Chomupachika kachiwiri Yesu Khristu.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Chitsutso.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Chitsutso.Ndipo tsopano, lero, ine ndikufuna kuti ndiwerenge Lemba lina, miniti chabe, kuchokera mu Mawu oyera, opatulika a Mulungu, opezeka mu Bukhu la Luka Woyera. Mutu wa 23 wa Luka Woyera, kuti tiyambirepo, tipeze... nsanja ya chimene ine ndikufuna kuti ndinene, lingaliro la maziko pa chinthu chimene ine ndikufuna kuti ndiyankhulepo. Ndipo inu mukutembenuzira tsopano ku Luka Woyera, mutu wa 23, ndipo ine ndikufuna kuti ndiwerenge ndime imodzi. Ndizo zonse zomwe ine ndikusowa kwa maziko awa mmawa uno, kuti ndiziyikepo izi. Tsopano ife tikuwerenga ya 20 mutu wa 23, ndime ya 33 ya mutu wa 23.
Ndipo pamene iwo... anafika ku malo, amene amatchedwa Gologota, kumeneko iwo anamupachika iye, ndi ochita zoipa, mmodzi ku dzanja lamanja, ndi winayo ku lamanzere.
Tsopano ine ndikufuna kuti nditenge mawu anai kuchokera pamenepo, kuchokera pa kuwerenga uko, kuti tiyike maziko pa chimene ine ndikufuna kuti ndinene, “kumeneko iwo anamupachika Iye,” mawu anai. Ndipo tsopano phunziro langa likutchedwa^Ine_ine ndikubweretsa chitsutso kwa mipingo ya zipembedzo ya tsiku lino, ndiponso yambiri ya oyima paokha, chifukwa chomupachika Yesu Khrisu mwatsopano mu tsiku lino. Ndikuwatsutsa iwo. Mmawa uno, iwo ukutchedwa: Chitsutso.
Ndipo ine ndikufuna kukhala ngati kuligwiritsa ilo ntchito mochuluka ngati kuti chinali chipinda cha bwalo la mulandu, pamene izo zinali...Ndipo pakutibe, guwa ndi mpingo ndilo bwalo la mulandu. Baibulo linati, “Ndiwo mpando wachiweruzo....kuti icho chiyenera kuyambira mu nyumba ya Ambuye.” Ndipo izi ziri monga mpando wachifumu ndi nduna, ndi mboni, ndi ena otero. Ndipo ine ndiri nawo, lero, ngati mboni yanga, ndiwo Mawu a Mulungu. Ndipo chitsutso changa chiri chotsutsa mipingo ya lero. Tsopano ine sindiri kumubweretsa wochimwa kuti alowe mu izi. Ine ndikungoyankhula izi kwa mpingo. Ndipo izo ziri zoti zikhale mu ma matepi tsopano, ndipo ine ndiyesa kuti ndidutsemo mofulumira momwe ine ndingathere.
Ine ndikuwutsutsa m'badwo uno chifukwa chomupachika kachiwiri Yesu Khristu.
Ndipo tsopano kuti ndichite ichi mu m'badwo uno umene ife tikukhalamo, ine pochita ichi, ine ndiyenera kusonyeza umboni. Ngati ine ndingati ndibweretse chitsutso, iwe uyenera kusonyeza umboni wa mulandu wakuphawo umene wachitidwa. Ine ndiyenera, kuti ndiwatsutse iwo, ine ndiyenera kuti ndibweretse umboni kuti nditsimikizire izo, kuti izo ziri, kuti zimene ine ndikunena zionekere pamaso pa Woweruza wamkulu. Chimene, ndipo ine ndikudzitenga ndekha ngati nduna ku... pa chitsutso ichi. Kuti, Mawu a Mulungu, pokhala mboni yanga, ine ndikuwutsutsa m'badwo uno chifukwa cha kupachika.
