Uthenga wakulowa.
<< m'mbuyomu
lotsatira >>
Phiri la Sunset.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Ndi chiyani chokopa pa phiri?Si kale litali, nditaima pa guwa ili, izo zinanenedwa ndi Mzimu Woyera, “Tsiku lidzadza kuti pamene iwo atadzakhomerere pansi chikhomo patsogolo pa nyumba yako; iwo adzasuntha chipata chako. Chotero, kuti, iwe udzazilambalale izo, osakhala uli wokwiya.” Ine ndinawona chipata changa chikuphwasulidwa ndipo chitakaikidwa pambali pa phiri. Ine ndinawona phili patsogolo kwa ine, lonse litakumbidwapo, ma bolodi ndi zinthu ziri apo pamene chinachake chinali chitadziphwanya icho. Iye anati... Ine ndinayang'ana, ndipo apo panali Ricky wam'ng'ono yemwe anali atakwera pamenepo ndipo anachichotsapo chipata chimenecho, anachita izi. Ine ndinati, “bwanji iwe sunandiuze ine?” Iye anayamba kundichenjerera, ndipo ine ndinayenera kum'menya iye. Ndipo pamene izo zinatero, ine ndinati, “Ine sindinachite izi chichokereni mu bwalo la nkhonya, koma ine ndikungofuna kuti iwe udziwe,” ndipo pamene ine ndinamusasantha nayo imodzi. Ndipo pamene ine ndinamugwetsera iye pansi, ine ndinamudzutsa iye kachiwiri ndikumugwetsera iye pansi kachiwiri. Ine ndinamudzutsa iye, nthawi zitatu kapena zinai, ndiyeno ndinamukankhira iye pa mwamba pa phiri. Chotero ndiye ine ndinapita chakumeneko, ndipo ine ndinati, “izo sizabwino.” Ndipo ine ndinadzutsa iye ndipo ndinagwedeza manja ake, ine ndinati, “ine sindinakukwiire iwe, koma iwe ndimangofuna kuti iwe udziwe iwe sungamayankhule choncho kwa ine.” Ndiyeno pamene ine ndinatembenuka ndikubwereranso, Mzimu Woyera unali utaima pamenepo pachipata unati, “tsopano udzazilambalale izi. Pamene chikhomo icho chidzakhomeredwa pansi, udzatembenukire cha kumadzulo.”
Buku iri ndi chirichonse chimene ine ndikuchisowa,
Buku rli ndi chakudya chabwino.
(Njira imene imasonyeza momwe ndingapite Molambalala vuto langa).
Ameni! Ndipo Buku limenelo ndi Mawu ndipo Mawu amenewo ndi Mulungu, lambalala mavuto ako, ilo lidzakuwuza iwe choti uchite.Zaka zitatu zapitazo ine ndinamumva nzanga wa ine, wopima malo mu mzinda, amakhala kumusi kwa nsewu kuchokera kwa ine, akukhomerera chikhomo pansi. Ine ndinapita kumeneko ndinati, “Chavuta ndi chiyani, Mud?” mwana wa bambo King, nzanga wodziwana naye.
Anati, “Billy, iwo akuti akuze nsewu uno.”
Inu nonse mukumbukira. Ine ndinati, “iwo mwina udzakhala mulantho.” Ine ndinamuuza m'bale Woods, ine ndinati, “gwiritsa malo ako. Mwinamwake mulatho umenewu ubwera kudzadutsa pano, china chake.”
Njirayo inali itaphwasulidwa; njerwa, miyala, zitaponyedwa paliponse chirichonse. Chotero iye anati.... Ine ndinati, “gwilitsa malo ako.”
Ndiye pamene bambo King anandiuza ine kuti izo zimati zichitike. Ine ndinakalowa umo, ndinakanena kwa mkazi wanga atakhala pamenepo, “Wokondedwa, pali china chake chinalembedwa chokhudza. Ndi- PAKUTI ATERO AMBUYE, kwina kwake.”Ine ndinakalowa ndipo ndinakatenga buku langa, ndinayang'na nkatimo, ndipo ilo linati, “Izo zidzafika pochitika...” Zaka zisanu ndi zitatu mtsogolo!
Ndiye pamene ine ndinayang'ana pa izo, ine ndinati, “Ndinthawi tsopano wokondedwa, ife tiyenera kutembenukira kumadzulo.”
