Mzimu Woyera unali chiyani?.

<< m’mbuyomu

lotsatira >>

  Mndandanda kulandiridwa.

Ndiwo chisindikizo chanu.


William Branham.

Werengani akaunti yonse mu...
Mzimu Woyera unali chiyani?.

Tsopano, ine ndafunsa kachisi uyu... Tsopano, ife sitiri kulowa mu izi mwa msonkhano wankhoka chabe. Ine ndikufuna kuti ndilowe mu izi, ndipo ine ndikufuna inu, ndipo ndakupemphani inu, kuti muwotche mlatho uliwonse umene uli kumbuyo kwanu, ndi kukonza tchimo lirilonse, kuti ife tikubwera mu ichi ndi zonse zomwe ziri mu mitima yathu ndi miyoyo. Ife tiyenera kubwera muno mwa cholinga chokhacho cha kuifikitsa miyoyo yathu mokonzekera Kudza kwa Ambuye, ndipo mosakhala kwa cholinga china. Ndipo monga ine ndayankhula ndi kunena, kuti mwinamwake nthawiyina ine mwina ndingaphunzitse kapena kunena chinachake chomwe chingakhale chosiyana pang'ono ku chomwe winawake, momwe iwo ankakhulupirira icho. Ine sikuti ndabwerera mtsutsano, inu mukuona, ine ndabwera... Ife tiri pano kuti tikonzekere Kudza kwa Ambuye.

-----
Pa malo awa, ife tikukhumba kuti tiyandikire phunziro, limene ine ndikuganiza liri phunziro lopambana la lero, la... Kodi Mzimu Woyera Ndi Chiyani? Kodi Iwo ndi chiyani? Ndipo, tsopano, chifukwa chimene ine ndatengera phunziro ili mu mzere monga chonchi, iwe sungakhoze kubwera ndi kulandira Mzimu Woyera kupatula iwe utadziwa chimene Iwo uli. Ndipo iwe sungakhoze kuwulandira Iwo, ngati iwe ukudziwa chimene Iwo uli, kupatula iwe ukhulupirire Iwo waperekedwa kwa iwe, ndipo Iwo ndi wa iwe. Ndipo, ndiye, iwe sungakhoze kudziwa ngati iwe uli nawo Iwo, kapena ayi, kupatula iwe ukadziwa zotsatira zomwe Iwo umabweretsa. Kotero ngati iwe udziwa chimene Iwo uli, ndi kuti Iwo ndi wa kwa ndani, ndi machitidwe omwe Iwo umabweretsa pamene Iwo ubwera, ndiye iwe udzadziwa chimene iwe uli nacho pamene iwe uwulandira Iwo. Mwaona? Icho chingakhazikitse basi zimenezo.

Tsopano, pali kusiyana kwakukulu pakati pa Mkhristu chabe ndi Mkhristu wodzazidwa-Mzimu-Woyera. Ndipo tsopano ife tati tizipeze izi kuchokera mu Lemba, ndi kuzikhazikitsa izo chimodzimodzi basi mu Lemba. Malo oyamba, alipo Mkhristu odzitcha kuti ali Mkhristu. Koma ngati Mkhristu uyu sali atadzazidwa apabe ndi Mzimu Woyera, iye ali chabe mu dongosolo lakuti akhale Mkhristu. Mwaona? Iye akudzinenera kuti akuukhulupirira Iwo; iye akugwirira ntchito kumka ku Iwo, koma Mulungu sanamupatse iye apabe Mzimu uwu, wa Mzimu Woyera. Iye sanafike apabe malo amenewo ndi Mulungu, kuti Mulungu akuzindikira izo.

