Zochitika za makono zimamveka bwino ndi uneneri.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Nthawi yotsiriza mndandanda.

Mawu a Ambuye amadza kwa aneneri.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Zochitika za makono zimamveka bwino ndi uneneri.

Iwo anakuuzani inu a chi Pentekoste, zakamakumi anai ndi zisanu, makumi asanu zapitazo. Amayi ndi abambo anu, pameneanali Achipentekoste enieni, anatuluka kuchokera mubungwe ndipo anachitembererachinthucho ndikutuluka mu icho. Ndiye ngati galu kumasanzi ake, anabwerera kwaizo kachiwiri. Anachita chinthu chomwecho chimene chinaupha mpingo uwo, inumunadzipha eni anu ndi chinthu chomwecho. Palibe chowatsutsa anthu alimmenemowo, palibe chotsutsa izo, ndikachitidwe ka chinthu kamene kakuchititsaizo.

Ndipo zindikirani mu chochitika ichi,kutsimikizira kwa mauneneri a Mawu a Mulungu akukhala akukwaniritsidwa. Ngatiansembe awo.... Iwo anali atazikonza izo ndendende basi momwe Mesiya akanatiazadzere, iwo ankadziwa zomwe zikanati zidzachitike. A - a Farisi anali ndilingaliro lawo, a Saduki, a Herodia, ndi, o, iwo anali ndi malingaliro awo.Koma Iye sanabwere ayi.... Iye anabwera mosiyana ndi wina aliyense wa iwo, komandendende ndi Mawu. Yesu ananena chinthu chomwecho ali kuno: “Ngati inumukanandidziwa Ine, inu mukanati mulidziwe tsiku Langa. Ngati inu mukanandidziwa,inu muk... inu mukuti, 'Chabwino, Mose! Ife tiri naye Mose.'” Anati, “Bwanji,ngati inu mukanati muzimukhulupirira Mose, inu mukanati mundikhulupirire Ine;chifukwa, iye analemba za Ine.

“Koma, onani, pamene Mulungu anali akutsimikizira ndendende zomwe Iyeanalonjeza, iwo anali nazo izo mwa mtundu wina wa njira yapamwamba yomwe Yesuankayenera kuti adzadzere, ndi... ine ndikutanthauza Mesiya. Mesiya anali woti adzabwere ku gulu lawo lomwekapena iye sakanakhala Mesiya. Chabwino, ziri mwanjira imeneyo, pafupifupi,lero, ”Ngati iwe sukuona kupyolera m'magalasi anga, iwe sukuyang'ana konse.“ Mwaona, ndipo ndi momwe izo ziri. Ichondi choonadi. Ife sitimakonda kuganiza chotero, koma ndizo mwamtheradi Choonadi.

Mu Aheberi 1:1, Mulungu mu nthawi Zamakedzana analemba Baibulo mwa njira ya kusankha Kwake Komwe. Iye sanalilembe konse Ilo ndianthu ophunzira za Baibulo, ngakhalenso Iye samalitanthauzira ndi anthuophunzira za Baibulo. Panalibe konse nthawi yomwe - yomwe anthu ophunzira zaBaibulo anali nako konse kutanthauzira kwa Mawu a Mulungu. Kutanthauzira kumabwerakokha kwa mneneri. Ndipo njira yokha yomwe ife titi tidzachokere konse muchisokonezo ichi ndi kuti Mulungu atitumizire ife mneneri ameneyo, ndendende basi, njira yokha yomwe izo zitizichitikire. Izo zakhala zikukhulupiriridwa, kuyembekezeredwa, ndi kukwaniritsidwa. Onani, Ilo silinalembedwe ndi munthu, koma Ilo linalembedwa ndi Mulungu. Ilo sibuku la munthu, Ilo sibukhu laophunzira zaumulungu. Ilo ndi Bukhu la Mulungu, lomweliri Buku la uneneri lolembedwa ndi aneneri ndi kutanthawuziridwa ndi aneneri. Baibulo linati, “Mawu a Ambuye amadza kwa aneneri.” Ndendende!

