Tsiku Lija pa Gologota.


  Mndandanda Chiwukitsiro.

M'mandamo mulibe.


William Branham.
 

Werengani akaunti yonse mu...
Tsiku Lija pa Gologota.

Luka 23:33,
Ndipo pamene iwo anafika ku malo, amene amatchedwa Gologota, kumeneko iwo anamupachika iye, ndi ochita zoipa, mmodzi ku dzanja lamanja, ndi winayo ku lamanzere.

Ndi limodzi la masiku ofunikira kwambiri a masiku onse amene Mulungu anayamba wawalola kuti atulukire pa dziko lapansi. Ndipo ngati ilo liri lofunikira chotero kwa mtundu wa anthu, Gologota, ine ndikuganiza ndi zabwino kwa ife kuti tibwerere mmbuyo ndi kukayesa, ndi kungowona chimene izo zikutanthauza kwa ife. Chifukwa, ine ndikutsimikiza, mu ora lakumapeto ili limene ife tiri kukhalamo, ife tikufunafuna kufunikira kulikonse kwa Mulungu kumene ife tingakhoze kukudziwa. Ndi zonse zomwe ife tingakhoze kuzipeza, ife tiri pano kuti tidzaphunzire za izo, kuti tiwone chimene chiri cha ife, ndi zomwe Mulungu watichitira ife, ndi kuwona zimene Iye analonjeza kuti adzatichitira ife. Ndipo ndicho chimene ife timabwerera ku tchalitchi.

Ndicho chifukwa mlaliki amalalikira. Ndicho chifukwa iye amawerenga ndi kusinkhasinkha mu Lemba, ndi kufunafuna kudzoza, ndi chifukwa iye ndi wantchito wa pagulu kwa anthu a Mulungu. Ndipo iye akuyesera kuti apeze chinachake chimene chimene Mulungu angati ayankhule kwa anthu Ake, chinachake chimene chingati chiwathandize iwo. Mwina, icho chingakhale, chikuwatsutsa iwo mu machimo awo, koma chingakhale thandizo kuti chiwakwezere mmwamba iwo, kuti iwo akhoze kusiya machimo awo ndiyeno nkuwukapo kuti aziwatumikira Ambuye. Ndipo atumiki ayenera kumazifunafuna zinthu izi.

Ngati tsiku ili, pokhala lofunikira kwambiri, limodzi la masiku aakulu kwambiri, tiyeni ife tiyang'ane pa zinthu zitatu zosiyana zomwe tsiku limenelo linatanthauza kwa ife. Ife tikanakhoza kutenga mahandiredi. Koma, mmawa uno, ine ndangosankha zinthu zitatu zosiyana, zofunikira zimene ife tikufuna kuti tiyang'anepo, kwa mphindi pang'ono zotsatira, zomwe Gologota anatanthauza kwa ife. Ndipo ine ndikupemphera kuti izi zimutsutse wochimwa aliyense yemwe alipo; kuti izo zimupangitse woyera aliyense kuti apite pa maondo ake; kuti izo zimupangitse munthu wodwala aliyense kukwezera chikhulupiriro chake kwa Mulungu, ndi kuchokapo, atachiritsidwa; wochimwa aliyense, atapulumutsidwa; wobwerera mmbuyo aliyense abwerere, ndi kudzichitira manyazi yekha; ndi woyera aliyense, asangalale, ndi kutenga magwiridwe atsopano ndi chiyembekezo chatsopano.

Chinthu chimodzi, chofunikira chachikulu chimene Gologota imatanthauza kwa ife ndi dziko, ndicho, iyo inakhazikitsa funso la tchimo, kamodzi kwa konse. Munthu anapezeka wochimwa ndi tchimo. Ndipo tchimo linali chilango chimene panalibe munthu akanakhoza kulipira. Chilangocho chinali chachikulu kwambiri mpaka panalibe aliyense yemwe akanakhoza kulipira chilangocho. Ine ndikukhulupirira moona kuti Mulungu anakonzeratu izo mwanjira imeneyo, kuti chilangocho chidzakhale chachikulu kwambiri mwakuti palibe munthu akanati adzakhoze kulipira icho, chotero Iye akanakhoza kuchita izo, Mwiniwake. Tsopano, chilango cha tchimo chinali imfa. Ndipo ife tonse tinali titabadwa mu tchimo, titawumbidwa mu kusaweruzika, kubwera ku dziko, kumayankhula zabodza. Chotero panalibe mmodzi wa ife yemwe anali woyenera, kapena, iwo sanakhoze kumupeza wina aliyense pa dziko lapansi yemwe anali woyenera.

