Mbewu ya Chisokonezo.

<< m'mbuyomu

lotsatira >>

  Nthawi yotsiriza mndandanda.

Mvula imagwera pa olungama ndi osalungama.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Mbewu ya Chisokonezo.

Ine ndinali ndiri kupemphera mu mphanga kumene ine ndimapita kukapemphera. Munachita fumbi mu mphangamo, ndipo madzulo ena ine ndinakayenda kunja, ndinayika Baibulo langa pa chipika, ndipo mphepo inakupizira pa Ilo motsegula ku Ahebri, mutu wa 6. Womwe unanena, kuti mu masiku otsiriza, momwe izo zikanati zidzakhalire ngati ife tikanagwa kuchoka ku Choonadi ndi kudzikonza mwatsopano kachiwiri mwa kulapa, pakanakhala popanda nsembe inanso ya tchimo, ndipo momwe kuti minga ndi nthula, zomwe zinali zoyandikira ku kukanidwa, zomwe mathero ake ziri zoti ziwotchedwe; koma mvula imabwera pa dziko lapansi, mowirikiza, kuti idzatsirire ilo, kudzaliveka ilo; koma minga ndi nthula zidzakanidwa, koma tirigu adzasonkhanitsidwa. Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, ndi mphepo chabe yachita kuti apo patseguke.” Chabwino, ine ndinangoyika Baibuloyo pansi kachiwiri. Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, tsopano ine basi...” Ndipo apa panabwera mphepo ndi kulikupiza Ilo motsegula. Zimenezo zinachitika nthawi zitatu. Ndipo ine ndinaganiza, “Chabwino, tsopano, izo nzachirendo.”

Ndiyeno pamene ine ndinaimirira, ndipo ine ndinaganiza, “Ambuye, chifukwa chiyani Inu munachita kunditsegulira ine Baibulo kuti ndiwerenge zimenezo, ine... pamene ine ndinafika pansi ku izo, pamene ‘minga ndi nthula, zomwe zinali zoyandikira kukukanidwa, zomwe mathero ake ziri zoti ziwotchedwe’?” Ine ndinaganiza, “Chifukwa chiyani Inu munatsegulira kwa ine pamenepo?” Ndipo poyang'ana kunja.

Tsopano, masomphenya enieni awa amabwera popanda kukokera mu giyara iliyonse. Ameneyo ndi Mulungu basi. Mwaona? Ine ndinayang'ana ndipo ine ndinawona dziko lapansi lomwe linali kuzungulira patsogolo pa ine, ndipo ine ndinawona ilo lonse linali litalimidwa. Pamenepo panali mwamuna atavala mu zoyera, anapita apo akufesa tirigu. Ndipo iye atatha kupita chozungulira kobisika kwa dziko lapansi; mozungulira anabwera mwamuna, wowoneka mowopsya, ndipo iye anali atavala zakuda, ndipo iye anali akuponya mbewu za udzu paliponse. Izo zonse zinamerera limodzi. Ndipo pamene izo zinatero, izo zonse zinali ndi ludzu, chifukwa mvula inali kusoweka. Ndipo mmodzi aliyense ankawoneka ngati anali akupemphera, ndi mutu wake wawung'ono utaweramitsidwa, “Ambuye, tumizani mvula, tumizani mvula.” Ndipo mitambo yayikulu inatulukira, ndipo mvula inavumba pa izo zonse. Pamene iyo inatero, tirigu wamng'ono analumpha moyima ndi kuyamba kunena, “Ambuye alemekezeke! Ambuye alemekezeke!” Ndipo maudzu aang'ono analumpha moyima ku mbali yomweyo, ndipo anati, “Ambuye alemekezeke! Ambuye alemekezeke!”

Ndiyeno masomphenyawo anatanthauziridwa. Mvula imagwera pa olungama ndi osalungama. Mzimu womwewo ukhoza kugwera mu msonkhano, ndipo aliyense nkumasangalala mwa iwo: achinyengo, Akhristu, ndi onse palimodzi. Chimodzimodzi molondola. Koma ndi chiyani icho? Ndi zipatso zawo iwo amadziwika. Mwaona? Ndiyo njira yokha yomwe izo zingakhoze konse kudziwidwira.

