Chizindikiro.

<< m’mbuyomu

lotsatira >>

  Kuyenda kwa Chikristu mndandanda.

Chizindikiro.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Chizindikiro.

Eksodo 12:12-13.
12 Pakuti Ine ndidzadutsa kupyola mu dziko la Igupto usiku uno, ndipo ndidzakantha oyamba kubadwa onse mu dziko la Igupto, onse anthu ndi zinyama; ndi motsutsa milungu yonse ya Igupto Ine ndidzapereka chiweruzo: Ine ndine YEHOVA.
13 Ndipo magazi adzakhala ali kwa inu mwa chizindikiro pa nyumba yomwe inu mulimo: ndipo pamene Ine ndiwona magazi, Ine ndidzadutsa pa inu, ndipo mliri sudzakhala uli pa inu kuti ukuwonongeni inu, pamene Ine ndizikantha dziko la Igupto.

Tsopano ndi chiyani, poyamba, chizindikiro? Ndi mawu omwe amagwiritsidwa ntchito mwawamba pakati pa ife anthu oyankhula-Chingerezi, makamaka kuno ku Amerika. Chizindikiro ndi... Kwenikweni, dikishonare imanena kuti chizindikiro ndi chisonyezo, ndi chisonyezo cha dipo, mtengo woperekedwa, onani, kuti... dipo, kapena mtengo, mtengo wofunikira umene waperekedwa. Monga mtengo pa msewu wa njanji kapena mtengo wa pa basi. Iwe umapita umo ndi kukagula chako_chiphaso chako, ndiyeno iwo amakupatsa iwe chizindikiro, ndipo chizindikiro chimenecho sichingakhoze kugwiritsidwa ntchito kwa chirichonse koma pa msewu wa njanji umenewo. Ndipo icho ndi chizindikiro, kwa kampani ya njanji, kuti iwe walipira mtengo wako. Ndicho chizindikiro, ndipo iwe sungakhoze kuchigwiritsira ntchito kwa china chirichonse. Icho sichimagwira ntchito pa msewu wina uliwonse. Icho chimangogwira ntchito pa msewu umenewo wokha. Ndipo icho... ndi chizindikiro.

Tsopano pansi apa, zomwe ife tikuzikamba, pamene ife tikuyambirapo, ndi Mulungu akunena kwa Israeli, “Magazi a mwanawankhosa ali chizindikiro kwa inu.” Mwanawankhosa wa Israeli, ataphedwa, chinali chizindikiro chofunidwa ndi Yehova. Iwo ayenera kukhala magazi. Mulungu anapanga chizindikiro ndipo anachipereka icho kwa Israeli. Ndipo palibe chizindikiro china chiti chidzagwire ntchito, onani, icho sichingakhoze kuzindikiridwa.

Kwa dziko, Ndicho mulu wa zopusa. Koma, kwa Mulungu, Ili njira yokha. Chinthu chokha chimene Iye akuchifuna chiri Chizindikiro icho. Icho chiyenera kukhala pamenepo. Ndipo iwe sungakhoze kukhala nacho Chizindikiro mpaka mtengo utaperekedwa, ndiye iwe uli mwini wa Chizindikiro chimene chimakupatsa iwe_mwayi wa kudutsa mosavuta. “Pamene Ine ndiwona Magazi, Ine ndidutsa pa inu.” Ndi nthawi bwanji, iyo, ndi mwayi wanji, kudziwa kuti iwe wanyamula mkati mwako, Chiphaso. “Pamene Ine ndiwona Magazi, Ine ndidutsa pa inu.” Ndi chinthu chokha chimene Iye ati achizindikire. Si china chirichonse chimene chingakhoze kutenga malo Ake; palibe choloweza mmalo, palibe chipembedzo, palibe kanthu kalikonse. Izo zimatengera Icho. Mulungu anati, “Icho chokha Ine ndidzachiwona.”

Ziribe kanthu momwe iwo aliri olungama, momwe iwo analiri abwino, momwe iwo analiri ndi maphunziro, momwe iwo amavalira, chizindikiro chinali chinthu chokha. “Pamene Ine ndiwona chizindikiro, Ine ndidzadutsa pa inu.” Magazi anali chizindikiro kuti_chofuna cha Yehova chinali chitakwaniritsidwa, kuti icho chinali chitachitidwa. Magazi ankaima mmalo mwa chizindikiro. Magazi anali chizindikiro. Mwaona?

Mulungu anali atanena kuti, “Tsiku limene inu muti mudzadye za iwo, tsiku limenelo inu mudzafa.” Ndipo apo panali moyo wolowa womwe unatengedwa mmalo mwa moyo wa wokhulupirira. Mulungu, mu chifundo, anavomereza choloweza mmalo kwa munthu woyipitsidwa. Pamene mwana Wake anali atadziyipitsa yekha ndi tchimo, la kusakhulupirira Mawu, ndiye Mulungu, wolemera mu chifundo, anapanga choloweza mmalo; ndipo, icho chinali, chinachake chimayenera kuti chife mmalo mwake. Palibe chirichonse chikanakhoza kugwira ntchito.

