Chisindikizo Chachisanu.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Mndandanda Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri.

Miyoyo pansi pa guwa.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachisanu.

Chivumbulutso 6:9-11,
9 Ndipo pamene iye anali atatsegula chisindikizo chachisanu, ine ndinawona pansi pa guwa miyoyo ya iwo amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene iwo anali nawo:
10 Ndipo iwo analira ndi liwu lokweza, kunena, Mpaka liti, 0 Ambuye, woyera ndi wowona, muchite inu. kuweruza ndi kubwezera magazi athu pa iwo amene akukhala pa dziko lapansi?
11 Ndipo miinjiro yoyera inapatsidwa kwa mmodzi aliyense wa iwo; ndipo kunanenedwa kwa iwo, kuti iwo abapumula apobe kwa kanthawi pang'ono, mpaka antchito amzawo nawonso abale awo, amene ayenera kuphwedwa monga iwo anali, kuti zikwaniritsidwe.

Tsopano, ichi chiri kani chachinsinsi. Ndipo tsopano chifukwa cha matepi, ndi amuna awubusa ndi aphunzitsi amene akhala ali pano, tsopano, ngati inu muli nako kuyang'ana kosiyana kwa lchi; ine ndinatero, nanenso. Koma ine ndikungotenga lzo kuchokera ku kudzoza, kumene mwathunthu kunasintha kuyang'ana kwanga kwa lcho. Ndiyeno ine ndikupeza kuti, pamene inu mukuwona izi zikuwululidwa, lzo zikubwerera mmbuyo ndi kubweretsa mibadwo ya mpingo iyo ndi Malemba palimodzi kumene, ndi kuzimangiriza lzo. Ndipo ndicho chifukwa chake ine ndikukhulupirira kuti lzo zikuchokera kwa Mulungu.

-----
Zindikirani, apo palibe kutchula kwa Chirombo china, kapena chamoyo-Cholengedwa chamoyo, ku kulengeza uku kwa Chisindikizo Chachisanu. Tsopano kumbukirani, chinalipo, pa Chisindikizo Chachinai. Chinalipo, pa Chisindikizo Choyamba, Chachiwiri, Chachitatu, ndi Chachinai, koma palibe apa. Mukuwona? Tsopano, ngati inu mungazindikire, tiyeni tingowerenga mmbuyo, chimodzi cha Zisindikizo. Tiyeni tibwerere ku Chisindikizo Chachinai, mwawona. Ndipo ndiyo ndime ya 7, “Ndipo pamene iye anali atatsegula chisindikizo chachinai, ine ndinamva liwu la chamoyo chachinai likunena, Bwera.... udzawone.” “pamene iye anatsegula chisindikizo chachitatu, ine ndinamva liwu la chamoyo chachitatu likuti, Bwera ndipo udzawone.” kapena “chamoyo chachiwiri Bwera udzawone.” Ndipo chamoyo choyamba kunena, “Bwera ndipo udzawone.”

Koma ndiye pamene ife tikufika ku Chisindikizo Chachisanu, apo palibe Chamoyo. Tsopano ingozindikirani. “Ndipo pamene iye anali atatsegula chisindikizo chachisanu, ine ndinawona pansi paguwa...” Mwamsanga kumene! 0nani, apo palibe-palibe Chamoyo pamenepo. Ndipo Chamoyo chimayimira mphamvu. lfe tikudziwa zimenezo, mwawona. Apo palibe Cholengedwa chamoyo. Tsopano, chimodzi cha Zamoyo zimenezo... ife tikuzipeza, mu kuwerenga kwa vumbulutso mu mipingo, kuti chimodzi cha izo chinali nawo.chinali mkango; ndipo chimodzi china-chimodzi china chinali ng'ombe; ndipo chimodzi china chinali munthu; ndipo chimodzi china chinali mphungu. lfe tikupeza, mu mibadwo ya mpingo, kuti Zamoyo zinai izo, kutanthawuza mphamvu zinai, zinasonkhana mozungulira Machitidwe a Atumwi, basi momwe uja-kachisi mu chipululu....