Ndiye inu mukuona kuti tsopano, pakuti mbeu zakuthengo, kapena tirigu wakuthengo ndi njere nthawi zina zimatsanzira yeniyeni, njere zowetedwa, mwapafupi kwambiri kuti izo zikanati zinyenge Osankhidwa omwe. Ine ndikuganiza ife tikukhala mu m'badwo wa nthawi yake, yomwe zinthu izi ziyenera kuti zizilalikidwamo ndi kuyankhulidwamo.

Zindikirani mu ndime 41, ziwirizo nazonso moyandikana kwambiri, moyandikana kwambiri mu masiku otsiriza mpaka Iye sanachite izo... Iye sakanakhoza kudalira pa mpingo winawake kuti ulekanitse izo, titi, wa Methodisti kapena wa Baptisti, kapena wa Pentekoste, kuti ulekanitse izo. Iye anati, “Iye akutumiza angelo Ake kuti adzazilekanitse izo.” Mngelo akubwera kuti abweretse kulekanitsako, kusankha pakati pa olondola ndi olakwika. Ndipo palibe mmodzi angakhoze kuchita zimenezo koma Mngelo wa Ambuye. Iye ali Mmodzi yemwe ati adzadziwe chomwe chiri cholondola ndi chomwe chiri cholakwika. Mulungu anati Iye adzatuma angelo Ake pa nthawi zotsiriza. Osati angelo kutsika kupyola pano, koma angelo pa nthawi yotsiriza, ndipo adzasonkhanitsa pamodzi. Ife tikudziwa kuti uku ndiko kubwera kwa nthawi yokolola tsopano. Tsopano, mngelo ali makamaka kutanthauza “mtumiki.” Ndipo ife tikuwona kuti pali angelo asanu ndi awiri a mipingo isanu ndi iwiri, ndipo tsopano^ayi, kupyola mibadwo ya mpingo.

Zindikirani yemwe Iye anati ofesa anali, ndiponso chomwe mbewu inali. Mmodzi, wofesayo anali Iye, Mwana wa Mulungu, yemwe anapita uko akufesa Mbewu. Ndipo mdani anabwera mmbuyo Mwake, yemwe anali Mdierekezi, ndipo anafesa mbewu ya chisokonezo, mmbuyo mwa kufesa kwa Mbewu zabwino. Tsopano, amzanga, izo zachitika kupyola m'badwo uliwonse chikhalireni nalo dziko. Chimodzimodzi. Njira yonse kuchokera ku chiyambi, izo zinayamba chinthu chomwecho.

----
Ife tikuzindikira kuti wofesa woyamba wa mbewu ya chisokonezo anatchedwa “Mdierekezi,” ndipo ife tikudziwa izo zinali, mu Genesis 1. Tsopano ife tikupeza, ndipo cha apa mu Bukhu la Mateyu, mutu wa 13, Yesu akutcha chisokonezo chirichonse kwa Mawu Ake ngati kukhala “Mdierekezi.”Ndipo 1956 uyu, chirichonse chimene chikufesa chisokonezo, mosiyana ndi Mawu olembedwa a Mulungu, kapena kuyika kutanthauzira kulikonse kwa mseri kwa Iwo, ndiyo mbewu ya chisokonezo. Mulungu sadzalemekeza icho. Iye sangakhoze. Izo sizingasakanizikane. Izo sizidzatero ndithudi. Izo ziri ngati mbewu ya mpiru; iyo siyingasakanizikane ndi china chirichonse, iwe sungakhoze kuyisakaniza iyo, iyo iyenera kuti ikhale chinthu chenicheni. Mbewu ya chisokonezo!

Tsopano ife tikupeza, pamene Mulungu anafesa Mbewu Yake mu Munda wa Edeni, ife tikupeza kuti iyo inabala Abele. Koma pamene Satana anafesa mbewu yake ya chisokonezo, iyo inabala Kaini. Wina anabala mmodzi wolungama; wina anabala mmodzi wosalungama. Chifukwa kuti Eva anamvetsera ku mawu a chisokonezo, osiyana ndi Mawu a Mulungu, ndipo izo zinayambitsa mpira wa tchimo kugudubuzika apo pomwe, ndipo wagudubuzika chiyambireni. Ndipo ife sitidzatha kuzichotsa izo zonse mpaka angelo atabwera ndi kudzasiyanitsa chinthucho, ndipo Mulungu nawatenga ana Ake kumka ku Ufumu, ndipo namsongole adzawotchedwa. Zindikirani nthambi ziwiri izo.