-----
Mdulidwe uli choyimira cha Mzimu Woyera. Ndipo Mulungu anamupatsa Abrahamu... chizindikiro cha mdulidwe iye atamulandira kale Mulungu pa lonjezo Lake ndi kuyenda kupita mu dziko lachirendo. Mwaona? Icho chinali chizindikiro. Ndipo ana ake onse, ndi mbewu yake pambuyo pake, imayenera kukhala nacho chizindikiro ichi mu mnofu wawo, chifukwa icho chinali chowasiyanitsa. Icho chinali choti chiwalekanitse iwo kuchokera kwa anthu ena onse, chizindikiro ichi cha mdulidwe. Ndipo ndicho chimene Mulungu akugwiritsa ntchito lero. Ndi chizindikiro cha mdulidwe wa mtima, Mzimu Woyera, umene ukupangitsa Mpingo wa Mulungu Mpingo wolekanitsidwa kuchokera ku zikhulupiriro zina zonse, zikhulupiriro ndi zipembedzo. Iwo ali mu mitundu yonse ya zipembedzo, komabe iwo ndi anthu opatulidwa.

-----
Iwe ndiwe wosiyana kwambiri pamene Mzimu Woyera ubwera pa iwe, mpaka malingaliro a dziko lino samakukonda iwe, ndipo iwo amatsutsana nawe iwe, ndipo iwo samafuna kalikonse koti azichita ndi iwe, nkomwe. Ndiwe wobadwira mu Dziko lina. Iwe ndiwe mochuluka basi monga mlendo, nthawi khumi mlendo mochuluka momwe iwe ukanakhalira, ngati iwe ukanapita mu zigawo zikutali za nkhalango za Afrika. Iwe umakhala wosiyana pamene Mzimu Woyera ubwera, ndipo Ndiwo chizindikiro. Ndiwo chilemba pakati pa anthu. Tsopano, inu mukuti, “Ndiye, M'bale Branham, chizindikiro chija cha mdulidwe chinaperekedwa kwa Abrahamu?” Izo nzoona. “Ndi kwa Mbewu yake?” Inde.

-----
Tsopano, Aefeso 4:30 akuwerengeka monga chonchi:
Ndipo musakwiyitse ayi Mzimu woyera wa Mulungu, umene inu munasindikizidwa nawo kufikira tsiku la chiwombolo.
Ine ndichita kutenga molimba pang'ono pa izi tsopano, kuyala pansi. Tsopano, inu abale mwamalamulo ingokhalani chete kwa pang'ono pokha. Mwaona? Kodi inu munazindikira utali womwe chisindikizo chimenecho chimathera? Osati mpaka ku chitsitsimutso chotsatira, mpaka nthawi yotsatira pamene chinachake chichitike molakwika. “Mpaka tsiku la chiwombolo chako,” ndiwo utali womwe iwe umasindikizidwira. “Mpaka tsiku la chiwombolo chako,” pamene iwe uli woomboledwa kuti ukakhale ndi Mulungu, ndiwo utali womwe Mzimu Woyera umakusindikizira iwe. Osati kuchokera ku chitsitsimutso kukafika ku chitsitsimutso; koma kuchokera ku Muyaya mpaka ku Muyaya, iwe uli wosindikizidwa ndi Mzimu Woyera. Ndicho chimene Mzimu Woyera uli, Iwo ndi chisindikizo cha Mulungu, kuti Iye wapeza^iwe wapeza chisomo pamaso Pake, ndipo Iye akukukonda iwe, ndipo Iye akukukhulupirira iwe, ndipo Iye wayika chisindikizo Chake pa iwe. Kodi chisindikizo ndi chiyani, aliyense? Bwanji, chisindikizo chimakhazikitsa kapena chimatanthawuza “ntchito yotsirizidwa.” Ameni. Mulungu wakupulumutsa iwe, wakuyeretsa iwe, wakutsuka iwe, wapeza chifundo ndi iwe, ndipo wakusindikiza iwe. Iye watsirizitsa. Ndiwe chotuluka mwa Iye Chake mpaka tsiku la chiwombolo chako. Chosindikizidwa ndi “chinthu chotsirizidwa.” Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani? Iwo ndi chizindikiro. Ife tifika pa zimenezo kanthawi kena, mu Uthenga wina, chizindikiro chimene Paulo anachikamba. Malirime anali chizindikiro kwa okhulupirira... kapena osakhulupirira.

