Masomphenya mu Gehena.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Wamoyo Mawu mndandanda.

Miyoyo yomwe ili mu ndende tsopano.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Miyoyo yomwe ili mu ndende tsopano.

Ndiyeno ine ndinali kunja kokasaka nthawi yina, chomwe chimawoneka kuti chiri chikhalidwe chachiwiri kwa ine, kukonda kusaka. Ndipo ine ndinali kunja kokasaka ndi mnyamata, Jim Poole, mwana wokondeka. Ine ndikuganiza mnyamata wake amabwera ku tchalitchi kuno, Jim wamng'ono, ndi banja labwino la anthu. Ine ndikuwadziwa a Pooles. Jimmy ndi ine tinkagona limodzi ndi kumakhala limodzi kuyambira pamene ife tinali anyamata aang'ono mu sukulu. Ndife osiyana pafupi miyezi isanu ndi umodzi, mu usinkhu. Ndipo Jimmy analola mfuti yake iwombere, ndipo iyo inandiwombera ine kupyola mu miyendo yonse, pafupi kwenikweni ndi ine, ndi mfuti yayifupi. Ine ndinatengedwera ku chipatala, ndipo, kumeneko, nditagona pamenepo ndikufa, kopanda penicilini kapena kalikonse mu masiku amenewo. Ndipo, tsopano, iwo anali ndi mkwamba wa rabara pansi pa ine, ndipo ine ndikudziwa usiku umenewo... Iwo ankati andichite opareshoni mmawa wotsatira. Iwo anangonditenga ndipo ananditsuka pa balalo, ndipo zidutswa zazikulu za mnofu zitawomberedwa, ndipo iwo anatenga sizesi ndi kuyidula iyo, ndipo ine ndinachita kuwagwira manja a bamboyo. Ndipo iwo anachita kundigwira, kuti awachotse manja anga kuchokera pa mikono yake, pamene_pamene iwo anatsiriza. Ine ndinkakuwa ndi kulira, ndipo nditagwirira monga choncho, ndipo iwo akucheka gawo ilo la mwendo kulichotsapo. Ine ndinali usinkhu wa zaka khumi ndi zinayi, mnyamata chabe.

Ndipo usiku umenewo ine ndinkayesa kuti ndigone, ndipo iwo... ine ndinawuka, chinachake chinawaza. Ndipo apa panali magazi, pafupi theka la galoni, ine ndikuganiza, anali atabwera kuchokera mu misempha imeneyo. Ndipo iwo anali... iwo anajambula ekisire, ndipo iwo anati kuwomberako kunali kuli pafupi kwambiri ndi msempha umenewo, ku mbali zonse, kuti kukanda kwa pang'ono kokha kukanaudula iwo pawiri, ndipo ine ndikanayamba kuwukha magazi. “Chabwino,” ine ndinaganiza, “awa ndi mathero a ine.” Ndipo ine ndinayika manja anga pansi monga chonchi ndi kuyidzutsira iyo mmwamba, ndipo magazi anathamangira pansi mmanja anga, iwo anali magazi anga omwe ine ndinali kugonamo. Ine ndinayitana, ndinaliza belu. Namwino anabwera, ndipo iye anangonyika awo mu mpango chifukwa panalibe kanthu kamene iwo akanakhoza kuchita.

Ndipo mmawa wotsatira, pansi pa zikhalidwe zofooketsa izo, iwo sankapereka magazi mu masiku amenewo, inu mukudziwa, kotero iwo anandichita opareshoni ine. Ndipo iwo anandipatsa ine ifara. Ndipo pamene ine... Ifara wakaleyo, ine ndikuganiza inu mukukumbukira, ndiko kukomola kwachikale. Ndipo pansi pa ifara ameneyo, pamene ine ndinasisimukapo, ine ndinali kusisimuka kuchokera mu ifarayo atatha maora asanu ndi atatu. Iwo anachita kundipatsa ine wochuluka chotero, iwo ankaganiza kuti ine sindikanakhoza... ine sindisisimukapo. Iwo sakanakhoza kundisisimutsa ine.

