Fyuluta ya munthu woganiza.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Kuyenda kwa Chikristu mndandanda.

Fyuluta ya dziko lachipembedzo.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Fyuluta ya munthu woganiza.

Numeri 19:9,
Ndipo mwamuna yemwe ali woyera azikokolola phulusa la mwana wang’ombe, ndipo azikaliika ilo kunja kwa msasa pa malo oyera, ndipo ilo lizikasungidwira kwa osonkhanawo kwa osonkhana omwe ali ana a Israeli likhale la madzi olekanitsa: uko ndiko kuyeretsa kwa tchimo.

Phunziro lomwe ine ndikuligwiritsa ntchito usikuuno ndi: Fyuluta Ya Munthu Woganiza. Izo zikumveka mopitirira malire kuti likhale phunziro, kwa mtumiki yemwe ali wotsutsana kwambiri ndi kusuta, kuti angatenge nkhani yonga iyo, Fyuluta Ya Munthu Woganiza. Izo zinachitika, kuti, mmawa wina pamene ine ndinali nditapita kokasaka agologolo.

Ngati anthu inu kunjako pa--- kunjako pa wailesi, pa kuulutsa, kapena pa mphepo za telefoni, mukanati muwone kuwonetsera kwa pa nkhope za osonkhana awa pamene inendinalengeza nkhani yangayi, inu mukanati museke pa izo. Fyuluta Ya Munthu Woganiza.

Chabwino, izo zinachitika uko kumene Angelo a Ambuye anawonekera kwa ine mmawa wina, ndipo agologolo aja anayankhulidwa nakhalapo. Nonse inu mukukumbukira pamene izo zinachitika. Ndipo, aponso, basi pamwamba pa phiri pomwe ine ndinali nditaima, panali pamene... basi ndisanalalikire kumene Mibadwo Isanu ndi iwiri ya Mpingo, ndikupita kokasaka mmawa wina kuwala kwa tsiku kusanayambe. Apo panaima... ine ndinaganiza kuti dzuwa linali kutuluka, pafupi foro koloko mmawa. Mosazolowereka; ine ndinakuwona Kuwala uko, ndipo ine ndinapotoloka apo, ndipo apo panaima Zoikapo Nyali Zagolide Zisanu ndi ziwiri zitaima pamwamba apo kumeneko pamwamba pa phiri, ndi zokhala ngati utawaleza zikukwera mmwamba kupyolera mu mipope ndi kumadyetsera uko.

Mwamsanga zitachitika izo, Ambuye Yesu anawonekera kwa ife. Ndipo apo pomwe ine ndinamva Liwu lomwe linati, “Yehovah wa Chipangano Chakale ndi Yesu wa Chatsopano.” Ndipo apo Iye anali, patapita kanthawi, ataululidwa pambuyo pa Zoikapo Nyali Zisanu ndi ziwiri za Golide izo. Ndiye zindikirani izo. Ndi angati akukuimbukira nkhani ija? Ine ndinailemba iyo kuseri kwa--- kwa bokosi la--- la zipolopolo lomwe ine ndinali nalo mthumba mwanga. “Yehova wa Chipangano Chakale ndi Yesu wa Chatsopano.” Mulungu Kumwamba akudziwa kuti izo zinali zoona.

----
Ine ndinali nditawerenga uko mu Bukhu la Daniele, pamene iye anadza kwa “Wamasiku Amakedzana, Yemwe tsitsi lake linali loyera ngati ubweya.” Ndiye ine ndinamuwona Wamasiku Amakedzana uyo. Iye anali Wamasiku Amakedzana uyo, yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Mwaona, icho chinali chophiphiritsa, ndiye. Chifukwa chiani ubweya woyera? Ndiyeno ine... Mzimu Woyera unkawoneka kuti unkayankhula kwa ine za chithunzi chomwe ine ndinachiwona nthawi ina, cha woweruza wamakedzana. Ndiye ine ndinapita ku mbiriyakale; ine ndinabwerera mmbuyo mu mbiriyakale ya Baibulo ndi zonse, kuti ndikafufuze. Ndipo oweruza akale, monga wansembe wamkulu mu Israeli, iye ankayenera kuti azikhala ndi tsitsi loyera, longa-ubweya wotuwa ndi ndevu, chifukwa loyeralo pa iye linkasonyeza kuti iye anali ulamuliro wapamwamba wa oweruza a mu Israeli.

