Chifukwa chiyani Betelehemu wamng’ono?


  Mndandanda Khrisimasi.

Chifukwa chiyani Betelehemu wamng’ono?


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Chifukwa chiyani Betelehemu wamng’ono?

Ine ndikufuna kuwerenga kuchokera m'Bukhu la Mika, mneneri, mmodzi wa aneneri aang'ono, mutu wa 5 ndipo ndime ya 2. Iwo umawerengeka monga chonchi:

Koma iwe, Betelehemu Efrata, ngakhale ndiwe wamng'ono pakati pa zikwi za Yuda, koma kuchokera... komabe kuchokera mwa iwe adza... bwera kwa ine wina iye wakuweruza... wakudzakhala woweruza mu Israeli; amene maturukiro ake akhala kuchokera... kale, kuchokera ku nthawi zosatha.

Mwa malo onse amene ali mu Palestina! Ndipo mmenemo muli mizinda yayikulu yochuluka kwambiri, ndi malo ake, mizinda imene ili mwakuwoneka yodziwika mochuluka koposa mwa kuphunzira kwa mbiriyakale, ndi yotetezedwa bwino mizinda yaikulu. Ndipo chifukwa chiyani kuti Mulungu asankhe Betelehemu wamng'ono kuti akhale malo obadwirako Mwana Wake? Ilipo yambiri yomwe ili yayikulupo. Ndipo mwa chitsanzo, kuphunzira kwa mbiriyakale kwa Yerusalemu, Yerusalemu wosangalatsa, likulu la iyo yonse, ndipo ndiwo umodzi wa mizinda yayikulu kwambiri ya Palestina. Ndiyeno ife tikudabwa chifukwa chiyani Mulungu angatenge tawoni yaying'ono kwambiri iyo ya Betelehemu, kuti akhale malo obadwira Mwana Wake.

Koma monga Malemba anena, “Chimene Mulungu alinga kuchichita, icho chidzachitidwa.” Ndipo alipo Mulungu, anazikonzeratu izo kuti zidzakhale mwa njira iyo kapena izo sizidzakhala konse mwa njira iyo. Ndipo apo Lemba likunena, mu mutu wa 15 wa Machitidwe, kuti, “Palibe kalikonse ka mwa mwayi.” Mulungu anadziwa chirichonse. Ndipo basi izo sizinachitike kuti zichitike mwa njira iyo. Zinangokhala kuti Mulungu anazipanga izo mwa njira iyo.

Ndiyeno pamene ife mmalingaliro athu aang'ono okhala ndi malire tiyamba kulingalirapo, “Chifukwa chiyani Mfumu yayikulu ya Kumwamba ikanasankha malo aang'ono ngati awo, mmalo mwa likulu?” Mmalo mwa ena... Ngakhale uko analipo malo ambiri amene anali nawo maziko auzimu aakulu kuposa omwe Betelehemu anali nawo. Mwa chitsanzo, malo ena ngati Silo. Silo anali malo opembedzera akale a Israeli, kumene iwo onse ankabwera chaka ndi chaka ku malo aakulu awa kumene likasa la Ambuye linkapumira. Ndipo nkudabwa bwanji, ndiye, kuti Iye sanakabadwire ku Silo?

Ndiye kunali Giligala, malo ena auzimu aakulu opembedzerako. Chifukwa chiyani Mulungu sanamulole Iye kuti akabadwire ndiye ku Giligala? Ndipo uko kunali ena amodzi, Zioni. Zioni anali pamwamba pa phiri. Ndipo ife tikudabwa chifukwa chiyani kuti Yesu sanakabadwire ndiye mu Zioni, chifukwa iwo akhala chizindikiro chachikulu cha mbiriyakale a kumene Ambuye adalitsako anthu Ake mu mibadwo. Ndipo izo zikuwoneka ngati kuti mwina Iye akanasankha Zioni, kapena Giligala, kapena... kapena Silo, kapena amodzi mwa malo ena aakulu kumene kunali kutakhala madalitso aakulu ndi zophunzitsa zazikulu. Ndipo uko inalipo mizinda yina yayikulu, monga ngati Hebroni. Amenewo anali malo a munthu amene anali kufuna mzinda obisalako, malo a chitetezo. Uko kunali Ramoti- gileadi, nawonso, malo ena obisalako kumene anthu amakhoza kubwera, chimene chikanakhala choyenera kwambiri kuti iye akabadwireko.

