Kusankha kwa Mkwatibwi.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Kuyenda kwa Chikristu mndandanda.

Kusankha ndi chinthu chachikulu.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Kusankha kwa Mkwatibwi.

Tsopano mundime ya 9 ya mutu wa 21 wa Chivumbulutso.
Ndipo apo anadza kwa ine m'modzi wa angelo asanu ndi awiri omwe anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri isanu ndi iwiri yotsiriza, ndipo anayankhula ndi ine, nati, Bwera kunoko, ndipo ine ndikusonyeza iwe mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.

Mu zinthu zambiri za moyo ife timapatsidwa kusankha. Njira ya moyo, payokha, ndi kusankha. Ife tiri ndi ufulu wopanga njira yathu yathu, kusankha njira yathu yathu yomwe ife tikufuna kuti tizikhalira moyo. Maphunziro ndi kusankha. Ife tikhoza kusankha ngati tikufuna kukhala ophunzira, kapena ngati ife sitikhala tiri ophunzira. Uko ndi kusankha komwe ife tiri nako. Chokhoza ndi cholakwika ndi kusankha. Mwamuna aliyense, mkazi aliyense, mnyamata ndi msungwana, ayenera kuti asankhe ngati iwo ati ayesere kumakhala molondola kapena kusamakhala molondola. Ndi kusankha. Kusankha ndi chinthu chachikulu.

Kopita kwanu Kwamuyaya ndi kusantha. Ndipo mwinamwake, usiku uno, ena a inu mukupanga uko - kusankha uko kwa komwe inu muti mudzakakhale Mwamuyaya, utumiki uwu usanathe usiku uno. Padzakhala nthawi imodzi, yoti, ngati inu mumukana Mulungu nthawi zambiri, padzakhala nthawi imodzi yomwe inu muti mudzamukane iye kwa nthawi yotsiriza. Pali mzere pakati pa chifundo ndi chiweruzo. Ndipo ndi chinthu choopsa kwa mwamuna kapena mkazi, mnyamata kapena msungwana, kuti aponde kudutsa mzere umenewo, pakuti palibe kubwerera pamene inu muponda kudutsa mzere wa imfa uwu. Kotero, usiku uno, iyo ikhoza kukhala ili nthawi yomwe ambiri ati apange kwawo - kusankha kwawo, kumene iwo ati adzakakhale Mwamuyaya wosatha.

Pali kusankha kwina kumene ife tiri nako mu moyo, ndiye, mzako wamoyo. Mnyamata kapena msungwana, yemwe akufika mu moyo, wa - wapatsidwa ufulu wopanga kusankha. Mnyamata amasankha. Msungwana alinawo ufulu kuti avomereze kapena kukana izo. Koma uko ndikusankhabe, ku mbali zonsezo. Onse mwamuna ndi mkazi, iwo ali nao ufulu wa kusankha.

Ndiponso, inu muli ndi kusankha, monga Mkhristu. Inu muli nako kusankha kwa mpingo, muno mu Amereka, mpaka pano, kumene inu mungati mudzipitako. Uwo ndi mwayi wanu wanu wa Chimereka, kuti mudzisankha mpingo uli wonse umene inu mukufuna kuti mukhale wa iwo. Uko ndikusankha. Inu simumasowa kuti muzipita ku wina uliwonse wa iwo, ngati inu simukufuna kutero. Koma ngati inu mukufuna kusintha kochokera ku Methodisti kupita ku Baptisti, kapena Katolika kupita ku Chiprotestanti, kapena zina zotero, palibe winawake yemwe angakhoze kukuuzani inu kapena kukupangitsani inu kumabwera ku mpingo wina uliwonse. Uwo ndi wathu - uwo ndi ufulu wathu. Ndi chimene demokalase yathu ili. Munthu aliyense akhoza kudzisankhira yekha. Ufulu wa chipembedzo, ndipo ndicho - chinthu chachikulu. Mulungu atithandize ife kuti tizisunge izo utali wonse womwe ife tingankhoze.