Ndipo tchimo silinayambire pa dziko lapansi. Tchimo linayambira Kumwamba. Lusifara anali... Lusifara, Mdierekezi, anali cholengedwa choweruzidwa, chifukwa cha kusamvera kwake, iye asanagunde konse pa dziko lapansi. Tchimo linayambira Kumwamba, kumene Mulungu anawaika Angelo, ndi zina zotero, pa maziko omwewo amene Iye anaikapo anthu; nzeru, mtengo wa nzeru, mtengo wa Moyo ndi mtengo wa nzeru, pamene munthu akanakhoza kutenga kudzisankhira kwake. Ndipo pamene Lusifara anapatsidwa uyambiriro, kuti apange kusankha kwake, iye ankafuna chinachake chabwinoko kuposa chimene Mulungu anali nacho. Ndicho chinayambitsa vuto.

Ndipo panali chofunikira kwa tchimo. Chofunikiracho chinali imfa. Imfa inali chilango. Ndipo, ndizo kuti, ife tikanakhoza kupita mwa tsatanetsatane wamkulu wa izi, chifukwa ine sindiri kukhulupirira kuti iliponso kupatula imfa imodzi. Ulipo Moyo umodzi. Ine ndikukhulupirira kuti munthu yemwe ali nawo Moyo Wamuyaya sangakhoze konse kufa. Ndipo ine ndikukhulupirira kulipo kuthetsedwa kwathunthu kwa moyo uwo umene umachimwa, pakuti Baibulo limati, “Moyo umene umachimwa, iwo udzafa zedi.” Osati munthu; “moyo umene umachimwa.” Chotero, Satana ayenera ndithudi kufa, kuti awonongedwe kwathunthu. Momwe ine sindimagwirizanira ndi a universalist amene amanena kuti Satana adzapulumutsidwa! Iye anachimwa, ndipo iye ali woyambitsa wa tchimo. Ndipo moyo wake unachimwa; ndipo iye anali mzimu. Mzimu umenewo udzathetsedwa kwathunthu, kuti pasadzakhale kanthu kosiyidwa ka iwo.

Ndipo pamene tchimo linagunda pa dziko lapansi, mmbuyo pa chiyambi, monga mkwamba wa mdima ukugwa kuchokera mmiyamba, ilo linachititsa zanzi kumene dziko lapansi. Ilo linaponyera cholengedwa chirichonse, pa dziko lapansi, ndi chilengedwe chonse cha Mulungu, mu msinga. Munthu anali pansi pa msinga za imfa, matenda, mavuto, zisoni. Chilengedwe chonse chinagwa ndi ilo. Tchimo linali mankhwala omwe anachititsa zanzi kumene dziko lapansi. Ndiyeno ife tinakhazikidwa pano, opanda chiyembekezo, chifukwa cholengedwa chirichonse chinali chomvera kwa ilo. Ndipo aliyense wobadwa pa dziko lapansi anali womvera kwa ilo. Chotero, izo zinayenera kuchokera ku Malo ena ake kumene kunali kopanda tchimo. Izo sizikanakhoza kubwera kuchokera pa dziko lapansi.

Mmodzi wa ife sangakhoze kumuwombola wina. Izo zinkayenera kubwera kuchokera kwa Wina wake. Chotero, pamene munthu anazindikira kuti iye anali atalekanitsidwa kwa Mulungu wake, iye anakhala woyendayenda. Iwo ankalira. Iwo ankafuula. Iwo ankavutikira. Iwo ankayendayenda uku ndi uku, kudutsa mmapiri ndi kudutsa mzipululu, kufunafuna Mzinda womwe woumanga ndi woupanga wake anali Mulungu. Pakuti, iye ankadziwa kuti ngati iye akanangodzabwereranso mu Kukhalapo kwa Mulungu, iye akanakhoza kudzayankhulana izo nizitha ndi Iye. Koma panalibe njira yobwererera. Iye anakhala wotayika. Iye sanali kudziwa njira yoti abwererere, chotero iye anangowuyamba, woyendayenda, kuyesera kuti akapeze pena pake pamene iye akanakhoza kupeza njira yobwererera ku Malo amenewo. China chake mkati mwa iye chinkamuuza iye kuti iye anabwera kuchokera ku_ku Malo amene anali angwiro.

