Kodi Melkizedeki uyu ndi ndani?

<< m'mbuyomu


  Chinsinsi cha Khristu mndandanda.

Kodi Melkizedeki uyu ndi ndani?


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Kodi Melkizedeki uyu ndi ndani?

Ahebri 7:1-3,
1 Pakuti Melkizedeki uyu, Mfumu ya Salemu, wa nsembe wa Mulungu wa kumwamba mwamba amene anakomana naye Abrahamu akubwerera Kuchokera kokapha mafumu, namudalitsa iye;
2 Kwa Iyenso Abrahamu anamupatsa gawo la khumi la zonse; poyamba pokhala mwakumasulira Mfumu ya chilungamo ndipo zitatha izo naponso Mfumu ya Salemu, amene ali, Mfumu ya Mtendere;
3 Wopanda Bambo wopanda Mayi, wopanda kholo. Ngakhale chiyambi cha masiku, kapena mathero a moyo; koma anapangidwa ngati Mwana wa Mulungu; akhala wansembe mopitiriza.

Taganizani za Munthu wamkulu uyu, wankulu chotani Munthu uyu ayenera kuti anali! Ndipo tsopano, funso ndi lakuti, “Ndi ndani, Munthu uyu?” Amaphunziro a za umulungu akhala nawo malingaliro osiyana siyana.Koma kuyambira chitsegulireni cha zisindikizo zisanu ndi ziwiri, Bukhu la chinsinsi limene lakhala la chinsinsi kwa ife.... Molingana ndi Cibvumbulutso 10:1 mpaka 7, zinsinsi zonse zimene zalembedwa mu bukhu ili, zimene zakhala zitabisika konse kupyola mu m'bado wa okonzanso, ziyenera kubweretsedwa poonekera ndi mngelo wa m'bado wa mpingo wotsiriza. Ndi angati akudziwa kutiizo ndi zolondola? Uko nkulondola ziyenera kubweretsedwa. Zinsinsi zonse za Bukhu la chinsinsizili zoti zidzaululidwa kwa mtumiki wa Lodikaya wa M'bado umenewo.

Poona kuti pali kutsutsana kochuluka za Munthu uyu ndi phunziro ili, inendikuganiza icho chikutikakamiza ife kulowa mu izo, kuti tipeze yemwe uyu ali. Tsopano, alipo masukulu angapo alingaliro pa Iye. Imodzi ya masukulu awa amati, “Iye ali nthano chabe. Iye sanali munthu kweni kweni”.Ndipo ena amanena, kuti, “Iwo unali unsembe, uwo unali unsembe wa Malkizedeki”. Ndiyo ili yodziwika kwambri, yomwe imagwira bwino kumbali iyo kuposa momwe iwo amachitira kwa ina, ndi chifukwa iwo amanena kuti uwo unali unsembe. Izo sizingakhonze kukhala zimenezo pakuti mu mutu wa 4 Iwo ukunena kuti iyeanali Munthu “Mwamuna”. Kotero, kuti iye akhale Munthu, Iye ayenera kukhala nawo umunthu, “Mwamuna”. Osati dongosolo; koma Munthu! Kotero Iye sanali chabe dongosolo la unsembe, ngakhalenso kuti Iye anali nthano. Iye anali Munthu.

Ndipo Munthuyo ali Wamuyaya. Ngati inu mungazindikire, “Iye analibe bambo. Iyeanalibe mayi. Iye analibe nthawi imene Iye anatherapo”. Ndipo yense yemwe Iyeanali akadali wa moyo usiku uno, chifukwa Baibulo linanena apa, kuti, “Iyeanalibe ngakhale bambo, kapena mayi, chiyambi cha masiku, kapena mathero amoyo. Kotero Iye anayenera kukhala Munthu Wamuyaya. Nkulondola uko? Munthu Wamuyaya kotero Iye akhonza kokha kukhala Munthu m'modzi, ndiye Mulungu, chifukwa Iye ali M'modzi yekhayo amene ali Wamuyaya-Mulungu!