Ndipo ngakhale lero, ndi mpaka kufika zaka mazana ochepa zapitazo, mwina zaka mazana angapo apitawo, kapena mwinamwake osati monga choncho, mtsogolopo kuposa apo. Oweruza onse Achingerezi, zinalibe kanthu momwe iwo analiri aang’ono kapena momwe iwo analiri aakulu, pamene iwo ankapita kuti akaweruze, iwo ankavala tsitsi loyera; ndi kuti asonyeze kuti palibe ulamuliro wina uliwonse, mu ufumu umenewo, pamwamba pa mawu awo. Mawu awo ndiwo chodalirapo cha ufumuwo. Chimene iwo anena, ndizo zonse zake.

Ndipo tsopano, ndiye, ine ndinaziwona izo. Apo Iye anali ataima pamenepo, komabe ali Mnyamata, koma atavala tsitsi loyera. Iye anali Ulamuliro, wathunthu wapamwamba. Iye anali Mawu. Ndipo Iye ali nalo, atavala tsitsi loyera.

Ndiye, mtsogolo mwakemo pamene ife tinatsiriza, ndi--- ulaliki, ndipo ndinapita kumadzulo, ndipo pamene Angelo a Ambuye anawonekera kumeneko kwa Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, ndipo iwo ankapita mmwamba mu mlengalenga (chomwe ife tiri nacho chithunzi chake muno, ndi ku dziko lonseli), apo Iye anali ataima pamenepo, atavekedwabe tsitsi ndi ulamuliro wapamwamba umenewo. Iye ndi Mutu wa Mpingo. Iye ndi Mutu wa Thupi. Palibe chirichonse chonga Iye, kulikonse. “Iye anapanga zinthu zonse mwa Iyeyekha. Iye anadzipangira zinthu zonse kwa Iyeyekha, ndipo popanda Iye kunalibe kanthu kanapangidwa.” “Iye ali nawo ulamuliro wonse Kumwamba ndi padziko lapansi,” ndipo chirichonse ndi cha Iye. “Ndipo mwa Iye muli chidzalo cha Umulungu mu thupi.” “Ndipo Mawu anali Mulungu, ndipo anapangidwa thupi pakati pathu.” Ndipo Iye anali Mmodzi Yemwe anachiulula chinsinsi chonse cha dongosolo lonse la chipulumutso, zomwe aneneri onse ndi anthu anzeru anali atayankhulapo. Iye yekha anali Mmodzi wovala tsitsiyo ndi ulamuliro wapamwamba.

Tsopano, ine ndinali nditaima, pamwamba pa phiri mmawa wina, pankawoneka ngati panali agologolo ena omwe anali akubudula pamwamba apo. Ndipo ine ndinayamba kuti ndizikhala pansi. Ndipo ine ndinali nditangokhala apo kwa mphindi, pamene, tchire linakhudzidwa ndi ine, ndipo munthu wina wamkulu kwambiri ali ndi mfuti ya masketi ya mipope iwiri anabwera akuyenda uko kudutsa mu tchirelo uko, ndipo zinakhala ngati zawopsyeza kuwala kwa tsiku mwa ine. Ine ndinapitirirabe pamwamba, ndinamyata pansi; ine ndinkachita mantha kuti ndisunthe, kuwopa kuti iye angandiwombere ine. Ndipo tchire linali likugwedezeka, kotero ine ndinangokhala bata kwenikweni.

