Mbewu ya Serpenti.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Wamoyo Mawu mndandanda.

Wochenjera Serpenti.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Mbewu ya Serpenti.

Genesis 3:1-7,
Tsopano serpenti anali wochenjera kwambiri kuposa chinyama chirichonse cha kuthengo chimene AMBUYE Mulungu anali atachipanga. Ndipo iye ananena kwa mkaziyo, Eya, anati Mulungu kuti, Inu musadya za mtengo uliwonse wa m'munda?. Mkaziyo ananena kwa serpenti, ife tikhoza kudya zachipatso cha mitengo ya m'munda: Koma za chipatso cha mtengo. Mkati mwa munda, Mulungu wanena kuti, Inu musadye za icho, ngakhale inu kuchikhudza icho, kuwopa kuti inu mungafe. Ndipo serpenti ananena kwa mkaziyo, Inu sikuti mudzafa ndithu: Pakuti Mulungu akudziwa kuti tsiku limene inu muti mudzadye za icho, ndiye maso anu adzakhala otseguka, (mukuona kusaka kuwala kwa tsopano), ndipo inu mudzakhala monga milungu, odziwa chabwino ndi choyipa.

Zindikirani tsopano pano pali chimene chinachitika. Ine ndikukhulupirira, ndipo ine ndikhoza kuzithandizira izo mwa Baibulo, kuti ndi serpent amene anachita izo. Serpent ndiye munthu wosowayo pakati pa chimpanzii ndi munthu. Chifukwa, mvetserani, zindikirani izi tsopano, kuti serpent sanali wokwawa. Iye anali kwambiri “wochenjera” mwazinyama zonse za kuthengo. Tsopano, ine ndinapita ndipo ndinakatenga madikishonare lero, ochokera kulikonse, kuti ndikayang'anemo mawu awa, chimene mawu woti wochenjera amatanthauza. Iwo amatanthauza “kukhala wodziwa kwambiri, kukhala wothyathyalika,” ndipo, kutanthauzira kwa bwino kwa - kwa chiHebri kuchokera ku m- a- h- a- h, amatanthauza “kukhala nacho chidziwiwitso choona chazofunika za moyo.”

Tsopano tiyeni tipenyeni mphindi yokha. Iye ndi wodziwa kwambiri, wothyathyarika, komabe iye akutchedwa “Serpenti.” Koma, kumbukirani, iye anali chinthu chodziwa zinthu kwambiri chimene chinalipo, ndipo chofanana kwambiri ndi munthu kuposa china chirichonse chimene chinalipo m'munda; chapafupi kwa munthu wokhalapo. Iye sanali chokwawa ayi. Themberero linamupanga iye chokwawa. Ndipo iye anali.... Baibulo linati iye anali wokongola kwambiri wa zonse.

Ndipo ngakhale themberero silinatenge kukongola kwake konse kukuchotsa; komabe mangamanga aulemerero anjoka ndi okongola, ndipo chisomo chake ndi kuthyathyalika kwake. Ngakhale themberero silinasunthe izo nkuzichotsa. Koma, kumbukirani, Mulungu anamuwuza iye kuti miyendo yake ichotsedwa ndipo kuti iye adzidzayenda ndi pamimba yake. Ndipo inu simungakhoze kupeza fupa limodzi mwa njoka limene limawoneka ngati munthu, ndipo ndicho chifukwa sayansi yatayika. Koma iye ali apo.

Mulungu anazibisa izo ku maso anzeru ndi aluntha, ndipo analonjeza kuti adzaulula izo kwa ana a Mulungu, mumasiku otsiriza pamene ana a Mulungu atadzawonetseredwe, pamene, “Ana a Mulungu amene ankasangalala ngakhale maziko adziko asanayikidwe.” Pamene vumbulutso lalikulu la Umulungu ndi zinthu ziti zidzabweretsedwe pansi mumasiku otsiriza, iye akanati adzawonetsere zinthu izi kupyolera mwa ana a Mulungu. Inu mukudziwa kuti Lemba limaphunzitsa zimenezo. Ndipo ndife tiri pano.