Tsopano zindikirani, koma, mu ichi, Mzimu Woyera ndi chizindikiro.... Ine ndikutanthauza,Ndipo Mzimu Woyera ndiwo chisindikizo. Iwo ndi chizindikiro chimene Mulungu anapereka kwa ana Ake osankhidwa. Kuwukana Iwo, ndi kuti udulidwe kuchoka kwa anthuwo; ndipo kuwulandira Iwo, ndi kukhala utatsirizana nalo dziko ndi zinthu zonse za mdziko, ndi kukhala chinthu chomwe Mulungu wayikapo chisindikizo cha kuvomereza.

Ine kale ndinkagwira ntchito ku njanji kunja kuno ku Harry Waterberry, ndipo ife tinkakhoza kupita kumusi kuti tikalongeze magalimoto. M'bale wanga, Doc, wayima kumbuyo ukoyo, amathandizira kulongeza magalimoto. Pamene galimoto ikulongezedwa, iwo amapita modutsa galimoto imeneyo, wofufuza, ndipo ngati iye apeza chirichonse chogwedera, pamene iyo ingakhoze kugwa ndi kusweka, kapena chirichonse chimene chikanakhoza kuwononga; iye sakanati ayisindikize galimoto imeneyo mpaka galimoto imeneyo ili yolongezedwa kwathunthu, mpaka iyo ili yolongezedwa chotero pansi ndi mwa dongosolo chotero, kuti kugwedera kwa kukwera sikuti kuvutitse zinthu zimene ziri mkatimo.

Ndilo lomwe liri vuto kuti ife sitimakhala osindikizidwa kwambiri chotero; ndife ogwedera kwambiri nazo zinthu. Pamene Wofufuza akupita chodutsa, kuti afufuze moyo wanu, kuti awone ngati inu simuli ogwedera pang'ono chabe nazo zinthu, wogwedera pang'ono nawo moyo wanu wa pemphero, wogwedera pang'ono nako kupsya mtima kuja, wogwedera pang'ono nalo lirime limenelo, poyankhula za ena, Iye sadzaisindikiza konse galimoto imeneyo. Zizolowezi zina zoyipa, zinthu zina zauthakati, malingaliro ena auve, Iye sangakhoze kuisindikiza galimotoyo. Koma pamene Iye achipeza chirichonse mu malo ake, Wofufuza, ndiye Iye amayisindikiza iyo. Asayese wina kuyerekeza kuchitsegula chisindikizo chimenecho mpaka galimoto imeneyo itafika kumene iyo ikupita kumene iyo yasindikiziridwira! Ndi imeneyo apo. “Musati mukhudze wodzozedwa Wanga; musawachitire aneneri Anga chowapweteka ayi. Pakuti ine ndikuti kwa inu, izo zikanakhala bwino kwa inu kuti mphero ikanati imangidwe pa khosi panu, ndipo inu mukanati muponyedwe mwa kuya kwa nyanja, kuposa ngakhale kuti inu muyesere kukwiyitsa kapena kugwedeza pang'ono pa aang'ono a awa omwe akhala atasindikizidwa.” Kodi inu mukuona chimene icho chikutanthauza?