Ndipo mwina, ngati ine ndikanamaganizira izo, ine ndikanadzamubweretsa Iye ku Kadesh-barnea pakuti uko kunali mpando wachiweruzo, ndi malo othawirako. Mwina ine ndikanadzamubweretsa Iye ku dziko ilo kukakhala malo obadwirako Ake, kapena mwina ife tikanadzasankha yina ya mizinda yina. Koma, inu mukudziwa, ine ndiri wokondwa kwambiri kuti ngakhale zinthu zazing'ono chabe zosalabadiridwa mu Baibulo zimatanthauza mochuluka kwambiri. Ine ndikukhulupirira kuti uyo anali Yesu amene ananena izi, kuti, “Inu mumalambalala, ndi kuchita zinthu zolemerera za lamulo,” kani, “koma mumalambalala pa zinthu zazing'ono.” Ndipo nthawi zina ndi zinthu zazing'ono zimene zimagwirizira zinthu zazikulu palimodzi. Koma, zonse mu zonse, magudumu aakulu akutembenuzika chimodzimodzi basi mwa njira yomwe Mulungu anakonzera kuti iwo aziyitana^sipadzakhala limodzi liti lidzaphonye malo ake. Mulungu wakonzeratu zinthu zonse, ndipo izo ziyenera kugunda chimodzimodzi basi ku malo amenewo.

Ndipo pamene ife tipeza chikhulupiriro chotere, ndi kuyamba kuganiza za, “Ndani ali kuseri kwa izi zonse? Ndi sipuring'i yaikulu iti imene ikutembenuza chuma chachikulu cha Mulungu ichi?” Ife tikupeza kuti ndiwo Mzimu Woyera. Sizinasiyidwe mmanja a munthu kuti achite zinthu; koma mmanja a Mzimu Woyera. Ndipo Iye ali sipuring'i yaikulu, kuti ngati Iye angakhoze kupeza zipangizo zonse, izo zidzagwira ntchito mwangwiro kumene ndi kusunga chimodzimodzi nthawi ya Mulungu. Ndiyeno ife tikuona izo ndipo ife tikudadwa mmalingaliro athu ndiye, pamene ife tiyang'ana pa zinthu zazikulu ndi momwe ife tikanadzakhalira nazo izo; ndiyeno chimatipatsa ife chitonthozo chochuluka lero kuganiza kuti, mwina ngati ife tiri gulu laling'ono la anthu, mwina ngati ife tiri osadziwika kwa dziko ndi kwa mipingo yayikulu ya zipembedzo, komabe Mulungu amagwiritsa ntchito zinthu zazing'ono izo nthawizina.

Pakuti zinalembedwanso m'Malemba, “Musawope, nkhosa zazing'ono, ndi chifuniro chabwino cha Atate anu kuti akupatseni inu Ufumu.” Ndi chitonthozo chotani, kuti, ine ndikudziwa izo motsimikiza basi monga Yesu anayenera kukabadwira mu Betelehemu wamng'ono, kotero zidzakhala nkhosa zazing'ono zimene Atate ati adzazipatse Ufumu, chifukwa izo zinalembedwa. Ndipo Malemba onse anapatsidwa mwa kudzoza, ndipo Malemba sangakhoze kuswedwa. Iwo ayenera kukwaniritsidwa. Kotero izo zikutipatsa ife chiyembekezero icho, kudziwa kuti_kuti zidzakhala nkhosa zazing'ono zimene ziti zidzalandire Ufumu, nkhosa zazing'ono zokhulupirika za okhulupirira. Ine ndikudalira kukhala imodzi mwa nkhosa zimenezo, kapena, mu nkhosa zazing'ono izo, ine ndiyenera kunena. Ndiyeno ife tikuyidziwa nkhani, ambiri a ife tikudziwa nkhani ya momwe Israeli anabwerera mu Palestina mwa lonjezo la Mulungu. Ndipo ife tikudziwa kuti Yoswa wamkulu uyo anali mmodzi amene anagawira fuko lirilonse gawo lawo.