Ndicho chifukwa Mulungu akutsegulira zinthu izi kwa ife. Mulungu akuwabweretsa ana Ake mukuwonetseredwa. Iye akupita kudutsa malire anzeru iliyonse ya umunthu, kutali mpaka mumavumbulutso auzimu, ndikulibweretsa ilo pansi. Kodi ife sitinakhale tikuphunzitsa, mu Baibulo ili, “Pano ziri kwa iye amene alinayo nzeru”? Osati zimene iye anaphunzira museminare ina; koma zimene iye anaphunzira pamawondo ake pamaso pa Mulungu, ndi chimene chinamukondweretsa Mulungu kuti amupatse iye. Ana amuna a Mulungu kukhala akuwonetseredwa!

Pano pali Serepenti, tsopano pano pali chimene serpenti anali; ine ndikupatsani inu kufotokoza kwanga kwa iye. Ife tiri ndi.... Ife tabwera pansi, kuchokera kwa chule, kupitirira mpaka kwa mbululu ija, ndipo kupitira pansi, ndikupitirira, zakuti - ndi zakuti, mpaka inu potsiriza munafika kwa nyani, kwa chimpanzii. Ndipo kuchokera kwa chimpanzii, tsopano ife talumpha kuchoka kwa chimpanzii kufika kwa munthu, ndipo ife tikudabwa chifukwa chiyani. “Chabwino,” sayansi imanena kuti, “tsopano dikirani! Ife tikhoza kubalitsa mkazi kwa nyani ndi kwa chimpanzii, ndiyeno mosinthanitsa, mwamuna kubalitsa kwachimpanzii.” Izo sizingagwire ntchito. Kubalitsa iye kwa chinyama chirichonse; izo sizingagwire ntchito. Magazi sangasakanizane; kutenga magazi anu, aliwonse palimodzi magazi osiyana, palimodzi. Pali magazi ena pakati apa, ndipo iwo sangakhoze kuchipeza chinyamacho. O, Aleluya, ine ndikuyamba kumverera mwachipembedzo pakalipano.

Zindikirani. Nchifukwa chiyani? Mulungu anazibisa izo kwa iwo. Palibe fupa mwa njoka limene limawoneka ngati fupa la munthu. Iye anachiika chinthucho kutali kwambiri mwakuti icho sichikanakhoza kupezedwa ndi munthu wa nzeru.

Ndipo ine ndikuwonetsani inu kumene munthu wa nzeru ameneyu anachokera, kumene - kumene iye aliko, mulimonse. Mwaona, iye sangakhoze kubwera kupyolera muzimenezo Izo ziyenera kubwera mwa vumbulutso, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa....” “Pathanthwe iri Ine ndidzamangapo Mpingo Wanga; ndipo zipata za ku gehena sizingakhoze kuulaka iwo,” vumbulutso la uzimu. Motani... anadziwa motani Abele kuti apereke mwana wa nkhosa, mmalo mwa Kaini wopereka zipatso zakumunda? Izo zinawululidwa mwauzimu kwa iye. Iwe sumazipeza izo mwa maseminare iwe sumazipeza izo kupyolera muzipembedzo. Iwe umazipeza izo kuchokera kumwamba.

