Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani?
<< m’mbuyomu
lotsatira >>
Mulungu ali mu Mpingo Wake.
William Branham.Werengani akaunti yonse mu...
Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani?.Yohane 14:26,
Koma Mtonthozi, yemwe ali Mzimu Woyera, yemwe Atate ati adzamutumize mu dzina langa, iye adzakuphunzitsani inu zinthu zonse, ndi kubweretsa zinthu zonse izi ku kukumbukira kwanu, chirichonse chimene ine ndanena kwa inu.Usiku watha ife tinali kuyankhula, “chimene Iwo unali.” Mzimu Woyera Unali Chiyani? Ndipo ife tinawupeza Iwo kukhala uli basi pafupifupi chirichonse, chimene Mulungu analonjeza kwa ife. U-nhu. Mwa Iwo ife tinapeza basi chimene Mpingo wa Mulungu ukanati usowe. Ife tinawupeza Iwo kuti uli chisindikizo, Mtonthozi, mpumulo, ndi chisangalalo, ndi mtendere, ndi chiwukitsiro. Ndipo zonse zimene Mulungu analonjeza kwa Mpingo Wake, zagona mkati mwa Mzimu Woyera.
-----
Tsopano, ndipo mawa... Usikuuno ife tikuphunzitsa pa: Kodi Chanji Cholinga Chotani Kuti Mulungu Atumize Mzimu Woyera? Kodi Iwo ndi wa chiyani? Ngati Iwo uli chinthu chachikulu chotero, ndiye nchifukwa chiyani Mulungu anawutumiza Iwo? Ndiye, mawa usiku ife tikufuna kuti tidzayankhule pa: Kodi Iwo ndi wa Inu? ndi Kodi Iwe Umawulandira Chotani Iwo? ndi Kodi Iwe Umadziwa Bwanji Pamene Iwe Uli Nawo Iwo?-----
Tsopano, cholinga, chinali chiyani... cholinga cha Mulungu chinali chiyani pa kutumiza Mzimu Woyera? Tsopano, ine ndikanati ndizilembe zimenezo apo, Yohane 14, kuyambira pa ndime ya 14, ndi kuwerenga kudutsa mu mutuwo, mwa maziko. Cholinga cha Mulungu, ife tikupeza apa, mu kutumiza Mzimu Woyera, chinali cholinga chimodzi, kuti Mulungu iyemwini akhoze kumakhala mu Mpingo Wake ndi kupitiriza madongosolo Ake kupyolera mu Mpingo. Kuti, Mulungu anali mwa Khristu, akupitiriza madongosolo Ake kupyolera mwa Khristu; kuchokera kwa Khristu, kupita mu Mpingo, kupitiriza ntchito Yake kupyolera mu Mpingo.Tsopano, ife tikudziwa chimene Mzimu Woyera uli. Ife tinapeza, usiku watha, kuti Ndiwo Mulungu. Tsopano, pamene ife tiganiza za Mulungu, Atate, monga Yesu anamukamba pano, Atate Ake; Mulungu, Mwana, monga Yesu; Mulungu, Mzimu Woyera, monga chomwe ife tikuwutcha Iwo lero. Tsopano, izo sizikutanthauza kuti pali atatu apawokha, Amulungu osiyana. Izo zikutanthauza kuti pali Mulungu mmodzi mu maudindo atatu. Mulole ife tinene izo monga chonchi. Zonse zimene Mulungu anali, Iye anazitsanulira mwa Khristu, chifukwa Iye anadzikhuthula Iyeyekha ndipo anazitsanulira Izo mwa Khristu. “Ndipo Khristu anali chidzalo cha Umulungu mu thupi.” Zonse zimene Yehova anali, Iye anazitsanulira izo mwa Khristu. Ndipo zonse zomwe Khristu anali, Iye anazitsanulira mu Mpingo; osati mwa munthu mmodzi, koma mu Thupi lonselo. Pamenepo, pomwe ife tibwera limodzi mu umodzi, ife tiri ndi Mphamvu. Zonse zimene Mulungu anali, zinali mwa Khristu; ndi zonse zimene Khristu anali, ziri mwa inu. “Pakuti Mulungu anapangidwa kukhala thupi, ndipo anakhala pakati pathu.” Timoteo Woyamba 3:16, ngati inu mukuzilemba izo, “Popanda kutsutsana chinsinsi cha umulungu ndi chachikulu: pakuti Mulungu anawonekera mu thupi, ndipo ife tinamugwira Iye. Mulungu, Yehova, anapangidwa kukhala thupi, ndipo ankayenda pa dziko lapansi, ndipo ife tinamuwona Iye ndi maso athu.”