-----
Pamene ine ndinasisimuka kuchokera pansi pa ifara ameneyo, panali chinachake chimene chinachitika kwa ine pamenepo. Ine nthawizonse ndachikhulupirira icho kuti ndi masomphenya. Chifukwa, ine ndinali wofooka kwambiri, ndipo ine^Iwo ankaganiza kuti ine ndinali kufa. Iye anali akulira. Pamene ine ndinatsegula maso anga kuti ndipenye, ine ndinkakhoza kumumva iye akuyankhula, ndiyeno ine ndinabwereranso kukagona, ndipo ndinawuka, nthawi ziwiri kapena zitatu. Ndiyeno ine ndinali ndi masomphenya pamenepo. Ndiyeno ine ndinali....

Pafupi miyezi isanu ndi iwiri kenako, ine ndinkayenera kuti ndipite ndi kukachotsedwa thonje la mfuti ndi zovala zamafuta zaposaka pa miyendo yanga; adokotala sanazipeze izo. Ndipo kotero ine ndinali ndi chiphe cha mmagazi, miyendo yonse inali itatupa kukula pawiri mmbuyo pansi pa ine, ndipo iwo ankafuna azichotse izo pa miyendo yonseyo pa ntchafu zanga. Ndipo ine basi... ine ndinati, “Ayi, ingobwerani mmwamba ndi kuzidulira izo apa.” Ine sindikanakhoza basi kupirira zimenezo, mukuona. Ndipo kotero potsiriza, Dokotala Reeder ndi Dokotala Pirtle, ochokera ku Louisville, anachita opareshoniyo, ndipo anazidula mmenemo ndi kuzichotsamo izo; ndipo lero ine ndiri ndi miyendo yodabwitsa, mwa chisomo cha Mulungu.

-----
Tsopano mu nthawi iyi, pamene ine ndinali ndi masomphenya awa, ndi kumaganiza kuti ine ndinali nditadutsa kuchoka ku moyo uno kumka mu kuzunzika. Ndipo miyezi isanu ndi iwiri kenako, kuno ku Chipatala cha Clark County Memorial, ine ndinali ndi opareshoni yachiwiri. Ndipo pa nthawi imeneyo, pamene ine ndinasisimuka, ine ndinkaganiza kuti ine ndinali kuyima kunja Kumadzulo. Ine ndinali ndi masomphenya ena. Ndipo panali mtanda wawukulu wagolide mu milengalenga, ndipo Ulemerero wa Ambuye ukuyenderera kuchokera pa mtanda umenewo. Ndipo ine ndinayima ndi manja anga otambasula monga chonchi, ndipo Ulemerero umenewo unali kugwera mu chifuwa changa. Ndipo ine... Masomphenyawo anandichokera ine. Bambo anga anali atakhala pamene akuyang'ana pa ine, pamene masomphenyawo ankabwera.

Ine nthawizonse ndamverera, inu... Anthu onse omwe andidziwa ine zaka zonse izi, akudziwa kuti ine nthawizonse ndafuna kuti ndipite Kumadzulo. Inu mukudziwa momwe izo ziriri. Icho chakhala nthawizonse chinachake cha Kumadzulo. Koma chifukwa mkasidi anandiuza ine nthawi yina, chinthu chomwecho, kuti ine ndiyenera kupita kumadzulo... Nyenyezi, pamene izo ziwoloka mikombero yawo ndi zina zotero, ine ndinabadwa pansi pa chizindikiro chimenecho, ndipo ine sindikanadzakhala wopambana konse Kummawa; ine ndikanayenera kuti ndipite Kumadzulo. Ndipo chaka chatha ine ndinauyamba, wa Kumadzulo, kuti ndikakwaniritse chomwe chikhumbo cha moyo wonse chakhala chiri, mwaona, kuti ndichite icho.

