Mulungu wa m’badwo woipa uno.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Nthawi yotsiriza mndandanda.

Ukuitanira Mkwatibwi kwa Khristu.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Mulungu wa m’badwo woipa uno.

Tsopano, phunziro langa mmawa uno, ndiro: Mulungu Wa M'badwo Woipa Uno. Monga ife tawerengera mu Malemba, “Mulungu wa dziko lino, m'badwo woipa uno.” Tsopano, Uthenga uwu ukuloza zoipa za m'badwo woipa uno, ndipo iwo ukukwanira ku ulosi wa m'badwo woipa uno. Ndipo ndikukhulupirira kuti aliyense... kuti Baibulo liri nalo yankho lirilonse la m'badwo uliwonse, linalembedwa kale mu Baibulo, la wokhulupirira wa m'badwo umenewo. Ine ndikhulupirira kuti chirirchonse chimene ife timachisowa chinalembedwa momwemu Umu, zikungosowa kuti zitanthauziridwe ndi Mzimu Woyera. Ine sindikukhulupirira kuti munthu aliyense pa dziko lapansi ali nawo ufulu woika kutanthauzira kwake kwake ku Mawu. Mulungu samasowa aliyense kuti atanthauzire Mawu Ake. Iye ndi Wodzitanthauzira Iye Mwini. Iye anati Iye akanadzachita izo, ndipo Iye akuchita izo.

Monga ine ndanenapo nthawi zambiri. Iye anati, “Namwali adzaima,” Iye analankhula zimenezo kudzera m'milomo ya mneneri, ndipo iye anatero. Palibe aliyense ayenera kutanthauzira zimenezo. Pachiyambi, Iye anati, “Kuwale,” ndipo zinachitika. Palibe amene ayenera kutanthauzira Izo. Iye anati, “Mu masiku otsiriza, Iye adzatsanulira Mzimu Wake pa mnofu wonse,” ndipo Iye anatero. Izo sizikusowa aliyense kuti atanthauzire Izo. Iye anati, “Mu masiku otsiriza, zinthu izi” (zimene ife tikuziwona zikuchitika tsopano) “zidzakhala pano.” Izo sizikusowa kutanthawuzira kulikonse. Izo zinatanthauzirirdwa kale. Mukuona?

Tsopano, zindikirani mwatcheru tsopano pamene ife tikuphunzira Mawu. Mulungu wa M'badwo Woipa Uno, umene ife tiri kukhalamo. Zikhoza kuwoneka zachilendo, chinthu chachilendo kwambiri, mu m'badwo uno wachisomo, pamene, “Mulungu akuwatenga anthu chifukwa cha Dzina Lake,” ameneyo ndi Mkwatibwi Wake, mu m'badwo woipa uno umene uyenera kutchedwa m'badwo wa zoipa. M'badwo umene “Mulungu akuwaitana anthu chifukwa cha Dzina Lake,” mwa chisomo, kuwatulutsa, ndipo uwo ukutchedwa m'badwo oipa. Tsopano ife titsimikizira mwa Baibulo kuti uno ndi m'badwo umene Iye anali kulankhula za iwo.

Chinthu chachilendo kwambiri kuti uchiganizire, kuti mu m'badwo woipa wonga uwu, kuti Mulungu ndiye angakhale akumaitana Mkwatibwi Wake. Inu mukuzindikira, Iye anati, “Anthu,” osati “Mpingo.” Bwanji? Komabe, iwo ukutchedwa Mpingo, koma Iye akanadzaitana “anthu.” Tsopano, mpingo ndi kusonkhana kwa anthu ambiri a mapangidwe onse osiyanasiyana. Koma Mulungu akumuitana m'modzi apa.... Iye sanati, “Ine ndidzawaitana a Methodisti, Baptisti, Pentekoste.” Iye anati Iye adzawaitana anthu. A chiyani? a Dzina Lake. Mwaona, anthu; m'modzi kuchokera ku Methodisti, m'modzi kuchokera ku Baptisti, m'modzi ukuchokera ku Lutheran, m'modzi kuchokera ku Katolika. Mukuona? Koma Iye akuitana, osati, gulu la mpingo, koma “anthu chifukwa cha Dzina Lake,” amene akulandira Dzina Lake, otomeredwa mu Dzina Lake, akupita ku chikwati kuti akakwatiwe ndi Iye, kuti akakhale gawo la Iye, mwaona, mwa kukonzedweratu. Chimodzimodzi monga mwamuna amene amasankha mkazi woyenera mu moyo, anadzozedweratu kuti adzakhale gawo la thupi lake. Kotero, zimenezo ndizo, Mkwatibwi wa Khristu adzakhala, ndipo alipo tsopano, kuchokera kale, anadzozedwa ndi Mulungu kuti adzakhale gawo la Thupi limenelo. Mukuona? O, Malemba ndi okhathamira kwambiri, odzaza uchi!