Ndicho chimene Mzimu Woyera uli. Ndiwo chitsimikiziro chanu. Ndiwo chitetezero chanu. Ndiwo umboni wanu. Ndiwo chisindikizo chanu. Ndiwo chizindikiro chanu, kuti, “Ndine womka Kumwamba. Mopanda kusamala zimene mdierekezi akunena! Ndine womka Kumwamba. Chifukwa chiyani? Iye anandisindikiza ine. Iye anawupereka Iwo kwa ine. Iye anandisindikizira ine kulowa mu Ufumu Wake, ndipo ndine Womka-kuulemerero! Lekani mphepo iwombe, lekani Satana achite zimene iye akufuna kuchita. Mulungu wandisindikiza kale ine mpaka tsiku la chiwombolo changa.” Ameni! Ndicho chimene Mzimu Woyera uli. O, inu muyenera kumawufuna Iwo. Ine sindikanakhoza kumapitirirabe wopanda Iwo. Zochuluka kwambiri zikanakhoza kunenedwa pamenepo, koma ine ndikutsimikiza inu mukudziwa chimene ine ndikuchikamba.

Tsopano, ndiponso, tiyeni ife titembenuzire ku Yohane 14, kwa miniti chabe. Ine ndimangowakonda Mawu! Ndiwo Choonadi. Tsopano, Mzimu wa Mulungu, Mzimu Woyera, kodi Mzimu Woyera ndi chiyani? Iwo ndiwo Mzimu wa Khristu mwa inu. Tsopano, ife tisanati tiwerenge, ine ndikanafuna kuti ndinene mawu pang'ono ochitira ndemanga apa. Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani? Iwo ndi chisindikizo. Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani? Iwo ndi pangano. Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani? Iwo ndi chizindikiro. Kodi Mzimu Woyera ndi chiyani ndiye? Ndiwo...Mzimu wa Yesu Khristu mwa iwe. Mwaona? “Kanthawi pang'ono,” anatero Yesu, “ndipo dziko silindiwonanso Ine; komabe inu mudzandiwona Ine, pakuti Ine ndidzakhala ndiri ndi inu, ngakhale mkati mwa inu, mpaka ku mapeto a dziko.”

Mzimu wa Mulungu mu Mpingo Wake! Wa chiyani? Kodi Iye anachitiranji izo? Izi ndi pang'ono za phunziro la mawa usiku. Koma kodi Iye anachitiranji izo? Nchifukwa chiyani Iye anachita, nchifukwa chiyani Mzimu Woyera... Chiyani, kodi Iye anadzera chiyani? Kodi Iye anabwereranji mkati mwa inu, kodi Iye anabwereranji mkati mwa ine? Zinali kuti adzapitirize ntchito za Mulungu.

“Ine nthawizonse ndimachita izo zimene ziri zokondweretsa kwa Atate Anga. Ine sindinabwere kuti ndidzachite chifuniro Changa changa, koma cha Atate omwe anandituma Ine. Ndipo Atate amene anandituma Ine ali ndi Ine; ndipo monga Atate Anga andituma Ine, chotero Ine ndikukutumani inu.” O, mai! Atate anamutuma Iye, anapita mkati mwa Iye. Atate omwe anamutuma Yesu anabwera mkati mwa Iye, ankagwirira ntchito kupyolera mwa Iye. Yesu amene amakutumani inu, amapita ndi inu ndipo ali mkati mwa inu. Ndipo ngati Mzimu umenewo, wokhala moyo mwa Yesu Khristu, unamupanga Iye kupanga ndi kumachita momwe Iye ankachitira, inu mukhala nalo lingaliro lina wamba momwe Iwo uti uzichitira pamene Iwo uli mkati mwa inu, chifukwa Moyo umenewo sungakhoze kusintha. Iwo uzipita kuchokera mu thupi kupita ku thupi, koma Iwo sungakhoze kusintha chikhalidwe Chake, pakuti Iwo ndiwo Mulungu.