-----
Masomphenyawo atatha kundikhudza ine, ndipo ine ndinali wofooka kwambiri, ndipo ine ndinali nditataya magazi onse amenewo, ndipo ndinapita... ine ndinkaganiza ine ndinali ndikumira mu Umuyaya wopanda mathero. Ambiri a inu mwandimva ine ndikunena izi kalepo, ndipo ndikumira mu Umuyaya wopanda mathero. Choyamba, ine ndinali kupyola zokhala ngati mitambo, ndipo kenako kupyola mu mdima, ndi kumamira mopitirira mpaka pansi, pansi, pansi. Ndipo chinthu choyamba inu mukudziwa, ine ndinakafika mu zigawo za otayika, ndipo mkati mmenemo ine ndinakuwa. Ndipo ine ndinayang'ana, ndipo apo, basi chirichonse, panalibe maziko kwa icho. Ine sindikanakhoza konse kusiya kugwa. Kwa Umuyaya, izo zinkawoneka ngati, ine ndikanati ndizigwa. Panalibe kuyima, paliponse.

Ndiyeno zinali zosiyana bwanji ndi masomphenya omwe ine ndinali nawo kuno, osati kale litali, a kukhala mu Ulemerero ndi anthu, kusiyana! Koma mu awa, pamene ine ndinali kugwa, ine potsiriza, ine ndinakuwa kufuna abambo anga. Zoona, pokhala kamwana chabe, ndicho chimene ine ndikanati ndichite. Ine ndinakuwa kufuna abambo anga, ndipo bambo anga kunalibe kumeneko. Ndipo ine ndinakuwa kufuna amayi anga, “Winawake andigwire ine!” Ndipo kunalibe amayi kumeneko. Ine ndinali ndikumangopita. Ndipo ine ndinakuwira ndiye kwa Mulungu. Kunalibe Mulungu kumeneko. Kunalibe kalikonse kumeneko.

Ndipo patapita kanthawi ine ndinamva phokoso lakubuula kwambiri limene ine ndinayamba ndalimvapo, ndipo iko kunali kumverera kowopsyesetsa. Palibe njira... Ngakhale moto weniweni woyaka ukanakhala chosangalatsa pambali ya chomwe ichi chinali. Tsopano masomphenya amenewo sanayambe akhalapo olakwika. Ndipo iko kunali basi kumodzi kwa kumverera kowopsya kwambiri kumene ine ndinayamba ndakhalapo nako, ndipo nchiyani chinkachita....

Ine ndinamva phokoso, linkamveka monga mtundu wina wa... chochitika mwa malubwelubwe. Ndipo pamene iko kunali, ine ndinayang'ana, akubwera, ndipo iwo anali akazi. Ndipo iwo anali ndi zinthu zobiriwira, iwe umakhoza kuwona nkhope zawo chabe, ndipo iwo anali ndi zinthu zobiriwira pansi pa maso awo. Ndipo maso awo ankawoneka ngati opita mmbuyo, monga... akazi lero amapakira utoto maso awo, opita mmbuyo monga choncho, ndipo maso awo okha ndi nkhope. Ndipo iwo anali akuti, “Huu, huu, huu, huu!” O, mai!

Ine ndinangokuwa apo, “O Mulungu, chitirani chifundo pa ine. Ndichitireni chifundo, O Mulungu! Kodi inu muli kuti? Ngati Inu muti mundirole kokha ine kubwerera kumbuyo ndi kukakhala moyo, ine ndikukulonjezani Inu, kuti ndikakhala mnyamata wabwino.” Tsopano, ndicho chinthu chokha chomwe ine ndingakhoze kunena. Tsopano, Mulungu akudziwa, ndipo pa Tsiku la Chiweruzo, Iye adzandiweruza ine chifukwa cha neno limenelo. Ndicho chimene ine ndinanena, “Ambuye Mulungu, ndiroleni ine ndibwerere kumbuyo, ndipo ine ndikulonjezani Inu ine ndikakhala mnyamata wabwino.”

Ndipo pamene ine ndinawomberedwa, ine ndinali nditanena zabodza, ine ndinali nditachita pafupifupi chirichonse chomwe chinalipo choti nkuchitidwa, chinthu chimodzi chokha chimene ine ndikuti^ine kuli bwino kuti ndingochiyeretsa icho pamene ine ndikanali pomwe pano tsopano. Ndipo pamene ine ndinayang'ana pansi ndi kuwona kuti ndinali nditaphulitsidwa mwatheka pawiri, pafupifupi, ine ndinati, “Mulungu, chitirani chifundo pa ine. Inu mukudziwa ine sindinayambe ndachitapo chigololo.” Icho chinali chinthu chokhacho chimene ine ndikanakhoza kunena kwa Mulungu. Ine ndinali ndisanalandire konse kukhululukira Kwake, ndi zinthu zonse izi. Ine ndingoti, ndikanakhoza kunena, “Ine ndinali ndisanayambe ndachitapo chigololo.”