Ine ndiyenera kusonyeza, ndipo ndisonyeza, kuti mzimu womwewo uli pa anthu lero umene unabweretsa kupachikidwa koyamba, ndipo akuchita chinthu chomwecho. Ine ndiyenera kuchita izo, ngati icho chiti chikhale kupachika, kuti iwo amupachika. Ine ndiyenera kusonyeza kanthu kuti kachitidwe komweko mwa anthu lero kali kuchita chinthu chomwecho, mwauzimu, chimene iwo anachita mwathupi apo. Iwo anamupachika, mwathupi, Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu.
Ndipo tsopano, lero, mwa Mawu omwewo, ndi mwa Mzimu Woyera womwewo ndi Mawu omwewo, ine ndikukhumba kuti ndiyisonyeze mipingo apo pamene iyo ikuima, kuti iwo akuchita chinthu chomwecho lero, ndipo Baibulo linati iwo akanadzachita izo, ndipo kutsimikizira kuti ili ndi tsiku limene ife tiri kukhalamo. Izo sizikanakhoza kukhala zikuchitidwa zaka zingapo zapitazo. Ine ndikuti, zaka makumi asanu zapitazo izo sizikanakhala zikuchitidwa, koma lero izi ziri mu nthawi yake. Ndipo izo sizikanakhala zikuchitidwa, mwinamwake, zaka khumi zapitazo, koma izo zikhoza kuchitidwa lero chifukwa nthawi yatha. Ife tiri pa nthawi yotsiriza. Ndipo ine ndikukhulupirira, monga wantchito Wake, kuti ife tiri basi pafupi kuti tiwoloke kuchokera mdziko lino, kupita ku Lina.
Chotero, nthawi ya kulapa, kwa fuko, iyo yapita. Ine ndikukhulupirira kuti fuko lino silingakhoze kulapa. Ine ndikukhulupirira kuti ilo lawoloka mzere wa pakati pa chifundo ndi chiweruzo. Ine ndikukhulupirira kuti ilo likuzandima mu muyezo.
“M'bale Branham, inu musanati muyambe mulandu wanuwo, kodi inu mutsimikizira chotani izo?” Izi zokha, kuti ife tiri olakwa ndi machimo omwewo amene Mulungu anawonongera nawo dziko, mu dziko la chigumula. Ndife olakwa ndi machimo omwewo amene Iye anawonongera dziko mu Sodomu ndi Gomora. Ndipo, tsopano, ndipo ife tiri nawo umboni wonse wofanana wauzimu uli pano patsogolo pathu, umboni wonse wofanana, wodziwika konsekonse mdziko, umene unabweretsa pansi zifundo za Mulungu pa mibadwo imeneyo. Kuti, iwonso, pokana, zinabweretsa chiweruzo. Kotero ngati m'badwo uno wakana chifundo chomwecho chimene chinakanidwa mu masiku amenewo, Mulungu angakhale wosalungama kuti awasiye iwo kuti adutse nazo opanda chiweruzo.
Tsopano, ife tikudziwa kuti mwauzimu iwo akuchita chinthu chomwecho lero, chifukwa iwo akuchita icho, nawonso, mwa cholinga chomwecho, ndipo mwa njira yomweyo imene iwo anachitira mu kupachikidwa kwa Ambuye, mwathupi. Iwo akuchita izo chifukwa cha nsanje, chifukwa cha khungu lauzimu. Kuti, iwo sakufuna kuti apenye. Iwo sangamvetsere kwa Izo. Yesu, mu ulendo Wake kuno pa dziko lapansi, Iye anati, “Yesaya anayankhula bwino za inu, 'Inu muli nawo maso ndipo simungakhoze kupenya, ndi makutu ndipo simungakhoze kumva.'”
