Chisindikizo Chachinai.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Mndandanda Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri.

Wokwera kavalo wotumbululuka.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachinai.

Tsopano, ine ndikuyesetsa mwakukhoza kwanga tsopano, ndipo pamene chinachake, mkati, pakati pathu, chikupanga njira Yake mopyola. Ndipo tsopano ife tiyesa, usiku uno, mwa chisomo cha Mulungu, kuti titenge Chisindikizo Chachinai ichi, ndi kuwona chimene Mzimu Woyera udzakhala nacho choti ulankhule kwa ife, mu lcho. Tsopano ine ndiwerenga Chivumbulutso, mutu wa 6, ndi kuyambira nayo ndime ya 7; ya ndi ya 8. Pali nthawizonse ndime ziwiri; yoyamba ili kulengeza, ndipo ndime yachiwiri ili chimene iye anawona.

Ndipo pamene iye anali atatsegula chisindikizo chachinai, ine ndinamva liwu la chachinai-chamoyo chachinai chikuti, Bwera ndipo udzawone.
Ndipo ine ndinapenya, ndipo tawonani kavalo wotumbululuka: ndipo dzina lake amene anakhala pa iye (amene anakhala) linali Imfa, ndipo Gehena anamutsatira iye. Ndipo mphamvu inapatsidwa kwa iwo pa ngodya zinai za dziko lapansi, kukapha nalo lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndipo ndi zirombo za dziko lapansi.

Tsopano, Ambuye atithandize ife tsopano kuti timvetse lzi. Ndi chinsinsi.

Tsopano, kuwoneratu pang'ono chabe, kuti tibwerere mmbuyo, monga ife tinachitira mibadwo ya mpingo, okwera awa ndi kumatula uku kwa zisindikizo izi. Tsopano, kotero ife tingozitenga izo mmalingaliro athu, kulankhula pang'ono mpaka ife titamverera kuti ndiyo nthawi yoyenera kulankhula. Tsopano, ife tazindikira tsopano, kuti, kumatula kwa isindikizo, ndilo bukhu losindikizidwa la Chiwombolo. Ndiyeno wukhu liri lokulungidwa ngati sikololo, monga momwe njira yakale inaliri. lyo siyinali buku la mtundu uwu; chifukwa ili langobweramo posachedwapa, mabuku a mtundu uwu, mu mapeto, o, ine ndikuganiza zaka zana ndi makumi asanu, kapena chinachake, mazana awiri. Ndiyeno iwo ankayikulungiza iyo, ndiye nkusiya mapeto osamanga. Monga ine ndinakuwuzirani inu momwe izo zinalikuchitikira, ndipo Malemba, poti muwapeze iwo, ndi mu Yeremiya, ndi ena otero. Ndiye otsatira ankakulungidwa pamwamba, ndiye mapeto ankawasiya osamanga, ndipo iwo monga chonchi. Ndipo chimodzi chirichonse chinali Chisindikizo. Ndipo ilo linali wukhu losindikizidwa-pasanu ndi pawiri, ndipo ilo linali bukhu losindikizidwa-pasanu ndi pawiri la Chiwombolo.

Ndipo, ndiye, panalibe mmodzi Kumwamba kapena mu dziko lapansi, kapena pansi pa dziko lapansi, anali woyenera kulitsegula llo kapena ngakhale kuyang'ana pa llo. Ndipo Yohane analira, chifukwa iye sanakhoze kupeza munthu aliyense. Chifukwa, ngati wukhu limenelo silinatengedwe kuchokera mdzanja la Mwini wapachiyambi.Kumene, llo linali litatayidwa ndi Adamu ndi Eva, ndipo linabwerera, atatha iwo kupinyolitsa mawufulu awo a Mawu, malonjezo, cholowa chawo. lwo, kumbukirani, iwo akulamulira dziko lapansi. lye anali- iye anali kamulungu kakang'ono, pakuti iye anali mwana wa Mulungu. Ndipo mwana wa Mulungu ali ka- ka- kamulungu kakang'ono. Tsopano, zimenezo siziri zosiyana kwa Lemba. lne ndikudziwa kuti izo zikumveka mwachirendo. Koma Yesu anati, “Ngati inu mukuwatcha iwo, amene Mawu a Mulungu anafikirako.” Ndipo Mawu a Mulungu amafikira kuti? “Ngati inu mumawatcha iwo, amene Mawu a Mulungu amafikirako, 'milungu,' inu munganditsutse lne bwanji pamene ine ndikuti lne ndine Mwana wa Mulungu?” Mukuwona?