-----
Tsopano ife tati tifunse tsopano... Analonjeza kwa ife mu masiku otsiriza! Woyimira mulandu uyu, chisindikizo, lonjezo, chirichonse chimene ife takamba zokhudza Iye usikuuno, ndi zikwi khumi kuchulukitsa zoonjezerapo, Iwo unapangidwa lonjezo kwa ife mu tsiku lotsiriza. Iwo analibe Iwo mu tsiku limenelo. Iwo anangokhala ndi chisindikizo mu mnofu wawo, monga chizindikiro ndi chisonyezo, kukhulupirira kuti Iwo unali kudza, ndipo iwo ankayenda mwa mthunzi wa lamulo. Chimene, iwo ankadulidwa mu mnofu.

Lero ife sikuti timayenda mwa mthunzi wa lamulo. Ife timayenda mwa mphamvu ya chiwukitsiro. Ife tikuyenda mwa mphamvu ya Mzimu, Umene uli chisindikizo chathu choona, Wotiyimira mulandu wathu woona, Mtonthozi wathu woona, chizindikiro chathu choona kuti ife tabadwa kuchokera Kumwamba; achilendo, anthu osamvetseka, ochita moseketsa, omutenga Mulungu pa Mawu Ake, kuchitcha china chirichonse cholakwika. Mawu a Mulungu ndi owona. Ndizo... O, mai! Ndicho chimene Mzimu Woyera uli.

-----
Tsopano, tsopano ife tati tipeze, iwo atadzazidwa kaye, iwo anasindikizidwa kufikira motalika bwanji? Ndi angati muno ali nawo Mzimu Woyera? Tiyeni tiwone manja anu. Alipo ambiri omwe ali nawo Mzimu Woyera kuposa omwe alipo opanda. Ife tikufuna inu kuti mukhale amodzi a ife, m'bale, mlongo. Pamene inu mumvetsa chimene Iwo uli, Iwo ndi Mzimu wa Mulungu ukukhala mwa inu, kuti uzichita ntchito za Mulungu. Pamene Mulungu atumiza konse uliwonse wa Mzimu Wake mwa aliyense wa antchito Ake, aliyense wa aneneri Ake, aliyense wa aphunzitsi Ake, aliyense wa atumwi Ake, iwo anali nthawizonse okanidwa ndi dziko. Iwo ankayesedwa openga, mu m'badwo uliwonse umene iwo analimo. Ngakhale pamene Paulo anayima pamaso pa Agrippa, iye anati, “Mu njira yomwe izo zikutchedwa zosokonezeka...” Kodi chosokonezeka ndi chiyani? “Kupenga.” “Mu njira yomwe iwo amaitcha zopenga, gulu la zitsiru, ndi momwe ine ndimapembedzera Mulungu wa Makolo athu.” [M'bale Branham akuwombetsa manja ake palimodzi kamodzi_Mkonzi.] Ine ndine wokondwa kwambiri kuti ine ndingakhoze kunena kuti ndine mmodzi wa iwo. Inde, bwana. Ndiko kulondola. Ine ndine wokondwa kwambiri kuti ine ndingakhoze kunena kuti ndine mmodzi wa iwo.

Tsopano, zitachitika izi Mzimu Woyera utagwera pa iwo, Iwo unawapangitsa iwo amitima yokoma kwambiri kufikira chirichonse chinali cha limodzi. Ndi kulondola uko? Mai, mai, ndi chiyanjano bwanji! Ife timayimba nyimbo imeneyo nthawizina, “O, ndi chiyanjano bwanji! O, ndi chisangalalo Chauzimu bwanji!” Ndi chimenecho. Iwo sanali kusamala, iwo sanali kusamala kaya... dzuwa liwala kapena siliwala. Iwo sanali kupempha kama wamaluwa a zofewa. “Tsopano, ine ndilandira Mzimu Woyera,” amatero anthu ena kwa ine, “Bambo Branham, ngati inu muti mundipatse ine chitsimikizo kuti ine ndikhala wamamilioni, ngati inu muti mundipatse ine chitsimikizo kuti ndipeza zitsime za mafuta, ndipo ine ndipeza migodi ya golide, ndipo ine....” Mwaona, anthu amaphunzitsa zimenezo, ndipo iwo amaphunzitsa bodza. Mulungu sanalonjeze zinthu zimenezo.