Palibe munthu muno mwa omvetsera owoneka awa, mmawa uno, kapena mwa omvetsera a pa tepi yamaginito, kumene iyo iti idzapite kuzungulira dziko, palibe mmodzi wina muno, kapena kulikonse, koma yemwe akufunafuna ungwiro umenewo. Inu mukalipira ngongole zanu, inu mumaganiza, “Kuti izo zikhazikitsa icho.” Pamene inu mwalipira ngongole zanu, ndiye pamakhala wina akudwala m'banja mwanu. Pamene matendawo akupeza bwino bwino, ndiye inu mumakhala ndi ngongole zina zoti mulipire. Chinthu choyamba inu mumadziwa, tsitsi lanu likusanduka la imvi, ndiyeno inu mumafuna mubwerere ku ubwana. Ndipo pamakhala chinachake nthawi zonse, mowirikiza, ndi chifukwa cha funde ilo la tchimo. Koma mu mtima wanu, chifukwa chakuti inu mukuchifunafuna icho, izo zikusonyeza kuti ulipo Ungwiro pena pake. Pena pake, pali china chake.

-----
Potsiriza, tsiku lina, ilo ndi tsiku lija pa Gologota, panali Mmodzi yemwe anabwera pansi kuchokera ku Ulemerero. Mmodzi, Dzina lake Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Yemwe anabwera kuchokera ku Ulemerero, ndipo Gologota inapangidwa. Ilo linali tsiku limene mtengo unalipidwa, ndipo funso la tchimo linakhazikitsidwa kwa nthawizonse. Ndipo anatsegula njira ya ku chinthu ichi chimene ife tiri kuchichitira njala ndi ludzu. Icho chinabweretsa malo a kukhutitsidwa.

Palibe munthu yemwe anayamba wakacheza pa Gologota, nakawona apo momwe izo zinaliri, yemwe angakhoze kukhala chimodzimodzibe. Chirichonse chimene iye anayamba wachikhumba kapena kuchiyembekezera, chimapezeka, pamene iye afika pa malo amenewo. Ilo linali tsiku lofunikira kwambiri, ndipo chinthu chofunikira chotero, ilo linagwedeza dziko. Ilo linagwedeza dziko, momwe ilo silinayambe lagwedezekerapo kale. Pamene Yesu anafa pa Gologota ndipo atalipira funso la tchimo.

Dziko lochimwitsitsa ili linachita mdima. Dzuwa linalowa pakati pa tsiku, linali ndi kulowerera kwa manjenje. Ndipo miyala inagwedezeka, mapiri anang'ambika, ndipo matupi akufa anatulukira kuchokera mmanda. Kodi ilo linachita chiani? Mulungu anazifikitsa pachimake, pa Gologota. Iye anachivulaza chinyama chija, chotchedwa Satana, kwa nthawizonse.

Tsopano iye wakhala ali waukali kwambiri kuyambira apo, chifukwa izo zinabweretsa Kuwala kwa mtundu wa anthu. Ndipo aliyense amadziwa kuti chinyama chovulazidwa ndicho choononga kwambiri, chikukwawa chozungulira ndi nsana wake utathyoka. Tsopano, Satana anagwetsedwa, pa Gologota. Dziko lapansi linatsimikizira kuti zinali choncho. Mtengo waukulu kwambiri umene unayamba waperekedwapo, ndipo Mmodzi yekha yemwe akanakhoza kuulipira iwo, anabwera ndipo anadzachita izo pa Gologota. Ndi pamene mtengo waukulu unaperekedwa. Ndicho chimodzi cha zinthu.