Inu muli nakonso kusankha. Kaya... Pamene, inu musankha mpingo uno, inu mukhoza kusankha kaya inu, mu mpingo uno, kaya inu musankha mpingo omwe uti ukutsogolereni inu mpaka kupita kwanu Kwamuyaya. Inu mukhoza kusankha mpingo umene uli ndi kachinkhulupiriro kena kake, komwe inu mukhoza kuganiza kuti kachikhulupiriro ako kali basi chimene inu mumafuna. Kapena mpingo wina uli ndi kachikhulupiriro kawo. Ndiyeno pali Mawu a Mulungu, omwe inu muli nawo kusankha kwake. Inu mumayenera kupanga kusankhako. Pali lamulo losalembedwa pakati pathu, la kusankha.

Ine ndikukhulupirira anali Eliya, nthawi ina, pamwamba pa Phiri la Karimeli chitatha chiwonetsero, mu ora lalikulu la zovuta lomwe ife tiri pafupi kuti tibweremo pakali pano. Mwinamwake, iyo ikhoza kukhala kwa inu kapena inu, usiku uno, kuti tipange kusankha uku, monga chochitika cha pa Phiri la Karimeli. Moona, ine ndikuganiza izo zikuchitika, mu dziko kulikonse, tsopano. Koma posachedwapa pakhala nthawi yomwe inu musowa kuti mupange kusankha.

Ndipo inu amuna pano, a mipingo yanu ya zipembedzo, ingokhulupilirani izi, kuti ora liri pa inu pomwe, pamene inu muti mupange kusankha. Inu mwina mudzapita mu World Council, kapena inu simudzakhala konse chipembedzo aponso. Inu mudzayenera kudzapanga izo, ndipo kusankha kumeneko kukubwera posachedwa. Ndipo ndi chinthu choopsa kuti udikire mpaka ora lotsiriza ilo, aponso, chifukwa inu mukhoza kutengera chinachake chimene inu simungakhoze kudzisansa kwa icho. Inu mukudziwa, pali nthawi yomwe inu mungakhoze kuchenjezedwa, ndiye, ngati inu muwoloka kudutsa mzere uwo wakuchenjeza, ndiye inu mwaikidwa kale chizindikiro cha kumbali inayo, kusindikizidwa.

Kumbukirani, pamene chaka cha chomasulidwa chibwera, ndipo wa - wansembe ankakwera ndikuwomba kwa lipenga lake, kuti kapolo aliyense akanakhoza kupita ali mfulu. Koma ngati iwo akana kuti avomereze ufulu wawo, ndiye iye ankayenera kuti atengedwere ku kachisi kunsanamira, ndipo chisongole chimamubowola iye mu khutu, ndiyeno iye ankatumikira mbuye wake nthawi zonse. Icho chinkayikidwa pa khutu lake ngati choimira, chakumva. “Chikhulupiriro chimadza pakumva.” Iye analimva lipenga lija, koma iye sanali kufuna kuti amvetsere kwa ilo.

Ndipo nthawi zambiri, amuna ndi akazi amamva Choonadi cha Mulungu, ndipo amachiwona Icho chikuvomerezedwa ndi kutsimikiziridwa, Choonadi, komabe iwo samafuna kuti amvere Icho. Pali chifukwa chinachake. Pali kusankha kwina kwake kumene iwo ali nako, kuposa kuti ayang'anizane nacho Choonadi ndi zowona, chotero makutu awo akhoza kutsekedwera kwa Uthenga. Iwo sadzaumvera konse iwo. Langizo langa kwa inu, pamene Mulungu ayankhula kwa mtima wanu, inu mudzichitapo apo pomwe. Eliya anawapatsa iwo kusankha komwe iwo akanayenera. “Sankhani inu lero yemwe muti muzimutumikira. Ngati Mulungu ali Mulungu, zimutumikirani Iye. Koma ngati Baala ali Mulungu zimutumikirani iye.”