Ndipo Yoswa, akugawaniza, anagawa gawo la Yuda. Ngati inu mudzazindikire pa mapu, ndizo... mwachirengedwe chakumadzulo chabe kwa chigwa cha nyanja, mailosi pang'ono kummwera kwa Yerusalemu, likulu. Ndipo pamene Yuda anali kutenga gawo lake, kapena gawo lake kani, mu dziko, dera lake, ife tikanalitcha ilo, ndi zachirendo, koma mzinda wawung'ono uwu sunatchulidwe nkomwe, Betelehemu. Komabe iwo unali pamenepo, chifukwa chakuti Abrahamu... Kapena, ine ndikukhulupirira anali Rabeka amene anayikidwa pa malo amenewo. Koma iwo uyenera kukhala mudzi wawung'ono chabe wa mtundu wina, chifukwa ngati inu muwerenga Yoswa 5, inu mudzapeza kuti inalipo mizinda yayikulu zana ndi khumi ndi isanu pansi pa ulamuliro wa Yuda, kupatula midzi ndi matawoni aang'ono; mizinda zana ndi khumi ndi asanu, amene akutchulidwa. Ndipo mwina pamene iyo inagawanizidwa, kuti Betelehemu anali wamng'ono kwambiri, mwina chabe ka_kanyumba kakang'ono kapena ziwiri, sunatchulidwe nkomwe mu cholowa. Ndiyeno ife tikupeza kuti iwo sunafike podziwika kwenikweni....

Mmodzi amene anawuyambitsa iwo anali mwana wamwamuna wa Kalebu, mwana wamwamuna wa Kalebu, amene dzina lake linali, Salma, ndipo iye anawuyambitsa iwo. Baibulo linati iye anali tate wa iwo, chimene chikutanthawuza kuti iye anali woyambitsa wa Betelehemu. Mwa kulankhula kwina, iye ayenera kuti anasunthira mmenemo nayambitsa malonda a mtundu wina, ndi zogulitsa, ndi malonda, ndi zina zotero, izo zinakulitsa iwo. Ndipo kenako ife tidzapeza kuti chifukwa chenicheni cha iwo, kuti malo onse anali kuchitira nsanje kachidutswa ka dziko kakang'ono aka; kamene kanali kumpoto, ndi kummawa, ndi masitso pang'ono cha kummwera, pa mpita uwo. Ndipo iwo unali wachonde kwambiri mwa yonse ya Palestina. Iwo unali ko... kolima chimanga ndi kolima tirigu, ndipo uko kunali minda ya azitona yayikulu, ndi zina zotero, pa iwo, mu gawo ilo la Betelehemu, kapena Palestina, mapeto a chigawo cha Yuda.

Ndipo ife tikupeza kuti uko kunadzakhalanso kwawo kwa hule Rahabu. Pamene Israeli anali atadutsa mzere wa mmalire wa Mtsinje wa Yorodani, kulowa mu Palestina, ife tikuyidziwa nkhani ya Rahabu hule. Tiyeni timuwone iye mmawa uno kwa maminiti pang'ono tsopano, ngati do... dona wamng'ono, mkazi wamng'ono wokongola amene tsoka lina mu moyo anakakamizidwamo, pokhala wachikunja, anakakamizidwa kulowa mmoyo umene iye anali kukhala. Ndipo nthawi zambiri anthu amakakamizidwa mu moyo umene iwo amakhala.

Ndipo ine ndikhoza kuwonjezera apa, kodi inu mukudziwa kuti iye ankayimira Mpingo wa Amitundu? Iye anali wa Amitundu, ndipo iye anali choyimira cha Mpingo wa Amitundu, pamene iwo anamva uthenga. Ife tinali tonse kunja mu chiwerewere chauzimu, tikuchita ziwerewere zauzimu motsutsana naye Mulungu Wakumwamba, mu mitundu yonse ya zinthu, mitundu yonse ya mipingo ndi zipembedzo. Koma pamene ife tinamva kuti panali Mulungu amene amakhalabe moyo, amene akhoza kuchita zozizwitsa, mwamsanga ife tinalandira Uthenga.