Zindikirani, osati zimene winawake wanena, zimene winawake waziitana; koma zimene Mulungu anazisankha asanaikidwe maziko a dziko lapansi, ndipo akuwaitana anthu awa m'masiku otsiriza; osati bungwe. “Anthu chifukwa cha Dzina Lake.” Ndipo m'badwo woipa uno ndi pamene Iye akuchita izo, m'badwo uno kumene wa chinyengo.

Sabata yathayi, mu Mateyu 24, iwo unali m'badwo wachinyengo wa mibadwo yonse. Mibadwo yonse ya chinyengo, kuyambira m'munda wa Edene, njira yonse mpaka m'musi, sipanayambe pakhalapo m'badwo wachinyengo kwambiri ngati m'badwo uno. “Aneneri onyenga adzauka ndipo adzasonyeza zizindikiro ndi zodabwitsa, ngati nkotheka kuti akanyenge Osankhidwa omwe.” Mukuona? Tsopano, mipingo yozizira basi, yofunda, yokhuthara, ndi zina zotero, ya mbalume zopangidwa ndi anthu, zomwe sizingakhale; wosankhidwa sadzapereka tcheru chirichonse kwa izo. Koma ziri kumeneko pafupifupi ngati chinthu chenichenicho. Kungowasiya Mawu amodzi ndi zonse zimene inu muyenera kuchita. Zolonjezedwera m'badwo; nthawi zopambana zedi! Akhristu, konsekonse, musamalitse ora limene ife tiri nkukhalamo! Mulembe, ndipo mukawerenge, ndipo mukamvetsere mwatcheru.

Kodi Mulungu akuwaitaniranji anthu atuluke mu m'badwo woipa uno, a Dzina Lake? Chifukwa chake ndi chakuti, amuyese Iye, Mkwatibwi Wake. Ndikuti.... Pamene Iye akuwonetseredwa, akuyesedwa, akutsimikiziridwa, akutsimikiziridwa kwa Satana. Monga izo zinali pachiyambi, chomwecho izo zidzakhala pamathero.

Monga mbewu imayambira mu nthaka, iyo imabwera kudzera mwa zotengera, moyo wa iyo, koma iyo imadzatsirizira kukhala mbewu yomweyo mmene iyo inaliri pamene iyo inkapita mu nthaka. Ndipo mwanjira yomweyo mbewu yachinyengo inagwera mu nthaka, mu Edene, ndipo mwanjira yomweyo ikudzathera mu masiku otsiriza. Chimodzimodzi basi monga m'mene Uthenga unali pamene iwo unadzagwera kwa chipembedzo ku Nicaea, Roma, iwo ukudzathera mu bungwe lapamwamba. Chimodzimodzi basi monga mbewu ya mpingo inagwera kumbuyo uko, ndi zizindikiro, zodabwitsa, ndi Khristu wamoyo pakati pawo, iyo ikudzathera mu masiku otsiriza pansi pa utumiki wa Malaki 4, ndi kudzabwezeretsanso Chikhulupiriro chapachiyambi chimene chinaperekedwa kamodzi.

Ife tikupeza tsopano, m'badwo woipa uno uli wakuti udzatsimikizire, kwa Satana, Iye sali monga Hava, kuti Iye sali monga mkazi wa mtundu umenewo. Ndipo Iye adzayesedwa ndi Mawu Ake, Mkwatibwi, monga mkwatibwi wa Adamu anayesedwa ndi Mawu. Ndipo mkwatibwi wa Adamu anakhulupirira chidutswa chirichonse cha Mawu, onse, koma anasokonezaka pa lonjezo limodzi, lakuti, “Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawi zonse,” lero, mwaona; koma analephera pa lonjezo limodzi, pansi pa yesero la mdani, maso ndi maso. Ndipo tsopano, anthu amene akuitanidwira Dzina Lake, zoona, ali Mkwatibwi Wake. Iye ayenera kukomanizana nacho chinthu chomwecho; osati kokha mwa choonadi cha chipembedzo kapena chinachake, koma Mawu aliwonse!

Pakuti, pachiyambi cha Baibulo, munthu anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti azikhala nawo moyo. Mawu amodzi, atatanthauziridwa molakwika ndi - munthu wotchedwa Satana, mwa munthu wa chinyama wotchedwa serpenti. Satana, mwa munthu uyu, amakhoza kulankhula ndi Hava, ndipo anatanthauzira molakwika Mawu kwa iye, ndipo anataika. Mwaona, Izo ziyenera kukhala Mawu aliwonse.