Inu mukudziwa, mu mutu womwewo, wa Yohane 14, Filipo anati, “Ambuye, tiwonetseni ife Atate, ndipo icho chitikwanira ife.” Yesu anati, “Ine ndakhala ndiri ndi iwe motalika chotere, Filipo, ndipo iwe sukundidziwa Ine? Pamene iwe wandiwona Ine, iwe wawaona Atate. Ndipo iwe unena bwanji kwa Ine, 'Tiwonetsereni ife Atate'?” Mulungu anapangidwa kukhala thupi.
Tsopano ndi izi apa. Atate anali Mulungu pamwamba pa inu, ife timati. Ife takhala tiri kuyambira pa Adamu. Mulungu, Atate, anali pamwamba pa Mose ndi ana a Israeli, mu Lawi la Moto. Kenako, Mulungu nafe, mwa Khristu; anayenda ndi ife, anayankhula ndi ife, anadya ndi ife, anagona ndi ife. Mulungu pamwamba pa ife; Mulungu nafe; ndipo tsopano Mulungu mwa ife. Zonse zimene Mulungu anali, zinabwera mwa Khristu; zonse zimene Khristu anali, zinabwera mu Mpingo. Ndi chiyani icho? Mulungu akugwira ntchito mwa inu. Kulikonse mu dziko kumene Iye angafune kuyitana pa inu, inu muli komweko, kugwira ntchito mwa inu kuti achite chifuniro Chake chabwino. Momwe ife tiyenera kumuthokozera Mulungu chifukwa cha zimenezo! Mulungu, Mzimu Woyera, watumizidwira pa cholinga chakuti Mulungu azikhala mu Mpingo Wake, akuyenda kupyolera mu m'badwo uliwonse, akuchita chifuniro Chake Chaumulungu.
-----
Ndipo ndimo momwe Mulungu anachitira, anatsatira malamulo Ake Omwe. Mulungu sangakhoze kutsatira, kukupatsani inu lamulo limodzi kuti mulitsatire ndipo Iye nkumatsatira lina. Iye amatsatira malamulo Ake Omwe. Ndiye, Mulungu, pofuna kuti awombole mpingo wotayika, dziko lotayika, chirengedwe chotayika; Mulungu, Yemwe ali wopanda malire mu Mzimu, kuti awombole mtundu wa anthu wotayika, Mulungu Mwiniwake anadzakhala wachibale, Munthu, Mwana yemwe Iye anamulenga mu chibelekero cha Maria. Ndiyeno Iye anapanga chisonyezo, kapena umboni; kunja kwa zipata za Yerusalemu, Iye anatukulidwira mmwamba pakati pa mmwamba ndi dziko lapansi, ndipo anafa, ndipo anawombola chirichonse. Ndipo mu kuwukha magazi, Iye anawuyeretsa Mpingo kuti Iye Mwiniwake akakhoze kumakhala mmenemo, ndi kuyanjana ndi kuyankhulana nawo, malo otayika a chiyanjano aja kuchokera ku munda wa Edeni kumene Mulungu ankabwera pansi usiku uliwonse, nthawi ya mpingo. Kodi inu munazindikira, Mulungu amabwera pansi mu kachisisira ka tsiku, mkulowa kwa dzuwa. Pali chinachake chokhudza pamene kuyamba kuti kukhale usiku, anthu amaganiza za mpingo ndi za Mulungu; Akhristu. Inu mumawona dzuwa likulowa, inu mumazindikira kuti dzuwa lanu likulowa.Ndipo mu chisisira cha usiku Iye amakhoza kubwera pansi ndi kuyankhulana nawo iwo. Ndipo pamenepo Iye anataya chiyanjano chimenecho, chifukwa tchimo silikadamulola Iye kuchita izo. Ndiyeno Iye anapangidwa thupi ndipo anakhala pakati pathu, polinga kuti Iye akanakhoza kubwereranso kachiwiri kwa munthu, ndi kumakhala mwa munthu, ndi kumubwezeretsa munthu ku chikhalidwe cha chiyanjano ndi Iye kachiwiri, ndi kumupatsanso iye ufulu wopatsidwa ndi Mulungu. Ndicho chimene Iye anachita.