Chifukwa chomwecho, chofanana. Cholinga chofanana ndi zifukwa zofanana, iwo akubweretsa kupachikidwa kwa Khristu mwatsopano, mochitanso, (monga ife titi tifike ku izo pakapita kanthawi), pa zifukwa zomwezo zimene iwo anachitira apo. Iwo sangakhoze kupeza kanthu kena kotsutsira Izo. Iwo sangayerekeze kuti ayesere kuzitsutsa Izo. Ndipo iwo amadziwa kuti umboni ulipo. Ndipo iwo amadziwa kuti Baibulo limanena chomwecho. Ndipo chinthu chokha chimene iwo angakhoze kuchita ndi kuchitira mwano Iwo. Ndizo ndendende. Kotero, ndipo zonse izi, zifukwa zofanana.
Ndipo tsopano, pa maziko awa, ine ndikuchita makani kwa m'badwo uno pa kumupachika Yesu Khristu; chifukwa chomupachika, ndi olakwa; ndi manja akuda, authakati, awumbombo, azazipembedzo ali nawo pa kumupachika Kalonga wa Moyo yemwe ankafuna kuti adzipereke Iyeyekha kwa anthu.
Inu mukuti, “Munthu yemweyo?”
“Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anapangidwa thupi, ndipo anadziwonetsera Iwowokha.” Mawu anawonetseredwa mu thupi, ndipo iwo analiweluza thupi ndipo analiyika Ilo ku imfa, chifukwa Mawu anali atawonetseredwa. Ahebri 13:8, amati, “Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse.” Ndi Mawu omwewo. Mwaona? Ndipo, mwa chifukwa chomwecho, iwo akuyesera kuti awapachike Mawu.Tsopano, ku mutu wanga, kuti ndiswere mmbuyo pa phunziro limene ine ndikufuna kuti ndilitenge pamenepo, mawu anai. Tiyeni tifotokoze, “kumeneko.” “Kumeneko,” mzinda woyera kwambiri mu dziko, Yerusalemu. “Kumeneko,” mzinda wachipembedzo kwambiri mu dziko. Kumeneko, “iwo,” anthu achipembedzo kwambiri mu dziko, pa phwando la chipembedzo, phwando la Paskha. “Kumeneko,” malo achipembedzo kwambiri, mzinda wachipembedzo kwambiri, bungwe lalikulukulu mwa mabungwe onse, mutu wa zinthu zonse, kumeneko, “iwo,” anthu achipembedzo kwambiri pa dziko lonse, anali atasonkhana kuchokera konsekonse mu dziko. Iwo “anamupachika,” imfa yochititsa manyazi kwambiri yomwe ikadakhalapo, kumupha, munthu akanakhoza kuphedwa nayo; wamaliseche, atamuvula zovala kuzichotsa pa Iye. “Iye ananyoza chitonzo.” Mtanda uli nako kasanza katakulungidwa pa Iye; koma iwo anamuvula zovala Zake. Yochititsa manyazi kwambiri...
“Kumeneko,” (mzinda wawukulukulu wachipembedzo,) “iwo,” (anthu achipembedzo kwambiri,) “anamupachika,” (imfa yamanyazi kwambiri,) “Iye,” (Munthu wofunika kwambiri.)
Ngati izo siziri zokwanira kuti ziwutsutse m'badwo uno! “Kumeneko,” bungwe lachipembedzo kwambiri, lalikulukulu kwa mipingo yonse itasonkhana palimodzi mu malo amodzi. “Iwo,” anthu achipembedzo kwambiri a mitundu yonse, anthu amene ayenera kukhala ali omupembedza kumene a Mulungu. Iwo anasonkhana pa phwando lalikulukulu lopatulika limene iwo anali nalo, kuyeretsa kwa Paskha, pamene iwo anabweretsedwa kuchokera ku msinga kumka mu kumasuka. Ndipo “kumeneko” mu nthawi imeneyo, “iwo” pa nthawi imeneyo, anthu achipembedzo kwambiri, mu phwando lachipembedzo kwambiri, pa malo achipembedzo kwambiri, anabweretsa pa Kalonga wa Moyo chinthu chochititsa manyazi kwambiri chimene chikanakhoza kuchitidwa, kumuvula Mwamuna ndi kumupachika Iye pa mtengo. Chifukwa, “Wotembereredwa ali iye,” litero lamulo limene iwo ankapembedza nalo, “wotembereredwa ali iye amene apachikidwa pa mtengo.” “Ndipo Iye anapangidwa themberero chifukwa cha ife.” Kumuvula zovala zake, kumumenya Iye, ndi kumutonza Iye, Mulungu yemwe wa Kumwamba; kutenga zovala Zake kuzichotsa pa Iye, ndi kumukhomera Iye pa mtanda. Iye! “Kumeneko iwo anamupachika Iye,” pansi pa chilango chachikulu cha Chiroma.
