Nthawi yotsiriza mndandanda.

  Nthawi yotsiriza mndandanda.

Iwo odzozedwawo pa nthawi yotsiriza.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Iwo odzozedwawo pa nthawi yotsiriza.

Mateyu 24:23-24,
23 Ndiye ngatimunthu aliyense adzanena kwa inu, Onani, kuno kuli Khristu, kapena uko;musakhulupirire izo ayi.
24 Pakutipamenepo padzawuka a Khristu onyenga, ndi anenerionyenga, ndipo adzawonetsazizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa; mochuluka chotero kuti, ngati kukanakhalakotheka, iwo akanadzanyenga osankhidwaomwe.

Inendikufuna inu kuti muzindikire apa mu Mateyu 24, Yesu anagwiritsa mawu akuti“aKhristu,” a - K - h - r - i - s - t - u, “aKhristu.” Osati Khristu, koma “aKhristu,” ambiri, osati mmodzi. “aKhristu.” Chotero, mawu Khristu amatanthauza “Iye Wodzozedwayo.” Ndiyeno ngati ndiwo “odzozedwa,” sipadzakhala osati mmodziyekha, koma ambiri, odzozedwa, “Iwo odzozedwawo.” Mwaona? Mwinamwake,ngati Iye akufuna kuti aziswe izo kotero ife tikanati mochuluka kapenamwapang'ono timvetse bwinoko izo, Iye akanati, “Mu masiku otsiriza pamenepokudzauka iwo odzozedwa, monyengawo.” Tsopano, izo zikuwoneka pafupifupi zosatheka, mwona, mawu a “Odzozedwa.” Koma zindikirani mawu otsatira omwe, “ndi aneneri onyenga,” a - n - e - n - e - r - i, ambiri.

Tsopano, iyewodzozedwayo, ndi, “yemwe ali ndi Uthenga.” Ndipo njira yokhayo imene Uthengaungakhoze kuti ubweretsedwe ndi kupyolera mwa yemwe ali wodzozwdwa, ndipo ameneyo akanakhala ali mneneri, wodzozedwa. “Pamenepo padzauka aphunzitsiodzozedwa monyenga.” Mneneri amaphunzitsa chimene Uthenga wake uli. Aphunzitsiodzozedwa, koma anthu odzozedwa okhala ndi kuphumnzitsa kwa bodza. Iwoodzozedwawo, “aKhristu,” ambiri; “aneneri,” ambiri. Ndipo ngati pamenepo palichinthu chotero monga khi - Khristu, m'modzi, ndiye awa akanayenera kuti akhale “iwo odzozedwawo,” amene uneneri wawo wa zomwe iwo anali kuphunzitsa ukanakhalakusiyanako, chifukwa iwo ali iwo odzozedwawo, odzozedwa.

Tsopano, ndi phunziro la Sande sukulu, ife tikufuna kuti - kuti tiyese kubweretsa izi kuchiwonetsero chenicheni, mwa Malemba, osati mwa zimene wina wake wanena za izo,koma kungowerenga Malemba kokha. Inu mukhoza kunena, “Izi zingakhozekukhala motani? Akanakhala iwo odzozedwawo....” Kodi iwo anali chiyani? “aKhristu,” a - K - h - r - i - s - t - u, odzozedwa. “aKhristu, ndi aneneri onyenga.”Iwo odzozedwawo, koma aneneri onyenga!

Yesuananena, kuti, “Mvula imavumbira pa olungama ndi osalungama.” Tsopano, wina wakeakhoza kunena kwa ine, “Kodi inu mukukhulupirira kuti kudzoza uko pa anthuamenewo kukutanthauza kuti iko ndi kudzoza kwa Mzimu Woyera?” Inde, bwana,Mzimu Woyera weniweni wa Mulungu pa munthu, ndipo komabe iwo ndi onyenga. Tsopanomvetserani mwatcheru ndi kuwona zimene Iye ananena. “Ndipo iwo adzasonyezazizindikiro ndi zodabwitsa, mochuluka chotero kuti izo zikanadzanyengaOsankhidwa amene ngati kukanakhala kotheka.” Ndipo iwo ali odzozedwa ndi MzimuWoyera weniweni. Ine ndikudziwa kuti izi zikumveka mopusa kwambiri, koma ifetitenga nthawi ndi kufotokoza izo mwa Mawu, kuti ndizo mwamtheradi PAKUTI ATEROAMBUYE, Choonadi.