Ndicho cholinga cha Mzimu Woyera. Ndiwo Atate, kachiwiri, Mulungu Atate kukhala mwa inu, kuchita zolinga Zake, kuti atsirize dongosolo Lake la chiwombolo; kugwira ntchito kupyolera mwa inu, kukupangani inu wogwira ntchito ndi Iye; kukupatsani inu malo, kukupatsani inu gawo chifukwa cha m'bale wanu wakugwa, ndi mlongo wotayika; kukupatsani inu Mzimu Wake ndi chikondi Chake, kuti mupite mukasake wotayika, monga Iye anachitira mu munda wa Edeni. “Adamu, Adamu, uli kuti iwe?” Ndicho chimene Mzimu Woyera umachita kwa mwamuna kapena mkazi. Pamene Iwo ukhudza mu mtima mwawo ndi kutenga pokhala Pake, pali ludzu ndi njala yofuna miyoyo yotayika. Ndilo lomwe liri vuto ndi misonkhano lero. Mulibe kukhudza kokwanira kwa Mzimu mmenemo, kukafunafuna miyoyo ya otayika ndi omwe akufa. Zachuluka ndi za kupanga dzina, kapena mpingo, kapena nyumba, kapena chipembedzo, mmalo mwa dongosolo lopindula-miyoyo. Ndi zachisoni bwanji! Ife tikanakhoza kungokhala pa izo mochuluka.
-----
Tsopano mu m'badwo uno umene ife tiri kukhalamo tsopano, m'badwo uno, iwo wapyola pa Pentekoste. Pentekoste yadzikhazikitsa yokha polowa mu mabungwe, ndipo yayamba kutengera zochuluka kwambiri za mabungwe, “Ife ndife ichi ndipo ndife icho.” Ndicho chibadwa basi. Inu basi simungachitire mwina. Ndi chibadwa. Iwo azichita zimenezo. Ndi dongosolo, la iwo kuti azichita zimenezo. Koma Mpingo wasunthira patsogolo. Iwo wapita mokulira, mwamphamvu zochuluka. Ndiko kubwezeretsa kwa mphatso. Ndipo anthu ambiri a Chipentekoste sakhulupirira mu machiritso Auzimu, utumiki wa Angelo, ndi mphamvu za Mulungu. Achipentekoste ambiri amawatcha masomphenya awa omwe ine ndimawaona, “mdierekezi.” Mabungwe ambiri sangathe ngakhale kukhala ndi kanthu kochita ndi Iwo, mu Pentekoste. Mwaona, ife tasuntha kudutsa zimenezo. Kungokhala monga Amethodisti anatcha Chipentekoste, “kupenga,” chifukwa choyankhula mu malirime. Kungokhala monga Alutera anatcha Amethodisti, “openga,” chifukwa chofuula. Mwaona? Koma izo zonse ndizo kubwera kwa Mzimu Woyera, mpaka Mpingo waukulu ukhale utadzazitsidwa, ndi kukhomereredwa modzaza, aleluya, ndi zimphamvu zazikulu za Mulungu Wamphamvuzonse. Mpaka, iwo ukhale utafika pa malo amene mpaka ntchito zomwe zimene Yesu anazichita ziziwonetseredwa zokha mu Mpingo momwe tsopano. Ife tiri pafupi, amzanga.Ndiroleni ine ndiyime apa, kwa miniti chabe, kuti titenge chifukwa chimene Mulungu anawuyikira Mzimu Woyera mu Mpingo, kukupatsani inu choyimira china kotero kuti inu mudziwe. Kubwerera mu Chipangano Chakale, pamene... mwana... Mwamuna ankadzipangira iyeyekha nyumba. Iye akapeza mkwatibwi wake, ndicho chinthu choyamba. Ndiye iye amakhala munthu wamkulu, monga bungwe. Izo zinali zabwino. Chinthu chotsatira chinali kuchitika, uko kumabwera kubadwa mu nyumba mmenemo. Ndipo pamene Mzimu Woyera, onani, mzimu wina unabwera mmenemo, umene unali mwana wamwamuna. Mwana wamwamuna ameneyo, iye sanali mu ulamuliro wathunthu, ngakhalenso iye sanali wolamulira kufikira iye atafika pa usinkhu wina. Ndipo iye ankayenera kuti atsimikizidwe, choyamba. Inde. Ndiyeno iwo anali nalo lamulo la kulandiridwa. Kwa inu atumiki, “kukhazikitsidwa kwa mwana wamwamuna,” ndi chimene ine ndikuchikamba tsopano, mwaona, ndiye pamene iye afika pa malo pomwe iye anali kulandiridwa.