-----
Tsopano, usiku watha ife tinali nako kutsegula kwa c-Chisindikizo Chachitatu. Choyamba chinali kavalo woyera, ndipo chotsatira chinali kavalo wofiira, ndiyeno kavalo wakuda. Ndipo ife tikupeza kuti okwera anali wokwera yemweyo, nthawi zonse; ndipo ameneyo anali wotsutsakhristu, kuyamba ndi kuyamba. lye analibe- analibe korona, koma iye analandira mmodzi kenako. Ndiyeno ife tikupeza kuti ndiye iye anapatsidwa lupanga, kuti achotse mtendere pa dziko lapansi, ndipo ife tikupeza kuti iye anachita izo. Ndiye iye analowa umo ndi miyambi ya kupereka, mpingo ndi ndalama, poyeza rupiya kugula ichi, ndi marupiya awiri kugula icho. Koma iye analetsedwa kukhudza Mafuta ndi vinyo, zomwe zinali pang'ono zomwe zinatsalira. Ndiyeno ife tinapereka, tinasiyira usiku watha, ndi kuwonetsera kwa zomwe Mafuta ndi vinyo zinali, ndi mphamvu yomwe lzo zinali nayo. Ndipo ife.lzo mwina zinamveka mwamwano pang'ono, koma ine.izo ziri chabe Chowonadi chimodzimodzi.

-----
Kumbukirani, ngati Chowonadi chawululidwa, Chowonadi nachonso chimatsimikiziridwa. Mulungu, mowirikiza, ziribe kanthu kaya munthuyo ali wophunzira bwanji, kaya akhala wanzeru bwanji mu malingaliro ake; ngati Mulungu sayikira kumbuyo zomwe iye akunena, pali chinachake cholakwika. Mwawona? Kulondola. Chifukwa, iwo ndi Mawu. Tsopano, pamene Mose anapita kumeneko pansi pa kudzoza kwa Mulungu, anati, Lolani ntchentche zibwere.“ Ntchentche zinabwera. Anati, Lolani achule abwere.” Achule anabwera. Penyani, bwanji ngati iye akanati, Lolani ntchentche zibwere,“ ndipo izo nkusabwera? Mukuwona, ndiye iye-iye sanalankhule Mawu a Ambuye, mukuwona; iye anangolankhula, iye analankhula mawu ake omwe.

lye mwina anaganizira kuti payenera kukhala ntchentche. Koma, apoapo sipanabwera ntchentche iliyonse, chifukwa Mulungu anali asanamuwuze iye choncho. Ndipo pamene Mulungu akuwuzani iwe chirichonse, ndi kuti, “lwe upite ukachite ichi, ndipo lne ndidzakhala nacho icho, pakuti awa ali Mawu Anga,” ndipo lye nkuchisonyeza icho mu waibulo, ndiye Mulungu amayima kuseri kwa icho. Ndipo ngati icho sichinalembedwe mu waibulo, Mulungu amayima kuseri kwa icho, chonchobe, ngati icho chiri Mawu a Mulungu. Mwawona.Ndiyeno ngati icho chiri kunja kwa ilo, icho chimawululidwa kwa aneneri. lfe tikuzindikira kuti zinsinsi zonse za Mulungu zimazindikiritsidwa kwa aneneri, ndipo iwo okha. Mwawona, Amosi 3:7.