Imfa yochititsa manyazi kwambiri lero siikanati ikhale kuwomberedwa. Imfa yochititsa manyazi kwambiri lero siikanati ikhale kuti ugundidwe ndi galimoto ndi kuphedwa, kumizidwa ndi madzi, kuwotchedwa ndi moto. Koma imfa yochititsa manyazi kwambiri lero ili chilango chachikulu chapoyera, kumene dziko lonse lingakuweruze iwe ndi kukutcha iwe wolakwa. Ndipo dziko lonse linaika manja awo pa Mwamuna uyu ndipo anamutcha Iye wolakwa, pamene Iye anali wosalakwa. Ndipo Iye anafa pansi pa adani, (osati abwenzi Ake, osati malamulo Ake), koma pansi pa kupachika kwa mdani. Kalonga wa Moyo, Munthu wofunika kwambiri yemwe anayamba wakhalapo, kapena ati adzakhalepo konse, Yesu Khristu. “Iye,” Munthu wofunika kwambiri! Sungani zimenezo mmalingaliro tsopano pamene ife tikumanga nsanja imeneyo mozungulirapo lero.
-----
Tsopano mawu anai aja, iwo, “Kumeneko iwo anamupachika Iye.” Tsopano, inu mukanali kusonyeza Baibulo, inu mukuona. Ndi mawu anai okha, koma Baibulo limachepetsa Zoonadi Zake. Tsopano, ine, ine ndiyenera kuti ndipite mozungulira, kuti ndifotokoze zimene ine ndikuziyankhula, koma Baibulo silisowa kuchita kufotokoza kanthu. Ilo basi liri lonse Choonadi, kotero Baibulo silisowa kuchita kufotokoza chirichonse. Ilo silimasowa kuchita kufotokoza izo, chifukwa Ilo liri lonse Choonadi.Pano pali mawu anai a unyolo Wake wawukulu wa Choonadi. Ine ndiyesera kuti ndiwafotokoze iwo. Ndipo kuti ndiyesere kuwafokoza Iwo, momveka, zingapange nyumba yazowerenga. Palibe njira kwa ine yoti ndingafotokoze mawu anai amenewo. Koma tsopano tiyeni ife, mwa kuthandiza kwa Iye Yemwe anapangitsa Iwo kuti alembedwe, tiyesere kufotokoza mawu anai awa, kuti tibweretse izo mwa njira yotero kuti anthu akhoze kumazimvetsa izo. Chimene ife tiri nacho patsogolo pathu tsopano, ife tiri nako kupachikidwa koyamba kutayikidwa patsogolo pathu; pa malo opatulika kwambiri, anthu achipembedzo kwambiri, imfa yochititsa manyazi kwambiri, kwa Munthu wofunika kwambiri. O, ndi zotsutsana chotero. Mai, o, mai, ndi chochititsa manyazi!