-----
Iwe suli wotembenuka kufikira iwe utalandira Mzimu Woyera. Ndiko kulondola. Iwe ukukhulupirira “kuloza.” Mzimu Woyera wayankhula kwa iwe, ndipo iwe wamuvomereza Iye poyera. Mdierekezi ali ndi chinthu chomwecho. “Ine ndikumukhulupirira Iye kuti ali Mwana wa Mulungu.” Chomwechonso amachita mdierekezi. Koma iwe ukuyendabe kupita kwa Iye. Pamene, Petro anali atayitanidwa ndipo atalungamitsidwa, pa kukhulupirira pa Ambuye Yesu Khristu; ndipo mu Yohane 17:17, Yesu anawayeretsa iwo kupyolera mu Mawu, pakuti Mawu anali Choonadi. Ndipo Iye anali Mawu. Pa 1, Yohane amati, “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anapangidwa thupi, ndipo anakhala pakati pathu.” Iye anali Mawu, kotero Iye anawayeretsa iwo. Iye anati, “Atate,” akuyankhula kwa Mzimu mkati mwa Iye, “Ine ndikuwayeretsa iwo kupyolera mu Mawu,” Iyemwini, pa kusanjika manja Ake pa iwo. “Mawu Anu ndiwo Choonadi.” Mwawamba chabe anamuyankhula Iye mu kukhalapo, mu chiberekero cha mkazi; o, zosatheka kwathunthu kuti Iye akhale njira ina iliyonse kuposa Mawu awa a Mulungu kukamupanga Iye kuwonekera. “Ine ndikuwayeretsa iwo.”-----
Tsopano, “Ntchito zimene Ine ndichita.” Mulungu ali mu Mpingo Wake, kuti apitirize ntchito Zake. Ndicho chifukwa Iye anatumizira Mzimu Woyera. Tsopano, Iye ankadziwa izo. Iye, Iye ankadziwa kuti izo sizikanakhoza, izo sizikanakhoza kuchitidwa mwa njira imeneyo, chotero mwanjira yina, chotero Iye amayenera kutumiza. Atate anatumiza Mwana, kuyika zonse zomwe ziri mwa kas-... Mwana mwa inu. Ndipo ntchito zomwezo zimene Iye ankachita, ntchito zomwe zomwezo tsopano zimene Yesu anachita, inu mudzazichita nanunso, Mpingo. Kodi inu simukanakonda kuti muzichita ntchito za Mulungu? Yesu anati, “Ngati inu mukufuna kuti muzichita ntchito za Mulungu, khulupirirani pa Ine.” Inu mungakhulupirire motani pa Iye? Inu simungakhoze kuchita izo mpaka inu mutalandira Mzimu Woyera. Chifukwa, palibe munthu angakhoze kunena kuti Iye ali Mwana wa Mulungu; inu mukunena chimene winawake ananena.“Baibulo linanena kuti Iye ali Mwana wa Mulungu; ine ndikukhulupirira Baibulo. Chabwino. ”Baibulo limati Iye ali Mwana wamwamuna wa Mulungu; ine ndikulikhulupirira Baibulo. Abusa amati Iye ndi Mwana wa Mulungu; ine ndikuwakhulupirira abusa. Amayi amati Iye ndi Mwana Mulungu; ine ndikuwakhulupirira amayi. Bwenzi wanga amati Iye ndi Mwana wa Mulungu; ine ndikumukhulupirira bwenzi wanga.“ Koma njira yokha yomwe ine ndingakhoze kunena kuti Iye ali Mwana wa Mulungu, ndi pamene Mzimu Woyera ubwera mkati ndi kumachitira umboni wa Iwowokha, ndiye ine ndidziwa kuti Iye ali Mwana wa Mulungu.