Tsopano penyani serepenti, serepenti iyi imene inali poyamba. Tiyeni tiyijambule chithunzi cha iye tsopano. Iye ndi munthu wamkulu kwambiri. Iye ali pakati pa chimpanzii ndi munthu. Ndipo, serpenti; mdierekezi, Lucifara, ankadziwa kuti awa magazi okhawo amene akanakhoza kusakanizikana ndi magazi a munthu, munthu yekhayo amene iye akanakhoza kuchita ndi zinthu zosiyana. Iye sakanakhoza kuchita ndi chimphazii, magazi amewo sakanatha kusakanizana. Iye sakanakhoza kuchita ndi zinthu zosiyana. Iye sakanakhoza kuchita ndi nkhosa. Iye sakanakhoza kuchita ndi kavalo. Iye sakanakhoza kuchita ndi chinyama chirichonse; iye anayenera kuti achite ndi serepenti iyi. Tiyeni timutenge iye tsopano ndi kuwona m'mene iye amawonekera. Iye ali munthu wamkulu kwambiri, chimphona cha mbiri yakale yoyambirira. Ndiko kumene iwo amapeza mafupa a akulu awa, ndipo ine ndikuwonetsani inu izi mu Baibulo. Tsopano penyani mwatcheru. Chabwino. Munthu wamkulu kwambiri uyu, tiyeni tinene kuti iye -anali utali wamapazi khumi, mapewa a akulu kwambiri; amkawoneka basi ngati munthu. Ndipo magazi ake; atatha kubwera pansi, kukweranitsa nyama imodzi kwa imzake.

Inu mukhoza kusemphanitsa zinyama. Ndipo izo zinapitirira kumatenga magazi, mawonekedwe apamwamba a moyo, mawonekedwe apamwamba, mpaka izo zikukwera mpaka kudera la munthu. Koma kulumikizana kotsiriza apa, pakati apa, chinadulidwa kuchokapo. Ndi angati amene akudziwa kuti sayansi singakhoze kupeza chilumikizo chosowacho? Nonse a inu mukudziwa zimenezo. Chifukwa chiyani? Apa iye ali, serepenti.

Apa iye analipo, munthu wamkulu kwambiri. Ndipo mdierekezi akubwera pansi pano, tsopano, iye akuti, “Ine ndikhoza kudzoza.” Tsopano pamene inu mupita mukuyang'ana pa akazi, ndi zochita za azimayi, kumbukirani, inu muli mwodzozedwa ndi mdierekezi (uyo simkazi wanu yemwe.) Zindikirani, tsopano, mdierekezi anabwera pansi ndipo analowa mwa serepenti. Ndipo iye anamupeza Hava m'munda wa Edene wa maliseche, ndipo iye anayankhula za chipatso pakati. Pakati amatanthauza “Chirikati,” ndi zina Zotero; inu mukumvetsa, mugulu losakanizana. Ndipo iye anati, “Tsopano, ndichokongola. Ndi chabwino kwa diso.”

Ndipo kodi iye anachita chiyani? Iye anayamba kupanga chikondi kwa Hava, ndipo iye anakhala naye iye, ngati mwamuna wake. Ndipo iye anawona kuti icho chinali chokondweretsa. Kotero iye anapita ndipo anakamuuza mwamuna wake, koma iye anali kale ndi pakati pa satana. Ndipo iye anabala mwana wake oyamba wa mwamuna, amene dzina lake linali Kaini, mwana wa satana. “Tsopano,” inu mukuti, “ndiko kulakwitsa.”Chabwino, ife tingopeza ngati ziri zolakwika kapena ayi. “ndipo Ine ndidzaika udani pakati pa mbewu yako ndi mbewu ya Serepenti.” Chiyani? mbewu ya serepent! Iye analinayo mbewu, ndipo iye anali nayo mbewu. “Ndipo Iye adzavulaza mutu wako, ndipo iwe udzavulaza chidendene Chake.” Ndipo kuvulaza, pamenepo, kukutanthauza, “kupanga chitetezero.” Tsopano ndi imeneyotu “mbewu” yanu ya serepenti. Tsopano, zindikirani, apa pakutulukira amuna awiri awa. Tsopano, serepenti uyu, pamene iye anayima apo, chimphona chachikulu kwambiri ichi chamunthu chinayimirira pamenepo, iye anali olakwa pakuchita chigololo ndi mkazi wa Adamu. Kodi tchimo liri kuti lero? Ndichiyani chimene chikupangitsa zinthu momwe izo ziri lero? (Tsopano, ine - ine.... Ndithudi inu mukhoza kugwira chimene ine ndikukamba za icho. Ndipo apo icho chinali.)