Masiku awiri zitachitika izo, nditayima muchipinda pafupi teni koloko m'mawa wina, ine ndinapita mu Mzimu wa Mulungu. Ine ndinawona kuwundana kwakung'ono, kuja kwa nkhunda zikuwuluka, ndiyang'ana pambalame zazing'ono izo. Inu mukukumbukira izo. Ine ndinawona Angelo asanu ndi awiri mumawonekedwe a pilamidi, akubwera kuthamangira kwa ine. Anati, “Tembenukira chakudzulo, pita ku Tucson ukakhale mailosi makumi anai cha ku mpoto. Ndipo iwe udzakhala ukuchotsa chisoso,” kapena namutu wa ng'ombe, iwo amazitcha izo uko, “kuchokera pa zovala zako.”M'bale Fred Sothmann wakhala kumbuyo uko akuyang'ana pa ine pakali pano, anali kumeneko m'mawa umenewo. Ine ndinali nditaiwala za izo.
Ine ndinati, “Kuphulika kunachita monga chivomezi, kumene kunagwedeza pafupi chirichonse chimene chinalipo mu dzikolo. Ine sindikuona momwe munthu akanati apulumukire ku icho.” Ine ndinachita mantha. Ine ndinayima ku Phoenix, inu nonse amene mukumvetsera usiku uno mundichitire ine umboni. Ine ndinalalikira pa ulaliki, Mabwana, Ndi Nthawi Yanji Ino? “Kodi ife tiripati?” Ine ndinapita kumadzulo. Ambiri a inu pano muli nayo tepi imeneyo, ambiri a inu pano munazimva izo zikunenedwa, chaka kapena mochuluka izo zisanachitike.Ine ndinapita kumadzulo ndikudabwa chimene chikanati chichitike. Tsiku lina ndinalandira kuitana kuchokera kwa Ambuye. Ine ndinamuuza mkazi wanga, ine ndinati, “Wokondedwa, ine ndiri.... Mwina ntchito yanga yatha.” Ine sindinali kudziwa. Ine ndinati, “Ine Mulungu mwina wathana ndi ine tsopano ndipo ine ndikhala ndikupita kwathu. Iwe upite ukamutenge Billy, uwatenge ana. Mulungu akupangira njira iwe, mwina mwake. Pitirira ndikukhala moona kwa Mulungu. Ona kuti ana atsirize sukulu, uwalere iwo mwa malangizo a Mulungu.”
Iye anati, “Bill, iwe sukudziwa kuti izo ndi zoona.”
Ine ndinati, “Ayi. Koma munthu sakanakhoza kupulumuka pa izo.”
M'mawa umodzi Ambuye anadidzutsa ine, anati, “Pita uko Mu Sabino Canyon.” Ine ndinatenga chidutswa chapepala ndi Baibulo langa.
Mkazi wanga anati, “Kodi iwe ukupita kuti?”
Ine ndinati, “sindikudziwa. Ndikuwuza iwe ndikabwerako.”Ine ndinapita pa mwamba mu Canyon, ndinakwera pamwamba pamene mphungu zinali kuwuluka mozungulira. Ine ndinali kuyang'ana agwape ena atayima pamenepo. Ine ndinagwada pansi kuti ndipemphere, ndipo ndinakweza m'mwamba manja anga, ndipo Lupanga linakhudza dzanja langa. Ine ndinayang'ana pozungulira. Ine ndinaganiza, “Nchiani chimenecho? Ine sindinasokonezeke. Apa pali Lupanga ilo m'dzanja langa; lowala, kung'anima, ndikunyezimira mudzuwa.” Ine ndinati, “Tsopano, kulibe anthu mamailosi kuchokera kwa ine, kutali kuno mu Canyon iyi. Ilo lingachokere kuti?”
Ine ndinamva Liwu, linati, “Ilo ndi Lupanga la a Mfumu.”
Ine ndinati, “Mfumu amamupatsa munthu udindo ndi Lupanga.”
