakhale munthu wofooka pakati pathu, mu maminiti faivi enawa. Sipangakhale aliyense pano wokhumba Mzimu Woyera koma amene angaulandire Iwo, ngati inu mutangokonza chinthu china icho.
Tsopano, apo ndi pamene nkhondo imayambikira, mmalingaliro mwanu kumene, kaya inu mufuna. Tsopano kumbukirani, si Sayansi ya Chikhristu, tsopano, malingaliro kuposa zowoneka. Izo ziribe... Malingaliro amavomereza Moyo, umene uli Mawu a Mulungu, ndipo pamenepo umabweretsa Moyo. Maganizo anu okha samachita zimenezo. Koma, Mawu a Mulungu, akabweretsedwa mu mpita wa malingaliro anu. Mukuona? Si ganizo, monga Sayansi ya Chikhristu imapangira izo, malingaliro kuposa zowoneka. Ayi. Izo si zimenezo.
Koma, maganizo anu amawavomereza Iwo. Iwo amawambwandira Iwo. Kodi maganizo anu amalamuliridwa ndi chiani? Mzimu wanu. Ndipo mzimu wanu umawagwira Mawu a Mulungu, ndipo icho ndicho chinthu chimene chiri ndi Moyo mwa Icho. Icho chimaubweretsa Moyo mwa inu. O, m'bale! Pamene izo zichitika, pamene Moyo ubwera kudzera mu mpita umenewo, kubwera mwa inu, Mawu a Mulungu amawonetseredwa mwa inu. “Ngati inu mukhala mwa Ine, ndi Mawu Anga mwa inu, ndiye mupemphe chimene inu mukufuna ndipo chidzaperekedwa kwa inu.”
Ndiye ndi chiani chimachita zimenezo? Kuyambira pakati pa mtima, pamene pali moyo, kuyambira pamenepo pamatulutsa, nkumadyetsera mpita uliwonsewo. Pali vuto ndi pakuti, ife timaima apa ndi kukaikira kochuluka, timayesera kuti tilandire zimene ziri kunja uko. Inu muyenera kusiya zimenezo; ndipo mubwere chotsika mpita umenewo ndi Mawu owona a Mulungu, ndiyeno izo zimatuluka, zokha zokha, mosadzipangitsa. Ndi chimene chiri mkatimo. Ndicho chinthu chimene chimapangitsa izo, ndi cha mkaticho. Mafikidwe a Satana amakhala ochokera mkati.
Tsopano, inu mukuti, “ine sindimaba. Ine sindimamwa. Ine sindimachita zinthu zimenezi.” Zimenezo ziribe chochita chirichonse ndi icho. Mukuona, ndi chamkatimo. Ziribe kanthu kuti ndinu wabwino bwanji, ndinu wamakhalidwe bwanji, ndinu wachilungamo bwanji, zinthu zimenezo zimalemekezedwa. Koma Yesu anati, “Kupatula ngati munthu abadwa kachiwiri.” Mukuona? Payenera kukhala chinachake chochitika mkati. Ngati iwe sutero, zimenezo wangoziveka, pakuti pansi mu mtima mwako iwe umakhumbira utazichita izo mulimonse.
Izo sizingakhale zongoziveka. Izo ziyenera kukhala chenicheni. Ndipo ulipo mpita umodzi wokha umene ungatsikire mmusi, ndipo zimenezo ndi mwanjira ya kuchita mwakufuna kwako, kubwera mu moyo, mwa malingaliro ako. “Monga mmene munthu alingalira mu mtima, chomwecho iye ali.” “Ngati inu mudzanena kwa phiri ili, 'Suntha,' ndipo nkusakaikira mu mtima mwanu, koma kukhulupirira kuti chimene inu mwanena chichitika, inu mukhoza kulandira zimene inu mwanena.” Mukumvetsa zimenezo? Ndi zimenezotu. Mukuona? Ndi amenewotu malo ankhondo. Ngati inu mutangoziyambitsa zimenezo, poyamba.
Ife timakhala ndi chidwi kuti tiziwone zinthu zikuchitika. Ife timakhala ofunitsitsa kuti timuchitire Mulungu chinachake. Dona wamng'ono uyu sikuti... ndi wofunitsitsa, mopanda kukaikira, akufunitsitsa kuti akhale moyo. Iye akufuna kuti akhale bwino. Ena ali pano, akufuna kuti akhale bwino. Ndipo pamene ife timva za matenda ajawa, monga adokotala, kuukitsidwa kwa wakufa, zinthu zazikulu zamphamvu zimene Mulungu wathu wazichita, ndiye ife timakhala ofunitsitsa. Ndipo chinthu cha icho ndichakuti, ife timayesera kuzifikira podzera mu zokhudzira izi, kuti tigwire chinachake apa, monga chikumbumtima.
