Chisindikizo Chachitatu.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Mndandanda Zisindikizo-Zisanu ndi ziwiri.

Wokwera kavalo wakuda.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachitatu.

O, Mulungu, tithandizeni ife! Ife tingoyimira apa. Koma, Mulungu tithandizeni ife kuti tipenye tsopano, pemphero langa, pamene ife tikubwera tsopano. Chifukwa, ine sindikufuna kukusungani inu mochedwa kwambiri. Mulungu tithandizeni ife kuti tipenye. Ine ndikukhulupirira mwinamwake, Mzimu pa ife, iwo ukanakhala pakali pano kuti Iye akanatithandiza ife kuwulula, kuchitsegula Chisindikizo ichi. Tiyeni tiwerenge. Pamene ife tikuwona chikhalidwe chimene mpingo ulimo, ife tikuwona pamene iwo wakhala uli, tinawona zimene iwo anachita, tinawona pamene iwo unkayenera kuti ufike, kuziwona izo apo, ndi kuwona zomwe iwo ankayenera kuti achite. Iwo anachita izo basi. Tsopano inu mukuwona pamene ife tiri? Inu muzichita kuweruzako. Ine sindingakhoze kuweruza. Ine ndiri nawo chabe udindo wobweretsa Mawu awa. Basi monga Iwo aperekedwera kwa ine, ine ndikhoza kuwapereka Iwo. Mpaka Iwo ataperekedwa kwa ine, ine sindingakhoze kuwapereka Iwo; palibe mmodzi aliyense angakhoze.

Ndipo pamene iye anatsegula chisindikizo chachitatu, ine ndinamva chamoyo chachitatu chikuti, Bwera ndipo udzawone. Ndipo ine ndinapenya, ndipo taonani kavalo wakuda; ndipo iye amene anakhala pa iye anali nayo miyeso iwiri mu dzanja lake. Ndipo ine ndinamva liwu pakati pa zamoyo zinai likuti, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; koma penya iwe usawononge mafuta ndi vinyo.

-----
Tsopano, yang'anani pamene ife tiri, usiku uno, m'badwo wa mpingo wina uja tsopano. Mwawona? Ife tikubwera mpaka ku m'badwo wa mpingo wachitatu tsopano. Mwawona? Chimodzimodzi basi pa m'badwo wa mpingo wachitatu, ziri basi chimodzimodzi monga kavalo wachitatu. Tsopano, m'badwo wa mpingo woyamba, iwo unali chiyani? Achinikolai anali nacho chiphunzitso, onani, chimodzi choyamba chokha. Chabwino. Ndiyeno, chinthu choyamba ife tikudziwa, chiphunzitso cha Chinikolai ichi, icho chikufika pololezedwa ndipo chinali cholondola, chinayamba kuchitapo kanthu. Ndipo iwo anamuveka korona munthu uyu. Ndiye, mzimu uwu, wotsutsakhristu, ukukhala mu thupi mwa munthu. Mwawona? Ndipo ife tikupeza, kenako, iye akukhala Mdierekezi mu thupi, nayenso; chiwanda chikuchoka, ndipo Mdierekezi akudzalowamo.

Ndipo monga momwe mpingo uwo uli wa mtundu umenewo, mpingo wotsutsakhristu, ukupambana; kotero ayenera Mkwatibwi kubwera motsatana nazo zinthu zosiyana: kupyola kulungamitsidwa, kuyeretsedwa, ubatizo wa Mzimu Woyera, ndi kumasuntha chopitirirabe, onani, basi monga choncho. Kokha, iwo atenga chitsitsimutso chawo poyamba, ndipo Mpingo ukutenga icho potsiriza. Zaka zawo zitatu zoyambirira.... masiteji atatu oyambirira a iwo amene anapyola m'badwo wa mdima; ndiye yachitatu, masiteji atatu, ukutuluka Mpingo; kuchokera ku kulungamitsidwa, kuyeretsedwa, ubatizo wa Mzimu Woyera, kukhala mwa thupi Mulungu kuwonetseredwa pakati pathu.