Ndipo pamene iye anatero, Mulungu anati, anayamba kumuitana Hava ndi Adamu. Ndipo iye anati, “Ine ndinali maliseche.” Ndipo Iye anati, “ndani anakuuza iwe kuti unali maliseche?” Ndiye iwo anayamba, kachitidwe ka a nkhondo, kukanilana cholakwikacho anati, “Chabwino, mkazi yemwe inu mwandipatsa ine, wachita icho. Iye anali m'modzi amene amandikakamiza ine.” Ndipo iye anati, “Serepenti anandipatsa ine apulo?” Chabwino, mlaliki, taganizani bwino. Iye anati, “Serepenti anandinyenga ine.” Kodi inu mukudziwa kunyenga amatanthauza? Icho chimatanthauza “kuipitsidwa.” Monga iye anali. Mdierekezi sanamupatse iye apulo. “Serepenti wandinyenga ine.” Ndiyeno themberero linabwera.

Iye anati, “chifukwa iwe unamvetsera kwa serepenti m'malo mwa mwamuna wako, iwe wauchotsa moyo kuchoka mudziko. Ndipo iwe udza - iwe udzachulukitsa zowawa zako; ndipo pokhala ndi pakati pako udzakhala kwa mwamuna wako,” ndi zina zotero. “Ndipo chifukwa iwe unamvetsera kwa mkazi wako, m'malo mwa Ine (Ine ndinakutenga iwe kuchokera kufumbi; mtundu wapamwamba), kubwerera kufumbi iwe upita.” “Ndipo, serepenti, chifukwa iwe wachita zimenezo, miyendo yako ikuchoka. Pamimba yako iwe udziyenda masiku wonse amoyo wako. Ndipo iwe udzakhala ukudedwa. Ndipo fumbi lidzakhala chakudya chako.” Ndi zimenezotu apo pali chilumikizo chosowacho.

Tsopano apa pakubwera Kaini, tiyeni tiwone zikhalidwe. Apa pakubwera Kaini. Kodi iye ali chiyani? Iye ndi munthu wamalonda wothyathyalika. Iye amalima munda. Wa nzeru, wa luntha; wa chipembedzo, wachipembedzo kwambiri; penyani zake - penya zikhumbo zake tsopano. Mungosuntha ndine utali wa mphindi pang'ono motalikirapo. Apa iye akubwerako. Iye akudziwa iye ndi wakhalidwe. Iye akufuna kupita kutchalitchi. Iye akumanga tchalicthi, akupanga nsembe. Akubweretsa guwa, ndi zonse. Kumanga guwa, kuika maluwa ake pailo. Kuikapo munda, zipatso za kumunda, kuzipereka izo kwa Mulungu. Anati, “Landirani izo inu Ambuye. Ine ndikudziwa kuti ife tinadya ma apulo, ndichomwe chimene chinapangitsa icho.” Ena otuluka mwaiye alinalo lingaliro la mtundu womwewo.

Akusonyeza kumene iwo anachokerako. Anabweretsamo ma apulo ake, kuchokera kumunda, kuziika izo pamenepo, anati, “Izi zipanga chitetezero.” Mulungu anati, “Iwo sanali ma apulo.” Koma, mwavumbulutso la uzimu, Abele anadziwa kuti iwo anali magazi. Kotero iye anabweretsa mwanawankhosa, anadula khosi lake, ndipo iye anafa. Ndipo Mulungu anati, “Ndiko kulondola. Ndicho chimene chinachita icho. Iwo anali magazi. (Inu mukudziwa magazi amene ine ndikuwakamba. Chabwino. ”Iwo anali magazi amene anachita izo.) Tsopano penyani.