-----
Zindikirani. Koma, apa, pamene ife tikufika ku Chisindikizo Chachisanu ichi tsopano, apo pali-apo paliapo palibe wokwera amene akutulukira, ndipo apo palibe Chamoyo choti chirengeze lcho. Yohane basi... Mwanawankhosa anatsegula lcho, ndipo Yohane anachiwona lcho. Apo panalibe mmodzi aliyense pamenepo kuti anene, “Tsopano bwera, yang'ana. Bwera, udzawone.” Zindikirani, panalibe mphamvu ya Cholengedwa chamoyo. Kapena apo pali. Ndipo pa Chisindikizo Chachisanu ndi chimodzi, palibe Chamoyo choti chirengeze lcho. Ndipo pa Chisindikizo Chachisanu ndi chiwiri, palibe Chamoyo choti chirengeze lcho. Palibe mphamvu yoti irengeze lcho. Mwawona, palibe mmodzi amene akuchita izo. Pa.... penyani... Chitachitika Chisindikizo Chachinai, palibe kulengeza mwa mphamvu ili yonse ya Chamoyo, kuchokera pa Chisindikizo Chachisanu, Chachisanu ndi chimodzi, kapena Chisindikizo Chachisanu ndi chiwiri, palibe konse.

Tsopano zindikirani. (lne ndikuzikonda izi). Monga mu nthawi za wokwera wa akavalo anai, wokwera (mmodzi) wa akavalo anai osiyana, apo panali Chamoyo chimene chinkalengeza mphamvu. Nthawi iliyonse wokwera ankakwera kavalo wina ndi kubwera kudzakwera, Chamoyo chamtundu wina chinkatuluka ndi kulengeza icho, Ndicho chinsinsi chachikulu. Mwawona? lcho chiri chinsinsi. Chifukwa? Kulengeza chinsinsi.

Chifukwa chiyani palibe chimodzi apa pa Chisindikizo Chachisanu, kuti chirengeze lcho? Apa icho chiri, molingana nalo vumbulutso limene Ambuye Yesu anandipatsa ine lero, onani, kapena mmawa uwu, mmamawa. Ndicho, kuti, chinsinsi cha mibadwo ya mpingo chatsirizika kale, pa nthawi iyi. Chinsinsi cha wotsutsakhristu chawululidwa, pa nthawi iyi. Wotsutsakhristu anatenga kukwera kwake kotsiriza, ndipo ife tinamupeza iye pa kavalo wotumbululuka wake, wosakanizidwa ndi mitundu yake yambiri, ndipo akukwera njira yonse mpaka ku chitayiko. (lfe tizipeza izo pa Malipenga, ndi zina zotero, pamene ife tiphunzitse zimenezo. lne ndikanapita kwa izo tsopano, koma ife tichoka ku phunziro kachiwiri.)

-----
Tsopano, pakuti iwo, pa nthawi iyi, ngati inu mungazindikire, Chisindikizo Chachisanu ichi kukhala chikutsegulidwa, onani, Mpingo wapita. lyo siyingakhale chabe, miyoyo yapansi Mpingo woyambirira. Tsopano, tsopano, chonde, ngati inu munachitapo perekani tcheru kwa ichi tsopano, chifukwa ichi chiri chitsutsano chachikulu.chitsutsano, kotero ine ndikufuna inu mumvetsere mwatcheru kwenikweni tsopano. Ndipo inu muli nawo mapepala anu, ndi zinthu zoti mulembe nazo. Tsopano, ine ndikufuna kuti inu muzindikire.

Tsopano, iyi siyingakhale miyoyo iyo. Chifukwa, m-miyoyo ya olungama, ophedwa, ndipo anthu olungama, Mpingo, Mkwatibwi, watengedwera kale mmwamba, kotero iwo sakanakhala pansi pa guwa. lwo akanakhala mu Ulemerero, ndi Mkwatibwi. Tsopano yang'anani. Pakuti, iwo apita mu Mkwatulo, mu mutu wa 4 wa Chivumbulutso. lwo anatengedwera mmwamba. Tsopano, ndi ndani miyoyo imeneyi, ndiye? Ndicho chinthu chotsatira. lwo ndi ndani, ndiye, ngati iwo sali Mpingo woyambirira? Uyu ndi lsraeli amene ati adzapulumutsidwe monga fuko, onse awo amene anakonzedweratu. Ndiye lsraeli. Ndiye lsraeli, iye yekha. lnu mukuti, “O, dikirani miniti.” lnu mukuti, “lwo sangakhale....”

