Patatu ichichiri cha Mulungu.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Wamoyo Mawu mndandanda.

Khristu ndi chinsinsi cha Mulungu woululidwa.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Khristu ndi chinsinsi cha Mulungu woululidwa.

NZindikirani, Mulungu wakhala ali nacho cholingachofutukuka patatu mu chinsinsi chobisika chachikulu ichi. Mulungu, mu chinsinsi Chake chobisika chachikulu chimeneIye anali nacho dziko lisanayambe, Iye ali nacho cholingachofutukuka patatu mu icho. Ndipo tsopano chimene ifetikufuna kuti tipitepo, mmawa uno, ndicho, cholingachofutukuka patatu chimenecho nchiani? Mukuona? Tsopano, ine ndikukhulupirira, mwa kuthandizidwa ndi... Mulungu, Yemwe alipo, ndipo Iye asonyeza izo kwa ife. Tsopano, ngati Iye anali nacho cholinga chofutukuka patatu ichi, ifetikufuna kuti tipeze chimene cholinga chofutukuka patatu ichichiri.

Chinthu choyamba chinali, kuti, Mulungu ankafuna kutiadziulule Iyemwini kwa anthu. Iye sakanakhoza kuchita izo monga Mulungu Yehovawamkulu Yemwe amaphimba danga lonse, nthawi, ndiUmuyaya. Iye sakanakhoza kutero. Iye ndi wamkulu kwambirikuti awululidwe konse kwa anthu, chifukwa ichochikanakhala chachinsinsi kwambiri. Chikanakhoza bwanjichinthu chachikulu icho chimene sichinachite kuyamba... kuti inu mutapita kupyola mkombero wa zaka mazana a mabilionindi matrilioni ndi matrilioni a danga la kuwala, ndi kupitirirampaka kukafika kopandamalire, mpaka mu Muyaya, ndipoCholengedwa chachikulu chimene anali zonse izo, ndipopanobe ali.

Koma chimene Iye anafuna kuti achite. Iye ankakondautate, pakuti Iye anali Atate. Ndipo njira yokha imene Iyeakanakhoza kufotokozera izo inali kuti akhale Mwana wamunthu. Ndicho chifukwa Yesu ankapitiriza kumati, “Mwanawa munthu.” Mukuona, iwo sanali kudziwa chimene Iye analikuchiyankhula, ambiri a iwo. Koma tsopano inu mukumvetsaizo? Mukuona? Iyeankafuna kuti adzifotokoze Yekha. Icho chinali Chake, chimodzi cha zolinga Zake zofutukuka patatu, chinali kutiadzifotokoze Yekha, adzizindikiritse Yekha ndi anthuokhalapo, kuti adziwulule Yekha mwa Khristu.

Chachiwiri, kuti akhale nawo uyambiriro mu Thupi Lakela okhulupirira, amene ali, Mkwatibwi Wake, kuti Iye akhozakumakhala mwa anthu.

Tsopano, Iye akanakhoza kuchita izo mwa Adamu ndi Eva, koma tchimo linawalekanitsa iwo, chotero tsopanopamayenera kukhala njira ina kuti azibwezeretse izokachiwiri. O, mai! O, tsopano, izi, izi ndi zolemera, kwa ine, basi kungoti ndingolingalira za izo. Mukuona? Mukuonachimene cholinga cha Mulungu chinali? Tsopano nchifukwachiani Iye sanangomusunga Adamu ndi Eva monga choncho?
Ndiye Iye sakanakhoza kukwanitsa kuti afotokoze chidzaloChake. Chikhumbo Chake chathunthu. Chifukwa, Iyeakanakhoza kukhala Atate uko, izo nzoona, koma naponso Iyendi Mpulumutsi. Inu mukuti, “Inu mukudziwa bwanji kuti Iyeanali?” Iye ali, chifukwa ine ndakhala nacho chondichitikira. Mukuona? Mukuona? Iye ndi Mpulumutsi, ndipo Iye ayenerakuti achifotokoze icho. Ndipo Iye akanakhoza kuchichitamotani icho? Kupyolera mwa Khristu yekha. Iye akanakhozabwanji kukhala Mwana? Kupyolera mwa Khristu yekha. Iyeakanakhoza bwanji kukhala Mchiritsi? Kupyolera mwaKhristu yekha. Mukuona, zinthu zonze zadzathera mwaMunthu mmodzi ameneyo, Yesu Khristu. O, mai!

Pamene ine ndikuganiza za izo, ine_ine ndikungowonazipembedzo zikuchoka powonekera, ndi china chirichonsechikupita basi, mwaona, pamene ine ndiwona cholingachachikulu cha Mulungu, akudziwulula Yekha. Ndi kukhalanako, poyamba, kuti adziwulule Yekha mwa Khristu, “chidzalo cha Umulungu mu thupi.” Ndipo, kenako, kutiabweretse icho “chidzalo cha Umulungu mu thupi” mwaanthu, kuti Iye akhoze kukhala nawo uyambiriro, kupenyeratu, kutsogolera.