Mulungu anali akuchifuna icho. Panalibe munthu yemwe anali woyenera. Panalibe munthu anali wokhoza. Panalibe munthu akanakhoza kuchichita icho. Ndipo Mulungu anabwera, Mwiniwake, ndipo anadzapangidwa umunthu, anadzakhala moyo wa umunthu, pansi pa zikhumbo zaumunthu, ndipo anapachikidwa pa Gologota. Ndipo pamenepo, pamene Satana ankaganiza kuti Iye sakanakhoza kuzichita izo, Iye sakanakhoza kupita napyola mu izo, Iye anapita nadutsa mu Getsemane ndipo yesero lirilonse limene munthu aliyense anayamba wayima nalo. Iye anapita napyola mu ilo basi monga munthu aliyense, koma Iye analipira mtengo wake. Ndipo ndicho chimene chinadetsa dziko lapansi.

Chinali monga mankhwala okomoletsa kwa opareshoni. Pamene adokotala amupatsa munthu mankhwala omukomoletsa, iye amayamba wamukomola, iye asanati achite izo. Ndipo pamene Mulungu anapereka opareshoni kwa Mpingo, dziko linkalandira mankhwala okomoletsa, chilengedwe chinali ndi kuphupha. Palibe zodabwitsa! Mulungu, mu mnofu waumunthu, anali akufa. Ilo linali ora limene dziko linali litaliyembekezera, komabe ambiri a iwo sanali kudziwa izo. Monga izo ziriri lero, ambiri akuzifunafuna zinthu izi, ndipo komabe iwo sali kuzizindikira izo. Iwo sakuizindikira njira yotulukiramo. Iwo akadalibe kufunafuna zosangalatsa ndi zinthu za mdziko, kuyesera kuti apeze njira yawo yotulukiramo.

Pakhala pali, zikwangwani zambiri zimene zinkalozera ku tsiku limenelo, mithunzi yotsogolera yaikulu yambiri. Imene inali itachita mthunzi motsogolera ndi mwanawankhosa, ndi mwana wa ng'ombe, ndi nkhunda, ndi zinthu zonse izi, komabe izo sizikanakhoza kumasula izo. Izo sizikanakhoza kumasula kugwira kwa imfa uko, pakuti Satana anali nalo dziko lapansi. Miyala yomwe imene iye anayamba wayendapo, chokwera ndi chotsika pa dziko lapansi, ikuyaka moto wa surfule! Lusifara anali mwana wa mmawa, ndipo iye ankayenda pa dziko lapansi pamene ilo linali chiphala chamoto choyaka. Miyala yomweyo yomwe inali itazizira, pamene Yesu anafa pa Kalvare, inageya utsi kuchokera pa dziko lapansi. Mtengo umene unalipiridwa, ndipo ukapolo wa Satana unathyoledwa.

Mulungu anaiyikanso mu manja a munthu, njira yobwererera ku chimene iye anali akuchiyembekezera. Iye samayenera kuti aziliranso. Anamenya, pamene Iye anathyola nsana wa Satana, apo pa Gologota, fupa la nsana wa tchimo, wa matenda! Ndipo izo zikubweretsa chinthu chachivundi chirichonse, pa dziko lapansi, kubwerera mu Kukhalapo kwa Mulungu, ndi machimo atakhululukidwa. Aleluya! Machimo athu akhululukidwa. Palibenso zakuti Satana azitichititsa chidima ife kwa Mulungu. Pali msewu waukulu wapangidwa. Ilipo telefoni yaikidwa apo. Chiripo chingwe cha ku Ulemerero, zikumubweretsa munthu aliyense pa kufikira mzere umenewo. Ngati munthu ali wodzaza ndi tchimo, izo zinamulumikiza iye pa likulu. Iye akhoza kukhululukidwa tchimo limenelo. Osati izo kokha, koma tchimo limenelo lalipiridwa. O! Inu simukusowa kumati, “Sindine woyenera.” Zedi, inu simuli, inu simukanakhoza kukhala muli konse. Koma Mmodzi woyenerayo anatenga malo anu. Ndinu mfulu. Inu simukusowa kuti muziyendayenda panonso. Inu simukusowa kuti mukhale munthu wofunafuna zosangalatsa kunja kuno pa dziko lapansi.

Pakuti pali kasupe wodzazidwa ndi Magazi,
Otengedwa kuchokera mu mitsempha ya Emanuele,
Momwe ochimwa amadziponyera pansi pa kusefukirako,
Amataya mabanga a zolakwa zawo zonse.