-----
Tsopano, Mateyu, mutu wa 5, ndime ya 45, tiyeni tiwerenge tsopano. Tiyeni titenge, kuyambira mu - m'mbuyo pang'ono mwa iyo, ya 44.
Koma Inendinena kwa inu, Kondani adani anu, dalitsani iwo amene akutembererani inu,chitirani zabwino kwa iwo amene amakudani inu... Apempherereni iwo ameneamakugwiritsani inu ntchito monyoza, ndi kukuzuzani inu; Kuti inumukakhoze kukhala ana a Atate wanu amene ali Kumwamba: pakuti iye amapangitsadzuwa lake kuti litulukire poyipa ndi... abwino, ndipo amatumiza mvula paolungama ndi... osalungama.
(Mvula imabwera pa oyipamofanana monga pa abwino.)

Ahebri 6:7-8,
7 Pakuti, (mvetserani) nthaka.... Imamwa mu mvula imene imabwera mowirikiza pa iyo, kutiibalepo therere lokwanira iwo amene adailimira, imalandira madalitso kuchokerakwa Mulungu:
8 Koma ikabala minga.... mitungwi itaika, niitsala pang'ono kutembereredwa; zimene mapeto ake ali otizikawotchedwe.

-----
Tsopanofanizirani izo ndi Mateyu 5:24 kachiwiri. Zindikirani, Yesu anati mvula ndi dzuwazimabwera pa dziko lapansi, zimene Mulungu amazitumiza izo kuti zikonzerechakudya ndi zinthu kwa anthu a dziko lapansi. Ndipo mvula imatumizidwachifukwa cha chakudya, therere. Koma namsongole, maudzu, pokhala m'munda,zimalandira chinthu chomwecho. Mvula yomweyo imene imapangitsa tirigu kukulandi mvula yomweyo imene imapanga maudzu kukula.

-----
Tsopano,chotero, mvula kugwera pansi pa zomera zachirengedwe za padziko lapansi, ndichoyimira cha mvula Yauzimu imene imapereka Moyo Wamuyaya, ikigwera pansi paMpingo, pakuti ife timayitcha iyo mvula ya nyundo ndi mvula ya masika. Ndipondiyo mvula, ikutsanulira apo kuchokera mu Mzimu wa Mulungu, pa Mpingo Wake.

Zindikirani,ndi chinthu chachirendo kwambiri pano. Mwaona? Pamene mbewu izo zinapita munthaka, mulimonse izo zinafikira mmenemo, izo zinali minga kuyamba ndi kuyamba. Koma kumeneko tirigu amene anapita mu nthaka, ndi therere, linali thererekuyamba ndi kuyamba. Ndipo therere lirilonse kudzibala lokha, mobwereza kachiwiri, zikusonyeza kuti ilo linali mu kuyamba kwapachiyambi. “Ndipoiwo akanadzanyenga Osankhidwa ngati izo zikanakhala zotheka,” chifukwa iwoakulandira mvula yomweyo, dalitso lomwelo, kusonyeza zizindikiro zomwezo, zodabwitsa zomwezo. Mukuona? “Iwo adzanyenga, kapena akanadzanyenga Osankhidwawongati izi zikanakhala zotheka.” Tsopano, minga siyingakhoze kudzithandizakukhala minga, ndipo ngakhalenso tirigu sangadzithandize kukhala tirigu; ndichochimene Mlengi wa chimodzi chirichonse analinga pa chiyambi. Ndiwo Osankhidwa. Mvula yomweyo!