Kukongola kwake momwe izo zinalongosoleredwa, kapena, kuwonetseredwa pamene Yesu anadza pa dziko lapansi,ndipo Yohane anali mneneri wa tsiku limenelo, ndipo iye - iye anali akunenera.Iwo anati, “O, inu mukutanthauza kunena kuti Mulungu adzaphwasula magulu athuaakuluwa kuno ndi zinthu zonse izi? Ndipo idzakhalapo nthawi, yomwe m'makachisi athu simudzakhala mukupembedzedwamo konse?” Iye anati, “Kunali kudza nthawi pamene Mulungu akanati adzapangae nsembe paMwana wa Nkhosa wa Mulungu, Munthu.” Ndipo iye ananena kuti - kuti iye akanatiadzamudziwe Iye pamene Iye adzadza. Ndipo iye akanati... Iye anali wotsimikizakwambiri ndi Uthenga wake, iye anati, “Iye waima pakati panu pakali pano ndipoinu simukudziwa izo.” Iye ali pakati pa inu pomwe ndipo inu simuli kuzidziwaizo.

Ndipo tsiku lina pamene Yesu anayendera uko, Yohane anayang'ana m'mwamba ndipoanachiona chizindikiro chija pamwamba pa Iye, iye anati, “Taonani, Mwana wa Nkhosawa Mulungu yemwe ati achotse tchimo la mdziko.” Mphindi yomweyo Yesu anadziwaapo kuti Iye anazindikiritsidwira pamaso pa anthu. Tsopano, Iye anali Mawu,kodi ife tikanati tikaikire izo? Baibulo linati Iye anali Mawu, “Pachiyambipanali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anapangidwa thupi ndipo anadzakhala pakati pathu.” Ndipo pano Iye ali a.... panopali Mawu a dziko lapansi (taonani! Mwangwiro!) akubwera apo kumene kudzalowa mmadzi kupita kwa mneneri.

Uko nkulondola, Mawu nthawi zonse amadzakwa mneneri Wake. Kotero ife sitingakhoze kuwayembekezera Iwo kuti abwere kwa ophunziraza umulungu. Ife sitingakhoze kuwayembekezera Iwo kuti abwere kwa zipembedzo. Iwo ayenera kubwera m'njira ya Mulungu tsopano yomwe Iye anatiuziratu ife, ndipo ndiyo njira yokha Iwo ati adzadzere konse. Iwo adzadedwa, adzanyozedwa,adzakanidwa. Pamene Iwo ati abwere, Iwo adzaponyedwera kunja ku mbali imodzi, ndi chirichonse, koma Mulungu adzazichita izo muli monse. Iwo anakanidwa mwaYesu Khristu, iwo anakanidwa mwa Yohane, iwo anakanidwa mwa Yeremiya, iwoanakanidwa mwa Mose. Izo ziri chomwecho nthawi zonse. Koma Mulunguamasunthirabe mtsogolo mwa njira yomwe Iye analonjezera kuti Iye akanadzachita izo. Inde, bwana, Iye samalephera konse kuzichita izo mwa njira yomweyo.

-----
Yang'anani mu Baibulo, inu muwone komwe,m'badwo umene ife tiri kukhalamo ndiye, pamene inu mukuwona zinthu zazikulu iziziri kupangitsidwa mowonetseredwa. Pamene Mulungu alonjeza kuti achita izo, iyenthawizonse amazichita izo pamapeto am'badwo uliwonse pamene mpingo wafika pamalo otembenukirapo, ndipo iwo akatembenuka kuchokera ku Mawu kubwerera kutchimo ndi chidziko. Chidziko ndilo tchimo. Baibulo linati, “Ngati inumulikonda dziko kapena zinthu za dziko, chikondi cha Mulungu sichiri mwa inu.”