“Palibe munthu angakhoze kumutcha Yesu 'Khristu,' kupatula mwa Mzimu Woyera.” Ha! Palibe munthu akuyankhula mwa Mzimu wa Mulungu anamutcha Yesu wotembereredwa, kapena kunena kuti Iye anali chinachake tsiku limenelo ndi chinthu chinachake lero. Izo zimamupangitsa Iye wofooka ndi wolakwitsa. Ayi, bwana. Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi nthawizonse. Mzimu woona uliwonse udzachitira umboni za zimenezo. Chabwino.
-----
Mzimu Woyera unabwera kudzakupatsani inu Mphamvu. Ine ndiri nawo Malemba ena apa, miniti yokha. Mzimu Woyera unabwera kuti udzakupatseni inu Mphamvu. Ine_ine ndiribe^Inu mukhoza kuzipeza izi; ine ndangopita kutali kwambiri, usikuuno. Kukupatsani inu Mphamvu, Mphamvu mu pemphero!Inu mumutenge munthu yemwe wakhala moyo wabwino, koma iwo nthawizonse ali ogonjetsedwa. “O, ine ndikuuzani inu...” Munthu wabwino, “O, zedi, ine ndimawakonda Ambuye, M'bale Branham.” Nthawizonse wogonjetsedwa, iwo pemphero lawo silimayankhidwa konse. Inu mumudzaze mkazi wamng'ono uyo ndi Mzimu Woyera nthawi imodzi, muone zomwe ziti zizichitika. Pamene iye apita pamaso pa Mulungu, iye sali wogonjetsedwa. Iye amabwera molimbamtima ku Mpandowachifumu wa Mulungu, akukhulupirira. Iye ali nawo ufulu chifukwa iye ali mwana wa Mulungu, mwa Kubadwa. Mtengeni mwamuna wachichepere uyo, wamantha kwambiri, bwana amamukankha pa malo ponsepo. Ati, “Dikirani miniti pano tsopano.” Chinachake chasintha, mwaona, iye ali nawo Mzimu Woyera.Iwo umakupatsa iwe Mphamvu. Moyo wako uli wodzaza Mphamvu.
-----
O, mai! Ine ndinali kuyankhula pa Mphamvu ya pemphero, Mphamvu ya kuyankhula, Mphamvu ya moyo wopatulika. Ameni. Ndicho chimene Mzimu Woyera uli woti uchite. Ena a inu anthu mumayenda motsatira, nkumati, “Chabwino, ine sindingakhoze basi kuleka kumwa. Ine sindingakhoze basi kuleka izi.” Mzimu Woyera umabwera kuti udzakhale mwa inu, kuti udzapange zonse izi “zosakhozekazi” kupita kutali ndi inu. Ndiko kulondola. Kuwapanga akazi kusiya kudula tsitsi lawo, kuwapanga iwo kusiya kuvala akabudula ndi zomasula. Popanda zowiringula. Kuwapanga iwo kusiya kulongolola. O, inde, ndicho chimene Iwo umadzera, kuti ukupangeni inu amoyo wopatulika. Iwo udzatsatira Malangizo a Baibulo nthawi iliyonse.Mkazi akati, “Kwatentha kwambiri basi; ine ndikungoyenera kuti ndivale izi. Zimandimvetsa ine mutu ngati ndizilola tsitsi langa kukula.” Koma palibe zowilungula ndi Mzimu Woyera. Iwo uli pamenepo kuti upangitse izo kutero. Iwo uzitsatira Mawu chimodzimodzi basi. Ndizo zomwe Mzimu Woyera uli woti uzichita. Ndi woti uzikupangani inu amuna kupotoloza mutu wanu kuchokera kwa akazi ovala mwatheka awo, ndi kuleka kuwakhumbira iwo, ndiwo ziwalo za mpingo. Ndizo zomwe Iwo uli woti uzichita.
Werengani akaunti yonse mu...
Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani?.