Ndipo apo panayikidwa Magazi a Ambuye Yesu, amene anapanga chingwe chofiira. Ndipo kuti tisapite mwatsatanetsatane, inu mukudziwa momwe iye anachipachikira icho kuchokera pa zenera lake, powonekera, Magazi anawonetseredwa poyera. Ndimo momwe Magazi ayenera kuwonetseredwa, poyera atapachikika kuchokera panja pa khoma; kusonyeza kuti, mkati, chinachake chinali chitachitika. Ndimo momwe wokhulupirira woona mwa Khristu aliri mmawa uno; kunjako kuli kuwonetsera kwa Magazi a Ambuye Yesu, izo zikusonyeza kuti chinachake chinachitika mkati.

Ndipo kupyolera mu izi, Mulungu anayang'ana pansi pamene mkwiyo unagwa ndipo malipenga anayamba kuwomba, Mulungu anawona chingwe chofiira icho chitapachikika apo ngati chikumbutso. Nthawizonse zamukondweretsa Iye kudutsa pa Mwazi. “Pamene Ine ndiwona Mwazi, Ine ndidzadutsa pa inu.” Iye anawuwona iwo. Ndipo pamene kugwedeza ndi Mzimu Woyera unagwedula dziko lapansi ndi kugwedezera pansi makoma awo, mapazi ena makumi awiri kunenepa, palibe mwala umodzi umene unagwera pamene chingwe icho chinali kulendewera. Kusonyeza chitetezero cha Mulungu woona kwa wokhulupirira woona, ziribe kanthu ndi mchikhalidwe chotani chimene inu mulimo pamene Iye akupezani inu, ngati inu mudzangovomereza chingwe chofiira icho. Icho chimalukana kupyola m'Baibulo.

Ndiyeno ife tikumuwona iye pamene iye anatengedwera mkati ngati mmodzi wa Aisraeli. Iye anakondana naye mwamuna, amene anali kapitao ndi kalonga mu Yuda. Iye anali kapitao wa ankhondo a Israeli. Dzina lake linali Salimoni, monga ngati mfumu, Solomoni. Ndipo iye anali kapitao, ndipo iye anakhala mu chikondi chachikulu ndi kapitao uyu, yemwe anali kalonga wa Yuda. Ndipo potsiriza iye anakwatiwa ndi iye. Ndipo pamene chuma chinakhazikitsidwa kwa Aisraeli, iye ndi mwamuna wake wokondedwa ankakhala mu Betelehemu.

Tsopano inu mwayamba kuziwona izo zikutseguka, sichoncho inu? Mwaona? Izo zikuyamba kutseguka pamene ife tikuona kuti mu Betelehemu iye ankakhala, pokhala mkwatibwi wa Amitundu, kwa Myuda. Chifukwa? Chifukwa iye anakhulupirira mwa Mulungu wochita-zozizwitsa. Ndipo mwa kuyang'ana kumene iye anachokerako, kuchokera pakukhala wochokera mnyumba ya mbiri yoyipa, ya uchiwerewere; kupyolera mu kutembenuka kwake ndi kupyolera mu chikhulupiriro chake chosalephera mwa Mulungu, izo zinamuchotsa iye kuchokera ku nyumba ya uchiwerewere, kupita ku nyumba yokongola mu Betelehemu. Nkusiyana kotani!

Ndimo momwe izo zimatichitira ife tonse. Kuchokera ku nyumba ya kusakhulupirira ndi zokhumudwitsa, machitidwe oyipa awo, ndi chirichonse; kupita ku malo, okhazikitsidwa mwa Khristu, chimene chiri chokongola kwambiri. Kuchokera ku chotonzedwa kupita ku chapamwamba, ndiko kusiyana kumene izo zimapanga kupyolera mu kutembenuka kwathu. Ndipo kodi inu munaona, iye anakwatiwa ndi kalonga wa nyumba ya Yuda, kapitao? Kapitao uyo ankayimira Khristu, anadzitengera kwa Iyemwini Mkwatibwi wa Amitundu. Kuchokera ku chotsika cha chotsikitsitsa, kupita ku chachikulu ndi malo abwino mu dziko, monga ife tidzafike ku izo kenako mu Uthenga wathu, kutsimikizira kuti sichinali chinanso chimene chikanakhoza kukhala koma icho. Iwo ali choyimira cha Mpingo wa Amitundu.

Werengani akaunti yonse mu...
Chifukwa chiyani Betelehemu wamng’ono?