O, inde, iwo ali woti adzapulumutsidwe. Apa, tiyeni tichikhazikitse icho, miniti chabe. lne ndiri nawo Malemba anai kapena asanu. lne nditenga limodzi. Tiyeni titenge Aroma, miniti yokha, ndipo tipeze ngati iwo ali. Tiyeni titenge Bukhu la Aroma, ndipo tipite ku mutu wa 11 wa Aroma, ndipo ife tizipeza. Basi.Tiyeni tingowerenga pamenepo, ndiyeno ife tidzipezera tokha izo. Aroma, mutu wa 11, ndime ya 25 ndi ya 26. Tsopano mverani kwa Paulo apa. Ndipo Paulo anati, Ngati wina aliyense, ngakhale Mngelo, akalalikira uthenga wina uliwonse,“ (chiyani?) iye anali woti akhale wotembereredwa.” Yang'anani.
Pakuti ine sindikanafuna, abale, kuti inu mukhale osadziwa za chinsinsi (aha!), kuti mungadziyese anzeru mwa kudzinyenga kwanu (ndi zimenezotu); kuchita khungu mwa gawo kwachitika kwa Israeli, mpaka kukwaniritsika.... chidzalo cha Amitundu chitabweramo.

-----
Zindikirani. Tsopano ine ndikufuna inu muyang'ane izi mwatcheru kwenikweni. “lwo anapatsidwa miinjiro.” lwo anali alibe iyo. lwo anapatsidwa miinjiro, miinjiro yoyera, aliyense wa iwo. Tsopano, oyera tsopano ali nayo, alinawo kale; iwo akuwupeza iwo kuno. Koma, uko, lwo anapatsidwa miinjiro. Ndipo oyera anali nayo kale yawo, ndipo atapita kale. Mukuwona? Mukuwona? lwo anali osati. lwo, onani, iwo analibe mwayi, chifukwa iwo anachititsidwa khungu ndi Mulungu, Atate wawo yemwe; kotero kuti chisomo cha Mulungu chikanakhoza kukwaniritsidwa, kotero Mkwatibwi akanakhoza kutengedwa kuchokera mwa Amitundu. Nkulondola uko?

-----
Tsopano yang'anani. lwo anali, mu khungu lawo, anapha Mesiya wawo, ndipo tsopano iwo anali kukolola chifukwa cha zimenezo. lwo anazindikira icho. lwo anazindikira icho, izo zitapita kale. lwo anamuwona lye ndiye, pamene iwo anabwera patsogolo pa guwa la Mulungu. Koma tsopano chisomo cha Mulungu chiri kwa iwo.

Yang'anani. Tsopano, iwo sakanakhoza, mwanjira iliyonse, kukhala oyera, chifukwa iwo anavekedwa kale mwinjiro. Koma apa iwo ali tsopano, basi miyoyo pansi pa guwa, chifukwa cha Mawu a Mulungu, ndi umboni umene iwo anagwira,“ kuti akhale anthu a Mulungu, Ayuda. Koma tsopano, yang'anani, chisomo cha Mulungu chikubwera kwa iwo. Ndipo Yesu akuwapatsa iwo, mmodzi aliyense, mwinjiro woyera, (o, mai, yang'anani; kutsidya uko, utatha Mpingo kupita), chifukwa iwo anali omvera kwa cholinga chawo. Ndipo iwo anachititsidwa khungu, ndipo iwo sanadziwe icho. lwo sanadziwe icho. lwo anali kusewera chimodzimodzi gawo limene Mulungu anali atalikonza kuti iwo akasewere. Ndipo apa, apa, Yohane akuyang'ana uko ndipo akuwona miyoyo pansi pa guwa. Tsopano yang'anani, iye akuwona miyoyo imeneyo. Yang'anani chimene iye akuwatcha iwo. lwo akulira, “Ambuye, mpakana liti?” Yang'anani! “Kanthawi kotalika pang'ono chabe.” (Tiyeni titenge icho, pamene ife tikupita mmusi, mpaka kupyola mu lemba tsopano.)