Tsopano, pamene ife tikuwona kuti zinthu zonse za chibadwa ndi zoimira za zinthu zauzimu, monga ife tinadutsira mu phunziro lathu m'mawa uja, monga dzuwa ndi chikhalidwe chake. Limenelo linali Baibulo langa loyamba. Ine ndisanawerenge konse tsamba mu Baibulo, ine ndinkamudziwa Mulungu. Chifukwa, Baibulo linalembedwa paliponse mu chilengedwe, ndipo izo zimangogwirizana ndi Mawu a Mulungu: momwe imfa, kuikidwa m'manda, chiukitsiro cha chirengedwe, ndi dzuwa kutuluka, kudutsa, kukalowa, kufa, kutuluka kachiwiri. Pali zinthu zochuluka kwambiri zomwe ife tingakhoze kudzifanizitsira, Mulungu mu chirengedwe, zomwe ife tiyenera kuzilambalala, chifukwa cha Uthenga uwu.

Tsopano, ngati zauzimu kapena... zathupi ziri zoyimira zauzimu. Ndiye, kusankha kwa mkwatibwi, mwa chibadwa, ndi choyimira cha kusankha Mkwatibwi, Mkwatibwi, mwa uzimu. Tsopano, ndi chinthu chotsimidwitsa pamene ife tipita kukasankha mkazi, mwamuna, pakuti malumbiro apa ali mpaka imfa mpomwe ife timalekana. Ndi momwe ife tiyenera kumalisungira ilo. Ndipo inu mumatenga lumbiro limenelo pamaso pa Mulungu, kuti imfa yokha ndiyo idzakulekanitseni inu.

Ndipo ine ndikuganiza ife tiyenera. Mwamuna mu kuganiza kwake kolondola, yemwe akukonzekera tsogolo, kuti iye ayenera adzimusankha mkazi ameneyo mosamala kwambiri. Mudzisamala zomwe inu mukuchita. Ndipo mkazi akamasankha mwamuna, kapena kuvomereza kusankha kwa mwamuna, ayenera kukhala wosamala kwenikweni pa zomwe iye akuchita, ndipo makamaka mu masiku ano. Mwamuna ayenera kuganiza ndi kupemphera iye asanamusankhe mkazi wake.

Ine ndikuganiza, lero, zomwe zatengera milandu yochuluka kwambiri ya chilekano tsopano, mokuti ife tikulitsogolera dziko lonse mu Amenereka, mu milandu ya chilekano. Ife tikutsogolera dziko lonse. Kuli zilekano zochuluka kuno kuposa kwina kulikonseko, fuko lino, ndipo liyenera kukhala liri, ndipo limaganiziridwa ngati, fuko la Chikhristu. Ndi chitonzo bwanji, bwalo lathu la milandu ya chilekano! Ine ndikuganiza, chifukwa chake, ndi chifukwa chakuti amuna apita kutali ndi Mulungu, ndipo akazi apita kutali ndi Mulungu. Ndipo ife tikupeza, kuti, ngati mwamuna apemphera ndi mkazi akapemphera pa nkhaniyo; osati kungoyang'ana pa maso awiri okongola, kapena mapewa aakulu amphamvu, kapena zonga izo, kapena zokonda zina za chidziko; koma akanati ayang'ane poyamba kwa Mulungu, ndi kuti, “Mulungu, kodi ili ndi dongosolo Lanu?”

-----
Ndipo ngati ife tikanati tiphunzire zomwe ife tikuchita pamene ife tikuti tikwatire, pamene ife tisankha mkazi wathu, mwamuna wathu, ngati ife tikanati tiziphunzire izo bwino! Mwamuna ayenera kumapemphera modzipereka, pakuti iye akhoza kuwononga moyo wake wonse. Kumbukirani, lumbirolo liri “mpaka imfa mpomwe ife tidzalekana,” ndipo iye akhoza kuwononga moyo wake pa kupanga kusankha kolakwika. Koma ngati iye adziwa pamene, iye akupanga kusankha kolakwika ndipo iye akukwatira mkazi yemwe sali kuyenera kuti akhale mkazi wake, ndipo iye akuzichita izo mulimonse, ndiye ilo ndi vuto lake. Ngati mkazi amutenga mwamuna ndi kumadziwa kuti iye si woyenera kuti akhale mwamunako kwa iwe, ndiye ilo ndi vuto lako lomwe, iwe utadziwa kale chomwe chiri cholondola ndi cholakwika. Kotero, inu musamachite izo mpaka inu mutadzipempherera bwino bwino.