Ndicho chifukwa maapulo a Kaini ndi mapichesi, ndi zina zotero, sizinagwire ntchito. Iwo unkayenera kukhala uli moyo umene unali ndi magazi mwa iwo, ndipo moyowo unali utapita kuchokera mu nsembe, ndipo tsopano magazi anali chizindikiro kuti dongosolo la Mulungu linali litachitidwa. Tsopano, kodi Mulungu ankafuna chiyani? Moyo; ndipo magazi ankasonyeza kuti apo pankayenera kukhala moyo utapita. Kotero magaziwo anali chizindikiro kuti moyo unali utaperekedwa, kuti chinachake chinali chitafa, chofuna cha Mulungu; kuti moyo unali utaperekedwa, ndipo magazi anali atakhetsedwa. Ndipo magazi ankaimira chizindikiro, kuti moyo unali utapita. Moyo wa chinyama umene Mulungu ananena kuti utengedwe, unali magazi amene ankayimira chizindikiro.

Wopembedza wokhulupirira ankazindikiridwa nayo nsembe yake, ndi chizindikiro. Ine sindikukhumba kuti ndikhale motalika kwambiri pa zobwereza zazing'ono izi, koma, zomwe iwe ungakhoze kutenga utumiki wathunthu pa chimodzi cha izo, koma ine ndikufuna kuti ndiyime pano mphindi kuti ndifotokoze izo. Wokhulupirira ankayenera kuti azindikiridwe ndi nsembe yake. Mwaona? Ngati iyo ili nsembe chabe ndipo itapangidwa kwinakwake kunja uko, iye anali atayipereka iyo; koma iye ankayenera kuti azindikiridwe mu iyo. Moona, iye ankayenera kuyika manja ake pa iyo, choyamba, kuti adzizindikiritse iyemwini ndi nsembe yake. Ndiyeno magazi ankaikidwa pamene iye amakhoza kuima pansi pa magazi. Magazi ayenera kukhala pamwamba pa iye. Ndipo icho chinali chizindikiro kuti iye anali atadzizindikiritsa iyemwini, wochimwa, ndipo anali atatsimikizira kuti choloweza mmalo chosalakwa chinali chitatenga malo ake.

Ndi chithunzi chokongola bwanji! O, woomboledwa! Mwaona, chilungamo chinali chitakwaniritsidwa, ndipo chofunika cha chilungamo choyera cha Mulungu chinali chitakwaniritsidwa. Ndipo Mulungu anati, “Tsopano Ine ndikufuna moyo wanu,” ndiyeno pamene moyo unachimwa. Ndiye choloweza mmalo chosalakwa chinatenga malo ake. Ndipo iwo anali magazi a chinyama; osati a apulo, pichesi. Izo ziyenera mwamtheradi kupanga mbewu ya serpenti kumveka bwino kwa aliyense, kuti iwo anali magazi. Ndipo magazi awa, amene sakanakhoza kubwera kuchokera mu chipatso, anabwera kuchokera kwa choloweza mmalo chosalakwa. Ndipo moyo unali utatuluka, nawonso... nawonso, mu malo ake, ndipo magazi anali chophiphiritsa kuti chinyama chinali chitafa ndipo magazi anali atatulukamo.

Ndipo wopembedza pa kudzipaka magazi pa iyemwini, zinkasonyeza kuti iye anali atazindikiritsidwa mu chiwombolo, chifukwa iye wadzizindikiritsa iyemwini ndi^pa nsembe, wadzilumikiza iyeyekha ku nsembe, ndipo magazi ankaimira chizindikiro. Ndi_ndi zodabwitsa bwanji! Ndi chithunzi bwanji chimenecho! Ndicho choyimira changwiro cha Khristu, ndendende basi, wokhulupirira lero atayima pansi pa Magazi okhetsedwa, akuzindikiritsidwa ndi Nsembe. Mwangwiro basi monga_monga izo zingakhalire! Ndipo momwe Khristu, osati kukhala chinyama^Inu mukuona, chi... chinyama chimafa, koma izo zinali.... Chinthu chosalakwa kwambiri chimene ife tiri nacho, ine ndikuganiza, chingakhale, chi_chinyama, m_mwanawankhosa. Pamene Mulungu anafuna kuti amuzindikiritse Yesu Khristu, Iye anamuzindikiritsa Iye ngati Mwanawankhosa. Ndipo pamene Iye anafuna kuti adzizindikiritse Iyemwini, Iye anadzizindikiritsa Iyemwini ngati mbalame, Nkhunda. Ndipo nkhunda ndi mbalame yosalakwa ndi yoyera kwambiri mwa moyo wa mbalame, ndipo_mwanawankhosa ndi wosalakwa ndi wangwiro kwambiri mwa moyo wa zinyama zonse.