-----
Zindikirani, “iwo,” opembedza, amuna amene anali atayang'anira lonjezo, amuna amene anali ataliyang'anira ilo, kupyola mu zaka ndi mibadwo, ndipo alibe chinthu choti nkuchita koma mu seminare imeneyo mowirikiza. Koma iwo anali atawagawaniza Mawu malingana ndi kuphunzitsa kwa seminare, ndipo iwo anali ataphonya Choonadi chomwe cha Iwo. “Iwo,” ansembe, utumiki wa tsiku limenelo! “Kumeneko,” ku likulu lawo, “iwo,” utumiki wa tsiku limenelo, unali kumupha Mulungu yemwe, Mwanawankhosa yemwe. Mmodzi yemweyo amene iwo amadzinenera kuti anali kumupembedza, iwo anali kupha.Ndipo, lero, ine ndikutsutsa gulu ili la atumiki odzozedwa; mu tizikhulupiriro tawo ndi zipembedzo, iwo akumupachika, kwa anthu, Mulungu yemweyo amene iwo akudzinenera kuti iwo amamukonda ndi kumutumikira. Ine ndikuwatsutsa atumiki awa, mu Dzina la Ambuye Yesu, pa kachiphunzitso kawo, kamene amati nako kuti “masiku a zozizwitsa anapita,” ndikuti “ubatizo wa madzi mu Dzina la Yesu Khristu suli wokwanira ndipo si wolondola.” Pa Mawu aliwonse awa, omwe iwo alowezeramo tizikhulupiriro, ine ndikuwatsutsa iwo, ngati olakwa, ndipo Magazi a Yesu Khristu ali mmanja mwawo, chifukwa chomupachika katsopano Ambuye Yesu, nthawi yachiwiri. Iwo ali kumupachika Khristu, ku gulu, kutenga kuchokera kwa iwo chinthu chimene iwo akuyenera kuti azichipereka kwa iwo. Ndipo iwo akulowezetsamo chinthu chinachake mu malo Ake; kachikhulupiriro ka mpingo, kuti atchuke.
-----
Ndipo ine ndikuliweruza gulu lomwelo lero, ndipo ine ndikuwatsutsa iwo, ngati olakwa pamaso pa Mulungu, mwa Mawu a Mulungu, kuti iwo akuchita chinthu chomwecho. M'badwo uno watsutsidwa. Kumbukirani Ahebri 13:8, “Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawizonse.” Kodi iwo anamutsutsa chotani Iye? Chifukwa kuti tizikhulupiriro tawo sitikanamulandira Iye, ndipo pansi mu mtima mwawo iwo ankadziwa mosiyana. Kodi Nikodimo, mu mutu wa 3 wa Yohane Woyera, sanafotokoze bwinobwino izo? “Mphunzitsi, ife, Afarisi,” alaliki, aphunzitsi, “ife tikudziwa Ndinu mphunzitsi wotumizidwa kuchokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu akanakhoza kumachita zinthu zimene Inu mukuchita kupatula ngati Mulungu akanakhala ndi iye.” Mwaona? Iwo mwapagulu anachitira umboni izo mwa mmodzi wa amuna awo otchuka, ndipo chifukwa cha tizikhulupiriro tawo, iwo anamupachika Khristu.Ndipo lero palibe mwerengi yemwe sangakhoze kuwerenga Machitidwe 2:38 mofanana monga ine ndingakhoze kuwawerenga Iwo, ndi ena onse a Iwo, mofanana basi monga ine ndingakhoze kuwawerenga Iwo. Koma chifukwa cha tizikhulupiriro tawo, ndi chifukwa cha matikiti achipembedzo chawo omwe iwo ali nawo mu thumba mwawo, zilemba za chirombo zomwe iwo akunyamula konsekonse ngati makadi achiyanjano; ndi, potenga zinthu zimenezo, iwo akudzipachikira kwa iwoeni Yesu Khristu katsopano, ndipo akumupachika Iye pamaso pa gulu, ndi kuchitira mwano Mulungu yemwe amene analonjeza kuti adzachita Ichi, kubweretsa tsoka pa mtunduwo.
Werengani akaunti yonse mu... Chitsutso.