Inu simukusowa kuti mukhale otayika. Ulipo msewuwaukulu, ndi Njira, ndipo iyo imatchedwa Njira ya chiyero. Wosayera samadutsa pa iyo. Pakuti, iye amabwera ku kasupe, poyamba, ndiyeno iye amadzalowa mu msewu waukulu.

Iye anaswa mphamvu za Satana. Iye anatsegula zitseko za ndende ya gehena, kwa munthu aliyense yemwe anatsekeredwa, mu dziko lapansi lino, mu ndende, kuwopa kuti pamene iye afa, chimene imfa ikanati ikhale kwa iye. Pa Gologota, Iye anatsegula zitseko za ndende izo, analola wamsinga aliyense kuti apite waufulu. Inu simukusowa kuti panonso muzing'ambidwa ng'ambidwa ndi tchimo. Inu simukusowa panonso kuti muzipereka ziwalo zanu kwa tchimo, kumwa, kusuta, njuga, kunena zabodza.

Inu mukhoza kukhala owonamtima, olungama, ndi owongoka. Ndipo Satana sangakhoze kuchita kanthu nazo, chifukwa inu mwachigwira chingwecho, chingwe cha Moyo ndi chozikika mu Thanthwe la Mibadwo. Palibe kanthu kangakhoze kukugwedezani inu kwa Ilo. Palibe mphepo zingakhoze kukugwedezani inu kwa Ilo. Palibe kanthu, osati ngakhale imfa iyoyomwe, kuti ingakhoze kukulekanitsani inu kwa chikondi cha Mulungu chimene chiri mwa Khristu Yesu.

Ndicho chimene Gologota inatanthauza. Amuna omwe anali mu msinga anamasulidwa. Amuna omwe nthawi ina anali pansi pa mantha a imfa sangakhoze panonso kuiwopa imfa. Munthu yemwe amafunafuna Mzinda, umene woumanga wake ndi woupanga, ndi Mulungu, iye akhoza kumayenda pa msewuwaukulu, ndi kuyang'anitsa nkhope yake choloza Kumwamba, chifukwa iye ali mfulu. Aleluya! Iye ndi woomboledwa. Iye sakusowa kuti aziyendayenda panonso, pakuti ilipo njira yodziwira ngati iwe ukulondola kapena ayi. Mulungu amatipatsa ife Moyo. Machimo athu apita. Tsiku lija pa Gologota linalipira mtengo wake.

-----
Choyamba, ife tiyenera kufunafuna chimene tsiku limenelo linatanthauza. Chachiwiri, ife tiyenera kuwona chimene tsiku limenelo latichitira ife, tsopano, chimene ilo linatichitira ife. Tsopano, chachitatu, tiyeni tiyang'ane pa chimene ife tiyenera kuti tizichita kwa tsiku limenelo. Kodi ife tiyenera kuti tizichita chiyani? Choyamba, ife tiyenera kumayang'ana kwa ilo, pakuti ilo ndi tsiku lalikulu, lalikulu kwambiri la masiku onse. Mtengo wa tchimo unakwaniritsidwa. Mphamvu ya Satana inathyoledwa. Ndipo tsopano ife tikufuna kuti tiwone chimene ife tiyenera kumachita pobwezera.

Tsopano, pobwezera, pamene Yesu anafa pa Gologota, pa Gologota tsiku lija, Iye sikuti anangopereka mtengo wa machimo athu, koma Iye aponso analipira mtengo ndipo anakonza njira kuti ife tizikhoza kumamutsatira Iye; pakuti ife, monga ma Adamu okugwa amene awomboledwa. Monga Mzimu unkamutsogolera Adamu (Adamu woyamba) mwa Mzimu, womwe unali nawo ulamuliro pa chirengedwe chonse, ndiye ife (Adamu wachiwiri), kapena anthu a padziko lapansi amene aomboledwa ndi Khristu, kuyambira pa tsiku la Gologota, tikhoza kumutsatira Iye.

Werengani akaunti yonse mu...
Tsiku Lija pa Gologota.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

N’chifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

2 Akorinto 5:17


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Chapter 9
- The Third Pull

(PDF Chingerezi)

Kale...

Pambuyo...

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)

“Sindine woyenera.”
Zedi, inu simuli,
inu simukanakhoza
kukhala muli konse.
Koma Mmodzi
woyenerayo anatenga
malo anu.



Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.