Kotero inu mukuona pamene... Yesu anabatizidwa ndi Yohane, ndipo Baibulo linati, “Ndipo iye anawona Mzimu wa Mulungu, monga nkhunda, ukubwera pansi pa Iye.” Chotero ngati izo zikanati zikhale... Ngati izo zikanati ikhale nkhandwe, kapena ngati icho chikanati chikhale chinyama china chirichonse, chikhalidwe cha nkhunda sibwezi chitagwirizana ndi chikhalidwe cha nkhandwe, kapenanso kuti chikhalidwe cha nkhunda sichikanagwirizana ndi cha chinyama chirichonse koma mwanawankhosa. Ndipo zikhalidwe ziwiri zimenezo zinabwera palimodzi, ndiye izo zimakhoza kugwirizana china ndi chimzake.

Tsopano kodi inu mukuwona kukonzedweratu? Iye anali mwanawankhosa pamene anafika pamenepo. Mwaona? Mukuona? A... Iye anali mwanawankhosa pamene iye... pamene iye anabweretsedwa. Iye anali mwanawankhosa. Iye anabadwa ali mwanawankhosa. Iye analeredwa, mwanawankhosa. Mwaona? Ndipo, chotero, uwo ndi mtundu wokha wa Mzimu woona umene ungakhoze kulandira Mawu, umene ungakhoze kulandira Khristu. Ina yonseyo imayesa, iwo anayesa kuti alandire Iwo, ndipo mukaika Mzimu wa Mulungu pa nkhandwe, taonani, yokwiya, yoyipidwa, yankhanza. Iwo sungakhale pamenepo. Mzimu Woyera umangothawapo. Iwo sungakhoze kuchita izo. Bwanji ngati Nkhunda iyo ikanati itsike pansi, ndipo, mmalo mwa Iyo kukhala Mwanawankhosa, apo pakanakhoza kukhala chinyama china chake? Iyo bwezi mwamsanga itathawa ndi kubwerera. Mwaona? Koma pamene Iye anapeza chikhalidwe chija chimene Iye akanakhoza kulumikizana nacho, Icho chinangokhala Chimodzi.

Ndiyeno Nkhunda inatsogolera Mwanawankhosa, ndipo, zindikirani, Iyo inatsogolera Mwanawankhosa kupita kokaphedwa. Tsopano, Mwanawankhosa anali womvera kwa Nkhunda. Mwaona? Zinalibe kanthu kumene Iyo inali kutsogolera Iyo, Iyo inali yololera kuti ipite.

Ine ndikudabwa, lero, pamene Mulungu akutitsogolera ife kumka ku... moyo wa kudzipereka kwathunthu ndi kumutumikira Iye, ine ndikudabwa ngati mizimu yathu ndiye nthawi ina siimaukira, kukhala ngati kusonyeza izo, ndikudabwa ngati ife tiri anaankhosa? Mwaona? Mwaona? Mwanawankhosa ndi womvera. Mwanawankhosa ndi wodzipereka yekha. Iye samati... iye samatenga, samadzinenera zayekha. Mukhoza kumugoneka iye pansi kumene ndi kumeta ubweya kuuchotsa pa iye. Ndicho chinthu chokha chimene iye ali nacho. Iye sama_samanena chirichonse cha izo; amangopereka nsembe chirichonse chimene iye ali nacho. Ndiye mwanawankhosa. Iye amapereka chirichonse kwa ake... amapereka chirichonse kwa ena, mwiniwake ndi zonse zomwe iye ali. Ndipo umo ndi momwe Mkhristu weniweni aliri, ngati iwo ali... odzipereka okha eniake, osasamala kanthu ka dziko lino, koma kupereka zonse zomwe iwo ali nazo kwa Mulungu. Mwaona?

Ndipo tsopano mmodzi uyu anali Mwanawankhosa wangwiro, Khristu anali. Ndiyeno kupyolera mu kukhetsa kwa mwanawankhosa uyu, mwanawankhosa wachibadwa mu Igupto, magazi ankaikidwa, ndipo, pamene iwo anatero, iwo ankaimira chizindikiro, ndiye nanga Magazi a Mwanawankhosa uyu akanati adzaimire chiyani? Mwaona? Chizindikiro chakuti ife tiri akufa kwa ifeeni ndi ozindikiridwa nayo nsembe yathu. Mwaona? Ndiye, Mwanawankhosa ndi... Magazi ndi munthu zimakhala zozindikiridwa palimodzi, Nsembe ndi wokhulupirira. Mukuona, inu mukuzindikiridwa mu moyo wanu, ndi Nsembe yanu. Yomwe imakupangani inu chimene inu muli.