Zindikirani, mbewu zawo zinakula limodzi chimodzimodzi basi monga Mulungu ananena cha apa naponso mu mutu wa 13, powerenga pathu usikuuno, wa Mateyu, “Zisiyeni izo zikulire limodzi.” Tsopano, Kaini anapita ku dziko la Nodi, anakadzipezera yekha mkazi, ndipo anamukwatira; ndipo Abele anaphedwa, ndipo Mulungu anawutsa Seti kuti atenge malo ake. Ndipo mibadwo inayamba kumasuntha mopitirira, pakati pa abwino ndi oyipa. Tsopano, ife tikuzindikira iwo ankasonkhana, mmodzi aliyense wa iwo, nthawi ndi nthawi, ndipo Mulungu anachita ku... Izo zinafika pauthakati kwambiri mpaka Mulungu anachita kuziwononga izo.

Koma izo potsiriza zinatulukira mpaka zonse za mbewu zimenezo, mbewu ya chisokonezo ndi Mbewu ya Mulungu, zinatulutsa mitu yake yeniyeni, ndipo izo zinadzathera mwa Yudasi Iskarioti ndi mwa Yesu Khristu. Pakuti, Iye anali Mbewu ya Mulungu, Iye anali chiyambi cha chirengedwe cha Mulungu, Iye sanali chinthu chotsika kuposa Mulungu. Ndipo Yudasi Iskarioti anabadwa ali mwana wachitayiko, anabwera kuchokera ku gehena, anabwerera ku gehena. Yesu Khristu anali Mwana wa Mulungu, Mawu a Mulungu atachita kuwonetseredwa. Yudasi Iskarioti, mu chisokonezo chake, anali mbewu ya Mdierekezi, kubwera ku dziko, ndipo kuti adzanyenge; basi monga iye analiri pachiyambi, Kaini, abambo ake akalelo.

Yudasi anali kungosewera zampingo. Iye sanali wodzipereka kwenikweni, iye analibe kwenikweni chikhulupiriro (iye sibwenzi atamupereka Yesu). Koma, inu mukuona, iye anafesa mbewu ija ya chisokonezo. Iye ankaganiza kuti iye akadakhoza kupanga ubwanawe ndi dziko, mammon, ndiponso kukhala nawo ubwenzi ndi Yesu, koma nthawi inali itatha kwambiri kuti iye achite chirichonse za izo. Pamene ora lotsiriza linafika, pamene iye anachita chinthu choyipa ichi, iye anawoloka mzere wolekanitsa pakati pa kupita kutsogolo ndi kubwerera mmbuyo. Iye ankayenera kuti azipita patsogolo mu njira yomwe iye ankapita, monga wonyenga. Iye anafesa mbewu ya chisokonezo, iye anayesa kuti apeze kukondedwa ndi mabungwe akulu amenewo a tsiku limenelo, ndi Afarisi ndi Asaduki. Ndipo ankaganiza kuti akanadzipangira yekha gawo la ndalama, ndipo nkukhala wotchuka pakati pa anthu. Ngati izo sizimawapangitsa anthu ambiri kufika mu chisokonezo chimenecho, kuyesa kuti apeze kukondedwa ndi anthu! Tiyeni tipeze kukondedwa ndi Mulungu, osati ndi munthu. Koma ndicho chimene Yudasi anachita pamene zisokonezo izi zinakula mwa iye.

Ndipo ife tikudziwa kuti Yesu anali Mawu, Yohane Woyera 1, anati, “Pa chiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu. Ndipo Mawu anapangidwa thupi ndipo anakhala kuno pakati pathu.” Ndiye, Mawu ndiwo Mbewu, ndiye Mbewu inakhala mnofu ndipo linakhala pakati pathu.