Gologolo anayamba kukwera phirilo, ndipo iye anawombera mipope yonseyo limodzi nayo. Ndipo chotero iye anamuphonya iye, ndipo chotero gologoloyo anapita mmusi mwa pamwamba pa phirilo. Ine ndinaganiza, “Tsopano ine ndichokepo, phokoso lonse ilo likupokosera. Iye waikhuthula Ndipo ine ndinayamba kutsika ndi phiri, ndipo mwamunayo anawombera kutsogolo kwanga komwe. Izo zinanditembenuzira ine mmbuyo kunjira iyi. Ndipo ine ndinauyamba cha uku, kuti ndizipita mmusi ndi njira ina, ndipo raifolo ya twente-thuu inayamba, ndipo zipolopolo zinali zikulira pamwamba pa ine. Ine ndinati, “Ndititu, ine ndiri pa malo owopsya.”

Chotero ine ndinapotoloka apo ndipo ndinapita mmusi cha ku mtsinje. Ndipo ine ndinaganiza, “Ine ndipita kumusi uku ndipo ndikabisala mpaka iwo atsirize, kuti ine ndikhoze kutulukako.” Ndipo ndiri panjira ndikutsika, ine ndinapezeka ndikukokedwa... Chidwi changa chinakokedwa kuti ndiyang’ane kumbali yanga ya kumanja. Ndipo, pamene ine ndinatero, apo panali paketi yopanda kanthu ya ndudu komwe wina wa iwo anaitayira pansi, mu kuthamanga konse kwa... pamene agologolo anali kudutsa mu tchirelo.

Ine ndikupempha kukhululukira kwanu. Ine ndinayang’ana pansi pa iyo. Ine sindinaitole iyo, chifukwa ine sindimakonda fungo la zinthuzo, pa kuyamba pomwe. Ndipo ine ndinayang’ana pansi apo, ndipo ndi---kampani inayake ya fodya yomwe ine ndikulingalira kuti ine ndisati nditchule dzina lake, koma inu mudziwa. Iyo inati pamenepo, “Fyuluta ya munthu woganiza ndi kukoma kwa munthu wosuta.” Ine ndinayang’ana pa chinthu chimenecho, ndipo ine ndinaganiza, “Fyuluta ya munthu woganiza?” Ine ndinaganiza, “Ngati munthuyo akanati aziganiza konse, iye sakanati azisuta konse. Iyo ingakhoze bwanji kukhala ‘fyuluta ya munthu woganiza’? Munthu woganiza sakanati azisuta konse.” Chabwino.

----
Ine ndinayang’ana pa iyo, ndipo ine ndinaganiza, “Ndi chinachake chonga--- zipembedzo za lerozi, mipingo yomwe ife tiri nayoyi.” Uliwonse wa iyo uli ndi fyuluta yakeyake; iwo ali nawo mtundu waowao wa fyuluta. Iwo amangolola kuti zizilowa zomwe iwo amazifuna, ndi zoti zisamalowemo; zomwe iwo amazisefera mkatimo ndi kuzisefera kunja, ndi mtundu waowao wa fyuluta. Iwo amangololeza zochuluka choncho za dziko kuti zilowemo kuti ziziwasangalatsa osakhulupirira omwe ali mmenemo. Iwo amawaloleza iwo kuti azilowa mopanda kusamala chomwe iwo ali, ngati iwo ali ndi ndalama. Iwo amawatengera iwo mmenemo mopanda kusamala kanthu chomwe iwo ali, ngati iwo ali otchuka. Koma pali chinthu chimodzi cha izo, inu simungakhoze kulowa mu Mpingo wa Mulungu monga choncho; osati mu chipembedzo tsopano, ine ndikutanthauza Mpingo weniweni, woona wa Mulungu.

----
Anthuwo, iwo amadziwa chomwe iwo amachifuna. Kotero ngati iwo angati apeze chomwe iwo akuchifuna, ndiye iwo ayenera kuti akhale ndi mtundu winawake wa fyuluta, ndi zochuluka za mdziko zimayankhulidwa mozidusitsa, kutiakhutitse kukoma kwawo kwa chidziko. “Fyuluta ya munthu woganiza, kukoma kwa munthu wosuta.” Fyuluta ya dziko lachipembedzo, ndi kukoma kwa munthu wa chidziko.