Iye...Liwulo, linabwerera, linati, “Osati lupanga la mfumu, koma, ‘Lupanga la a Mfumu,’ Mawu a Ambuye.” Anati, “Usawope ayi. Ndichikoka chachitatu basi. Ndiko kutsimikizira kwa utumiki wako.”Ine ndinali kupita kokasaka ndi mzanga, osadziwa chimene chikanati chichitike. Ndipo wina wake anandiitana ine, yemwe ankanditsutsa ine zachithunzi chija cha Mngelo wa Ambuye, yemwe anachijambula icho. Ine ndinapita ku Houston pazokhudza mwana wake, pakuti iye anali kupita mumzere wa imfa ndipo anali woti akaphedwa mumasiku pang'ono, ndipo iye anakomana nane ine m'menemo ndipo anatambasula mikono yake kundikumbatira ine, anati, “Taganizani, munthu yemweyo ine ndimamutsutsa akubwera kuti adzamupulumutse mwana wanga yekhayo!” Bungwe la za umunthu linandipatsa ine chimene iwo amachitcha Oskara, kapena chirichonse chimene inu mukufuna kuti muchitche icho, chifukwa chopulumutsa moyo.
Ndiye ife tinabwerera, ine ndinapita pamwamba pa phiri kuti ndikasakeake. Uko, m'bale Fred ndi ine, m'mawa wina pamene ndinatuluka, ndipo ine - ine ndinali nditapeza kale nguluwe yanga, ndipo ine ndinayang'ana ndipo ndinawona kumalo kumene izo zimapita. Ine ndinati, “M'bale Fred, pita ku phiri ilo molawila tsopano pafupi kutulukira kwa tsiku, ndipo ine ndipita palinalo. Ine sinditi ndiwombere panguluweyo, sindiipha iyo. Koma ngati izo ziyamba kubwerera kumbali iyi, gulu ilo, ine ndikawombera kutsogolo kwa izo ndikuzithamangitsa izo kuti zibwerere.”
M'bale Fred anapita uko ndipo kunalibe nguluwe. Iye anagwedeza kwa ine ndipo ine ndinawona. Ine ndinapita M'musi mu Canyon, mapompho ena aakulu, dzuwa linali likutuluka kumene. Ine ndinabwera kuzungulira mbali yina ya phiri, osalingalira kanthu zokhudza mauneneri. Ndinakhala pansi, kuyembekezera, kupumula; ine ndinaganiza, “Nchiyani chinachitika kwa nguluwe zija?”
Ine ndinanyamula yanga.... Ndinakhala pansi monga amachitira amwenye, inu mukudziwa, kupingatsitsa - miyendo. Ine ndinayang'ana pa mwendo wanga wa ovolosi, ndipo apo panali chisoso. Ine ndinachichotsa icho. Ndipo ine ndinati, “Izo ndizachilendo! Ine ndili kuno, pafupi mailosi makumi anai kumpoto cha ku m'mawa kwa Tucson. Apo pali mnyamata wanga wang'ono Joseph wakhala uko akundiyembekeza ine.” Ndipo pamene ine ndinayamba kuti ndidziyang'ana ine ndinawona gulu la nguluwe zikubwera uko pafupi mayadi chikwi zikubwera kwa ine, pamwamba pa phiri, ine ndinaponyera chisosocho pansi. Ine ndinati, “Ine ndikazipeza izo. Ine ndipita ndikamutenge M'bale Fred, ndipo ine ndipachika chidutswa cha pepala kuti ndimudziwitse njira yoti adzere ku Ocotillo muno, ndipo ife tikamupeza M'bale Fred.”
Ndipo ine ndinauyamba kukwera phiri ndikuthamanga dzolimba monga ine ndikanathera kumbali inayo. Zonse mwadzidzi, ine ndinaganiza kuti wina wake anandiwombera ine. Ine sindinayambe ndamvapo kuphulika koteroko; iko kunagwedeza dziko lonse. Ndipo, pamene iko kunatero, ataima patsogolo pa ine anali Angelo asanu ndi awiri mukuwundana.Ine ndinapezana naye M'bale Fred ndi iwo kanthawi kotsatira. Anati, “Chinali chiyani chija?”
Ine ndinati, “chinali chimenecho.”
“Muchita chiyani inu?” “Kubwerera kunyumba. PAKUTI, NDI ATERO AMBUYE, Zinsinsi zisanu ndi ziwiri zimene zakhala zitabisika mu Baibulo zaka zonse izi, zipembedzo izi ndichilichonse, Mulungu akuti akatsegule zinsinsi zisanu ndi ziwiri zimenezo kwa ife muzisindikizo zisanu ndi ziwiri.”