Zomwezo zimagwiritsidwa ntchito pa kusankha mpingo. Tsopano, inu muyenera kumapempherera pa mpingo umene inu muli kusonkhanamo. Kumbukirani, mipingo imanyamula mzimu. Tsopano, ine sindikufuna kuti ndikhale wotsutsa. Koma ine ndikuzindikira kuti ndine bambo wachikulire, ndipo ine ndiyenera kuti ndidzachoke kuno, limodzi la masiku awa. Ine ndiyenera kudzayankha pa Tsiku la Chiweruzo pa zomwe ine ndikuzinena usiku uno kapena nthawi ina iliyonse. Ndipo ine, kotero, ine ndiyenera kuti ndikhale wotsimikiza mwantheradi ndi wokhudzidwa kwathunthu. Koma, inu mukapita mu mpingo, ndipo ngati inu mungapenye khalidwe la mpingo umenewo, inu mungomupenya m'busayo kanthawi, ndipo inu kawirikawiri mudzapeza kuti mpingo umachita monga m'busayo. Nthawizina, ine ndimadabwa ngati ife sitimangotengerana mzimu wa wina ndi mzake m'malo mwa Mzimu Woyera. Inu mukafika pa malo pomwe m'busa ali wachikhazikitso kwenikweni ndi wopitiriza, inu mudzapeza kuti osonkhana ali a njira yomweyo. Ine ndikubweretsani inu ku mpingo kumene ine ndikuwona abusa akuima ndi, kumagwedeza mituyawo m'mbuyo ndi mtsogolo. Inu mudzawapenye osonkhanawo, iwo amachita chinthu chomwecho. Inu mumutenge m'busa yemwe amangomeza chirichonse, kawirikawiri mpingowo umachita chinthu chomwecho. Kotero, ngati ine ndikanakhala ndikusankha mpingo, ine ndikanati ndisankhe mpingo weniweni, wachikhazikitso, wa Uthenga Wathunthu, wa Baibulo, ine ndikanakhala ndikusankha wina woti ndiyikemo banja langa. Sankhani.

-----
Hiwiri, mtundu wa mkazi yemwe mwamuna angamusankhe, adzanyezimiritsa zokhumba zake ndi khalidwe lake. Ngati mwamuna asankha mkazi wolakwika, izo zimanyezimiritsa khalidwe lake. Ndi komwe iye amazimangiriza mwiniwakeko, kumasonyeza moona zomwe ziri mwa iye. Mkazi amanyezimiritsa zomwe ziri mwa mwamunayo pamene iye amusankha iye kukhala mkazake. Izo zimasonyeza chomwe chiri pansi mkati mwake. Ziribe kanthu zomwe iye anena kunjaku, penyani chimene iye akwatira.

Ine ndikapita ku ofesi ya munthu, ndipo iye nkumati ndi Mkhristu; zopachika ponse kuzungulira m'makoma, nyimbo zakale za kwasakwasa zija zikupitirira. Ine sindimasamala chimene iye anena. Ine sindimakhulupirira umboni wake, chifukwa mzimu wake umadyerera pa zinthu za m'dziko izo. Chiani, titi, ngati iye akanati akwatire msungwana wovina mu mabara, kapena bwanji ngati iye akanakwatira ngenge yodziwa chiwerewere, kapena ricketta wokongola wamakono basi? Izo zimanyezimiritsa. Izo zimasonyeza zomwe iye ali nazo mu malingaliro ake, cha chomwe banja lake la mtsogolo liti lidzakhale, chifukwa iye wamutenga iye kuti alere ana ake naye. Ndipo chirichonse chomwe iye ali, ndi momwe iye ati adzawalerere ana amenewo. Kotero, izo zimanyezimiritsa zomwe ziri mwa mwamunayo. Mwamuna yemwe amamutenga mkazi monga choncho, zimasonyeza basi zomwe iye akuganiza pa za tsogolo. Kodi inu mukanalingalira Mkhristu kuchita chinthu monga choncho? Ayi, bwana. Ine sindikanakhoza. Mkhristu woona sangati afunefune ngenge zokongola choterozo, ndi asungwana wovina mu mabara, ndi ngenge zodziwa chiwerewere. Iye akanafunafuna khalidwe la Chikhristu.