-----
Tsopano dzuwa limabwera modutsapo ndi kukhwimitsa njerezo. Tsopano, ilo silingakhozekuzikhwimitsa izo zonse mwakamodzi. Pamene izo zikupitirirabe, kumakhwima, izomowirikiza zimacha mpaka izo zimabwera ku mphonje yathunthu. Chotero izo ziri, lero, ndi Mpingo. Izo zinayamba mu ukhanda wake, kumbuyo mu m'badwo wa mdima, pamene iwo unali pansi pa nthaka. Iwo wakula tsopano kufika mu kukhwima. Ndipoife tikhoza kuziwona izo, mwangwiro, momwe kuti Mulungu kupyolera muchirengedwe nthawizonse....

Inusimungakhoze kusokoneza chirengedwe. Ndilo lomwe liri vuto lero. Ifetikuwulutsa mabomba, ndi kunja uko mu nyanja imeneyo, kuziswa izo ndikuziphulitsa izo mozungulira ndi ma bomba a atomiki. Inu mukungoswa zochulukaza dothi limenelo nthawi zonse, kugwetsera mkati mwa ilo. Inu mukamadulirapansi mitengo; mikuntho idzakutengani inu. Kupanga dziwe pa mtsinje; iwoudzasefukira. Inu muyenera kupeza njira ya Mulungu yochitira zinthu ndikumakhala mwa iyo. Ife tawapanga anthu chipembedzo mu mipingo ndi mabungwe; tapenyani zimene ife tirinazo! Khalani munjira yoperekedwa ndi Mulungu ya izo.

Koma, inumukuona, “Iye anatumiza mvula,” kubwera kuphunziro lathu, “pa olungama ndiosalungama.” Yesu akukuuzani inu apa tsopano, mu Mateyu 24, icho chidzakhalachizindikiro panthawi yotsiriza. Tsopano, ngati chizindikiro ichi chiri kokhachoti chikadziwike pa nthawi yotsiriza, ndiye izo zidzayenera kuti zikhale kutachitikakutseguka kwa Zisindikizo zimenezo. Mwaona? Ndi chizindikiro chamapeto. Ichochikanadzakhala, pamene zinthu izi zikuchitika icho chidzakhala pa nthawiyotsiriza. Ndipo icho chidzakhala chizindikiro, tsopano, kotero kuti Osankhidwaasadzasokonezeke mu zinthu zimenezi. Inu mukuziona izo? Ndiye, izo ziyenerakuwululidwa, kuyikidwa pa mbalambanda.

Zindikirani, zonse tirigu ndi maudzu zimakhala moyo mwa kudzoza komweko kuchokera Kumwamba. Zonse za izo zimasangalala pa Iko. Ine ndikukumbukira izi, polozera m'mbuyo kuchisanzoichi kumtunda uko tsiku lija ku Green's Mill. Ine - ine ndinawona masomphenyaaja akubwera uko. Ndipo apo panali dziko lalikulu, ndipo ilo linali lonselitalimidwa. Ndipo apo panapita Wofesa, choyamba. Ine ndikufuna kuziyika izopamaso panu. Penyani chimene chikuchitika apo koyamba, ndiye ndichiyanichikutsatira icho. Ndipo pamene munthu uyu atavala choyera anabwera apokuzungulira pa dziko lapansi, akufesa mbewu, ndiye kumbuyo kwa Iye kunabwera, mwamuna, wovala zovala zakuda, ankawoneka akuzemberera kwambiri, akunyang'amiramotsatira kumbuyo kwa Iye, akufesa maudzu. Ndipo pamene izi zinachitika, ndiyeine ndinaona mbewu zonse zitatulukira. Ndipo pamene izo zinatulukira, zimodzizinali tirigu ndipo zinzakezo zinali maudzu. Ndipo apo panabwera chilala,mwakuti pamenepo, zinkaoneka monga, zonse za izo zinali ndi mitu yawo pansiziri kumangolirira mvula. Ndiye apo panadza mtambo waukulu pamwamba padzikolapansi, ndi iyo inavumba. Ndipo tirigu anawuka ndipo anati, “Ambuyealemekezeka! Ambuye alemekeze! Ndipo maudzu anawuka ndipo anafuula, ”Ambuye alemekezeke! Ambuye alemekezeke!“ Zotsatira zofanana. Zonse za izozikupsyerera, zonse za izo zikupita. Ndiyeno tirigu akuwuka ndipo akumva ludzu. Ndipo chifukwa izo zidali munda womwewo, dimba lomwelo, malo omwewo, pansipakutsanulira kufanana, apo panamera tirigu ndipo apo panamera namsongole mwachinthu chofanana chomwecho. Zindikirani, madzi omwewo odzozeraakumeretsa tirigu, akumeretsa udzu.