Ndiyeno iwo ananditenga ine kunditulutsa kumeneko. Ndiyeno, mkati umo, ine ndinalira, “Mulungu, chitirani chifundo kwambiri pa ine. Ine ndikakhala mnyamata wabwino, ngati Inu muti mundirole kokha ine kubwerera kumbuyo,” chifukwa ine ndinkadziwa kuti kunali Mulungu kwinakwake. Ndipo chotero ndithandizeni ine, zolengedwa zotopa izo pozungulira ponse, ine ndinangokhala wofika mwatsopano. Ndipo mowopsya kwambiri, mochititsa mantha, kumverera kosakhala kwaumulungu mkati umo... Ankawoneka ngati maso aakulu kwambiri, zikope zazikulu monga choncho, ndipo zopita mmbuyo monga mphaka, monga chammbuyo monga chonchi; ndi zinthu zobiriwira, ndi ngati kuti izo zinali ziri kakata kapena chinachake. Ndipo iwo anali... iwo anali akupita, “Huu, huu, huu!” O, ndi kumverera kotani!

Ndiye mu nthawi ya mphindi, ine ndinali nditabwereranso ku moyo wachibadwa kachiwiri. Chinthu chimenecho chandisautsa ine. Ine ndinaganiza, “O, mulole izo zikhale kuti ine sindidzapita konse ku malo ngati amenewo; palibe munthu wina ati adzasowe kuti apite ku malo onga amenewo.” Miyezi isanu ndi iwiri kenako, ine ndinali ndi masomphenya nditayima Kumadzulo, ndi kuwona mtanda wagolide uja ukubwera pansi pa ine. Ndipo ine ndinadziwa kuti zinalipo zigawo za oweruzidwa kwinakwake.

Tsopano, ine sindinazizindikire izo konse mochuluka kwambiri kufikira pafupi masabata anayi apitawo. Mkazanga... Sindinaganize konse za izo mwa njira iyi. Pafupi masabata anayi apitawo, mkazanga ndi ine tinapita kumusi ku Tucson, kuti tikachite zogula zina. Ndipo pamene ife tinali titakhala... Mkazanga, ife tinapita mu zipinda zapansi, ndipo uko kunali gulu la anyamata achikazi anali ndi tsitsi lawo lotiwidwa, inu mukudziwa, monga akazi amachitira, ndi mabibo litapesedwera pansi apa kutsogolo, ndipo atavala mabuluku aatali kwenikweni awa, okhala ngati, ine ndikuganiza chibitiniki, kapena chirichonse chomwe inu mumawatcha iwo.

Kotero ine ndinapita zipinda zammwamba, ndipo ine ndinakhala pansi. Ndipo pamene ine ndinatero, panali chikepe, umo munali mu sitolo ya J.C. Penney, ndipo chikepecho chikuwakweza anthu mmwamba. Chabwino, ine ndinayamba kudwaladi mmimba mwanga, kuwawona akazi amenewo akubwera mmwamba umo; aang'ono, achikulire, ndi osayanjanitsika, amakwinya, aang'ono, ndi njira iliyonse, atavala akabudula aang'ono kwambiri; thupi lawo lonyansa, ndipo akazi ovala mwachigololo awo, ndi mitu yaikulu iyo monga choncho, ndipo apa iwo anali kubwera. Ndipo wina akubwera akutsika chikepecho, akumangomabwera chokwera monga choncho, pamene ine ndinali nditakhala mu mpando, nditakhala pamenepo ndi mutu wanga mozyolika.