Apo panali nkombero uja ukukwera kuchokera pa dziko, ngati kupangika kwa nthunzi. Pamene iwo unatero, iwo unakwera pa mwamba mu phiri, unayamba kupanga nkombero ukunka chakumadzulo, kuchokera komwe iwo unachokera. Sayansi inaupeza iwo patapita kanthawi, mailosi makumi atatu m'mwamba ndi mailosi makumi awiri ndi asanu chopingasa, ndendende basi mwa nkombero wa piramidi.Ndipo tsiku lina, nditaima pamenepo, ndinatembenuzira chinthunzicho kunja, ndipo apo pali Yesu monga Iye anali m'mibadwo Isanu ndi Iwiri ya Mpingo, atavala wigi yoyera, akusonyeza Umulungu Wapamwamba. Iye ndi Alefa ndi Omega; Iye ndi Oyamba ndi Otsiriza; Iye ndi Oweruza Wapamwamba wa Umuyaya wonse, akuima pamenepo, kukatsimikizira Uthenga wa ora lino. Ndipo kudzakhala kuli kuwala cha mu nthawi ya madzulo! Kodi zonsezo ndi zachiani? Chinali chiani icho?
Ine ndinapita chakumadzulo. Pa phiri lomwelo, ndikudutsa apo ndi Banks Woods kumeneko, anati, “Ponyera mwala m'mwamba. Nena kwa bambo Woods, ‘PAKUTI ATERO AMBUYE, iwe uwona Ulemelero wa Mulungu’.”
Tsiku lotsatira lomwe, nditaima pamenepo, kamvuluvulu anabwera pansi ndipo anawaphulitsa mapiri. Miyala inadula nsonga za mitengo. Pafupi mapazi atatu kapena anayi pamwamba pa mutu wanga. Kunapanga kuphulika kutatu kwa kukulu, ndipo abale anabwera kuno akuthamanga. Analipo pafupi amuna khumi ndi asanu ataima pamenepo, alaliki ndi china chilichonse. “Kodi chinali chiyani icho?” iye anati, “Kodi chinali chiani icho?”
Ine ndinati, “Chiweruzo chikukantha Gombe la kumadzulo.”Pafupi masiku awiri zitachitika izo, chivomezi chinali pafupi kuti chimize Alaska. Kuwala uku ndichiyani pa mwamba pa phiri la Sunset mu Nkhalango ya Coronado yaku Arizona? Ndichiyani chinthu ichi chachilendo chimene chinachitika kumtunda kemeneko, chimene anthu akhala akuyenda kuchokera kumadzulo kupita ku kum'mawa, kutola miyala imene inali kozungulira nkonseko kumene Icho chinakantha? Ndipo umodzi uliwonse wa iwo, mwala umodzi uliwonse, uli ndi ngodya zitatu pa iwo, umene Icho chinaswa. (Utatuwo ndi Mmodzi.) Iyo ili pa madesiki, pa zopsyinjira mapepala, ku fuko lonseli. Nchiyani chinthu chachilendo ichi pa phiri la Sunset mu Nkhalango ya Coronado?
Junior Jackson akumvetsera kuno, inu mukukumbukira loto limene iye anali nalo limene ine ndinatanthauzira, “Ndikupita cha kolowera kwa dzuwa?” Ndipo izi zinachitika pa phiri la “Sunset.” Ndi nthawi ya madzulo, nthawi ya kulowa kwa dzuwa. Uthenga wakulowa kwa dzuwa kupyolera mu kutha kwa mbiri ya kale, kutha kwa uneneri, kani, kukhala zikukwaniritsidwa. Ndipo kudzakhala kuli kuwala pa nthawi ya madzulo, pa Phiri la Sunset mu Nkhalango ya Coronado, mailosi makumi anai ku mpoto kwa Tucson. Kafikeni pa mapu ndipo mukaone ngati Nsonga ya Sunset apo. Ndi ndendende kumene izi zinachitikira. Ine sindinali kuzidziwa konse izo mpaka tsiku lina.