Iwo amafuna kuti azikhala achipembedzo. Iwo amaganiza kuti iwo amayenera kuti azikhala achipembedzo, chifukwa iwo ali nayo solo. Pamene ife tinabwera koyamba mu dziko lino, inu munadzawapeza Amwenye akupembedza dzuwa ndi zina zotero, chifukwa (chiani?) iye ndi munthu wokhalapo. Ife tikapita komwe mu nkhalango zaku Afrika, ife tikazipeza mbadwa zikupembedza chinachake. Bwanji? Iwo ndi anthu okhalapo, ndipo iwo amafuna, amayenera kupembedza. Kotero munthu wokhalapo ziribe kanthu momwe iye aliri wokugwa, iye amadziwabe kuti pali chinachake kwinakwake. Koma iye ali nako kukom uko kwa dziko, moti iye sangakhoze kutenga fyuluta yolondola. Iye amayenera kukhala ndi fyuluta yoipanga yekha. Aliyense kumapanga fyuluta ya mtundu wakewake.

----
Zindikirani mu Numeri 19, ine ndikufuna inu kuti mukawerenge izo pamene inu mupita kunyumba, pamene inu mukakhala ndi nthawi yochulukira. Zindikirani, pamene Israeli ankakhala atachita tchimo, choyamba iwo ankatenga mwana wang’ombe wofiira yemwe anali asanakhale ndi gori konse pa khosi lake. Izo zikutanthauza kuti iye sanali mugoli apabe ndi chirichonse. Ndipo iye ankayenera kuti akhale wofiira. Mtundu wofiira ndi--- mtundu wa chitetezero. Inu mukudziwa, sayansi imadziwa kuti ngati iwe utenga kufiira ndi kukuyang’ana kudutsira mu kufiira, kwa kufiira, ndi choyera. Kuyang’ana kudutsira mu kufiira, pa chofiira, ndi choyera. Iye amayang’ana kupyolera mu Magazi ofiira a Ambuye Yesu, ndipo machimo athu ofiira amakhala oyera monga chipale; chofiira kupyolera mu chofiira. Ndipo mwana wa ng’ombeyo ankaphedwa nthawi ya usiku, ndi gulu lonse la Israeli. Ndipo apo pankaikidwa milozo seveni ya magazi ake pa chitseko pamene osonkhana onse ankalowera; choimira cha Mibadwo Isanu ndi iwiri ya Mpingo, mwa Magazi.

Ndiyeno thupi lake linkatengedwa ndi kuwotchedwa. Ilolinkawotchedwa limodzi ndi zopondera, limodzi ndi chikopa, limodzi ndi matumbo, limodzi ndi ndowe. Chirichons chinkawotchedwera, palimodzi. Ndipo izo zinkayenera kuti zinyamulidwe ndi munthu woyera, ndipo zinkayenera kuti ziyikidwe mu malo oyera kunja kwa osonkhana. Chotero, ngati Israeli akanakhoza kokha kuwona choimiracho! Mawu a Mulungu awa sayenera kuti azigwiridwa ndi manja awutchisi wa kusakhulupirira. Iye ayenera kumakhala ali munthu woyera. Ndipo ngati iye ali woyera, iye ayenera kuti azibwera kudutsira mu Fyuluta ya Mulungu. Munthu woyera, manja oyera, ndipo ankayenera kuti akasungidwe mu malo oyera; osati pa malo pamene Ayezebeli, ndi Maricke, ndi chirichonse akuchitapo nao; ndi kumadya mgonero ndi zinthu, pamene iwo akuthamanga thamanga ndi akazi, ndi amuna, ndi mitundu yonse ya utchisi; kumapita kokavina ndi maphwando, ndi kumavala tsitsi lodulidwa, ndi zazifupi, ndi chinthu chirichonse, ndipo nkumadzitcha okha Akhristu. Ndi zoti zizisungidwa mu malo oyera, ndi kumagwiridwa ndi manja oyera.