Ndipo ine ndinatembenuka ndipo ndinayang'ana. Ndipo mmodzi wa iwo akubwera mmwamba pa masitepe anali akuti, “Huu, akuyankhula chi Spanish, kwa mkazi wina. Iye anali mkazi woyera akuyankhula kwa mkazi wa chi Spanish. Ndipo pamene ine ndinayang'ana, zonse mwadzidzidzi ine ndinasinthidwa. Pamenepo, ine ndinali nditaziwonapo izo kale. Maso ake, inu mukudziwa momwe akazi akuchitira tsopano, kupaka utoto maso awo, posakhalitsa kumenepa, monga mphaka, inu mukudziwa kuziyika izo mmwamba monga chonchi, ndi kuvala magalasi a mphaka ndi chirichonse, inu mukudziwa, ndi maso mmwamba monga chonchi, ndi chinthu chobiriwira icho pansi pa maso awo. Apo panali chinthu chimenecho chimene ine ndinachiwona pamene ine ndinali mwana. Apo panali mkaziyo chimodzimodzi basi. Ndipo ine ndinangochita zanzi paliponse, ndipo ndinayamba kuyang'ana pozungulira, ndipo apo panali anthu amenewo akung'ung'uza, inu mukudziwa, akumapitirira ndi mitengo ndi zinthu mu chipindacho.

Ndinawoneka ngati kuti ine ndinangosinthidwa kwa kamphindi. Ndipo ine ndinayang'ana, ndipo ine ndinaganiza, “Izo ndi zimene ine ndinaziwona mu gehena.” Apo iwo anali, kakata ameneyo. Ine ndinaganiza chifukwa iwo anali mu gehena chomwe chinawapangitsa iwo mwanjira imeneyo, buluu wonkera kukubiriwira pansi pa maso awo. Ndipo apa panali akazi awa odzipaka utoto wa buluu wonkera kukubiriwira, basi momwe masomphenya aja ananenera pafupi zaka makumi anayi zapitazo. Onani, pafupi zaka makumi anayi zapitazo, ndi zomwe izo zakhala. Ine ndiri makumi asanu ndi zinayi; ine ndinali khumi ndi zinayi. Kotero pafupi zaka makumi anayi zapitazo, ine... Ndipo ndicho... Ndicho chiwerengero, chonchobe, cha chiweruzo, inu mukuwona.

-----
Ine ndinaganiza ndiye, pamene ine ndinawazindikira maso owoneka-kakata awo pa akazi amenewo. Panali achi Spanishi, achi Frenchi, ndi Amwenye, ndi azungu, ndi onse palimodzi, koma mitu yaikulu iyo, inu mukudziwa, mwathengo, chipeso chimenecho, momwe iwo amalipesera ilo kumbuyo, lalikulu kwambiri, ndiyeno nkulitulutsa. Inu mukudziwa, inu mukudziwa momwe iwo amachitira izo, kulikonza ilo monga iwo amachitira izo. Ndiyeno maso owoneka-kakata awo, ndipo masowo ali ndi utoto, iwo amapita mmbuyo monga maso a mphaka. Ndipo iwo akuyankhula, ndipo apo ine ndinali kachiwiri, nditayima mmenemo mu sitolo ya J.C. Penney, nditabwerera mu gehena kachiwiri.

Ine-ine_ine ndinachita mantha kwambiri. Ine ndinaganiza, “Ambuye, zedi ine sindinafe, ndipo Inu mwandirola ine kubwera ku malo ano zitatha zonse.” Ndipo apo iwo anali ali, akupanga... pozungulira chabe monga choncho, mokhala ngati masomphenya aja, iwe ukanakhoza basi kumamva izo momveka ndi makutu ako, inu mukudziwa. Kung'ung'uza kokha ndi kupitiriza, kwa anthu, ndipo akazi amenewo akubwera mmwamba pa chikepe chimenecho ndi kumayenda pozungulira pamenepo, ndipo apo, “Huu, huu!” Panali obiriwiwa aja, maso-owoneka moseketsa, ndi mobuula.

Werengani akaunti yonse mu...
Miyoyo yomwe ili mu ndende tsopano.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,

Ahebri 9:27


“O, mulole izo
zikhale kuti...
palibe munthu
wina ati adzasowe
kuti apite ku malo
onga amenewo.”


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

The Pillar of Fire.

(PDF Chingerezi)

Mulungu kudzibisa
yekha mu kuphweka...

(PDF)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.