Pakati pa Baibulo, Yesu anabwera ndipo anati, “Munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu onse,” pamene Iye anadzayesedwa ndi Satana. Tsopano, Mulungu akutiuza ife kuno mu masiku otsiriza, kuti, “mulungu wa dziko lino adzauka mu masiku otsiriza.” “Ndipo aliyense amene adzawonjezera mawu amodzi kwa Iwo, kapena kuchotsera liu limondzi kwa iwo, gawo lake lidzachotsedwa kuchokera mu Buku la Moyo.” Mulungu atichitire ife chifundo! Ndipo asatitole ife kuti tiziyenda ngati Malaya okhuthara, zidali panja, mutu m'mwamba, odziwa zonse, pakuti ife nafenso nthawi ina tinali mu kusamvera. Tiyeni ife ndi chisomo, ndi chifundo, ndi kukhudzidwa mu mtima mwathu kwa Mulungu, tibwere modzichepetsa ku Mpando wa Chifumu wachisomo.

Zachilendo tsopano, patadutsa zaka zina mazana khumi ndi asanu ndi anayi za kulalikira Uthenga, ndipo tsopano iye, kameneko ndi kachitidwe ka chidziko, ndi koipa kwambiri kuposa mu masiku pamene izo, pamene iye anali kuno. Kachitidwe ka kachidziko ndi koipa kwambiri. Dziko lalunjika ku mapeto aakulu. Inu mukudziwa zimenezo. Ambuye akukwaniritrsa Mawu Ake paliponse.

Chivumbulutso 18:4-5,
4 Ndipo ine ndinamva liwu lina kuchokera Kumwamba, likuta, Tulukani mwa iye, anthu anga, kuti inu musakhale otenga nawo a machimo ake, kuti inu musalandire za miliri yake.
5 Pakuti tchimo lake lafikira M'mwamba, ndipo Mulungu akukumbukira kusaeruzika kwake.

----
Ndi chenjezo bwanji! Zimenezo zikuwuponyera mpingo ndendende m'mbuyo ku Chivumbulutso 3:14, mpaka ku m'badwo wa Laodikaya, wolekerera; wachipembedzo kwenikweni, koma wolekerera. “Iwe, chifukwa iwe unena kuti, 'Ife tiri olemera, sitisowa kanthu,' iwe sukudziwa kuti ndiwe wamaliseche, womvetsa chisoni, wakhungu, ndipo sukudziwa izo ayi.” Mwangwiro ndi Lemba la m'badwo uno, osati Lemba la m'badwo wa Daniele, osati, iwo a dzina la.... m'badwo wa Nowa, koma mu m'badwo wotsiriza uno, woipa.

Zindikirani apa, “Iwe uli wamaliseche.” Mulore zimenezo zilowerere mwakuya kwenikweni. Ine ndikudziwa ndikhoza kukhala ndi kusagwirizana kochuluka pa lingaliro ili, koma zafika pamalo akuti Mkhristu sizingatheke kutuluka m'nyumba yake ndipo nkusabweretsedwa mu kukhalapo kwa m'badwo woipa uno, ndi akazi ovala mosakwanira.

Akazi, ine ndinena izi, ndipo ine ndikufuna kuti inu mumvetsere. Ndipo, amuna ndi akazi, inu mukhoza kutsutsana nazo izi, koma ine ndikumverera kutsogozedwa kuti ndinene izi. Kodi inu mukudziwa, mkazi aliyense yemwe amadzivula yekha monga choncho mutu wake sukuyenda bwino? Kodi inu mukudziwa, iye ali, kaya iye akhulupirira izo kapena ayi, kapena sakuganiza chomwecho, iye ndi wachiwerewere? Ngakhale mkaziyo akhoza kuima ndi dzanja lake pamaso pa Mulungu ndi kulumbirira kuti iye sanayambe wakhudzidwapo ndi mwamuna aliyense koma mwamuna wake, ndipo izo zikhoza kukhala zoona zenizeni, komabe iye ndi wachiwerewere. Yesu anati, “Aliyense amene ayang'ana pa mkazi namukhumba iye wachita naye kale chigololo.” Ndipo mkaziyo akhoza kukhala....

Taonani, iye ali “wamaliseche,” Baibulo linatero, “ndipo sakudziwa izo ayi.” Mzimu umene ukumudzoza iye kuti azichita zoterozo ndi woipa, mzimu wachiwerewere. Mawonekedwe ake akunjaku, thupi lake, mnofu wake, iye akhoza kukhala woyera. Iye akhoza kusamachita chigololo chirichonse, ndipo akhoza kulumbira kwa Mulungu ndipo nkukhala zoona, kuti iye sanateropo, koma mzimu wake ndi mzimu wachiwerewere. Iye wachititsidwa khungu kwambiri ndi mulungu wa dziko lino wa fashoni; iye wadziveka yekha mwachigololo ndipo akumapita kunja uko.