Tsopano, mu Timoteyo woyamba 6:15 ndi 16, ngati inu mukufuna kuwerenga izo nthawi, ine ndikufuna kuti inu muwerenge izo. Tsopano chinthu chimene ine ndikulimbana nacho ndi chakuti, Iye anali Mulungu, chifukwa Iye ali Munthu yekhayo amene angakhonze kukhala wosafa. Ndipo tsopano, Mulungu kudzisintha Iye mwini mwa Munthu; ndicho chimene Iye anali, “wopanda Bambo, wopanda Mayi, wopanda chiyambi cha moyo, wopanda mathero a masiku”.

Tsopano ife tikupeza mu lemba kuti anthu ambiri amaphunzitsa kuti, “umunthu utatu mu Umulungu” kotero inu simungakhonze kukhala nawo umunthu ponda kukhala munthu. Zimatengera munthu kuti apange umunthu. Mtumiki wa Baptisti, masabata pang'ono apitawo, anabwera, ndipo ku nyumbayanga, ndipo anati,
“Ine ndikufuna ku dzakuongola iwe pa Umulungu nthawi ina pamene iwe ukhale nayo nthawi.” Anandiyitana ine, kani. Ine ndinati, “Ine ndiri nayo nthawi pakali pano, chifukwa ine ndikufuna kuwongoka, ndipo ife tinayika kumbali china chili chonse kuti tichite icho”. Ndipo iye anadza, iye anati, “M'bale Branham, inu mumaphunzitsa kuti pali Mulungu mmodzi chabe”. Ine ndnati, “Inde bwana” Iye anati, “chabwino”, iye anati, “Ine ndikukhiulupirira kuti pali Mulungu M'modzi, koma Mulungu m'modzi mwa anthu atatu”. Ine ndinati, “bwana bwerezaninso izo”. Iye anati, “Mulungu m'Modzi mwa anthu atatu”. Ine ndinati, “Inu munapita kusukulu yakuti?” Mukuona? Ndipo iye anandiuza ine ya- ya Baibulo koleji. “Ine ndinati, ndikhonza kukhulupirira izo. Iwe sungakhonze kukhala munthu wopanda kukhala umunthu. Ndipo ngati ndiwe munthu ndiwe umunthu umodzi kwa iwe mwini. Ndiwe padela, munthu mmodzi payekha”. Ndipo iye anati, “chabwino, a za umulungu sangakhonze ngakhale kufotokoza izo”. Ine ndinati, “zili mwa vumbulutso”. Ndipo iye anati, “Ine sindingakhonze kuvomereza vumbulutso”. Ine ndinati, “ndiye palibe njira yomwe Mulungu angafikire konse kwa inu,chifukwa, 'izo zina bisika ku maso a anzeru ndi aluntha ndi kuwululidwa kwa makanda, '[ kuwululidwa, vumbulutso,] 'kuwululidwa kwa makanda amene ati adzavomereze izo, kuphunzira'” Ndipo ine ndinati, “sipadzakhala njira yomwe Mulungu kuti afikire kwa inu; inu mukudzitsekereza nokha kwa Iye”.

Baibulo lonse liri vumbulutso la Mulungu. Mpingo wonse unamangidwa pa vumbulutso la Mulungu. Palibe njira ina yomudziwira Mulungu, kokha mwa vumbulutso; chiri chonse chili vumbulutso. Kotero, kula... Kusalandira vumbulutso,ndiye ndiwe wa za umulungu wozizira basi, ndipo palibe chiyembekezo kwa iwe.

Tsopano, tsopano, ife tikupeza kuti Munthu uyu “analibe Bambo, wopanda Mayi, wopanda chiyambi cha masiku kapena mathero amoyo”. Anali Mulungu - ‘en morphe’. Tsopano, dziko, mau ochokera mau a chi Griki amatanthauza, “kusintha”,ankagwiritsidwa ntchito. Kudzisintha iye mwini, en morphe, kuchokera kwa munthum'modzi ku.... Munthu m'modzi; mawu a chiGriki pamenepo, en morphe, amatanthauza... Iwo anatengedwa kuchokera kusewero la zisuzo, limene munthum'modzi akusintha chigoba chake, kuti zimupange iye khalidwe lina.