lwo akuzindikira kuti iwo anali atamupha Mesiya wawo. Mukuwona? Ndipo iwo sanali kudziwa icho, koma ndiye iwo anazindikira. lwo anapeza-iwo anaphedwa, kubwezera, kuti alipirire izo, pamenepo kuchita cholakwika. Ndipo tsopano yang'anani chinthu chimene iwo amayenera kuchita! Mukuwona, iwo anali olakwa pakupha, kotero iwo anaphedwa. Mukuwona? lwo Anafuwula, “Magazi Ake akhale pa ife!” Mukuwona? Uko nkulondola. Ndipo iwo anachititsidwa khungu. Tsopano, ngati iwo akadapanda kuchititsidwa khungu; Mulungu anati, “Asiyeni iwo okha. lwo sali oyenera.” Koma pokhala kuti iwo anachititsidwa khungu ndi Mulungu, chisomo Chake chinafikira pansi kwa iwo. Ameni! Kulankhula za chisomo chodabwitsa! Ndi kumupatsa mmodzi aliyense wa iwo mwinjiro, chifukwa lsraeli yense adzapulumutsidwa, mmodzi aliyense ali nalo dzina lake lolembedwa. Uko nkulondola.

-----
Tsopano zindikirani Ayuda awa. lne ndiyenera kuchita ichi, polinga kuti ndikuloleni inu kuwona vumbulutso la Chisindikizo ichi; kuwona chimene ilo liri, miyoyo iyi pansi pa guwa, ndi omwe iwo ali. Tsopano zindikirani. Mu nthawi ya Daniele, tsopano, theka lachiwiri la sabata la makumi asanu ndi awiri. Tsopano kumbukirani, “Mesiya anali woti adulidwe mkati mwake.” Ndipo pakati. Chabwino, theka la zisanu ndi ziwiri ndi chiyani? Zitatu ndi theka. Khristu analalikira motalika chotani? Uko nkulondola. Tsopano, Koma pali zoyikidwirabe, kwa anthu, (chiyani?) zaka zitatu ndi theka zina.

Chabwino, mu nthawi iyi, chifukwa, onani, chimene chikuchitika, chiri, Mkwatibwi Wamitundu akusankhidwa mu mibadwo isanu ndi iwiri ya mpingo, ndipo akupita mmwamba. Ndipo pamene zikuchitika mwanjira iyo, Ayuda onse amene anaphedwa motsatira kumeneko chifukwa cha khungu, okhala pansi pa guwa, Mulungu akubwera ndipo akuti, “lnu mwawona chimene icho chinali? Tsopano ine ndikupatsani mmodzi aliyense wa inu mwinjiro.” lwo anati, “Mpakana liti, Ambuye? Kodi ife tikupita mkati tsopano?” Anati, “Ayi, ayi, ayi, ayi. Anthu amzanu, Ayuda, ayenera kuvutikabe pang'ono pokha. lwo ayenera kuphedwa monga inu munaphedwera. Chirombo chiyenera kuwapeza iwo pamene icho chikuswa pangano lake.”

-----
lne ndikungomverera mosayenera pang'ono, onani. Mwawona? Penyani, ngati ena akuganiza kuti.lne ndikufuna inu mumvetse izi tsopano, mwawona. Ngati ena akuganizabe kuti Malaki 4, kudzabwezeretsa“ anthu, chiri chinthu chomwecho iye akukachita kumusi uko kwa Ayuda, ndi kuganiza izo ziri zonse zofanana, ndiroleni ine ndiwongole icho kwa inu, miniti yokha. Mwawona, izo zikanakhala zosokoneza pang'ono. Chifukwa, kumbukirani, mu Malaki 4, akuti, “Kubwezera Chikhulupiriro cha atate... kapena ana kubwerera kwa atate.” Mwawona, “kubwerera kwa atate!”