Apa iye akubwera mkati, monga wosutsakhristu, monga mneneri wabodza, ndiye chirombo, ndiye mu m'badwo wa mdima. Ndipo Mpingo ukubwera kuchokera mu m'badwo wa mdima uwo; kulungamitsidwa, kuyeretsedwa, ubatizo wa Mzimu Woyera, Mawu mu thupi, njirayo tsopano. Ndipo iye akupita mmusi. Aha. Inu mukuwona zimenezo? Iye akupita pansi. Mpingo ukupita mmwamba. Mwawona? Izo ziri basi mwangwiro monga izo zingakhalire. O, ndi zokongola. Ine ndikungozikonda izo.

Wokwera uyu ali mmodzi yemweyo, koma siteji yina ya utumiki wake. Siteji yoyamba, kavalo woyera, onani, iye anali mphunzitsi chabe, mphunzitsi chabe wotsutsakhristu. Iye anali kutsutsa Mawu a Mulungu. Ndipo tsopano inu mungakhale bwanji wotsutsakhristu? Aliyense amene akana kuti Mawu alionse a izi sali owona, ndi kuti akhale akuphunzitsidwa basi mofanana, ali wotsutsakhristu, chifukwa iwo akukana Mawu. Ndipo Iye ali Mawu.

-----
Tsopano, tsopano apa pali chinsinsi cha izi. Ndipo tsopano, Icho, pamene Icho chinawululidwa kwa ine molawirira mmawa uno, kuwala kwa tsiku kusanati. Ndiye ine ndinapita mwamsanga ku Lemba ndi kuyamba kuyang'ana, kuzifufuza izo. Apo izo zinali. zitatu za izo, mpaka apa, zakhala mwamtheradi, zikuwululidwa mwauzimu. Eya. Tsopano apa pali chinsinsi cha kavalo wakuda, malingana ndi chimene chinawululidwira kwa ine. Iye wayamba kumukwera iye mu nthawi ya mibadwo ya mdima. Ndicho chimene kavalo wakuda ankayimira, mibadwo yamdima, pakuti inali nthawi ya pakati pa usiku kwa okhulupirira owona amene anatsala. Yang'anani tsopano mu m'badwo wa mpingo umenewo, m'badwo wa mpingo wapakati uwo, m'badwo wa mpingo wamdima. Yang'anani momwe Iye akuti, “Iwe uli nazo mphamvu pang'ono zokha.” Iwo unali pakati pa usiku kwa iwo, kwa okhulupirira owona.

Tsopano yang'anani. Mwakuchitika chiyembekezo chonse chinali chitachotsedwa kwa Mpingo woona, pakuti munthu uyu ankalamulira zonse mpingo ndi dziko. Kodi iwo akachita chiyani? nani, Chikatolika chinali chitatenga malo, zonse mpingo ndi dziko. Ndipo onse, amene sanagwirizane nacho Chikatolika, ankaphedwa. Ndicho chifukwa chake iye anali pa kavalo wakuda. Ndipo yang'anani chinthu chakuda chimene iye anachita, onani, ndiye inu mukhoza kuwona. Ndipo inu basi. Ngati inu mukuyidziwa mbiriyakale yanu, iyang'aneni iyo, ndiye inu mudza. Chabwino, inu simudzasowa ngakhale kuyidziwa iyo, kuti mudziwe Ichi.

Tsopano yang'anani. Chiyembekezo chonse chinali chitapita. Ndiye kavalo wakuda wake. Tsopano, iye anakwera pa kavalo woyera wake, chenjerero. Ndiye iye anapatsidwa mphamvu; iye anatenga mtendere, anapha mamilioni. Ndicho chimene iye ankakachita pamene iye ankakwerabe mopyola. Ndipo iye akuchitabe icho. Mwawona? Tsopano, apa iye ali pa kavalo wakuda wake tsopano, akutulukira. M'badwo wa mdima, iyo inali nthawi imeneyo. Chabe pafupi nthawi mpingo utatha kukhazikika, ndi atakhala mu mphamvu, iwo anafafaniza china chirichonse. Ndi kupita kupyola, pafupi, mazana ndi mazana ndi mazana a chaka, ndi chimene muwerengi aliyense amadziwa ngati mibadwo ya mdima. Ndi angati amadziwa zimenezo? Ndithudi, mibadwo ya mdima. Apo pali kavalo wakuda wanu, kuyimira m'badwo wa mdima uja.