Chirichonse, chimene... Icho sichidzafa konse. Icho chingodzifunyulula chokha mopitiriza. Kuchokera ku chinthu chomwecho chikuchitika, mpaka kuchithunzi cha kukhala Yesu atayima akuyang'ana pa ife; ndipo tsopano ndendende pa phiri la Sunset, ndi kuwala kwa kulowa kwa dzuwa. Kuwala kwamadzulo kwafika, Mulungu akutsimikizira Yekha. Nchiyani ichi? Ndi zoona kuti Mulungu ndi Khristu ali mmodzi. Yoyera... Ndi angati analiwona ilo, wigi yoyera pa Iye, monga ife tinayankhula mu Chivumburutso 1? Mwaona, Umulungu wapamwamba, ulamuliro wapamwamba; palibe liwu lina, palibe Mulungu wina, palibe chinthu china! “Mwa Iye muli chidzalo cha uMulungu m'nthupi.” Angelo iwo omwe anali wigi Yake. Ameni.
Nchiyani chinachitika pa phiri la Sunset? Mulungu kutsimikizira Mawu Ake. Ichi ndicho chomwe phokoso lonseli liri. Zindikirani, ndi Mulungu akukwaniritsa Mawu Ake olonjezedwa kachiwiri, aChivumburutso 10:1 mpaka 7, “Ndipo mumasiku akuomba kwa Uthenga wa Ngelo wachisanu ndi chiwiri, chinsinsi cha Mulungu chiyenera kuti chitsirizidwe.” Chinsinsi chobisika cha Chivumburutso 10:1 mpaka 7, Uthenga wotsiriza kwa m'badwo wotsiriza. Zikukwaniritsa ndendende, mu m'badwo uno, Luka woyera 17:30, “Tsiku limene mwana wa mnthu ati adzaululidwe.”
“Ndipo kudzauka aneneri onyenga ndi aKhristu onyenga kusonyeza zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa mochuluka kuti zikanati ziwanyenge osankhidwa ngati nkotheka.” Anthu adakali mukukaika. Ndipo, mwachizolowezi, mpingo naonso ndiwodabwitsika basi.Ndipo sayansi, konse ku Tucson yense panobe iwo akulemba zidutswa ndikuziika mupepala. Kumbuyo komwe uko pa phiri la Lemmon, makamera akulu awo sanachiwone icho akukwera m'mwamba kuchokera pamene ife tinali titaima. Kutsetserekera cha kumadzulo, kusonyeza kuti nthawi yatha. Izo sizingakhoze kupita koma chidutswa chaching'ono m'menemo; ziri ku Gombe la kumadzulo. Chiweruzo chinangokantha mwanjira imene icho chinapitira. Kupita kumene m'mwamba pa Phoenix ndi modutsa kumene, mpaka ku Prescott ndi kudutsa mapiri mpaka kuchigwa chakumadzulo, kupitirirabe mpaka.... Kodi iwo anali akupita kuti? Kukwera pamene mpaka mu Alaska, ndipo Iye akubingula, kulunjika njira imeneyo.
Ndipo zoyang'ana m'mwamba ndiwonse aiwo mu Tucson akadafunsabe, ofufuza za Sayansi akuyesa kuti apeze icho chiri. Pamwamba kwambiri mwakuti sikungakhoze kukhala chifunga, nthunzi, kapena kanthu kena m'mwamba umo. “Nchiani chinachita izo? Kodi zirikuti izo?” Iwo angokhala odabwitsidwa ndikuwala kwa uzimu uko kutapachikika patali mumulengalenga monga iwo anali pamene Amagi ankabwera akutsatira nyenyezi, akuti, “Alikuti Iye yemwe wabadwa ali mfumu ya Ayuda?” Chinali chiyani icho? Mulungu kukwaniritsa Mawu Ake, “Ndipo kudzatuluka nyenyezi kuchokera kwa Yakobo.”
Ndipo Mulungu wakumwamba analonjeza kuti nthawi yamadzulo ikanati idzakhale ndi kuwala kwa madzulo. Zaka zitatu zapitazo chinsinsi ichi chinali uneneri, “Ndi nthawi yanji ino, bwana?” koma tsopano ndi mbiri yakale. Izo zadutsa.Lonjezo lakwaniritsidwa. Ndi nthawi yanji ino, bwana, ndipo nchiyani chokopa ichi? Mulungu akukwaniritsa Mawu Ake! Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse.
Werengani akaunti yonse mu...
Ndi chiyani chokopa pa phiri?