-----
Tsopano, “pamene Mwana wa nkhosa anali atatsegula chisindikizo Chachinai...” Tiyeni tiyimire apo tsopano. Chisindikizo Chachinai, tsopano, Ndani anatsegula lcho? Mwanawankhosa. Kodi analipo wina aliyense woyenera? Palibe mmodzi aliyense akanakhoza kuchita izo. Ayi. Mwanawankhosa anatsegula Chisindikizo Chachinai. Ndipo c-Chirombo chachinai, Cholengedwa chamoyo chonga mphungu, chinati kwa Yohane, “bwera, udzawone chimene chinsinsi chachinai cha dongosolo la chiwombolo, chakhala chitabisika mu wukhu ili,” chifukwa Mwanawankhosa anali kutsegula llo. Mwa kulankhula kwina, ndicho chimene iye anali kunena. “Pali chinsinsi chachinai apa. lne ndakuwonetsa iwe, mu chophiphiritsa.” Tsopano, Yohane, ine sindikudziwa kaya iwe wamvetsa lzo, kapena ayi. Koma, iye analemba zomwe iye anawona, koma izo zinali chinsinsi. Kotero, iye analemba zimene iye anawona. Mwana wa nkhosa anali kumatula zisindikizo, ndipo Mulungu anali samawululebe lzo. lzo zinasiyidwira kwa tsiku lotsiriza. Mwawona.

Tsopano, ife tinali nazo zophiphiritsa, ndipo ife tatokosa pa izo, ndipo tachita bwino kwambiri nthawizina, mwawona. Koma ife tikudziwa lzo zakhala zikusunthirabe patsogolo. Koma tsopano, mu masiku otsiriza, ife tikhoza kuyang'ana mmbuyo ndi kuwona kumene lzo zakhala ziri. Ndipo izo ziyenera kuchitika, izo, pa mapeto a m'badwo wa mpingo, Mkwatulo usanachitike kumene. Momwe wina angawutengere Mpingo kupita ukupyola mu Chisawutso, ine sindikudziwa. Koma lwo upyoleranji mu Chisawutso, pamene lwo ulibe-ulibe tchimo? lne ndikutanthawuza.ine sindikutanthawuza mpingo; mpingo udzapyola mu Chisawutso. Koma ine ndikulankhula za Mkwatibwi. Mkwatibwi, ayi, lye alibe tchimo lomutsutsa lye, nkomwe. llo lachotsedwa kale ndi bulitchi, ndipo palibe ngakhale a... Palibe ngakhale fungo la ilo, ndipo palibe kanthu katsalira. lwo ali angwiro, pamaso pa Mulungu. Kotero Chisawutso chirichonse nchachiyani kuti chiwayeretse iwo? Koma enawo akuchita. Mpingo ukuchita kupyola mu Chisawutso, koma osati Mkwatibwi. Tsopano, tsopano ife tizitenga chabe izo mu zophiphiritsa za mtundu uliwonse tsopano. Mongampingo, Nowa, mtundu wonyamulidwira pamwamba, anapitirira mpaka mu tchimo. onani, tsopano, iwo anachita kupita pamwamba. Koma, Enoki anapita poyamba, uwo unali mtundu wa oyera amene akanadzapita mkati, ndipo isanafike nthawi ya Chisawutso.

-----
Tsopano zindikirani. Palibe wa okwera enawo, palibe wa akavalo enawo, kapena palibe nthawi yomwe wokwera uyu anakwerapo, iwo analibe; munthu ameneyo analibe dzina. Koma tsopano iye akutchedwa lmfa. llo silikutchulidwa. Mukuwona? lye akuwululidwa tsopano. Chimene iye ali ali imfa. Chabwino, momwe ife tingachedwere pa icho kwa ulaliki, ndi kuchipangitsa icho kumveka kwenikweni! Koma chirichonse chimene chiri anti, ndicho chotsutsa chenicheni, chiyenera kukhala imfa. Chifukwa, apo pali mitu iwiri yokha, ndiyo, Moyo ndi imfa. Ndipo izo zikutsimikizira kuti vumbulutso la Mzimu Woyera la izi, mu tsiku ili, liri Chowonadi chimodzimodzi. Wotsutsa, iye ali imfa. Chifukwa, Mawu, monga ife titawonere patsogolo apa, ali Moyo. Mukuwona. Ndipo munthu uyu akutchedwa lmfa.