Ndiyeno pamene Kaini anamuwona m'bale wake woyera - wodzigubuduza kuti anali atalandiridwa pamaso pa Mulungu, ndipo zizindikiro ndi zodabwitsa zinali zikuchitika kumusi uko, iye anakhala wansanje naye iye. Iye anati naye, “Ife tiimitsa zinthu izi pakali pano.” Penyani pa abale ake, penyani ana ake, alipo lero. “Tsopano, ine ndine wanzeru kuposa iye ali,” kotero iye anakhala okwiya. Kodi kukwiyako kunachokera kuti. Kodi inu mukanakhoza kunena kuti kukwiya.... Iye anamupha m'bale wake. Iye anali wakupha. Kodi inu mukanakhoza kumutcha Mulungu wakupha?

Ndipo Adamu anali mwana wa mwamuna wa Mulungu. Baibulo linanena, kuti, “Adamu anali mwana wa mwamuna wa Mulungu,” chiyambi chija changwiro kumbuyo uko. Adamu anali mwana wa mwamuna wa Mulungu. Ndipo nsanje imeneyo ndi kuipidwa, ndi chirichonse, sizikanakhoza kubwera kuchokera mu mtsempha wa ngwiro uwo. Izo zinayenera kubwera kuchokera mumalo ena. (Malo opanda mau pa tepi - Mkonzi) Ndipo izo zinabwera kuchokera kwa satana yemwe anali wakupha, kuyamba ndi kuyamba. Baibulo linati, “iye anali wabodza ndi wakupha, kuyamba ndi kuyamba.” Ndipo apo izo ziri. Ndipo iye anamupha m'bale wake. Ndipo icho chinali choimira cha imfa ya Khristu. Ndiye, kuchokera kumeneko, zoona, iye anaukitsa Seti kuti atenge malo ake. Imfa, kuikidwa m'manda, ndi kuuka kwa Khristu.

Ndipo penyani, ndiye, apa pakubwera zimphona zanu. Ndiye Kaini anapita kudziko la Nodi. Ngati adadi ake anali chimphona chachikulu cha munthu nanga Kaini akanakhala monga chiyani? Adadi ake. Ndipo iye anapita kudziko la Nodi, ndipo anatenga mmodzi wa azilongo ake. Njira yokha imene iye akanakhoza kuchitira. Uku kunalibe akazi enanso amene akanakhoza kubwera, koma kokha kupyolera mwa Hava. Iwo amanena kuti iwo anali ndi ana amuna ndi ana aakazi makumi asanu ndi awiri. Ngati - ngati uko kunalibe wamkazi.... Baibulo silimalemba akazi pamene iwo anali kubadwa, amuna okha. Ndipo pamene, ngati uko kunalibe akazi enanso kuposa Hava, pamene iye anafa, mtundu wa anthu ukanasiya kukhalapo. Iye amayenera kukhala ndi ana akazi. Ndipo iye amayenera akwatire mlongo wake yemwe.

Iye anapita kudziko la Nodi ndipo anakatenga - ndipo anatenga mkazi wake. Ndipo pamene iye anamukwatira iye kumeneko, uko ndi kumene iwo anapeza zimphona zazikulu zija, zimene zinali ana a amuna akugwa a Mulungu; amene anadza ku pyolera mwa a bambo awo, mdierekezi, kupyolera mwa Kaini. Apo pali chilumikizo chanu chosowa.

Werengani akaunti yonse mu... Mbewu ya Serpenti.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Umu ndi m’mene mkazi amachitira atachita chigololo: Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”

Miyambo 30:20


Ngati kudya ma
apulo zimawapangitsa
aakazi kuzindikira
kuti iwo ali
amaliseche, kulibwino
ife tiwalambalale ma
apulo kachiwiri.


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

The Pillar of Fire.

(PDF Chingerezi)

Mulungu kudzibisa
yekha mu kuphweka...

(PDF)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.