Anthu ambiri, nthawi zambiri, awapotoza Mawu. Ndipo ine ndakhala wosamvetsetseka ndi izi, popanga kuitanira ku guwa. Ine ndimati, “ine sindimakokomeza kwambiri zoitanira ku guwa,” sindimatanthauza kuti inu musamaitanire ku guwa. Koma wina amamugwira wina pa nkono, ndikuti, “O, M'bale John, inu mukudziwa chiani? Ine ndi inu takhala tiri oyandikana nthawi yonseyi. Bwerani kuno ku guwa, mugwadire pansi.” Kodi iye akuchita chiani? Ine ndikukhumba ndikanakhala ndi bolodi lakuda apa, ine ndikanakusonyezani inu zimene iye akuchita. Iye akuyesera kuti agwire ntchito podzera mmoyo mwake, pa kukonda. Izo sizimagwira ntchito. Mpita wake si umenewo. Ndithudi, si umenewo. Mwinamwake iye akugwira ntchito mu (chiyani?) kukumbukira, kudzera mu chokhudzira cha moyo wake. “O, M'bale John, iwe unali ndi amayi ako abwino. Iwo anamwalira nthawi yapitayo.” Kukumbukira! Mukuona? Inu simungathe kuchita zimenezo. Izo zimayenera kuti zibwere kudzera mu mzere wa kuchita mwakufuna kwako. Iwe, mwiniwake, kulola Mawu a Mulungu... Iwe sumabwera chifukwa chakuti amayi ako anali mkazi wabwino. Iwe sumabwera chifukwa chakuti ndiwe woyandikana nawo wabwino. Iwe umabwera chifukwa chakuti Mulungu wakuitana iwe kuti ubwere, ndipo iwe umamulandira Iye mogwirizana ndi Mawu Ake. Mawu amenewo ndi amene amatanthauza chirichonse. Mawu amenewo! Ngati iwe ungathe kuchotsa chirichonse pa njirayo, chikumbumtima chonse, zokhudzira zonse, ndi kungowalola Mawu kubweramo, Mawu amenewo adzabala zofanana chimodzimodzi.
Apa, mukuona chimene Iwo aphimbidwa nacho? Inu mukuti, “Chabwino, tsopano,” inu mukuti, “chabwino, izi, chikumbumtima ndi zokhudzira, ndi zina zotero, ziribe kanthu kochita ndi zimenezo, M'bale Branham?” Ndithudi, izo ziri nacho. Koma ngati inu muwalola Mawu kuti abweremo, ndi kudzawaphimba Iwo ndi chikumbumtima, ndiye Iwo sangathe kukula; iwo adzakhala mawu olumala. Kodi inu munayamba mwaiwonapo mbewu yabwino ya chimanga itabzalidwa mu nthaka, ndipo kamtengo ndi kugwera pa iyo? Iyo imamera mopindika. Nthambi iliyonse, chirichonse chimene chimamera, chimatero, chifukwa chinachake chatchinga icho.
Chabwino, ndi limene liri vuto ndi Chikhulupiriro chathu cha chipentekoste lero. Ife tazilola zinthu zambiri kuti zitchinge Icho, Chikhulupiriro chimene ife tinaphunzitsidwa, Mzimu Woyera umene wakhala ukukhala mwa ife. Ife taloleza zinthu zambiri, kuyang'ana pa munthu wina. Ndipo Mdierekezi nthawizonse amayesera kuti azikulozerani inu ku kulephera kwa munthu winawake, koma iye amayesetsa kuti mutalikirane nawo umboni weniweni umene uli woona. Iye amakulozerani inu kwa wachinyengo, nthawi zina, amene anapita ndi kumakatsanzira chinachake. Iye sanachite chimenecho, chifukwa iye amangotsanzira. Koma ngati izo zikubwera kuchokera ku gwero loona la Mawu a Mulungu, “Miyamba ndi dziko lapansi zidzapita, koma Mawu Anga sadzapita,” Iwo ayenera kukhala pamenepo. Inu mukuziwona izo, mlongo?
Iwo ayenera kuti alandiridwe mmalingaliro, kenako Iwo akhulupiriridwa ndi mtima. Zikatero Mawu a Mulungu amadzakhala chenicheni, ndiye chokhudzira chirichonse cha moyo ndi thupi zimangoyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Ndiye chokhudzira chanu cha Mulungu, chikumbumtima chanu cha Mulungu, chirichonse chimene chiri chaumulungu, chimayenderera kudutsa mwa inu. Apo sipamakhala kukaikira paliponse. Palibe chirichonse chimene chingadzukepo.
Palibe chimene chingabwerepo mu kukumbukira, ndi kudzati, “Chabwino, ine ndikukumbukira Mtsikana wa a Jones anayeserapo kuti azimudalira Mulungu, ndi Mtsikana wa Akuti-ndi-akuti. Mtsikana wa a Doe anayeserapo kuti amudalire Mulungu pa machiritso, nthawi ina, ndipo iye analephera.” Mukuona? Koma ngati mpita umenewo wayeretsedwa ndipo watsukidwa, ndipo wadzazidwa mkatimo ndi Mzimu Woyera, izo sizimakumbukiridwa nkomwe, ziribe kanthu za Mtsikana wa a Jones ndi zimene iye anachita. Izo zimakhala pakati pa inu ndi Mulungu, palimodzi, ndipo osati wina wakenso koma inu awiri. Ndi zimenezotu. Ndi imeneyo nkhondo yanuyo.
Werengani akaunti yonse mu...
Nkhondo yaikulu imene yakhala ikumenyedwa.