Ndiyeno pamene Israeli anachimwa, ndipo atazindikira kuti iwo anali atachita cholakwika, ndiye iwo ankakonkhedwa ndi mapulusa a mwana wang’ombe uyu pa iwo. Ndipo awo anali madzi olekanitsa, chiyeretso cha kwa tchimo.

Zindikirani. Ndi izi apa! Ndipo pamene Israeli, iwo asanati abwere mu chiyanjano mu kupembedza, iwo ankayenera choyamba kuti adutse mu madzi olekanitsa. “Kulungamitsidwa mwa chikhulupiriro; chimadza pa kumva, kumva Mawu.” Ndiye iwo ankalowa mu msonkhano pansi pa milozo seveni iyo, magazi, kuti asonyeze kuti chinachake chafa ndipo chapita patsogolo pa iwo, kwa tchimo lawo. Iwo ankalekanitsidwa ndi kumva kwa Mawu, madzi olekanitsa, ndiyeno ankalowa mu chiyanjano.

Malo okha omwe Mulungu ankakomana naye munthu anali kuseri kwa dongosolo limenelo. Iye sakanakhoza kukomana naye iye kwina kulikonse. Iye ankayenera kudzera kuseri kwa dongosolo limenelo. Mulungu ankakomana naye kokha Israeli pa malo amodzi. Ndipo Mulungu amangokomana nanu inu lero pamalo amodzi, ndipo amenewo ndi mwa Yesu Khristu; ndipo Iye ndi Mawu, madzi olekanitsa. Ndipo Magazi Ake anakhetsedwera kwa Mibadwo Isanu ndi iwiri yonseyo. Ndiyeno, mwa Mzimu Woyera, ife timalowa mu chiyanjano chimenecho, chomwe chimaperekedwa kwa Mpingo wokha. O, momwe Iye aliri wamkulu!

Ndiponso, tsopano, ife tikufuna kuti tiyang’ane pa Aefeso 5:26, anati, “Ndi kutsuka kwa madzi mwa Mawu,” madzi olekanitsa. Kodi Iwo amachita chiani? Ndiye, Fyuluta ya Mulungu ndiyo Mawu. Madzi olekanitsa, “kutsuka kwa madzi, olekanitsa, mwa Mawu,” Fyuluta ya Mulungu.

Ndiye, inu simungakhoze kubwera mwa Khristu kupyolera mu fyuluta ya mpingo. Inu simungakhoze kubwer mwa fyuluta ya chipembedzo kapena fyuluta ya kachikhulupirirPali Fyuluta imodzi yokha, yomwe inu mungakhoze kulowera nayo mu malo oyera awo, ndiyo kupyolera mu “kutsuka kwa madzi mwa Mawu.” Mawu a Mulungu ndiyo Fyuluta ya munthu woganiza.

Mpingo uzikuweruzani inu kuno ngati inu muli membala wabwino, kapena ayi. Iwo adzakupatsani inu maliro abwino, ndi kutsitsa-mwatheka mbendera pa imfa yanu, kutumiza nkhata zazikulu za maluwa n---ndi kukuchitirani inu chirichonse. Koma pamen izo zidzafika ku solo yanu kukomana ndi Mulungu, iyo idzayenera kukhala nao Moyo Wamuyaya. Ndipo ngati iwo uli Moyo Wamuyaya, iwo ndi gawo la Mawu. Ndipo monga mawu anga omwe sangakhoze kukana... Dzanja langa lomwe silingakhoze kulikana dzanja langa. Maso anga omwe sangakhoze kulikana dzanja langa, kapena phazi langa, kapena chala changa, kapena gawo lirilonse la ine. Ilo silingakhoze kuzikana izo. Ndipo sangakhozenso munthu yamwe ali gawo la Mawu a Mulungu, kapena mkazi, kulikana gawo limodzi la Mawu a Mulungu. Ndiye, akazi, pamene inu mukuganiza kuti inu mukhoza kukhala ndi tsitsi lodulidwa ndi kumabwera mu Kukhalapo kwa Mulungu, inu mukulakwitsa. Inu mukuziona izi? Inu mukulakwitsa; inu simungakhoze kubwera kudutsira mu Fyuluta ya Mulungu kumene inu mumatsukidwa ndi madzi a Mawu. Ndiye inu mumalowa mu chiyanjano. Inu mukuganiza kuti inu muli, koma simungakhoze kukhala muli mpaka inu mutabwera kupyolera mu Mawu, ndipo malo aang’ono aliwonse, Mawu aang’ono aliwonse a Mulungu. “Munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu ali onse.” Izo ziyenera kubwera kudutsira mu kusefedwa uko, kubwera modutsa. Ndipo izo zimapereka kukoma kwa munthu wolungama, chifukwa ndi zomwe iye akufunafuna, kufunafuna chinachake choti chimuyeretse iye.