Tsopano, ndiye, pamene ife tisintha kupita m'mbuyo tsopano mu mphindi, kupita ku mbali yauzimu. Ndipo pamene inu muwuona mpingo umene uli mu dziko, ukuchita monga dziko, kumayembekezera za mu dziko, kumachita nawo za m'dziko, kumawerengera malamulo a Mulungu ngati kuti Iye sanawalembe konse Iwo, ndiye I - inu mukhoza kungolingalira Khristu sadzatenga Mkwatibwi woteroyo. Kodi inu mungakhoze kulingalira kuutenga mpingo wamakono wa lerowu kukhala Mkwatibwi? Osati Ambuye wanga. Ine sindiri... Ine sindingakhoze nkomwe kuziwona izo. Ayi. Kumbukirani, tsopano, mwamuna ndi mkazi wake ali m'modzi. Kodi inu mukanadziphatikiza nokha kwa munthu wonga uyo? Ngati inu mungatero, izo ndithudi zingakhale ngati zikhumudwitse chikhulupiriro changa mwa inu.

Nidpo, ndiye, nanga bwanji Mulungu kudzilumikiza yekha kwa chinachake chonga icho, wachiwerewere chachipembedzo mwachizolowezi? Inu mukuganiza Iye akanachita izo, “Ali nawo mawonekedwe aumulungu koma kumakana mphamvu yakeyo”? Iye sakanati achite konse izo. Iye ayenera kukhala nalo khalidwe Lake mwa iye. Mpingo weniweni, wobadwa - kachiwiri moona uyenera kukhala - ndi khalidwe limene linali mwa Khristu, chifukwa mwamuna ndi mkazi wake ali m'modzi. Ndipo ngati Yesu ankachita kokha izo zomwe zinkamukondweretsa Mulungu, ankasunga Mawu Ake ndipo ankawawonetsera Mawu Ake, Mkwatibwi Wake adzayenera kukhala ali wa mtundu womwewo wa khalidwe. Iye sakanakhoza, mwa njira iliyonse, kukhala chipembedzo. Chifukwa, ndiye, ziribe kanthu momwe inu mukufuna kunena kuti, “ayi,” iye amalamulidwa ndi gulu kwina kwake, lomwe limamuuza iye choti achite ndi chimene iye sangakhoze kuchichita, ndipo, nthawi zambiri, mailosi milioni zitachoka ku Mawu owona.

Izo ndi zoipa kwambiri kuti ife tinachoka konse kwa Mtsogoleri weniweni yemwe Mulungu anatisiyira ife kuti aziutsogolera Mpingo. Iye sanatumize konse oyang'anira wa dzikolo. Iye sanatumize konse mabishopu, makadinolo, ansembe, mapapa. Iye anatumiza Mzimu Woyera kwa Mpingo, kuti uziutsogolera Mpingo. “Pamene Iye Mzimu Woyera adzadza, Iye adzakutsogolerani inu mu Choonadi chonse, kuululira zinthu izi kwa inu, zomwe ine ndakuuzani inu, kuzibweretsa ku kukumbukira kwanu ndipo uzidzakusonyezani inu zinthu zomwe ziri nkudza.” Mzimu Woyera unali woti uzidzachita zimenezo.

Tsopano, mpingo wamakono umadana nazo Izo. Iwo samazikonda Izo, kotero kodi iye akanakhoza bwanji kukhala Mkwatibwi wa Khristu? Anthu, lero akusankha, chipembedzo chamakono. Chomwe izo zimachita, izo zimanyezimiritsa kokha kumvetsa kwawo kosauka pa Mawu. Ine sindikutanthauza kuti ndipweteke, koma ine ndikutanthauza kuti ndizilore izo zizame mwakuya kokwanira mpaka inu muziyang'ana pa izo.

Werengani akaunti yonse mu...
Kusankha kwa Mkwatibwi.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo.

Deuteronomo 30:19


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)
 

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

As the Eagle
Stireth her nest.

(PDF Chingerezi)

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.