Munthu yemwe amalandira konse Mzimu Woyera samasamala kaya iye azipempha mkate, kapena ayi. Sizimapanga kusiyana kulikonse kwa iye. Iye ndi cholengedwa chomka-Kumwamba. Iye sasamala... Iye alibe zingwe kuno, nkomwe. Ndiko kulondola. Iye samasamala. Siyani zibwere, siyani zipite, kaya chiyani. Asiyeni iwo azitsutsa, kukhala akunyodola. Kutaya kutchuka kwanu, inu mukusamala chiyani? Inu muli pa ulendo wanu waku Ulemerero! Aleluya! Maso anu akhazikika pa Khristu, ndipo inu muli pa msewu wanu. Inu simukusamala chimene dziko likunena. Ndi chimene Mzimu Woyera uli. Ndiwo Mphamvu, Ndiwo chisindikizo, Ndiwo Mtonthozi, Ndiwo Woyimira mulandu, Ndiwo chizindikiro. O, mai! Ndiwo chitsimikizo chakuti Mulungu wakulandirani inu.

Ndi nthawi yochuluka chotani yomwe ine ndatenga? Ine ndatsala ndi maminiti asanu ndi atatu okha owonjezera. Chabwino. Ndiri ndi malemba ambiri pano. Ine sindikuganiza kuti ndingakhoze kuwatengera iwo mkati, koma ife tiyesa mwakukhoza kwathu. Tsopano, munthu atadzazidwa kaye ndi Mzimu Woyera, kodi nkotheka kuti mazunzo ndi zinthu zingati zimupangitse iye kuti abwerere mmbuyo ndi^Tsopano, iye sataya, iye akadali mwana wamwamuna wa Mulungu, iye adzakhala nthawizonse ali, chifukwa iwe wasindikizidwa motalika chotani? [Osonkhana akuti, “Kufikira tsiku la chiwombolo.”] Ndiko kulondola. Ndicho chimene Baibulo linanena.

Werengani akaunti yonse mu...
Mzimu Woyera unali chiyani?.


Chinsinsi cha Khristu.

Chingerezi Kalatayi
webusaiti.

Buku la
Chivumbulutso.

Mulungu ndi Sayansi
Index. - Archaeology.

Mkwatulo ukubwera.

Nkhani yabwino. Yesu
adafera machimo ako.

Ubatizo wamadzi.

 

Mtambo wauzimu.

Lawi la Moto.

Kuyenda kwa
Chikristu.

Mulungu ndi mbiriyakale
mndandanda Index.

M'mandamo mulibe.
Iye ali wamoyo.

Wamoyo Mawu
mndandanda.

Nthawi yotsiriza
mndandanda.

Mibadwo isanu ndi
iwiri ya mpingo.

Mndandanda wathu wa
uthenga.

Chingalawa cha Nowa.

Zisindikizo Zisanu
ndi ziwiri.

Dzina la Mulungu.

Tchimo loyambirira.
Kodi awa anali apulo?

Archaeology.
Sodomu ndi Gomora.

Mndandanda
Khrisimasi.

  Lemba linena...

Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.

Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu.

Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu.

Yohane 14:16-18


Dinani pa chithunzi tsitsani chachikulu chithunzi kapena PDF.


Acts of the Prophet

(PDF Chingerezi)

Chapter 11
- The Cloud

(PDF Chingerezi)

Lawi la Moto.

Mtambo wauzimu.

Ife tiyenera
kubwera muno mwa
cholinga chokhacho
cha kuifikitsa
miyoyo yathu
mokonzekera Kudza
kwa Ambuye.



Uthenga Hub... Sankhani chilankhulo chanu ndikutsitsa mauthenga aulere ochokera kwa M'bale Branham.