Ngati Yudasi anali mbewu ya mdani ndi chisokonezo, iyo nayonso inakhala mnofu ndipo inakhala pakati pathu mwa munthu wa Yudasi Iskarioti. Iye analibe konse chenicheni, chikhulupiriro chenicheni. Iye anali nacho chimene iye ankaganiza kuti chinali chikhulupiriro. Chiripo chinthu chotero monga kukhala nacho chikhulupiriro; ndi chikhulupiriro chodzipangitsa kukhulupirira. Ndipo chikhulupiriro chenicheni cha Mulungu chidzakhulupirira mwa Mulungu, ndipo Mulungu ndiye Mawu, icho sichidzawonjezera konse kanthu kwa Iwo. Baibulo limatiuza ife kuti ngati ife tiwonjezera mawu amodzi, kapena kuchotsapo Mawu amodzi, gawo lathu lidzachotsedwa ku Bukhu la Moyo, Chivumbulutso 22:18, mutu wotsiriza wotseka.

Mu chiyambi choyamba, Bukhu loyamba la Baibulo, Mulungu anawauza iwo kuti asaswe Mawu amodzi a Ilo, “Mawu aliwonse ayenera kusungidwa,” iwo ayenera kumakhala moyo mwa Mawu amenewo. Yesu, mkati mwa Bukhu, anabwera motsatira ndipo anadzanena izo mu m'badwo Wake, ndipo anati, “Munthu sadzakhala moyo ndi mkate wokha, koma ndi Mawu onse omwe_omwe atuluka kuchokera mkamwa mwa Mulungu.” Ndipo mu m'badwo wotsekera wa Chivumbulutso, zinaloseredwa kwa ife, kuti “Yense yemwe ati adzachotse Mawu amodzi kuchokera m'Bukhu, kapena kuwonjezera mawu amodzi kwa Ilo, gawo lake lidzachotsedwa kuchokera m'Bukhu la Moyo.”

Chotero apo sipangakhoze kukhala kanthu mwamthunzi, Mawu a Mulungu enieni okha, osakhudzidwa basi! Ndiwo ana a amuna a Mulungu, ana aakazi a Mulungu, omwe sali obadwa mwa chifuniro cha munthu, kapena mwa kugwedeza kwa dzanja, kapena mtundu wina wa ubatizo; koma kubadwa mu Mzimu wa Mulungu, mwa Mzimu Woyera, ndipo Mawu akudziwonetsera Okha kupyolera mwa iwo. Ndiyo Mbewu yeniyeni ya Mulungu!

Mdani amajowina mpingo ndipo amakhala wachi orthodox kwambiri mu kachikhulupiriro kapena chinachake. Koma sindizo ayi... Ndicho chisokonezo, chirichonse chomwe chimasokonezana ndi mphamvu ya Choonadi chenicheni cha Mawu a Mulungu.

Ndipo ife timadziwa bwanji? Ife tikuti, “Chabwino, iwo, inu muli nawo ufulu woti muziwatanthauzira Iwo?” Ayi, bwana! Palibe munthu yemwe ali nawo ufulu kuti azitanthauzira Mawu a Mulungu. Iye ali wodzitanthauzira Yekha. Iye amalonjeza izo, ndiye Iye amazichita izo, ndiko kutanthauzira kwake. Pamene Iye analonjeza Izo, ndiye Iye amazikwaniritsa Izo, ndiko kutanthauzira kwa Iwo. Chirichonse chosiyana kwa Mawu a Mulungu chiri chisokonezo! Mwamtheradi!

Tsopano, monga ine ndanena, Yudasi analibe chikhulupiriro chenicheni. Iye anali nacho chikhulupiriro chodzipangitsa kukhulupirira. Iye anali ndi_ndi chikhulupiriro chimene iye ankaganiza kuti uyo anali Mwana wa Mulungu, koma iye sanali kudziwa kuti ameneyo anali Mwana wa Mulungu. Iye sibwenzi atachita izo. Ndipo munthu yemwe ati adzanyengerere pa Mawu a Mulungu awa kukhala Choonadi, iye ali nacho chikhulupiriro chodzipangitsa kukhulupirira. Wantchito weniweni wa Mulungu adzakanirira pa Mawu amenewo.

Werengani akaunti yonse mu...
Mbewu ya Chisokonezo.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Nthaka yolandira mvula kawirikawiri n’kubala mbewu zopindulitsa oyilima, Mulungu amayidalitsa.

Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa m’moto.

Ahebri 6:7-8


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Marriage and Divorce.

(PDF Chingerezi)

Mbiri ya moyo wanga.

(PDF)

Momwe ngelo anadzera
kwa ine olalikidwa ndi.

(PDF)




Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.