Chimodzi china, usiku, ngati inu simunaipeze tepi, inendinalalikira pano usiku wina, pa Wamndende wa YesuKhristu. Paulo, wamndende! Mukuona? Pamene Mulunguakutenga iwe kuti ukhale wamndende Wake, ndiye iwesungakhoze kuchita kanthu koma chimene Mzimu unena kutiuchite. Paulo, ndi luntha lake lonse lalikulu, iyeanaphunzitsa... iye anaphunzitsidwa ndi Gamaliele kutiadzakhale wansembe wamkulu kapena mphunzitsi, tsiku lina. Ndipo iye anali ndi zokhumba zapamwamba. Iye analimwaluntha munthu wamkulu, ulamuliro waukulu, munthuwamkulu mu fuko. Koma iye anayenera kupereka chidutswachirichonse cha izo, mwaona, kuti akhale gawo la Mawu, kutiafotokozere Yesu Khristu. Iye ankadziwa chimene icho chinalikuti anene... Iye anali ndi lingaliro kuti apite ku malo enaake, abaleenaake anali atamuitana iye, koma iye analetsedwa ndi Mzimukuti achite chifuniro chake chake. O, ngati_ngati anthuauzimu mwatheka akanakhoza kuzimvetsa izo! Mukuona? Iyeanaletsedwa kuti achite chifuniro chake chake. Iyeakanakhoza kungochita... “Mzimu unandiletsa ine.” Mukuona? Iye anali wamndende kwa Khristu.

Ndiye, wambwebwe wamng'ono uyu tsiku lina, yemwe iyeankadziwa, Paulo ankadziwa kuti iye anali ndi mphamvu yotiatulutsire mdierekezi ameneyo, koma iye akanakhoza kokhakuchita izo pamene Mulungu akanaloleza izo. Tsiku ndi tsikuiye ankamutsatira iye, akufuulira pa iye, koma tsiku linaMzimu unamupatsa iye chilolezo. Ndiye iye anamudzudzulaiye, mzimu umene unali mwa iye. Mukuona? Iye ankadziwachimene chinali kukhala wamndende.

Mose, luntha lake, iye ankayenera kuti alitaye ilo polingakuti apeze Khristu, kuti akhale wamndende. Ndiye pameneMulungu anapuntha chidziko chonse mwa iye, ndi umwamunawamphamvu wonse womwe iye anali, ndi kudzaima muKukhalapo kwa Lawi la Moto tsiku lija, iye anapezeka basiwopanda chonena. Iye sanati nkomwe, sankakhoza ngakhalekuyankhula, iye anati. Mulungu anali ndi wamndende apo. Mukuona? Inu simungati muziyesa izo mwa kufufuza kwanukwanu. Ndiye Mulungu anachita kumupatsa munthu uyu, kumuveka iye ndi mphamvu zokwanira kuti iye akanakhozakupita kumeneko.

Ndipo iye anati, “Ambuye, ine ndinamuuza Farao chimeneInu munanena, ndipo iye samakhoza kuzichita izo.” Iye anati, “Ndiye tenga iyi, ndodo yako,” Mulunguakuyankhula, awo ndi Mawu a Mulungu, “pita kunja ukondipo ukailozetse iyo cha Kummawa, ndipo ukaitanentchentche.” Ndipo ntchentche zinabwera polengedwa, chifukwa Iye anali ndi wamndende yemwe Farao sakanakhoza kumugula ndi kanthu. Palibe munthu wina aliyenseakanakhoza kumutembenuzira iye njira iliyonse. Iye analiwamndende kwathunthu mu unyolo wa Mawu a Mulungu, womangidwa ku PAKUTI ATERO AMBUYE yekha.

O, ngati Mulungu angakhoze kudzipezera Iye amndendeonga awo! Tsopano, ndi pamene Iye angakhoze kufotokozerauyambiriro, inu mukuona. Iye, Iye wamupeza mwamuna, kapena munthuyo, mwakuti iye sakudziwa kanthu kena komaKhristu. Inu mukumvetsa zimene ine ndikutanthauza? Chabwino. Ndichochachiwiri.
Choyamba, kuti adzifotokoze Yekha mwathunthu, Mulungu mwa Khristu. Chachiwiri, kuti adzakhale nawo uyambiriro, mwa ichi, mu Mpingo Wake, umene uli Thupi Lake, Mkwatibwi, mpakaIye atakhala nawo uyambiriro kuti adzifotokoze Yekhakupyolera mwa iwo. Chabwino.

Ndipo chachitatu, kuti abwezeretse Ufumu ku malo akeoyenera, umene unagwa ndi tchimo ndi Adamu woyamba, kubwerera kumene Iye ankayenda mu madzulo ozizira ndianthu Ake, kuyankhula ndi iwo, kuyanjana ndi iwo. Ndipo tsopano tchimo ndi imfa zinali zitawalekanitsa iwoku Kukhalapo Kwake ndi chifotokozero chake chonse. Kodiinumukuwerengaizo? Asanaikidwemazikoadziko, kutiafotokozere Zake zonse_Zake_zikhumbo Zake, chimene Iyeanali.