Monga mu -mu sukulu, posachedwa kumene, ine ndikukhulupirira Rebekah, asanatsirize kumene sukulu, iwo anali nalo limodzi la sewero la Shakespear. Ndipo mnyamata mmodzi amachita kusintha zovala zake nthawi zingapo, chifukwaiye ankasewera magawo awiri kapena atatu osiyana; koma munthu yemweyo. Iyeanatuluka, nthawi imodzi, iye anali mthakati; ndipo pamene iye anatuluka nthawiyotsatira, iye anali khalidwe lina. Ndipo tsopano mau a chi Griki, en morphe, amatanthauza kuti iye anasintha chigoba chake.

Ndipo ndicho chimene Mulungu anachita, ali Mulungu yemweyo nthawi zonse. Mulungu mawonekedwe a Atate, ali Mzimu, Lawi la Moto. Mulungu yemweyo anapangidwa nthupi nakhala pakati pathu, en morphe, anatulukira kotero kuti Iye akhoze kuwonedwa. Ndipo tsopano Mulungu yemweyo ali Mzimu Woyera. Atate, Mwana, Woyera... osati Mulungu atatu; maudindo atatu, machitidwe atatu a Mulungu m'modzi. Baibulo linati, “Pali Mulungu mmodzi”, osati atatu. Koma ndimomwemo iwo sangakhonze... inu simungankhonze kuwongola izi ndikukhala nawo a Mulungu atatu. Inu simungam'gulitse muyuda izo. Ine ndikuuzani izo. M'modzi yemwe amadziwabwino, iye amadziwa kuti pali Mulungu m'modzi yekha.

Zindikirani, monga osema, iye amabisala, ndi - chigoba pa iye. Ndicho chimene Mulungu wachita pa m'bado uno. Izo zabisika. Zinthu zonse izi zabisika ndipo zikuyenera kuwululidwa mu m'badwo uno. Tsopano, Baibulo limanena kuti izo zidzaululidwa mu nthawi za mtsogolo. Zilingati osema kusunga yake - chidutswa cha ntchito yake chonse chophimbidwa mpaka nthawi imene iye achotsa chigoba cha icho ndipo apo icho chili.

Ndipo chimene Baibulo lakhala liri. Iyo yakhala ntchito ya Mulungu imene yaphimbidwa. Ndipo izo zabisika chikhazikitsireni maziko a dziko, ndipo ndicho chinsinsi chofutukuka pa sanu ndi pawiri. Ndipo Mulungu analonjeza mutsiku ili, pa m'badwo wa mpingo wa Lodikaya uwu, kuti adzachotsa chigoba kwa chinthu chonsecho ndipo ife tikhonza kuchiona icho ndi chinthu chaulemelero bwanji! Mulungu, en morphe, anaphimbidwa mu Lawi la Moto. Mulungu, en morphe, mwa Munthu wotchedwa Yesu. Mulungu, en morphe, mu Mpingo Wake. Mulungu pa mwamba pathu, Mulungu nafe, Mulungu mwa ife, kuzichepetsa kwa Mulungu. Pamwamba apo, oyera, palibe m'modzi akanakhoza ku mukhudza Iye, Iye anakhala pa phiri ndipo ngakhale ngati chinyama chi kanakhudza phirilo, chikanafa.

Ndiyeno Mulungu anabwera pansi ndi kusintha hema Lake, ndipo anabwera pansi nakhala nafe, kukhala m'modzi wa ife. “Ndipo ife tinamugwira Iye”, Baibulo linatero. Timoteyo woyamba 3:16 “Popanda kutsutsana chinsinsi cha umulungu m'chachikulu, pakuti Mulungu ana wonetseredwa muthupi, anagwiridwa ndi manja”. Mulungu kudya nyama. Mulungu anamwa madzi. Mulungu anagona. Mulungu analira. Iye anali m'modzi wa ife. Mokongola, kuyimiridwa m'baibulo! Uyo anali Mulungu pa mwamba pathu, mulungu nafe, tsopano ndi Mulungu mwa ife Mzimu Woyera. Osati Munthu wachitatu Munthu yemweyo!

Mulungu anabwera pansi ndikukhala thupi ndipo anafa imfa, mwa Khristu, kotero Iye akakhonze kuyeretsa Mpingo, polinga kuti alowemwa iwo, kufuna chiyanjano. Mulungu amakonda chiyanjano. Ndicho chimene iye anamupangira munthu pa nthawi yoyamba, chinali chifukwa cha chiyanjano, Mulungu amakhala yekha, ndi a Kelubi.