Ndikulankhula usiku watha, ine ndinali kulankhula zedi - za nsembe yomwe inkaperekedwa, mwana wa Nkhosa. Iye anali woti adzikhala ali masiku asanu ndiawiri kuimirira mibadwo isanu ndi iwiri. Kunali koti kusamakhale chotupitsa chopezekapakati pa anthu, kopanda chotupitsa kwa masiku asanu ndi awiri. Izo zikutanthauza kuti pasamakhale chirichonse chosakaniza ndi iwo, iwo ndiwosatupitsidwa, mowirikiza. Ndipo ife sitikufuna tidzikhulupiriro ayi,zotupitsa ndi zinthu zosakanizidwa ndi ife. Ife sitikufuna dziko lisakanizidwendi ife. Iwo uyenera kukhala uli Mkate wosatupitsidwa wa Mulungu, Mawu aMulungu, Mawu osasokonezedwa a Mulungu, womwe, “Munthu adzakhala moyo ndi Mawu wonse omwe amachokera mkamwa mwa Mulungu.”

Kachitidwe kathu kachipembedzo,ndikusagwirizana ndi zinthu, zaika zotupitsa mwa ife, ndipo ichi ndi icho ndidziko ndi fashoni. Ndipo, o, izo zafika kwambiri pafupifupi Hollywoodpaliponse. Izo potsiriza zifika pofanana ndi England, ndipo kuitanidwira kuguwachidzikhala chamanyazi. Mai! Monga m'bale anati, “Inu mungapezeno bwanji nsombamungalawa?” Uko nkulondola.

Ife tiyenera kukhala nawo Uthenga ukalalikidwa muchidzalo Chake, ndi mphamvu yaMulungu kuti idzitsimikizira izo molingana ndi lonjezo la m'badwo umenewo ndikumawonetsera kuti izo ziri ndendende chifuniro cha Mulungu. Kunja kwa Izondiwe membala chabe wa mpingo, ziribe kanthu momwe iwe ukuyesera, iwe ukumayeserakuti udzimuchitira Mulungu Ntchito. Inu mukhoza kumapita kuphwando loluka - ndikusoka, inu mukhoza kukhala wokhulupirika kwa mpingo; koma kupatula nyongolotsiya Moyo wa Muyaya iyo ikakhala kuti inadzozedweratu mwa inu, kuti mudzakhalemwana wa mwamuna kapena wamkazi wa Mulungu, inu mudzakula nkudzakhala china chake chopunduka; koma osakhala konse weniweni, mwana wa mwamuna kapena wamkazi woonawa Mulungu.

-----
Zindikirani, ife tikupeza lero kutianthu.... Alipo anthu ochuluka omwe sakukhoza basi ku ukhulupirira iwo, ngakhaleanthu odzazidwa ndi - Mzimu. Ine ndikuptsani inu chimodzi china chomwe chitichikutsamwitseni inu. Ubatizo wa Mzimu Woyera siumatanthauza kuti iwe ukupitakukalowa, palibe konse, osati paizo, ziribe zochita chirichonse ndi solo yako.Uwo ndi ubatizo, mwaona. Apa pali solo yamkatiyo, mkati umu, iyo iyenerakuchokera kwa Mulungu. Komano kunjako inu muli ndi zokhudzila zisanu, ndipo zisanumwa.... Zolowera mwainu.... zokhudzila kwanu kwa dziko lapansiri. Mkatimo, inumuli ndi mzimu, ndipo mmenemo inu muli ndi zotulutsira zisanu: chikumbumtimachanu, ndi chikondi, ndi zina zotero, zotulutsira zisanu za za mzimu umenewo.Kumbukirani, mumzimu umenewo inu mukhoza kubatizidwa ndi Mzimu weniweni waMulungu ndipo komabe mkudzataika. Ndi solo yokha yomwe imakhala moyo, yomweinadzozedwa ndi Mulungu.

Kodi Yesu sanati, “Ambiri adzadza kwa ine mu tsiku ilo, ndikumati, 'Ambuye,kodi ine sindinatulutse ziwanda, kuchita ntchito zazikulu ndi zamphamvu,kulosera, mphatso zazikulu za Mulungu?'” Iye adzati, “Chokani kwa Ine, inuochita zakusaweruzika, Ine sindinali kukudziwani inu nkomwe. Ambiri adzabweramu tsiku limenelo.”