Ndiye magazi anali chizindikiro, kapena chizindikiritso. Magazi ankazindikiritsa kuti wopembedza anali atapha mwanawankhosa, ndipo wavomereza mwanawankhosa, ndipo wapaka chizindikiro pa iyemwini, kuti iye sanali wamanyazi. Iye sanali kusamala yemwe waona icho. Iye ankafuna kuti aliyense awone icho, ndipo iwo anali kupakidwa pa malo otero kuti wina aliyense akamadutsa apo amakhoza kuwona chizindikiro chimenecho.

Mukuona, anthu ambiri amafuna kuti akhale Akhristu, ndipo iwo amakonda kumachita izo mwamseri kuti munthu wina anga... angadziwe kuti iwo anali Akhristu. Kapena, oyanjana nawo omwe iwo amathamanga limodzi nawo, ena a iwo nkumaganiza, “Chabwino, tsopano, tapenyani, ine ndikufuna kuti ndikhale Mkhristu, koma ine sindikufuna kuti Wakuti-ndi-wakuti adziwe za izo.” Mwaona? Chabwino, tsopano, inu mukuona, icho si Chikhristu. Chikhristu chiyenera kumawonetsera Chizindikiro chake, mukuona, poyera, mu moyo wapoyera, ku ntchito, pa msewu, pamene vuto liri pozungulira, chirichonse, mu mpingo, pena paliponse. Magazi ndiwo Chizindikiro, ndipo Chizindikiro chiyenera kuikidwa, mukuona, kapena (palibepo) ngakhale pangano siliri kuchita kanthu.

Magazi anali chizindikiro, kapena chizindikiritso, kuzindikiritsa kuti munthu uyu wawomboledwa kale. Tsopano, chabwino, zindikirani, iwo anali, iwo anali atawomboledwa pasanakhale chirichonse chitayamba kuchitika konse. Mwa chikhulupiriro iwo anapaka magazi. Mukuona, izo zisanachitike kwenikweni, magazi anali atapakidwa mwa chikhulupiriro, akukhulupirira kuti izo zikanati zichitike. Mwaona? Mkwiyo wa Mulungu usanati udutse mdzikolo, magazi ankayenera kuti apakidwe, choyamba. Izo zinali mochedwa kwambiri mkwiyo utagwa kale. Tsopano ife tiri ndi phunziro apo lomwe ife tingakhoze kwenikweni, mwinamwake kulibweretsa ilo ku ganizo lanu, mphindi yokha. Penyani, izo zisanati zichitike, pakuti ikudza nthawi yomwe inu simudzatha kupaka Magazi aliwonse.

Mwanawankhosa ankaphedwa nthawi ya madzulo, atatha kusungidwa kwa masiku khumi ndi anai. Ndiyeno mwanawankhosa ankaphedwa ndipo magazi ankapakidwa mu nthawi ya madzulo. Inu mukumvetsa izi? Chizindikiro sichinali kudza pokhalapo mpaka nthawi ya madzulo.

Ndipo ino ndi nthawi yamadzulo ya m'badwo umene ife tiri kukhalamo. Ino ndi nthawi ya madzulo kwa_kwa Mpingo. Ino ndi nthawi yamadzulo kwa ine. Ino ndi nthawi yamadzulo ya Uthenga wanga. Ine ndikufa. Ine ndikupita. Ine ndikuchokapo, mu nthawi ya madzulo ya Uthenga. Ndipo ife tabwera kupyola mu kulungamitsidwa, ndi zina zotero, koma ino ndi nthawi yomwe Chizindikiro chiyenera kuti chipakidwe. Ine ndinakuuzani inu Lamlungu latha kuti ine ndinali nacho chinachake chimene ine ndimafuna kuti ndiyankhule kwa inu za icho; chimenecho ndi ichi. Nthawi yomwe pamene inu_inu simungati muzingosewera nacho Icho. Icho chiyenera kuti chichitidwe. Ngati icho chiti chichitidwe konse, icho chiyenera kuti chichitidwe tsopano. Chifukwa, ife tikhoza kuwona kuti mkwiyo uli pafupi wokonzeka kuti udutse mdzikomu, ndipo chirichonse chimene chachoka pansi pa Chizindikiro chimenecho chiwononongeka. Magazi, ali ndi chokuzindikiritsani inu.

Werengani akaunti yonse mu... Chizindikiro.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.

1 Yohane 2:2



Kuyenda kwa Chikristu mndandanda.
Akupitiriza pa tsamba lotsatira.
(Ubatizo wamadzi.)


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Chapter 9
- The Third Pull

(PDF Chingerezi)

Kale...

Pambuyo...

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.