Tsopano, chiyembekezo chonse chitapita; popanda chiyembekezo konse. Chirichonse chinkawoneka chakuda, kwa okhulupirira aang'ono. Tsopano, ndicho chifukwa chake iwo ukutchedwa, kuyimiridwa, kavalo wakuda. Miyeso yake, kapena milingo yake, mu dzanja lake, inu mukuwona. Kuyitanira uko, “Muyezo wa tirigu wogula rupiya, ndi miyezo itatu ya barele yogula rupiya.” onani, makamaka, ameneyo ali, tirigu ndi barele ndi zakudya zathupi za moyo. Ndicho chimene buledi ndi chakudya chimapangidwa nazo. Koma, inu mukuwona, iye anali kulipiritsira izo. Chomwe icho chimatanthawuza, kuti, iye anali kulipiritsa omumvera ake kwa mtundu wa chiyembekezo cha moyo umene iye anali kutumiza kwa iwo, mwa kupanga. Iye anayamba mu nthawi yomweyo, ya kuwapanga iwo kulipirira mapemphero, kulipiritsira pemphero. Iwo akuchitabe zimenezo; manovena. Chifukwa, anali kuchita chiyani iye? Kulanda chuma cha mdziko. Mulingo, kumayezetsa, “Muyezo wa tirigu wogula rupiya; miyezo itatu ya barele yogula rupiya.” Wokwera pa kavalo wakuda, mukuwona, iye anali kupanga.kuwalanda omumvera ake ndalama zawo. Pamene, Baibulo likuneneratu kuti iye akugwirizira, pafupi, chuma cha mdziko. Monga ife tinanena usiku watha za Iussia, ndi zonse izo, iwo akutenga basi ndalama zonse ndi kungowalanda anthu chirichonse chimene iwo alinacho, chirichonse. Kotero, ndi zimenezotu.

-----
Zindikirani. Apa pali gawo labwino tsopano. Zindikirani, “onani kuti iwe usawononge ayi vinyo uyu ndi mafuta”. Pang'onong'ono chabe a Iwo anatsalira kumeneko. “Koma usati iwe uwakhudze Iwo” Tsopano, mafuta ali.amaphiphiritsira Mzimu, Mzimu Woyera. Ine ndikupatsani inu ndime pang'ono ngati inu mukufuna kutero. Pali Malemba awiri. Mu Levitiko 8:12, pamene Aroni, iye asanalowe mkati, ankayenera kudzozedwa ndi mafuta, inu mukudziwa. Ndipo mu Zakariya 4:12, za mafuta kubwera, akutsanuliridwa kupyola mmipope, ndipo anati, “Uwu ndi Mzimu Wanga, Mafuta.” Chinthu china, ngati inu mukufuna kuwona Mateyu 25, apo panali mkwatibwi wopusa (25:3), namwali wopusa analibe Mafuta, analibe Mzimu. Ndipo Mateyu 25:4, namwali wochenjera anali nawo Mafuta mu nyali yake, wodzazidwa-Mzimu. Mafuta amayimira Mzimu. Inu mwamvetsa zimenezo? Chabwino.

Tsopano, mafuta amayimira Mzimu. Ndipo vinyo amaphiphiritsira kukondoweza kwa vumbulutso. M'bale, ine ngati kuti ndi thamange pa malo onse. Ndikudabwa ine sindinawadzutse oyandikana nawo, pamene Ambuye anandiwonetsa ine zimenezo. Kukondoweza kwa vumbulutso. Mwawona. Mafuta ndi vinyo, mu Baibulo, zimagwirizana pamodzi, nthawizonse. Ine ndiri nayo milozo ndipo ndinayang'ana. Ulipo mndandanda wa iwo, kuyi monga-monga choncho, kumene vinyo ndi mafuta amapita limodzi, nthawi zonse. Mukuwona?