Kodi Kayafa sanalosere? Iye anali mdierekezi. Ife tikuzipeza apo.... Ndipo ansembe aja, amuna aakulu mu masikuamenewo, amayenera kukhala atsogoleri opambana m'masiku awo, ali ndikudzichepetsa ndi china chrichonse, koma analephera kuti awawone Mawu a Mulungu Iwo eni ali kuwonetseredwa patsogolo pa iwo Ife tikhoza kungotenga mulu wa izo zomwe ine ndazilemba apa. Nanga bwanji Balaamu? Iye anali... Inu mukuti, “Mulungu amasintha malingaliro Ake.” Iye samasintha malingaliro Ake! Pamene Balaamu anapita uko ngati mneneri, ndipo anapita uko, bishop, mlaliki, chirichonse chimene inu mukufuna kumutcha iye, iye anali mwamuna wamkulu. Koma pamene iye anafunsira Mulungu za kupita uko ndi kukatemberera Israeli; iye sankawakondaiwo pa kuyamba pomwe, kotero iye anapempha kuti apite. Mulungu anati, “Usatiupite!”
“Ndiye iwo anatumiza nthumwi zina... mwina mwake wa mabishopu kapena akulu,kapena chinachake, uko, anati... wamaphunziro ochulukirapo kuti amukakamize iye.Iye anapita ndipo anakamufunsa Mulungu kachiwiri. Inu simumasowa kutimuzimufunsa Mulungu nthawi yachiwiri! Pamene Mulungu ananena izo koyamba, ndizomwezo! Inu simusowa kuti muziyembekezera china chirichonse.

Rebeka sanayembekez ere kuti apeze kulamulira kwachiwiri. Iwo anamufunsa iye, anati,“Kodi iwe upita?”
“Musiyeni iye anene.”
Iye anati, “Ine ndipita!” Iye anali atadzozedwa molimba ndi Mulungu. Iyeanakhala mmodzi wa mfumukazi za Baibulo chifukwa chochita pa kututuma kwa Mzimuwa Mulungu umene unasunthira pa iye kuti alandire chimene mwamtheradi chinalichoonadi, ndipo iye azikhulupirira izo.

Tsopano ife tikumupeza, Balamu, ndithudi, iye sankakhoza kuwona. Iye anapita uko ndipo anakayang'ana paanthuwo, anati, “tsopano, mphindi yokha! Ndife anthu aakulu, opambana kuno, inu mwangokhala gulu lobalalika.” Inu mukuona? “Ndipo ife tonse - ife tonse tikumukhulupirira Mulungu yemweyo.”

Izo zoonadi. Iwo onse ankamukhulupirira Mulungu yemweyo, ndipo iwo onse ankampembedza Yehova. Tayang'anani pa nsembe ya Balaamu: maguwa asanu ndiawiri, chiwerengero changwiro cha Mulungu; mipingo isanu ndi iwiri, mwaona; anaankhosa asanu ndi awiri, kuyankhula za kudza kwa Ambuye. Mwachikhazikitso, iyeanali mwachikhazikitso basi monga Mose analiri; koma, inu mukuona, apo panalibe kutsimikizidwira kwa Umulungu. Mmenemo, iwo onse anali aneneri. Koma pansi pa utumiki wa Mose, uko kunali Lawi la Moto lauzimu, Kuwala kumene kunkapachikikapa msasawo. Uko kunali machiritso a Uzimu, uko kunali mfuu wa Mfumu mu msasa, zizindikiro zazikulu, machiritso a Uzimu ndi zodabwitsa ndi zinthu zochitidwa pakatipawo. Icho chinali chizindikiro cha Mulungu wa moyo pakati pa anthu Ake.

Mwachikhazikitso,iwo onse anali kulondola. Ndipo Baalamu anayesera kuwakakamiza anthuwo, ndipo anawalodza iwo kuti alowemo. Liti? Iwo asanafike kumene ku Dziko Lolonjezedwalo. Tsiku lina kapena awiri, akanati akakhale ali mu Dziko Lolonjezedwa.

Werengani akaunti yonse mu...
Zochitika za makono zimamveka bwino ndi uneneri.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri.

Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye.

Hebrews 1:1-2


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

 

Kodi Ichi Ndi
Chizindikiro Cha
Mapeto, Bwana?

(PDF) Komwe
Mtambo udawonekera.

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.