Mzimu Woyerawomwewo umene umadzoza Mpingo, umene umawapatsa iwo chikhumbo kuti azipulumutsamiyoyo, umene umawapatsa iwo mphamvu kuti azichita zozizwitsa, Iwo umagwera paosalungama mofanana monga olungama. Mzimu womwewomwewo! Tsopano, inusimungakhoze kuupanga iwo mwanjira ina iliyonse ndikumvetsetsa Mateyu 24:24. Iye anati, “Padzauka aKhristu onyenga,” iwo odzozedwa, mwabodzawo. Odzozedwandi Chinthu chenicheni, koma kukhala aneneri onyenga a Icho, aphunzitysi onyengaa Icho. Mchiani chimene chikanati chimupange munthu kufuna kuti akhalephunzitsi wa bodza wa china chake chimene chiri Choonadi? Tsopano ife tifika m'musikuchilemba chachilombo mumphindi pang'ono, ndipo inu mudzawona chipembedzochake. Mwaona? Aphunzitsi onyenga; onyenga, odzozedwa. AKhristu odzozedwa, komaAphunzitsi onyenga. Ndiyo njira yokha imene inu mungakhoze kuwonera izo.

-----
Zindikirani, koma ndi chimene iwo amabala chimene chimakuuza iwe kusiyana. “Ndi chipatsochawo,” Yesu anati, “Inu mudzawadziwa iwo.” “Munthu samasonkhanitsa mpesa kuchokerapa nthula,” ngakhale nthula zitakhala ziri m'munda wa mpesa womwe. Izozikanakhoza kukhala zotheka, koma chipatso chidzafotokoza izo. Chipatso ndi chiyani? Mawu, a chi... chipatso cha nyengoyo, Ndicho chimene icho chiri, kuphunzitsakwawo. Kuphunzitsa kwa chiyani? Kuphunzitsa kwa nyengoyo, nthawi imene iyo ili. Chiphunzitso cha munthu, chiphunzitso cha chipembedzo, koma, kapena Mawu aMulungu a nyengoyo?

Tsopano, nthawi ikuthamanga mwansanga kwambiri, kuti ife tikanapirira pa izo nthawiyayitali. Koma ine ndikutsimikiza kuti inu amene muli pano, ndipo inendikutsimikiza kuti inu mu fuko lonseli, mukhoza kuwona zimene ine ndikuyesakukuuzani inu, pakuti ife tiribe kutalikira kochuluka kwambiri kuti tikhale paizo.

Koma inumukhoza kuwona kuti kudzoza kumafika pa osalungama, aphunzitsi onyenga, ndikumawapangitsa iwo kuti achite chimodzimodzi zimene Mulungu anawauza iwo kutiasamachite; koma iwo adzazichita izo, mulimonse. Chifukwa chiyani? Iwosangakhoze kudziletsa izo. Nthula zingakhoze bwanji kukhala chinthu chinachirichonse koma nthula? Ziribe kanthu kaya ndi mvula yochuluka bwanji imeneyakonkhedwera pa izo, izo ziyenera kukhala nthula. Ndicho chifukwa Yesu anati, “Izo zidzakhala zoyandikana kwambiri izo zikanadzanyenga Osankhidwa omwe,” amene ali mizu, “ngati izo zikanakhala zotheka,” koma izo nzosatheka. Tirigusangakhoze kuchita kanthu koma kubala tirigu; ndizo zonse zimene iye angakhozekubala.

Werengani akaunti yonse mu...
Iwo odzozedwawo pa nthawi yotsiriza.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli m’manja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

Chivumbulutso 11:15


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Iwo odzozedwawo pa
nthawi yotsiriza.
(PDF)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

As the Eagle
Stireth her nest.

(PDF Chingerezi)

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.