-----
Tsopano yang'anani, yang'anani mu waibulo apa. llo linati dzina lake linali Gehena, ndipo.lne ndikutanthawuza dzina lake linali Imfa, ndipo gehena inamutsatira iye. Tsopano, gehena nthawizonse imatsatira imfa, mwachibadwa. Pamene munthu wachibadwa amwalira, gehena imamutsata iye; ndiwo manda, hade, mwawona, ndizo mwa chibadwa. Koma mwauzimu, ndiyo Nyanja ya Moto, mwawona, chabwino, kulowa mu kulekanitsidwa Mwamuyaya, kumene iwo akuwotchedwa. Ndipo Malaki 4 anati, osawasiyira iwo ngakhale chiputu kapena nthambi, kapena kanthu kalikonse. Ndiyo njira yomwe dziko liri nako kudziyeretsera ilo lokha apanso, kuti kukhale zakchikwi. Mukuwona.

-----
Zindikirani. Kodi izi zikubwera pati? Tsopano, ife tiri nawo chabe pafupi khumi ndi awiri, maminiti khumi ndi anai apa, ine ndikuganiza. onani kumene zonse izi zikubwera. Nchiyani icho? lzo zikubwerera mmbuyo kumene momwe izo zinachitira, ndipo zinayambira Kumwamba. lzo zikufika ku nkhondo ya nthawi yotsiriza. Chinthu choyamba, Kumwamba, chinali nkhondo. Lusifala anakankhidwa kunja, ndi kubwera ku dziko lapansi. Ndiye iye anawononga Edeni; ndiye iye wakhala akuwononga kuyambira pamenepo. Ndipo tsopano, kuchokera ku nkhondo ya Kumwamba, zikubwera ku nkhondo pa dziko lapansi; ndipo iyo ili yoti itsirizikire ku, pa dziko lapansi, pa nthawi yotsiriza, mu nkhondo yotchedwa Armagedoni. Tsopano, aliyense amadziwa zimenezo. Nkhondo inayambira Kumwamba, woyera, ndipo kotero iwo anamukankhira iye panja. Mikaeli ndi Angelo Ake anamugonjetsa iye, anathamangitsidwa. Ndipo pamene iwo anatero, anatsikira komwe ku Edeni, ndipo apa anayamba nkhondo pansi apa.

-----
Tsopano, nkhondo inayambira Kumwamba. lyo idzatsirizikira pa dziko lapansi, mwa mawonekedwe a Armagedoni. Tsopano tiyeni tiyang'ane ndipo tichiwone icho chikufutukuka. Ndipo mwinamwake ife tikhoza kuchifutukula icho. Ambuye atithandize ife pakali pano kuti tichite ichi tsopano. Penyani icho chikufutukuka.

Wokwera wachinsinsi, (yang'anani chimene iye akuchita tsopano;) anatsutsa,“ anakana kulapa ndi kuti abwererenso ku Mawu Amagazi apachiyambi. Mawu anakhala Magazi ndi thupi. Mukuwona? lye anakana kubwerera kwa lwo. Ali wotsutsakhristu! Mkwatibwi wa Mawu owona, ali wotsu... iye ali wotsutsa kwa Mkwatibwi wa Mawu owona. Akutenga mkwatibwi wakewake! lye akutsutsana naye Mkwatibwi woona uyu, nayenso. Ndipo iye akutenga mkwatibwi wakewake, ndi kumubweretsa iye kwa iye, mwa mawonekedwe a chipembedzo chotchedwa zikhulupiriro ndi miyambi. Mukuwona.