Mawu, Mawu a Mulungu ndi Fyuluta ya munthu woganiza, ndipo Iyo imapangitsa kukoma kwa munthu wolungama. Ife tikudziwa kuti izo nzoona; kulisefa tchimo lonse la kusakhulupirira lichoke. Sipamakhala kusakhulupirira kwinanso pamene inu mubwera kudutsira mu Fyulutayo, chifukwa iko ndi kukoma koona kwa wokhulupirira.

Wokhulupirira woona amafuna azikhala wolondola, mulimonse. Iye samafuna basi kungoti, “Chabwino, ine ndi wa mmaudindo achitukuko. Ine ndi wa mpingo, mpingo waukulu mu tauni.” Ine sindikusamala ngati ili mishoni ya pa ngodya, kaya ndi ku gombe la pa tchire, kwinakwake, munthu woganiza amadziwa kuti ayenera kudzakomana ndi Mulungu. Ndipo mosasamal zomwe mpingo unena, kapena wina aliyense anena, iye ayenera kuti abwere pa zofuna za Mulungu. Ndipo zofuna za Mulungu ndi Mawu a Mulungu.

“Chabwino,” iwo amati, “ ‘Mawu a Mulungu.’” Zedi, onse awo amakhulupirira kuti Iwo ndi Mawu a Mulungu, koma kodi inu mungasefe kudutsira mu Iwo? Inu mungamulole bwanji mkazi wa tsitsi lodulidwa kudutsira Pamenepo? Inu muchita bwanji izo? Inu mungamulole bwanji mwamuna kubwera kudutsira apo yemwe sangagwiritse ku Chiphunzitso ichi? Mwaona? Uko si kukoma kwa munthu woganiza. Ayi. Mwamuna woganiza angaganize, mwamuna woganiza angaganize kawiri asanati adumphire mu chinachake chonga icho.

Zindikirani, Mawu awo sangakhoze kudzikana Okha. Ndiye iwo akhutitsidwa, kapena iwo ndi chokhumba. Ndi chokhumba cha chiani? Nchiani chinakupangani inu kuwakhumba Iwo, mu malo oyamba momwe? Chifukwa pansipo mu solo yanu munali mbewu yokonzedweratu yomwe inali Moyo Wamuyaya, nthawizonse ili mmenemo, nthawizonse inali mmenemo. “Onse omwe Atate andipatsa Ine adzadza kwa Ine. Palibe aliyense wa iwo ati adzatayike.”

Kukoma kwa munthu woganiza, pamene munthu woganiza amva Mawu a Mulungu, “Nkhosa Zanga zimamva Mawu Anga, mlendo izo sizingamutsatire,” pakuti pansi mkatimo muli Moyo, ndipo Moyo umalumikizana ndi Moyo. Tchimo limalumikizana ndi tchimo, ndipo tchimo ndi lachinyengo kwambiri mpaka ilo limaganiza kuti lapulumutsidwa pamene ilo silinapulumutsidwe. Ilo liri mu kuya kumene kwa chinyengo.

Werengani akaunti yonse mu...
Fyuluta ya munthu woganiza.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha m’malo mwa mpingowo

kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.

Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro.

Aefeso 5:25-27


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)
 

Chapter 11
- The Cloud

(PDF Chingerezi)
 

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)