Pamene Chowonadi cha Mawu olonjezedwa a Mulungu chakhala chitawululidwa mowona kwa oyera Ake amene adzazidwa nawo Mafuta, iwo onse amakondowezedwa. Vinyo ali kukondoweza. Ulemerero! Ine ndikumverera iko pakali pano. Kukondowezedwa nacho chisangalalo, kufuwula! Mwawona? Ndipo, pamene Iko kutero, Iko kumakhala nako kuchita komweko pa iwo kumene-kumene vinyo amachita pa munthu wachibadwa. Chifukwa, pamene vumbulutso laperekedwa, la Chowonadi cha Mulungu, ndipo wokhulupirira wowona atadzazidwa nawo Mafuta, ndipo vumbulutso liri lowululidwa, kukondoweza kumakhala kwakukulu kwambiri mwakuti Ilo limamupanga iye kuchita mosakhala mwachizolowezi. Kulondola. Ulemerero! Onani, ndilo vuto ndi iwo tsopano. Ndiko kulondola, kukuwapangitsa iwo kuchita mosayenera.

-----
Pamene ine ndinawona kuti Mulungu analonjeza kuchita chinthu china chake mu tsiku ili, pamene Iye analonjeza kudzamatula zisindikizo izi mu tsiku lino lotsiriza!... Ndipo inu simukudziwa chisangalalo, ulemerero, pamene ine ndinamuwona Iye akuwulula izi, kuyima pamenepo ndi kuziwona izo zikuchitika! Ndi kudziwa kuti nditengera munthu aliyense, ku makani: Iye sananene konse chinthu chimodzi kwa ife koma chimene chinachitika njira yotero. Ndiyeno kuwona chisangalalo chimene chiri mu mtima mwanga, pamene ine ndikuwona lonjezo Lake la masiku awa otsiriza, monga Iye analonjeza kudzachita zimenezo. Ndipo apa ine ndikuziwona izo zikutsimikiziridwa ndi kupangidwa kulondola mwangwiro.

Inu mukandimva ine ndikunena, “Ine ndikumverera mwachipembedzo.” Ndilo liri vuto. Kukondoweza kwandifikapo kwambiri, moti ine pafupi kupita kukuduladula, inu mukudziwa. Kukondoweza, kuchokera ku vumbulutso. Chabwino. Iwo amakhala okondowezedwa kwambiri, pa-vumbulutso, kuti iwo anazindikiritsidwa, chabwino, lonjezo. Tsopano, o, mai! Apo panafalikira chisangalalo cha kukondoweza, mpaka anthu anati, “Iwo aledzera naye vinyo watsopano”, pamene Mulungu anawulula lonjezo Lake kwa iwo. Ndipo Iye sanangowulula kokha ilo, koma Iye anatsimikizira ilo. Ndicho chimene ine nthawizonse ndanena. “Munthu akhoza kunena chirichonse, eya, iye akhoza kukakamizidwa chabe kuti anene chirichonse; koma pamene Mulungu abwera mozungulira ndi kuchitsimikizira icho....”

Tsopano, Baibulo linati, “Ngati pali mmodzi pakati pa inu, yemwe amati ali wauzimu kapena mneneri, ngati iye anena zinthu izi ndipo izo nkusachitika, ndiye musati mupereke chidwi kwa iye. Musati mumuwope iye, konse. Musati mumuwope munthu ameneyo. Koma ngati iye anena icho ndipo icho nkudzachitika; ameneyo ndi Ine, inu mukuwona. Ine, ndiri mu icho. Icho chikutsimikizira chifukwa ndiri Ine.”

Werengani akaunti yonse mu...
Chisindikizo Chachitatu.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m’menemo zidzapsa.

Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu.

2 Petro 3:10-11


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet.

(PDF Chingerezi)

Lawi la Moto.
-Phewa.

Maluwa a moto.

 
 

Magaleta amoto.

Eliya anagwira-
mmwamba.

Lawi la Moto.
- Houston 1950

Kuwala pa mwala
wa piramidi.


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.