Tsopano ndiroleni ine ndikuwonetseni inu kusiyana kwa utumiki wawo. Ngati iye abwera kudzabwezera Chikhulupiriro cha ana kubwerera kwa atate, iye akanadzamukana Khristu. lye akanadzabwerera ku lamulo. Kulondola uko? Atate ankasunga lamulo. lnu mwamvetsa izo? Zindikirani, pamene Elisha, pamene iye anabwera kudzakwaniritsa utumiki wake mu Malaki 4, onani, monga Malaki 4, Eliya anali mwa yekha Koma pamene iye akubwera kudzatumikira kwa Ayuda, a Chivumbulutso 11, iye ali naye Mose ndi iye. Kotero, apo palibe kusokonezeka, ayi konse. Mwamvetsa? Pamene Elisha akubwera, wa Malaki 4, iye ali mwa yekha. Eliya adzathamanga; (osati Eliya ndi Mose.) Eliya adzafika.

Koma kudzoza komweko, kumene, anati Eliya adzabwera kwa gawo lotsiriza la m'badwo wa mpingo, kudzabwezeretsa Chikhulupiriro cha ana kubwerera ku Chikhulupiriro chapachiyambi cha atate,“ Chikhulupiriro cha atumwi, chomwe inu mukuyenera kubwererako. Ndipo wotsutsa Khristu wawatulutsamo iwo onse. Kuti abwezeretsenso,” monga Malemba ena onse agwirizana pamodzi. Mwawona, iye akubwera mwa yekha. Mukuwona? Koma pamene iye akubwera kwa Mpingo, Baibulo.... kapena kubwera kwa zikwi zana limodzi makumi anayi ndi zinayi, Baibulo momveka likunena kuti onse iye.... Pali awiri a iwo, osati amodzi a iwo. Awiri a iwo.

Ndipo utumiki wake woyamba sukanawatenga Ayuda ndi kuwayika iwo mobwerera ku lamulo, akukhala iye... chifukwa iye akubwera, akulalikira Khristu kwa zikwi zana limodzi makumi anayi ndi zinayi, ameni, Apo lye ali, Mesiya uyo amene anadulidwa. Ameni! Ndi zimenezo, kotero musatenge izo mosokoneza. lzo siziri chisokonezo. Lemba si limanama, ayi konse Ulemerero! O, pamene ine ndinawoza kuwala kuja ndinangoti....

lne ndinati, “Zikomo lnu, Ambuye,” pamene ine ndinali kuyang'ana icho chikuchitika kunja uko. Ndinamuwona Eliya uyo akutulukira kumeneko kwa m'badwo woyamba uja, mwa yekha, ndipo iye anali mwa yekha. Ndiye pamene ine ndinamuwona iye akubwera kachiwiri, kutali cha kwinakwakenso, apo panali awiri a iwo kumeneko pamene izo zimachitika. Anati, “Ndi zimenezo. lzo, zikuchita icho, Ambuye. Ameni! lne ndachiwona icho tsopano!” Aleluya! Ndizo chimodzimodzi. Ngati ine ndikanapanda kutchula izo, izo zikanakhala zosokoneza pang'ono kwa winawake. Koma lye anandiwuza ine kuti ndinene izo, kotero ine ndinatero.

Zindikirani, amuna awa asungidwa amoyo ndi Mulungu, kuchokera ku utumiki wawo wapachiyambi, kwa ntchito ya mtsogolo; iwo anatumikira iyo mwabwino zedi. Mukuwona? Tangoganizani, mzimu uwo wa Eliya ukutumikira nthawi zisanu; Mose, kawiri. Chiyani? Kusungidwa amoyo kwa kupitiriza, ntchito ya mtsogolo. lwo sanali ngakhale mmodzi wa iwo wakufa tsopano; inu musakhulupirire zimenezo. lwo onse anawoneka, amoyo, akulankhula kwa Yesu pa Phiri la Chiwalitsiro. Koma, kumbukirani, iwo ayenera kufa.

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachisanu.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

N’chiyani tsopano? Chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sanachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa mtima.

Aroma 11:7


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

Phiri ndi chitsamba
mu chipale chofewa
mu China.

Chapter 13
- God is Light

(PDF Chingerezi)

Kale...

Pambuyo...

lwo anali,
mu khungu lawo,
anapha Mesiya wawo,
ndipo tsopano iwo
anali kukolola
chifukwa cha
zimenezo.



Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.