Ndipo tsopano, powona Mkwatibwi woyera, iye ali kutsutsana naye lye. Koma iye akupanga mkwatibwi wakewake, wotchedwa wotsutsakhristu, mwa kuphunzitsa kotsutsakhristu, kumene kuli kosagwirizana ndi Khristu. Mukuwona momwe iye aliri wothyathyalika? Ndipo tsopano, mmalo mokhala nawo umodzi wa chikondi, kulamulira, kupembedza pansi pa Magazi, iye ali nacho chipembedzo. Mmalo mokhala nawo Mawu, iye anatenga zikhulupiriro, miyambi, ndi zina zotero.

-----
Yang'anani... Kusonkhana, pa kavalo wawo wamitunduyosanganikirana. Ndipo, onani, iye ali kusonkhanitsa chinthu ichi pamodzi, chosanganikirana ndi zikhulupiriro, chipembedzo, ziphunzitso zopangidwa ndi anthu. Nkulondola uko? Ndithudi, mtundu wosanganikirana, mtundu wosanganikirana wa kavalo wotumbululuka, wakufa wa mdziko! Tsopano, uko nkulondola. Mitundu yosanganikirana ya kavalo wakufa, mawonekedwe a chidziko a kavalo wotumbululuka, o, mai, wopanda Magazi oyera a Mawu, konse!

Ndipo yang'anani. Kuchokera ngodya. Kuchokera ku ngodya zinai za dziko lapansi, iwo akuwasonkhanitsa iwo; kuwasonkhanitsira iwo ku Armagedoni,“ waibulo linatero. lne ndikuyesa kuganiza za Malemba, monga ine ndawalembera iwo pansi apa. lne sindikuwatchula iwo; koma chabe pamene iwo alembedwapo, kuwona chimene iwo ali. Kuwasonkhanitsa iwo pamodzi, ku tsiku lalikulu la nkhondo ya Ambuye Mulungu.

-----
Tsopano apa iwo ali, kudzilumikiza okha pamodzi, kubwera ku chiwonetsero icho, ku Armagedoni, ndi kukwera pa kavalo wamitundu-yosakanikirana; ndi kavalo mmodzi woyera, kavalo mmodzi wofiira, kavalo mmodzi wakuda. zitatu, zosiyana zandale-mphamvu zandale, mphamvu yauzimu, zolamuliridwa ndi mphamvu ya ziwanda, imene ili yotsutsakhristu. Kusakaniza zonsezo pamodzi, ndipo inu muli nacho chotumbululuka, chinthu chowoneka modwala chimene iye akukwerapo. Kulondola. Tsopano zindikirani. Yang'anani chimene iye akukwerapo, wamawonekedwe-otumbululuka uyu, kavalo wamtundu-wotuwa, wosakanizika ndi kuda, kufiira, ndi kuyera; kubwera ku nkhondo, kusonkhanitsa omumvera ake kuchokera ku fuko lirilonse pansi pa Kumwamba!

Kodi Daniele sanamasulire loto, ndi kuwona nsempha wa chitsulo uwo ukuyenderera kulowa mu ufumu uliwonse, wa Ioma? Apa iwo akubwera, akusonkhana. Tsopano khalani phee potseka, miniti chabe, ndipo mverani mwatcheru. lwo akusonkhana mmenemo tsopano kudzachita izo, kubweretsa omumvera ake kuchokera ku ngodya zinai za dziko lapansi; akukwera kavalo wotumbululuka, wodwala, wamitundu-itatu, wosanganikirana. Munthu yemweyo!

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachinai.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Ndinayang’ana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo m’dzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa.

Tsono mngelo wina anatuluka m’Nyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana”

Chivumbulutso 14:14-15


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

Kodi ichi ndi
chizindikiro cha
mapeto, Bwana?
(PDF)
Komwe mtambo
udawonekera.

Chapter 11
The Cloud

(PDF Chingerezi)

Kale...

Pambuyo...


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.