----
Munthu wakunjayu ndi chinthu chogwirika chimene chimalamuliridwa ndi zokhudzira zisanu ndi chimodzi...kapena zokhudzira zisanu, kani. Munthu wamkatiyo ndi munthu wauzimu amene amalamuliridwa ndi zokhudzira zisanu; chikumbumtima, ndi chikondi, ndi zina zotero. Munthu wakunjayu; kuwona, kulawa, kukhudza, kununkhiza, kumva. Koma mkati mwa mzimu umenewo muli solo, ndipo iyo imalamulirirdwa ndi chinthu chimodzi, kufuna kwanu. Inu mukhoza kuvomereza zimene mdierekezi akunena kapena kuvomererza zimene Mulungu akunena. Ndipo zimenezo zidzatengera mzimu umenewo uli m'menemo. Ngati iwo uli Mzimu wa Mulungu , Iwo uzidzadya pa zinthu za Mulungu, ndipo Iwo sudzadya pa chirichonse cha mdziko. Yesu anati, “Ngati inu mulikonda dziko kapena zinthu za m'dziko, ndi chifukwa chakuti chikondi cha Mulungu sichinalowe nkomwe mu gawo la mkatili.” Satana wakunyengani inu. “Ndipo munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu onse otuluka kuchokera mkamwa mwa Mulungu.”

Zindikirani tsopano, ife tikupeza kuti iye ali “Wamiseche,” wachisembwere ndi wambulanda. Ndipo dziko likuwoneka kuti liri mu m'badwo woipa kwambiri umene unayamba wakhalapo. Palibepo mu m'badwo uliwonse m'mene akazi anayamba achitapo monga choncho, ayi nkomwe koma basi chisanachitike chigumula cha dziko. Ndipo Yesu analozera kwa izo. Ife tifika kwa izo pakapita kanthawi.

Kodi Mulungu wataya ulamuliro, kapena kodi Iye akungoloreza nthumwi ina kuti ilamulire? Ine ndikudabwa. Yankho loona kwa funso ili ndiro, mwa kulingalira kwanga, ilipo mizimu iwiri yotsutsana mu dziko lero, imene ikugwira ntchito. Tsopano, sipangakhalenso yoposa iwiri, mitu iwiri. Ndipo Umodzi wa iyo ndi Mzimu Woyera ukugwira ntchito; umodzi winawo ndi mzimu wa mdierekezi, ndipo, mu masiku otsiriza ano, mu chinyengo. Tsopano ine ndikhazikitsa malingaliro anga pomwe apa kwa phunziro lonseli, wonsewu.... Uthenga wathu.

Mizimu iwiri. Umodzi wa iyo, Mzimu Woyera wa Mulungu; winawo, mzimu wa mdierekezi, ukugwira ntchito mwa chinyengo. Anthu a padziko lapansi tsopano akupanga kusankha kwawo. Mzimu woyera uli pano ukuitanira Mkwatibwi kwa Khristu. Iye akuzichita izo pa kuwatsimikizira Mawu Ake a lonjezo kwa Iye, a m'badwo uno, kusonyezera kuti Iwo ndi Khristu. Ngati chala chiyenera kuti chisunthe mu m'badwo uno, chalacho chisuntha. Ngati phazi liyenera kuti lisunthe mu m'badwo uno, phazilo lisuntha. Ngati diso liyenera kuti lipenye mu m'badwo uno, disolo lipenya. Mukuona? Mzimu wa Mulungu, pamene Iwo wakula kukhala thunthu lamphumphu la Mulungu, ndiwo m'badwo umene ife tiri kukhalamo tsopano. Mzimu Woyera uli pano ukutsimikizira Uthenga wa orali. Ndipo Mzimu Woyera ukuchita zimenezi, kuti anthu amene akumukhulupirira Mulungu aitanidwe atuluke kuchoka mu chisokonezeko ichi. Mzimu wosayera wa mdierekezi uli pano ukuitana mpingo wake mwa kulakwitsa, mwanthawi zonse, mwa kupotoza kwa Mawu a Mulungu, monga iye anachitira pachiyambi. Mukuziwona izo zikubweranso kudzafika ku nthawi ya mbewu iyo kachiwiri, kuchokera ku Edene? Ndi izi apa kachiwiri.

Werengani akaunti yonse mu...
Mulungu wa m’badwo woipa uno.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero.

Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa.

Chivumbulutso 18:1-2



 

Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Mulungu kudzibisa
yekha mu kuphweka...

(PDF)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.