Ndipo zindikirani tsopano iye anapanga munthu, ndipo munthu anagwa. Kotero iye anabwera pansi namuombola munthu, chifukwa Mulungu amakonda kupembedzedwa. Mawu omwewo akuti Mulungu amatanthauza “chinthu chopembedzedwa”. Ndipo ichi ndi chimene chimabwera pakati pathu, ngati Lawi la Moto, ngati china chake chimene chinasintha mitima yathu, ameneyo Ali Mulungu yemweyo amene anati “apo pakhale kuwala”, ndipo panali kuwala. Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zonse.

Tsopano, pachiyambi Mulungu ankakhala yekha, ndizokhumba Zake, monga ine ndina lankhulira m'mawa uno. Ndiwo malingaliro ake. Panalibe kanthu, Mulungu yekha basi, koma iye anali nawo malingaliro. Monga ngati womanga wamkulu akhoza kukhala pansi, m'maganizo ake, najambula zimene iye akuganiza ndizo iye akupita ku kamanga. Kulenga, tsopano, iye sanga khonze kulenga. Iye akhonza kutenga china chake chimene chalengedwa ndi kuchipanga icho mwa ma wonekedwe osiyana; chifukwa Mulungu ali njira yokhayo... M'modzi yekhayo amene akhoza kulenga. Koma iye amatenga m'maganizo mwake zimene iye atachite, ndipo iye ndiwo malingaliro ake, ndizo zokhumbazake. Tsopano ndilo lingaliro, ndiyeno amaliyankhula ilo, ndipo ndiwo Mawu ndiye. Ndipo liu liri... Lingaliro, pamene ilo lifotokozedwa liri mawu. Lingaliro lofotokozedwa liri mawu,koma ilo liyenera kukhala lingaliro koyamba. Kotero, ndilo zikhumbo za Mulungu; ndiye ilo limakhala lingaliro, kenaka liwu.

Zindikirani. Iwo amene ali nawo, usiku uno, moyo wa Muyaya, anali naye Iye ndi mwa Iye, mukuganiza kwake, pasakhale konse ngelo, nyenyezi, kelubi, kapena chiri chonse. Ndiwo Umuyaya. Ndipo ngati inu muli nawo moyo wa muyaya, inu nthawi zonse munalipo. Osati umunthu wanu apa, koma thunthundi mawonekedwe amene Mulungu wopanda malire...

Ndipo ngati iye sali wopanda malire, iye sali Mulungu. Mulungu ayenera kukhala wopanda malire. Ife tirinawo malire Iye ali wopanda malire. Ndipo iye anali wopezeka pali ponse, wodziwa zonse, ndi wamphamvu zonse. Ngati Iye sali, ndiye Iye sangakhale Mulungu. Amadziwa zinthu zonse, malo onse, chifukwa chakupezeka pali ponse kwache. Kudziwa zonse ku mamupangitsa iye kupezeka paliponse. Iye ali Munthu; iye sali ngati mphepo. Iye ali Munthu, Iye amakhala mu nyumba. Koma pokhala wodziwa zonse, kudziwa zinthu zonse, ku mamupangitsa iye wopezeka paliponse, chifukwa iye amadziwa chiri chonse chimene chikuchitika.

Sipangakhonze kukhala utitiri wophethira maso ake koma chimene Iye akudziwaicho. Ndipo iye anadziwa icho pasanakhale dziko, nthawi yochuluka chotani iyoiti idzaphetire maso ake, ndiponso kuchuluka kwa mafuta amene iyo inali nawo, dziko lisanakhalepo nkomwe. Uko ndiye kupanda malire. Ife sitingakhonze kumvetsa izo m'maganizo mwathu, koma amaneyo ndiye Mulungu. Mulungu, wopanda malire!

Werengani akaunti yonse mu...
Kodi Melkizedeki uyu ndi ndani?


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.

Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti,

“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”

Mateyu 1:21-23


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Madzi ochokera
m’thanthwe.

Kale...

Pambuyo...

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

Pearry Green personal
testimony.

(PDF Chingerezi)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

As the Eagle
Stireth her nest.

(PDF Chingerezi)

Chapter 14
- Sabino Canyon

(PDF Chingerezi)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.