Chotero, ngati Wautatu aliyense pano ngati mutangotimungodzisiya nokha momasuka miniti yokha, inu mukhozakuwona kuti Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera si Amulunguatatu. Ndi zikhumbo zitatu za Mulungu yemweyo. Mukuona, ndi zifotokozero. Atate, Iye anali, ankafuna kuti akhale Atate. Iye anali Atate, Iye anali Mwana, ndipo Iye ali Mzimu Woyera. Ndipo Atate ndi Mzimu Woyera ndi Mzimu womwewo. Kodiinu simukuwona? Inu mukumvetsa izi? Osati amulungu atatu. Adierekezianakuwuzani inu zinthu zimenezo, kuti akupangeni kukhalawopembedzamafano. Mukuona? Ndi Mulungu mmodziakufotokozeredwa mu zikhumbo zitatu. Kuti akhale Atate, kuti akhale Mpulumutsi, kuti akhale Mwana, kuti akhaleMchiritsi, mukuona, ndizo zifotokozero Zake.

Ine ndikufuna kuti ndiyende pang'ono pokha chotero kutingakhale anthu pomvetsera ku tepiyi adzakhoze kulimvalingalirolo, kuti angakhoze kuwona. Izo zikanati zinditengereine kuzungulira, zungulira koloko iyo, lirilonse la maphunziroawo lokha. Koma ine ndikuyembekeza kuti ndikuzipanga izokumveka mokwanira kuti inu mukhoza kuwona chimene inendiri kubwerapo. Mukuona?

Mulungu, anafotokozedwa mwa Yesu Khristu, Yemweanali zonse Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera, “chidzalo chaUmulungu mu thupi.” Tsopano “chidzalo chathunthu cha Umulungu mu thupi” chikukhala mu Mpingo Wake, uyambiriro. Zonse zimeneMulungu anali, Iye anazitsanulira mwa Khristu; ndipo zonseKhristu anali, zinatsanuliridwa mu Mpingo, okhulupirira. Osati chipembedzo! Ife tifika kwa izo mu maminitipang'ono, ndipo icho chichotsa izo mu malingaliro anukwanthawizonse, mukuona; kukusonyezani inu chimenechimayambitsa izo, mwa kuthandiza kwa Mulungu, ngati Iyeati angoziloleza izo kwa ife.

Cholinga Chake ndi chiyani tsopano? Kudzifotokoza Yekhangati Mwana, mukuona, ndipo, tsopano, kuti mwa Iyemukhoze kukhala “chidzalo cha Umulungu mwa thupi.” Ine, ine ndiri naye Akolose ali apa, patsogolo panga pomwe. Mukuona? Kuti, monse kudutsa Lemba, ndicho chimenecholinga cha Mulungu chinali. Ndiye, ndi kupyolera mu Moyouwu wa Mwana uyu, mtanda Wake, “Magazi,” iwo akuteroapa, “a mtanda Wake,” kuti Iye akhoze kuyanjanitsa kwaIyemwini Thupi, Mkwatibwi; yemwe ali Eva, Eva wachiwiri. Ndipo Mulungu anapereka izo mwa choyimira, monga Iyeanachitira ndi Mose ndi onse awo. Chinthu chomwechochimene Iye anachita mwa Adamu ndi Eva, kuperekachoyimira, kuti iwo anali Khristu ndi Mkwatibwi. Iye ndiyeAdamu wachiwiri; Mpingo ndiwo Eva wachiwiri.

Ndipo monse pamene Eva wachiwiri anyengerera natsutsaMawu, kodi iye sali kuchita chinthu chomwecho chimene Evawoyamba anachita? [Osonkhana ati, “Ameni.”_Mkonzi.] Kuyesera kuti aziti, “Chabwino, izo zinali za m'badwowinawake.” Ndipo ife tifika ku izo mu maminiti angapo, ngatiIye anati kuti izo zinali za m'badwo wina. Kodi izo zingakhozebwanji kukhala m'badwo wina, pamene Iye ali “yemweyodzulo, lero, ndi kwanthawizonse”? Koma Mulungu walinga izo ndipo “wazibisa izo kwa masoa luntha ndi anzeru, ndi waziwulula izo kwa makandaokonzedweratu” amene anakonzedweratu kuti azilandire izo.

Werengani akaunti yonse mu...
Khristu ndi chinsinsi cha Mulungu woululidwa.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Thupi ndi limodzi, ngakhale kuti lapangidwa ndi ziwalo zambiri. Ndipo ngakhale ziwalo zake zonse ndi zambiri, zimapanga thupi limodzi. Momwemonso ndi mmene alili Khristu.

Pakuti tonse tinabatizidwa ndi Mzimu mmodzi m'thupi limodzi. Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu tonse tinapatsidwa kuti timwe Mzimu mmodzi yemweyo.

1 Akorinto 12:12-13


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)


 


Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.